Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 28

Kodi Mumakhulupililadi Kuti Muli na Coonadi?

Kodi Mumakhulupililadi Kuti Muli na Coonadi?

“Pitiliza kutsatila zimene unaphunzila ndi zimene unakhulupilila pambuyo pokhutila nazo.”—2 TIM. 3:14.

NYIMBO 56 Khulupilila Coonadi Iwe Mwini

ZIMENE TIKAMBILANE *

1. Kodi titanthauzanji tikati “coonadi”?

“KODI munaphunzila bwanji coonadi?” “Kodi munabadwila m’banja la Mboni?” “Kodi mwakhala m’coonadi kwa nthawi yaitali bwanji?” N’kutheka kuti imwe munafunsako ena mafunso aconco, kapena wina anakufunsankoni mafunso amenewa. Kodi titanthauzanji tikati “coonadi”? Tikakamba kuti “coonadi,” nthawi zambili timatanthauza zimene timakhulupilila, zimene timacita polambila Mulungu, komanso mmene timakhalila pa umoyo wathu. Anthu amene “ali m’coonadi” amadziŵa zimene Baibo imaphunzitsa, ndipo amatsatila mfundo za m’Baibo pa umoyo wawo. Zotulukapo zake n’zakuti, amamasuka ku ziphunzitso zabodza za cipembedzo, komanso amakhala na umoyo wacimwemwe ngakhale kuti ali m’dziko loipali la Satana.—Yoh. 8:32.

2. Malinga na Yohane 13:34, 35, n’ciani cingamukope munthu poyamba kuti abwele m’coonadi?

2 N’ciani cinakukopani poyamba kuti mubwele m’coonadi? Mwina linali khalidwe labwino la anthu a Yehova. (1 Pet. 2:12) Kapena cinali cikondi cimene iwo amaonetsana. Anthu ambili amaona cikondi cimeneci akapezeka pa misonkhano kwa nthawi yoyamba, ndipo cimawakopa kwambili kuposa ciliconse cimene aphunzila pamsonkhanowo. Zimenezi n’zosadabwitsa cifukwa Yesu anakamba kuti ophunzila ake adzadziŵika cifukwa ca cikondi cimene amaonetsana. (Ŵelengani Yohane 13:34, 35.) Koma pali zina zimene tifunika kucita kuti tikhale na cikhulupililo colimba.

3. N’ciani cingacitike ngati cikhulupililo cathu n’cozikidwa cabe pa cikondi cacikhristu cimene abale na alongo amaonetsa?

3 Cikhulupililo cathu sicifunika kuzikidwa cabe pa cikondi cimene anthu a Mulungu ali naco. Cifukwa ciani? Cifukwa ngati cikhulupililo cathu n’cozikidwa cabe pa cikondi cimeneco, cingakhale cosavuta kutaya cikhulupililoco. Mwacitsanzo, tingaleke kutumikila Yehova ngati m’bale kapena mlongo, mwina ngakhale mkulu kapena mpainiya wacita chimo lalikulu. Tingalekenso kutumikila Yehova ngati m’bale kapena mlongo watikhumudwitsa, kapena ngati wakhala wampatuko n’kumakamba kuti zimene timakhulupilila n’zabodza. Conco, kuti tikhale na cikhulupililo colimba, tifunika kukhala pa ubale wolimba na Yehova. Ngati cikhulupililo canu mwa Mulungu n’cozikidwa cabe pa zimene anthu ena amacita osati pa ubale wanu na iye, ndiye kuti n’cosalimba. Mmene mumaonela Yehova komanso anthu ake, zingakuthandizeni kukulitsa cikhulupililo canu pa mlingo winawake. Koma cina cofunika kwambili ni kuphunzila Baibo mozama, kumvetsetsa zimene mukuphunzilazo, ndiponso kufufuza n’colinga cakuti mukhutile kuti zimene mumaphunzila ni coonadi conena za Yehova. Mufunika kudzipezela maumboni inu eni oonetsa kuti Baibo imaphunzitsa coonadi ponena za Yehova.—Aroma 12:2.

