Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 27

“Musamadziganizile Kuposa Mmene Muyenela Kudziganizila”

“Musamadziganizile Kuposa Mmene Muyenela Kudziganizila”

“Ndikuuza aliyense wa inu kumeneko kuti musamadziganizile kuposa mmene muyenela kudziganizila. Koma aliyense aziganiza m’njila yakuti akhale munthu woganiza bwino.”—AROMA 12:3.

NYIMBO 130 Khalani Wokhululuka

ZIMENE TIKAMBILANE *

1. Malinga na Afilipi 2:3, kodi kudzicepetsa kumatithandiza bwanji kukhala pa ubale wabwino na ena?

TIMAMVELA Yehova modzicepetsa cifukwa timadziŵa kuti nthawi zonse iye ndiye amadziŵa zimene zili zabwino kwa ife. (Aef. 4:22-24) Kudzicepetsa kumatisonkhezela kuika cifunilo ca Yehova patsogolo osati zofuna zathu. Kumatisonkhezelanso kuona ena kukhala otiposa. Ndipo zotsatilapo zake n’zakuti timakhala pa ubale wabwino na Yehova komanso na okhulupilila anzathu.—Ŵelengani Afilipi 2:3.

2. Kodi Paulo sanatanthauze ciani pokamba kuti ‘tisamadziganizile kuposa mmene tiyenela kudziganizila’? Kodi tikambilana ciani m’nkhani ino?

2 Komabe, ngati sitingasamale tingayambe kutengela makhalidwe a anthu a m’dzikoli, omwe ni odzikuza komanso odzikonda. * Cioneka kuti izi n’zimene zinacitika kwa Akhristu ena m’nthawi ya atumwi, cifukwa mtumwi Paulo analembela Akhristu a ku Roma kuti: “Ndikuuza aliyense wa inu kumeneko kuti musamadziganizile kuposa mmene muyenela kudziganizila. Koma aliyense aziganiza m’njila yakuti akhale munthu woganiza bwino.” (Aroma 12:3) Apa Paulo sanatanthauze kuti tizidziona kuti ndife osafunika. Koma anatanthauza kuti tiyenela kukhala odzicepetsa. Kudzicepetsa kumatithandiza kuti tizidziona moyenela. M’nkhani ino, tikambilana mbali zitatu zokhudza umoyo wathu, ndipo pa mbali zimenezi, tiona mmene kudzicepetsa kungatithandizile kupewa kudziona ofunika kwambili kuposa ena. Mbali zimenezi ni (1) cikwati cathu, (2) maudindo amene tingakhale nawo m’gulu la Yehova, komanso (3) kuseŵenzetsa malo ocezela pa intaneti.

ONETSANI KUDZICEPETSA M’CIKWATI

3. N’cifukwa ciani n’zosadabwitsa anthu kukangana m’banja? Nanga ena amacita ciani pofuna kuthetsa mavutowo?

3 Yehova anayambitsa cikwati n’colinga cakuti mwamuna na mkazi azikhala osangalala. Koma cifukwa ca kupanda ungwilo, n’zodziŵikilatu kuti iwo sangagwilizane pa zinthu zina. Ndipo ngakhale mtumwi Paulo anakamba kuti okwatilana adzakhala ndi nsautso. (1 Akor. 7:28) Ena amangokhalila kukangana na mnzawo wa m’cikwati, ndipo angafike poganiza kuti si woyenelelana. Ngati okwatilana amayendela nzelu za dziko, amathamangila kukhala na maganizo akuti kusudzulana ndiyo njila yothetsela mavutowo. Iwo angaone kuti ni bwino kungosudzulana kusiyana n’kuti azingovutika m’cikwati.

