Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 29

“Pamene Ndili Wofooka, M’pamene Ndimakhala Wamphamvu”

“Pamene Ndili Wofooka, M’pamene Ndimakhala Wamphamvu”

“Ndimasangalala ndi kufooka, zitonzo, zosowa zanga, mazunzo ndi zovuta zina, chifukwa cha Khristu.”​—2 AKOR. 12:10.

NYIMBO NA. 38 Mulungu Adzakulimbitsa

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1. Kodi mtumwi Paulo anavomereza chiyani?

MTUMWI Paulo ananena kuti nthawi zina ankafooka. Iye anavomereza kuti thupi lake linali litayamba kuchepa mphamvu, ankavutika kuchita zinthu zoyenera komanso kuti nthawi zina Yehova sankayankha mapemphero ake m’njira imene ankayembekezera. (2 Akor. 4:16; 12:7-9; Aroma 7:21-23) Paulo ananenanso kuti anthu amene ankamutsutsa ankamuona kuti ndi wofooka. * Koma sanalole kuti mmene anthu ena ankamuonera komanso zofooka zake zimupangitse kumadziona ngati wachabechabe.​—2 Akor. 10:10-12, 17, 18.

2. Mogwirizana ndi 2 Akorinto 12:9, 10, kodi Paulo anazindikira mfundo yofunika kwambiri iti?

2 Paulo anazindikira mfundo yofunika kwambiri yakuti munthu akhoza kukhala wamphamvu ngakhale pamene akudziona kuti ndi wofooka. (Werengani 2 Akorinto 12:9, 10.) Yehova anauza Paulo kuti mphamvu yake imakhala ‘yokwanira iyeyo akakhala wofooka,’ kutanthauza kuti Yehova ankamupatsa mphamvu zimene ankafunikira. Choyamba, tiyeni tione chifukwa chake sitiyenera kukhumudwa adani athu akamatinyoza.

MUZISANGALALA MUKAMANYOZEDWA

3. N’chifukwa chiyani tiyenera kumasangalala anthu akamatinyoza?

3 Palibe amene amasangalala akamanyozedwa. Koma ngati timakhumudwa kwambiri adani athu akamatinyoza, tikhoza kufooka. (Miy. 24:10) Ndiye kodi tiyenera kukhala ndi maganizo otani adani athu akamatinyoza? Mofanana ndi Paulo, nafenso tikhoza kumasangalala anthu akamatinyoza. (2 Akor. 12:10) Chifukwa chiyani? Chifukwa choti tikamanyozedwa komanso kuzunzidwa zimasonyeza kuti ndife otsatira enieni a Yesu. (1 Pet. 4:14) Yesu ananena kuti otsatira ake adzazunzidwa. (Yoh. 15:18-20) Zimenezi ndi zomwe zinachitikira Akhristu a munthawi ya atumwi. Pa nthawiyo, anthu amene ankatengera chikhalidwe cha Agiriki ankaona kuti Akhristu ndi anthu opanda nzeru komanso otsalira. Komanso Ayuda ankaona kuti Akhristu monga Petulo ndi Yohane anali anthu “osaphunzira ndiponso anthu wamba.” (Mac. 4:13) Akhristu ankaonedwa ngati anthu ofooka chifukwa sankachita nawo zandale kapena kumenya nkhondo moti anthu sankawalemekeza.