4. Kulingana na Mateyu 13:3-6, 20, 21, kodi ena amacita ciani cikhulupililo cawo cikayesedwa?

4 Yesu anakamba kuti ena amalandila coonadi “mwacimwemwe,” koma akakumana na mavuto cikhulupililo cawo cimafooka. (Ŵelengani Mateyu 13:3-6, 20, 21.) Mwina iwo amafooka cifukwa cakuti poyamba sanazindikile kuti ngati munthu wasankha kutsatila Yesu, akhoza kukumana na mavuto. (Mat. 16:24) Mwinanso anali kuganiza kuti munthu akakhala Mkhristu ndiye kuti basi sazikumana na mavuto alionse, azingolandila madalitso okha-okha. Koma popeza tikukhala m’dziko loipali, tidzakumanabe na mavuto. Nthawi iliyonse zinthu zingasinthe mu umoyo, ndipo cimwemwe cathu cingacepe.—Sal. 6:6; Mlal. 9:11.

5. Kodi abale na alongo athu ambili akuonetsa bwanji kuti amakhulupilila kuti anapeza coonadi?

5 Abale na alongo ambili amaonetsa kuti amakhulupililadi kuti anapeza coonadi. N’cifukwa ciani takamba conco? Cifukwa safooka m’cikhulupililo ngakhale pamene wokhulupilila mnzawo wawakhumudwitsa kapena pamene wacita chimo. (Sal. 119:165) M’malomwake, iwo akakumana na ciyeso, cikhulupililo cawo cimalimbilako, osati kucepa. (Yak. 1:2-4) Kodi mungacite ciani kuti mukhale na cikhulupililo colimba ngati cimeneco?

DZIŴANI “MULUNGU MOLONDOLA”

6. Kodi cikhulupililo ca ophunzila a m’nthawi ya Atumwi cinazikidwa pa ciani?

6 Ophunzila a m’nthawi ya atumwi anali kudziŵa Malemba na ziphunzitso za Yesu Khristu, kutanthauza “coonadi ca uthenga wabwino.” Izi zinawathandiza kukhala na cikhulupililo colimba. (Agal. 2:5) Coonadi cimeneci ni mfundo zonse zimene ife Akhristu timakhulupilila, kuphatikizapo zokhudza nsembe ya dipo la Yesu na kuukitsidwa kwake. Mtumwi Paulo anali kukhulupilila kuti ziphunzitso zimenezi n’zoona. N’cifukwa ciani takamba conco? Cifukwa iye anali kuseŵenzetsa Malemba pofuna kupeleka “umboni wolembedwa [potsimikizila anthu] kuti kunali koyenela kuti Khristu avutike ndi kuuka kwa akufa.” (Mac. 17:2, 3) Ophunzila a m’nthawi ya Atumwi anakhulupilila ziphunzitso zimenezo, ndipo anadalila mzimu woyela kuti uwathandize kumvetsetsa Mawu a Mulungu. Anafufuza kuti atsimikizile ngati ziphunzitso zimenezo zinalidi zozikidwa pa Malemba. (Mac. 17:11, 12; Aheb. 5:14) Cikhulupililo cawo sicinali cozikidwa cabe pa mmene anali kuonela Yehova ndi anthu ake. Komanso sanali kutumikila Yehova cabe cifukwa cokonda kuyanjana na Akhristu anzawo. M’malomwake, cikhulupililo cawo cinazikidwa pa “kumudziŵa Mulungu molondola.”—Akol. 1:9, 10.

7. Kodi kukhulupilila coonadi ca m’Baibo kungatithandize bwanji?

7 Coonadi ca m’Baibo sicisintha. (Sal. 119:160) Mwacitsanzo, coonadi ca m’Baibo sicisintha ngati wokhulupilila mnzathu watikhumudwitsa kapena ngati wacita chimo lalikulu. Komanso sicisintha ngakhale pamene takumana na mavuto. Motelo, tiyenela kuzidziŵa bwino ziphunzitso za m’Baibo ndiponso kukhutila kuti ziphunzitso zimenezo n’zoona. Monga mmene nangula amatetezela boti ku cimphepo camkuntho, cikhulupililo cathu colimba cozikidwa pa coonadi ca m’Baibo cidzatithandiza kuti tisafooke pamene takumana na mayeselo. Kodi mungalimbitse bwanji cikhulupililo canu cakuti muli na coonadi?