4. Kodi tiyenela kupewa ciani?

4 Tiyenela kupewa maganizo akuti cikwati cathu calephela. Timadziŵa kuti maziko okha a m’Malemba othetsela cikwati ni cigololo. (Mat. 5:32) Conco tikakumana na nsautso imene Paulo anakamba, tiyenela kupewa kukhala na maganizo akuti: ‘Niona kuti mnzangayu saniŵelengela. Sanikonda kweni-kweni. Mwina ningakhale wosangalala n’tapeza wina womanga naye banja.’ Kukhala na maganizo otelo n’kudzikuza. Mukamaganiza conco, ndiye kuti mukuganizila za imwe mwekha cabe, osati za mnzanuyo. Ngati mumayendela nzelu za dziko, mudzangotsatila zofuna za mtima wanu na kucita zimene muona kuti zingakukondweletseni inuyo, ngakhale kuti zimenezo zingatanthauze kuthetsa cikwati. Koma Baibo imatilangiza kuti ‘tisamaganizile zofuna zathu zokha, koma tiziganizilanso zofuna za ena.’ (Afil. 2:4) Yehova amafuna kuti muziyesetsa kuteteza cikwati canu. Safuna kuti musudzulane. (Mat. 19:6) Iye amafuna kuti muziika patsogolo zofuna zake osati zofuna zanu.

5. Mogwilizana na Aefeso 5:33, kodi mwamuna na mkazi wake ayenela kucitilana zinthu motani?

5 Mwamuna na mkazi wake ayenela kucitilana zinthu mwacikondi komanso mwaulemu. (Ŵelengani Aefeso 5:33.) Baibo imatilimbikitsa kukhala na mtima wopatsa osati wongofuna kulandila. (Mac. 20:35) Kodi ni khalidwe liti limene lingathandize a m’cikwati kuti azionetsana cikondi na kulemekezana? Ni khalidwe la kudzicepetsa. Amuna na akazi amene ni odzicepetsa, samangodzifunila zopindulitsa iwo okha, koma ‘zopindulitsanso ena.’—1 Akor. 10:24.

Ngati mwamuna na mkazi wake ni odzicepetsa, amacitila zinthu pamodzi ndipo amapewa kukangana (Onani ndime 6)

6. Kodi mwaphunzilapo ciani pa zimene m’bale Steven na mkazi wake Stephanie anakamba?

6 Kudzicepetsa kwathandiza mabanja ambili acikhristu kukhala na cimwemwe cacikulu m’cikwati cawo. Mwacitsanzo, mwamuna wina dzina lake Steven anati: “Ngati mwamuna na mkazi wake ni ogwilizana, amayesetsa kucitila zinthu pamodzi maka-maka ngati pali mavuto. M’malo moganiza kuti ‘kodi ine ningakonde ziti? ni bwino kuganiza kuti ‘kodi ise tingakonde ziti?” Mkazi wake Stephanie amaonanso cimodzi-modzi. Iye anati: “Palibe amene angakonde kukhala na munthu wa mikangano. Ngati pabuka mkangano, timayesetsa kupeza cimene capangitsa vutolo. Ndiyeno timapemphela, kufufuza, na kukambilana mmene tingalithetsele. M’malo molozana zala, timayesetsa kulimbana na vutolo.” Mwamuna na mkazi wake amakhala na cimwemwe coculuka ngati aliyense wa iwo amapewa kudziona wofunika kwambili kuposa mnzake.

TUMIKILANI YEHOVA “MODZICEPETSA NTHAWI ZONSE”

7. Kodi m’bale ayenela kukhala na maganizo otani akapatsidwa udindo m’gulu la Yehova?

7 Timaona kuti ni mwayi kutumikila Yehova pa utumiki uliwonse umene tingakwanitse. (Sal. 27:4; 84:10) Timayamikila ngati m’bale wadzipeleka kucita zambili m’gulu la Yehova. Baibo imati: “Ngati munthu aliyense akuyesetsa kuti akhale woyang’anila, akufuna nchito yabwino.” (1 Tim. 3:1) Koma m’bale akapatsidwa udindo, sayenela kudziona kuti ni wofunika kwambili kuposa ena. (Luka 17:7-10) Ayenela kukhala na colinga cotumikila ena modzicepetsa.—2 Akor. 12:15.