4. Kodi Akhristu a munthawi ya atumwi ankatani anthu ena akamawanenera zoipa?

4 Kodi Akhristu a munthawi ya atumwi analolera kusokonezedwa ndi maganizo a adani awowa? Ayi. Mwachitsanzo, mtumwi Petulo ndi mtumwi Yohane ankaona kuti ndi mwayi kuzunzidwa chifukwa chotsatira Yesu komanso kuuza ena zimene Yesu ankaphunzitsa. (Mac. 4:18-21; 5:27-29, 40-42) Otsatira a Yesu sankachita manyazi. Ngakhale kuti anthu a m’madera amene ankakhala sankawalemekeza, Akhristuwa anathandiza anthu ambiri kuposa adani awowo. Mwachitsanzo, mabuku a m’Baibulo omwe ena mwa Akhristuwa analemba anathandiza anthu ambirimbiri komanso kuwapatsa chiyembekezo. Ufumu umene ankalalikira unayamba kulamulira kumwamba ndipo posachedwapa uyamba kulamulira dziko lonse lapansi. (Mat. 24:14) Mosiyana ndi zimenezi, ulamuliro wa Roma womwe unkazunza Akhristu pa nthawiyo, unatha. Komanso panopo Akhristu okhulupirikawo akulamulira monga mafumu kumwamba. Adani amene ankawatsutsawo anamwalira ndipo ngati angadzaukitsidwe, azidzalamuliridwa ndi Ufumu umene Akhristu omwe ankadana nawowo ankalalikira.​—Chiv. 5:10.

5. Mogwirizana ndi Yohane 15:19, n’chifukwa chiyani a Mboni za Yehova amanyozedwa?

5 Masiku ano, anthu ena amanyoza a Mboni za Yehova chifukwa amawaona ngati anthu opanda nzeru komanso achabechabe. Amationa choncho chifukwa timachita zinthu mosiyana ndi anthu ena. Timayesetsa kukhala odzichepetsa, ofatsa komanso omvera. Koma anthu a m’dzikoli amalemekeza anthu onyada, odzikweza komanso osamvera. Ifeyo sitichita nawo zandale ndiponso sitimenya nawo nkhondo. Popeza timachita zosiyana ndi zimene anthu a m’dzikoli amachita, amationa ngati otsalira.​—Werengani Yohane 15:19; Aroma 12:2.

6. Kodi Yehova amathandiza anthu ake kuchita zinthu ziti?

6 Ngakhale anthu a m’dzikoli amationa ngati otsalira, Yehova amatigwiritsa ntchito pochita zinthu zazikulu. Mwachitsanzo, panopa Yehova amatithandiza kugwira ntchito yolalikira yomwe ikugwiridwa kuposa kale lonse. Atumiki a Yehova masiku ano amamasulira komanso kufalitsa magazini m’zinenero zambirimbiri ndipo amagwiritsa ntchito Baibulo pothandiza anthu mamiliyoni kuti asinthe makhalidwe awo. Zonsezi zimatheka chifukwa cha Yehova yemwe amagwiritsira ntchito anthu omwe dzikoli limawaona ngati achabechabe. Koma nanga bwanji ifeyo aliyense payekhapayekha? Kodi Yehova angatithandize kuti tikhale amphamvu? Ngati ndi choncho, tingatani kuti azitipatsa mphamvu? Tsopano tiyeni tikambirane zinthu zitatu zimene tingaphunzire kwa mtumwi Paulo.

MUSAMADALIRE MPHAMVU ZANU ZOKHA

7. Kodi tikuphunzira chiyani kwa Paulo?

7 Chitsanzo cha Paulo chikutiphunzitsa mfundo yakuti: Sitiyenera kudalira mphamvu kapena luso lathu tikamatumikira Yehova. Paulo anali ndi zifukwa zokhalira wonyada komanso wodzidalira. Iye anakulira mumzinda wa Tariso, womwe unali m’chigawo cholamulidwa ndi ufumu wa Roma. Mzindawu unali wotukuka komanso unali ndi yunivesite yotchuka. Paulo anali wophunzira kwambiri. Iye anaphunzitsidwa ndi mtsogoleri wachiyuda wolemekezeka kwambiri, dzina lake Gamaliyeli. (Mac. 5:34; 22:3) Ndipo pa nthawi ina, Paulo anali munthu wofunika kwambiri pakati pa Ayuda. Iye anati: “Ndinali kupita patsogolo kwambiri m’Chiyuda kuposa anzanga ambiri a fuko langa, omwe anali amsinkhu wanga.” (Agal. 1:13, 14; Mac. 26:4) Koma zimenezi sizinachititse Paulo kukhala wodzidalira.