‘KHULUPILILANI PAMBUYO POKHUTILA NAZO’

8. Mogwilizana na 2 Timoteyo 3:14, 15, n’ciani cinathandiza Timoteyo kuti afike pokhulupilila kuti wapeza coonadi?

8 Timoteyo anakhulupilila kuti wapeza coonadi. Kodi n’ciani cinam’thandiza kukhulupilila zimenezo? (Ŵelengani 2 Timoteyo 3:14, 15.) Amayi ŵake na ambuye ŵake ndiwo anali oyamba kumuphunzitsa “malemba oyela.” Koma mosakayikila nayenso payekha anali kupatula nthawi yophunzila Malembawo mozama. Zotulukapo zake zinali zakuti ‘pambuyo pokhutila,’ iye anakhulupilila kuti m’malembawo muli coonadi. M’kupita kwa nthawi, Timoteyo, amayi ŵake, komanso ambuye ŵake anaphunzila ziphunzitso zacikhristu. Mosakayikila, Timoteyo anakopeka na cikondi cimene otsatila a Yesu anali kuonetsana, moti anayamba kufunitsitsa kuyanjana nawo na kuwathandiza. (Afil. 2:19, 20) Ngakhale n’conco, cikhulupililo cake sicinazikidwe pa cikondi cimene anali naco pa Akhristu anzake, koma cinazikidwa pa mfundo za m’Baibo zimene anazikhulupilila kuti ni coonadi. Mfundo zimenezo zinamusonkhezela kukhala pa ubwenzi na Yehova. Na imwe mufunika kuŵelenga Baibo kuti mufike pokhulupilila kuti zimene Baibo imaphunzitsa ponena za Yehova n’zoona.

9. Ni mfundo zitatu ziti zoyambilila za coonadi zimene mufunika kukhutila nazo?

9 Kuti inunso mukhulupilile kuti muli na coonadi, muyenela kumvetsetsa ziphunzitso zitatu zoyambilila na kukhutila nazo. Coyamba, mufunika kukhulupilila kuti Yehova Mulungu ndiye Mlengi wa zinthu zonse. (Eks. 3:14, 15; Aheb. 3:4; Chiv. 4:11) Caciŵili, mufunika kupeza umboni pa imwe mwekha wotsimikizila kuti Baibo ni uthenga wouzilidwa na Mulungu wopita kwa anthu. (2 Tim. 3:16, 17) Cacitatu, mufunika kukhulupilila kuti Yehova ali na gulu lolinganizidwa bwino la anthu amene amam’lambila motsogoleledwa na Khristu, na kuti gulu limenelo ni Mboni za Yehova. (Yes. 43:10-12; Yoh. 14:6; Mac. 15:14) Kuti mukhulupilile mfundo zoyambilila zimenezi sikuti mufunika kudziŵa mfundo zonse za m’Baibo. Cofunika kwambili ni kuseŵenzetsa “luntha [lanu] la kuganiza” kuti mulimbitse cikhulupililo canu cakuti muli na coonadi.—Aroma 12:1.

KHALANI OKONZEKA KUTHANDIZA ENA KUKHULUPILILA MFUNDO ZA COONADI

10. Kuwonjezela pa kudziŵa coonadi, kodi tifunikanso kucita ciani?

10 Mukakhulupilila mfundo zitatu zimene takambilana ponena za Mulungu, Baibo, ndiponso anthu a Mulungu, mufunika kuphunzila kuseŵenzetsa Malemba pothandiza ena kuti nawonso akhulupilile mfundo za coonadi zimenezi. Cifukwa ciani? Cifukwa ife Akhristu tili na udindo wophunzitsa coonadi anthu amene angamvetsele. * (1 Tim. 4:16) Ndipo pamene tithandiza ena kukhulupilila mfundo za coonadi, cikhulupililo cathu pa mfundo zimenezo cimalimbilako.

11. Monga mphunzitsi, kodi mtumwi Paulo anapeleka citsanzo cotani?

11 Pophunzitsa anthu, mtumwi Paulo anali “kugwilitsa nchito mfundo zokopa zokhudza Yesu, kucokela m’Cilamulo ca Mose ndi mu Zolemba za aneneli.” (Mac. 28:23) Kodi tingatengele bwanji citsanzo ca Paulo pophunzitsa ena coonadi? Sitifunika kungowauza cabe zimene Baibo imaphunzitsa. Tifunika kulimbikitsa anthu amene timaphunzila nawo kuti aziŵelenga Baibo na kuganizilapo mwakuya pa mfundo zimene aŵelengazo. Timafuna kuti iwo abwele m’coonadi, osati cifukwa cakuti amakonda ife, koma cifukwa cakuti akhulupilila kuti zimene amaphunzila ponena za Mulungu wathu wacikondi, ni coonadi.

Makolo, thandizani ana anu kukhala na cikhulupililo colimba mwa kuwaphunzitsa “zinthu zozama za Mulungu” (Onani ndime 12-13) *

12-13. Kodi makolo angacite ciani kuti athandize ana awo kukhalabe m’coonadi?