8. Tiphunzilapo ciani pa zimene Diotirefe, Uziya, na Abisalomu anacita?

8 M’Baibo muli zitsanzo zoticenjeza za anthu amene anacita zinthu modzikuza. Mwacitsanzo, Diotirefe anali munthu wodzikuza. Iye anali kufuna kukhala “woyamba pakati” pa ena mumpingo. (3 Yoh. 9) Nayenso Uziya pa nthawi ina anacita zinthu modzikuza. Anagwila nchito imene siinali udindo wake malinga na malamulo a Yehova. (2 Mbiri 26:16-21) Komanso, Abisalomu anakopa anthu mwacinyengo kuti akhale ku mbali yake cifukwa anali kufunitsitsa kukhala mfumu. (2 Sam. 15:2-6) Zitsanzo za m’Baibo zimenezi, zionetselatu kuti Yehova sakondwela ndi anthu amene amadzifunila ulemelelo. (Miy. 25:27) M’kupita kwa nthawi, anthu odzikuza komanso amene amafuna kuchuka amakumana na mavuto aakulu.—Miy. 16:18.

9. Kodi Yesu anatipatsa citsanzo cotani?

9 Yesu anali wosiyana kwambili ndi anthu odzikuza amenewo. Baibo imati: “Ngakhale kuti iye anali ndi maonekedwe a Mulungu, kukhala wolingana ndi Mulungu sanakuganizilepo ngati cinthu coti angalande.” (Afil. 2:6) Yesu sadziona kuti ni wapamwamba kwambili olo kuti ni Yehova yekha amene amamuposa mphamvu. Iye anauza ophunzila ake kuti: “Aliyense wokhala ngati wamng’ono pakati pa nonsenu ndi amene ali wamkulu.” (Luka 9:48) Ni dalitso lalikulu cotani nanga kuseŵenzela pamodzi na apainiya, atumiki othandiza, akulu, na oyang’anila madela amene amatengela citsanzo ca Yesu ca kudzicepetsa! Atumiki odzicepetsa a Yehova amathandiza kuti m’gulu la Mulungu mukhale cikondi, cimene ni cizindikilo ca anthu a Mulungu.—Yoh. 13:35.

10. Kodi muyenela kucita ciani ngati muona kuti akulu sakusamalila bwino nkhani inayake mumpingo?

10 Nanga bwanji ngati muona kuti mumpingo muli nkhani inayake imene akulu sakuisamalila bwino? M’malo moyamba kudandaula, mungaonetse kudzicepetsa mwa kucilikiza amene amatsogolela mumpingo. (Aheb. 13:17) Kuti mudziŵe mmene mungacitile zimenezi, dzifunseni kuti: ‘Kodi nkhaniyi ni yaikuludi moti ingafunike cisamalilo? Kodi ino ingakhale nthawi yabwino yofunika kuisamalila? Kodi ni udindo wanga kuisamalila? Kodi colinga canga n’cofunadi kulimbikitsa mgwilizano mumpingo, kapena nifuna cabe kudzichukitsa?’

Amene ali na maudindo safunika kudziŵika na maluso awo cabe, koma afunika kudziŵikanso kuti ni odzicepetsa (Onani ndime 11) *

11. Malinga na Aefeso 4:2, 3, kodi pamakhala zotulukapo zotani ngati titumikila Yehova modzicepetsa?

11 Kwa Yehova, cofunika kwambili ni kukhala wodzicepetsa kuposa kukhala na maluso. Iye amaonanso kuti kukhala ogwilizana n’kofunika kwambili kuposa cangu pa nchito. Conco, citani zonse zotheka kuti muzitumikila Yehova modzicepetsa. Mukamacita zimenezo, mudzathandiza mpingo kukhala wogwilizana. (Ŵelengani Aefeso 4:2, 3.) Khalani acangu mu ulaliki. Sakilani mipata yothandizila ena mwa kuwacitila zinthu zabwino. Komanso, khalani oceleza kwa onse, ngakhale kwa amene alibe maudindo mu mpingo. (Mat. 6:1-4; Luka 14:12-14) Mukamaseŵenzela pamodzi na mpingo modzicepetsa, ena adzaona maluso anu ndipo kuposa pamenepo, adzaona kudzicepetsa kwanu.