Paulo ankaona zinthu zam’dzikoli, zomwe anthu ena amaziona kuti n’zofunika, ngati “mulu wazinyalala” akaziyerekezera ndi mwayi wokhala wotsatira wa Khristu (Onani ndime 8) *

8. Mogwirizana ndi Afilipi 3:8, kodi Paulo ankaona bwanji zinthu zimene anasiya? Nanga n’chifukwa chiyani ‘ankasangalala ndi kufooka’ kwake?

8 Paulo anasiya zinthu zonse zomwe zinkachititsa anthu a m’dzikoli kumuona kuti ndi wamphamvu. Iye anafika poona zinthu zimene anali nazo poyamba ngati “mulu wa zinyalala.” (Werengani Afilipi 3:8.) Paulo anakumana ndi mavuto ambiri chifukwa chokhala wotsatira wa Khristu. Anthu a mtundu wake ankadana naye. (Mac. 23:12-14) Ndiponso anamenyedwa komanso kumangidwa ndi Aroma anzake. (Mac. 16:19-24, 37) Anazindikiranso kuti ankalephera kuchita zinthu zoyenera chifukwa chakuti anali wochimwa. (Aroma 7:21-25) Koma iye sanalole kuti adani ake komanso zimene ankalakwitsa zimusokoneze. M’malomwake ‘ankasangalala ndi kufooka’ kwake. N’chifukwa chiyani ankasangalala? Chifukwa pamene ankadzimva kuti wafooka m’pamene ankaona mmene Mulungu ankamuthandizira.​—2 Akor. 4:7; 12:10.

9. Kodi tiyenera kuona bwanji zinthu zimene zingachititse kuti tizidziona ngati ofooka?

9 Ngati tikufuna kuti Yehova azitipatsa mphamvu, sitiyenera kuganiza kuti thanzi, maphunziro, chikhalidwe komanso chuma chimene tili nacho n’zimene zimachititsa kuti tikhale ofunika. Zinthu zimenezi sizichititsa munthu kukhala wofunika kwa Yehova. Ndipotu pakati pa anthu a Mulungu si ambiri amene anthu amawaona kuti ndi anzeru, amphamvu komanso si ambiri omwe ali ochokera m’mabanja achifumu. M’malomwake Yehova wasankha kugwiritsa ntchito “zinthu zofooka za dziko.” (1 Akor. 1:26, 27) Choncho simuyenera kudziona kuti simungatumikire Yehova chifukwa choti mulibe zinthu zimene zatchulidwa kumayambiriro kwa ndimeyi. Koma muziona kuti zimenezi zingakupatseni mwayi woona mmene Yehova akukuthandizirani pokupatsani mphamvu. Mwachitsanzo, ngati mumachita mantha ndi anthu amene amatsutsa zimene mumakhulupirira, muzipempha Yehova kuti akuthandizeni kukhala olimba mtima kuti muzitha kuuza ena zimene mumakhulupirira. (Aef. 6:19, 20) Kapena ngati mukudwala matenda aakulu omwe amakulepheretsani kuchita zinthu zina, muzipempha Yehova kuti akupatseni mphamvu zimene zingakuthandizeni kuti muzimutumikira nthawi zonse. Mukaona kuti Yehova akukuthandizani, chikhulupiriro chanu chimalimba ndipo mumakhala amphamvu.

MUZITENGERA ZITSANZO ZA M’BAIBULO

10. N’chifukwa chiyani tiyenera kuphunzira zitsanzo za anthu okhulupirika otchulidwa m’Baibulo monga zimene zinatchulidwa pa Aheberi 11:32-34?