12 Makolo, mosakayikila mumafuna kuti ana anu akhalebe m’coonadi. Mwina mumaganiza kuti ngati anawo apeza mabwenzi abwino mu mpingo, adzapita patsogolo mwauzimu. Komabe, kuti ana anu akhulupilile kuti zimene amaphunzila ni coonadi, palinso zina zofunika osati cabe kukhala na mabwenzi abwino. Afunika kupanga ubale wawo-wawo na Mulungu komanso kukhulupilila kuti zimene Baibo imaphunzitsa n’zoona.

13 Kuti makolo aphunzitse ana awo coonadi ponena za Mulungu, afunika kukhala citsanzo cabwino pa nkhani yoŵelenga Baibo mwakhama. Afunikanso kukhala na nthawi yosinkha-sinkha pa zimene aŵelengazo. Akatelo, adzakwanitsa kuthandiza ana awo kuti nawonso azicita zimenezi. Makolo afunika kuphunzitsa ana awo kuseŵenzetsa zida zathu zofufuzila, monga mmene amathandizila maphunzilo awo a Baibo. Mwa kucita zimenezi, adzathandiza anawo kukonda Yehova na kukhulupilila kapolo wokhulupilika ndi wanzelu, amene iye amamuseŵenzetsa potipatsa cakudya cauzimu. (Mat. 24:45-47) Makolo, musamangowaphunzitsa cabe mfundo zoyambilila za m’Baibo ana anu. Athandizeni kukhala na cikhulupililo colimba mwa kuwaphunzitsa “zinthu zozama za Mulungu,” kulingana na zaka zawo komanso luso lawo lomvetsa zinthu.—1 Akor. 2:10.

PHUNZILANI MAULOSI A M’BAIBO

14. N’cifukwa ciani tifunika kuphunzila maulosi a m’Baibo? (Onaninso bokosi lakuti “ Kodi Mungakwanitse Kufotokoza Maulosi Awa?”)

14 Maulosi a m’Baibo ni mbali yofunika kwambili ya Mawu a Mulungu. Amatithandiza kukhala na cikhulupililo colimba mwa Yehova. Kodi ni maulosi ati amene alimbitsa cikhulupililo canu? Mwina mungayankhe kuti ni maulosi okamba za “masiku otsiliza.” (2 Tim. 3:1-5; Mat. 24:3, 7) Koma kodi ni maulosi ena ati amene anakwanilitsidwa kale amene angalimbitse cikhulupililo canu? Mwacitsanzo, kodi mungafotokoze mmene maulosi a pa Danieli caputa 2 kapena Danieli caputa 11 anakwanilitsidwila m’mbuyomo, komanso mmene akukwanilitsidwila masiku ano? * Ngati cikhulupililo canu n’cozikidwa zolimba pa Baibo, mosakayikila simudzagwedezeka mukakumana na mavuto. Ganizilani citsanzo ca abale athu ku Germany, amene anazunzidwa koopsa pa Nkhondo Yaciŵili ya Padziko Lonse. Ngakhale kuti iwo sanali kuwamvetsetsa bwino maulosi a m’Baibo okamba za masiku otsiliza, anali na cikhulupililo colimba m’Mawu a Mulungu.

Tikamaphunzila Baibo kuphatikizapo maulosi, tidzakhalabe olimba pa nthawi ya mayeselo (Onani ndime 15-17) *

15-17. Kodi kuphunzila Baibo kunawathandiza bwanji abale athu amene anali kuzunzidwa mu ulamulilo wa Nazi?

15 Mu ulamulilo wa Nazi ku Germany, abale na alongo athu masauzande anatumizidwa ku ndende zacibalo. Hitler pamodzi na mkulu wa gulu la asilikali la SS, dzina lake Heinrich Himmler, anali kuzonda kwambili Mboni za Yehova. Kulingana na zimene mlongo wina anakamba, Himmler anauza gulu la alongo athu m’ndende ina yacibalo kuti: “N’kutheka kuti Yehova wanuyo akulamulila kumwamba, koma pano padziko ndise tikulamulila! Tiona amene adzapambana, imwe kapena ise!” Kodi n’ciani cinathandiza anthu a Yehova kukhalabe okhulupilika?

16 Ophunzila Baibo amenewo anali kudziŵa kuti Ufumu wa Mulungu unali utayamba kulamulila mu 1914. Conco zinali zosadabwitsa kwa iwo kuona kuti akuzunzidwa kwambili. Olo zinali telo, anthu a Yehova anali kukhulupilila kuti palibe boma la anthu limene lingalepheletse cifunilo ca Mulungu kucitika. Anali kudziŵanso kuti Hitler sakanatha kufafaniza kulambila koona kapena kukhazikitsa boma lamphamvu kuposa Ufumu wa Mulungu. Abale athu anali kudziŵa kuti m’kupita kwa nthawi, ulamulilo wa Hitler udzatha.