KHALANI ODZICEPETSA POSEŴENZETSA MALO OCEZELA PA INTANETI

12. Kodi Baibo imatilimbikitsa kukhala na mabwenzi? Fotokozani.

12 Yehova amafuna kuti tizisangalala poceza na a m’banja lathu komanso mabwenzi athu. (Sal. 133:1) Yesu anali na mabwenzi abwino. (Yoh. 15:15) Baibo imafotokoza mapindu amene timapeza tikakhala na mabwenzi abwino. (Miy. 17:17; 18:24) Imatiuzanso kuti si bwino kudzipatula. (Miy. 18:1) Anthu ambili amaona kuti kuceza pa intaneti kumawathandiza kukhala na mabwenzi ambili, ndiponso kumawathandiza kuti asamakhale osungulumwa. Komabe, tiyenela kukhala osamala tikamaseŵenzetsa malo ocezela pa intaneti.

13. N’cifukwa ciani anthu ena amene amaseŵenzetsa malo ocezela pa intaneti amakhala osungulumwa komanso ovutika maganizo?

13 Ocita kafuku-fuku anapeza kuti anthu amene amataila nthawi yaitali kuona zimene anzawo aika pa malo ocezela pa intaneti, pamapeto pake akhoza kumakhala osungulumwa komanso ovutika maganizo. Cifukwa ciani? Cifukwa cimodzi cingakhale cakuti zithunzi zimene anthu amaika pa intaneti, nthawi zambili zimakhala zija zoonetsa zocitika zapadela mu umoyo wawo, wa mabwenzi awo, komanso zoonetsa malo ocititsa cidwi amene iwo anapitako. Munthu amene amaona zithunzi zimenezo, angayambe kudziona kuti ni wotsalila komanso kuti umoyo wake ni wosasangalatsa. Mlongo wina wa zaka 19 anati: “N’taona kuti anzanga amapita kokasangalala kumapeto kwa wiki, n’nayamba kusoŵa cimwemwe poona kuti ine nimangokhala panyumba.”

14. Kodi malangizo a m’Baibo a pa 1 Petulo 3:8, amatithandiza bwanji kuti tiziseŵenzetsa mwanzelu malo ocezela pa intaneti?

14 N’zoona kuti tingaseŵenzetse malo ocezela pa intaneti pa zifukwa zabwino monga kukambilana na acibululu komanso mabwenzi athu. Koma mwina mwaonapo kuti anthu ena amaika zinthu pa intaneti n’colinga cakuti ena aziwakhumbila. Zimaoneka kuti iwo amangofuna kuti anthu ena azingoganizila za iwowo basi. Ena amafika ngakhale polemba mawu onyoza ndi acipongwe pa mapikica yawo kapena ya ena pa intaneti. Ife Akhristu timalangizidwa kuti tiyenela kukhala odzicepetsa komanso oganizila ena. Conco, timapewa kuseŵenzetsa malo ocezela pa intaneti mwanjila yolakwika imeneyi.—Ŵelengani 1 Petulo 3:8.

Kodi zinthu zimene mumaika pa intaneti zimaonetsa kuti ndimwe wodzitama kapena wodzicepetsa? (Onani ndime 15)