17 Zimene abale na alongo amenewo anali kukhulupilila zinali zoona. Pasanapite nthawi yaitali, boma la Nazi linagwa. Ndipo Heinrich Himmler, amene anakamba mawu akuti “pano padziko ndise tikulamulila,” anayamba kuthaŵa kuti apulumutse moyo wake. Ali mkati mothaŵa, anakumana na M’bale Lübke, amene kale anali mkaidi. Iye anakumbukila kuti Lübke anali wa Mboni za Yehova. Conco poona kuti ulamulilo wawo watha, mkuluyo anafunsa m’bale Lübke kuti: “Iwe wophunzila Baibo, kodi cicitike n’ciani tsopano?” M’bale Lübke anauza Himmler kuti Mboni za Yehova zinali kudziŵa kuti ulamulilo wa Nazi udzatha, ndipo zidzapeza mpumulo. Himmler, amene poyamba anali kunyoza kwambili Mboni za Yehova, panthawiyi analibiletu mawu. Patangopita nthawi yocepa, iye anadzipha. Kodi tiphunzilapo ciani pamenepa? Tikamaphunzila Baibo kuphatikizapo maulosi, tidzakhala na cikhulupililo cosagwedela mwa Mulungu, ndipo tidzakhalabe olimba pa nthawi ya mayeselo.—2 Pet. 1:19-21.

18. Mogwilizana na mawu a pa Yohane 6:67, 68, n’cifukwa ciani tifunika “kudziŵa zinthu molondola, komanso kuzindikila zinthu bwino kwambili,” zimene Paulo anakambapo?

18 Aliyense wa ife afunika kuonetsa cikondi, khalidwe limene ni cizindikilo ca Akhristu oona. Koma tifunikanso “kudziŵa zinthu molondola, komanso kuzindikila zinthu bwino kwambili.” (Afil. 1:9) Izi zidzatithandiza kuti tisakhale “otengeka kupita uku ndi uku ndi mphepo iliyonse ya ciphunzitso conyenga ca anthu,” kuphatikizapo ampatuko. (Aef. 4:14) Pamene ophunzila ambili analeka kutsatila Yesu m’nthawi ya atumwi, mtumwi Petulo anakamba motsimikiza kuti Yesu ndiye anali na “mawu amoyo wosatha.” (Ŵelengani Yohane 6:67, 68.) Ngakhale kuti Petulo anali asanamvetse tanthauzo la mawu onse amene Yesu anakamba, anakhalabe wokhulupilika cifukwa anali kudziŵa kuti Yesu ndiye Khristu. Inunso mungalimbitse cikhulupililo canu pa zimene Baibo imaphunzitsa. Mukatelo, mudzakhalabe olimba m’cikhulupililo pamene mwakumana na mavuto. Komanso, mudzathandiza ena kukhala na cikhulupililo colimba.—2 Yoh. 1, 2.

NYIMBO 72 Tilalikile Coonadi ca Ufumu

^ ndime 5 Nkhani ino itithandiza kuona kufunika koyamikila ziphunzitso za coonadi ca m’Mawu a Mulungu. Tionanso zimene zingatithandize kukhala otsimikiza kuti zimene timakhulupilila ni coonadi.

^ ndime 10 Kuti mudziŵe zimene mungacite pokambilana na ena mfundo zoyambilila za m’Baibo, onani nkhani zakuti “Kukambilana Ndi Munthu Wina Nkhani za m’Baibulo,” zopezeka mu Nsanja ya Mlonda kuyambila mu 2010 mpaka mu 2015. Muli nkhani monga zakuti “Kodi Yesu Ndi Mulungu?” “Kodi Ufumu wa Mulungu Unayamba Liti Kulamulila?” komanso yakuti “Kodi Mulungu Amalanga Anthu Kumoto?”

^ ndime 14 Kuti mudziŵe mafotokozedwe a maulosi amenewa, onani Nsanja ya Mlonda ya June 15, 2012, komanso ya May 2020.

^ ndime 60 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Pa kulambila kwa pabanja, makolo akuphunzila pamodzi na ana awo maulosi a m’Baibo okamba za cisautso cacikulu.

^ ndime 62 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Banja limodzi-modzilo silikucita mantha na zimene zikucitika pa cisautso cacikulu.