15. Kodi Baibo ingatithandize bwanji kupewa mzimu wofuna kuti ena azitiona apamwamba kwambili?

15 Ngati mumaseŵenzetsa malo ocezela pa intaneti, dzifunseni kuti: ‘Kodi mameseji amene nimalemba, komanso mapikica na mavidiyo amene nimaika pa malo ocezela pa intaneti amapangitsa ena kuona kuti ndine wodzitama? Kodi izi zingapangitse ena kukhala na nsanje?’ Baibo imati: “Ciliconse ca m’dziko, monga cilakolako ca thupi, cilakolako ca maso ndi kudzionetsela ndi zimene munthu ali nazo pa moyo wake, sizicokela kwa Atate, koma kudziko.” (1 Yoh. 2:16) Mawu akuti “kudzionetsela ndi zimene munthu ali nazo pa moyo wake,” Baibo ina inawamasulila kuti “kufuna kudzionetsa kuti ndiwe wapamwamba kwambili.” Akhristu safunika kudziona kuti ni apamwamba kwambili kuposa ena kapena kufuna kudzipezela ulemu. Iwo amatsatila malangizo a m’Baibo akuti: “Tisakhale odzikuza, oyambitsa mpikisano pakati pathu, ndi ocitilana kaduka.” (Agal. 5:26) Tikakhala odzicepetsa, tidzapewa kutengela anthu odzikuza a m’dzikoli amene amafuna kuti ena aziwaona kuti ni apamwamba kwambili.

‘MUZIGANIZA M’NJILA YAKUTI MUKHALE WOGANIZA BWINO’

16. N’cifukwa ciani tifunika kupewa kukhala odzikuza?

16 Tifunika kukulitsa khalidwe la kudzicepetsa cifukwa cakuti anthu odzikuza sakhala ‘oganiza bwino.’ (Aroma 12:3) Anthu odzikuza amakonda kukangana na ena ndiponso amadziona kuti ni apamwamba kwambili kuposa ena. Zimene amaganiza na kucita, nthawi zambili zimabweletsa mavuto kwa iwo komanso kwa anthu ena. Ngati sangasinthe, Satana angapotoze na kucititsa khungu maganizo awo. (2 Akor. 4:4; 11:3) Koma munthu wodzicepetsa amakhala woganiza bwino. Iye amadziona moyenela, ndipo amazindikila kuti ena amamuposa m’njila zambili. (Afil. 2:3) Komanso amadziŵa kuti “Mulungu amatsutsa odzikweza, koma odzicepetsa amawasonyeza kukoma mtima kwake kwakukulu.” (1 Pet. 5:5) Anthu oganiza bwino amapewa kudzikweza cifukwa safuna kuti Yehova aziwatsutsa kapena kuti akhale mdani wawo.

17. Tifunika kucita ciani kuti tikhalebe odzicepetsa?

17 Kuti tikhalebe odzicepetsa, tifunika kutsatila malangizo a m’Baibo akuti tivule “umunthu wakale pamodzi ndi nchito zake, ndipo [tivale] umunthu watsopano.” Kucita zimenezi kumafuna khama. Tifunika kuphunzila za Yesu na kuyesetsa kutengela citsanzo cake mosamala kwambili. (Akol. 3:9, 10; 1 Pet. 2:21) Tikacita zimenezo, tidzapeza mapindu ambili. Tikakulitsa khalidwe la kudzicepetsa, tidzakhala na banja lacimwemwe, tidzathandiza mpingo kukhala wogwilizana, komanso tidzapewa kuseŵenzetsa molakwika malo ocezela pa intaneti. Koposa zonse, Yehova adzatidalitsa ndipo tidzakhala naye pa ubwenzi wabwino.

NYIMBO 117 Ubwino

^ ndime 5 Masiku ano, tikukhala m’dziko lodzala ndi anthu odzikuza komanso odzikonda. Koma tiyenela kukhala osamala kuti tisatengele makhalidwe awo. M’nkhani ino, tikambilana mbali zitatu zokhudza umoyo wathu, ndipo pa mbali zimenezo, tiona mmene tingaonetsele kuti sitidziganizila kuposa mmene tiyenela kudziganizila.

^ ndime 2 KUFOTOKOZELA MAWU ENA: Munthu wodzikuza amadziona kuti ni wofunika kwambili kuposa ena. N’cifukwa cake amakhalanso wodzikonda. Koma wodzicepetsa amakhala wosadzikonda. Kudzicepetsa kumatanthauza kusakhala wonyada komanso kusadziona kuti ndife ofunika kwambili kuposa ena.

^ ndime 56 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Mkulu amene ali na luso lokamba nkhani pa msonkhano wacigawo komanso kuyang’anila abale ena, akuyamikila mwayi wotsogoza makambilano a ulaliki na kuyeletsa pa Nyumba ya Ufumu.