10 Paulo ankakonda kuphunzira Malemba mwakhama. Iye anaphunzira mfundo zambiri kuphatikizapo zitsanzo za atumiki a Yehova okhulupirika zopezeka m’Mawu a Mulungu. M’kalata imene analembera Akhristu a Chiheberi, Paulo anawauza kuti aziganizira zitsanzo za atumiki a Yehova okhulupirika. (Werengani Aheberi 11:32-34.) Mmodzi mwa anthuwa ndi Mfumu Davide. Iye ankatsutsidwa ndi adani ake komanso anthu ena omwe pa nthawi ina anali anzake. Tikamakambirana chitsanzo cha Davide, tiona mmene kuganizira chitsanzochi kunathandizira Paulo komanso zimene tingachite potengera chitsanzo chake.

Davide sanaope kumenyana ndi Goliati ngakhale kuti anali wamng’ono ndipo ankaoneka ngati wopanda mphamvu. Iye anadalira Yehova kuti amupatse mphamvu zogonjetsera Goliati ndipo anamugonjetsadi (Onani ndime 11)

11. N’chiyani chinachititsa kuti Davide azioneka ngati wopanda mphamvu? (Onani chithunzi chapachikuto.)

11 Goliati yemwe anali msilikali wamphamvu ankaona kuti Davide ndi wopanda mphamvu moti atangomuona “anayamba kumuderera.” Goliati anali wamphamvu, anali ndi zida komanso anali wodziwa kumenya nkhondo. Pamene Davide anali kamnyamata komwe kanali kasanamenyepo nkhondo ndipo ankaoneka ngati alibe zida zokwanira. Koma zoona zake n’zakuti iye anali wamphamvu. Tikutero chifukwa Davide anadalira Yehova kuti amupatse mphamvu ndipo anagonjetsa mdani wakeyo.​—1 Sam. 17:41-45, 50.

12. Kodi Davide anakumananso ndi vuto lina liti?

12 Davide anakumananso ndi vuto lina lomwe likanamuchititsa kuti azidziona kuti ndi wofooka komanso wopanda mphamvu. Iye ankatumikira mokhulupirika Sauli, yemwe anali mfumu ya Isiraeli. Poyamba Sauli ankalemekeza Davide. Koma kenako, kunyada kunamuchititsa kuti azichitira nsanje Davide, moti anayamba kumuchitira zoipa komanso ankafuna kumupha.​—1 Sam. 18:6-9, 29; 19:9-11.

13. Kodi Davide anatani pamene Sauli ankamuchitira zinthu zopanda chilungamo?

13 Ngakhale Sauli ankamuchitira zinthu zopanda chilungamo, Davide anapitiriza kumulemekeza chifukwa ankadziwa kuti Sauliyo ndi mfumu yosankhidwa ndi Yehova. (1 Sam. 24:6) Davide sankaimba mlandu Yehova chifukwa cha zoipa zimene Sauli ankamuchitira. M’malomwake, Davide ankadalira Yehova kuti amupatse mphamvu kuti athe kupirira mayesero ovutawa.​—Sal. 18:1, timawu tapamwamba.

14. Mofanana ndi Davide, kodi Paulo anakumana ndi mavuto otani?

14 Mtumwi Paulo nayenso anakumana ndi mavuto ofanana ndi omwe Davide anakumana nawo. Anthu amene ankadana ndi Paulo anali amphamvu kuposa iyeyo. Atsogoleri achipembedzo komanso andale ankadana naye. Nthawi zambiri ankalamula kuti anthu amumenye komanso kumutsekera m’ndende. Mofanana ndi Davide, Paulo nayenso ankachitiridwa zinthu zopanda chilungamo ndi anthu omwe pa nthawi ina anali anzake. Ngakhalenso anthu ena mumpingo wa Chikhristu ankamutsutsa. (2 Akor. 12:11; Afil. 3:18) Koma Paulo anagonjetsa adani ake onse. Kodi anachita bwanji zimenezi? Iye sanasiye kulalikira ngakhale kuti ankamutsutsa. Komanso sanasiye kukonda abale ndi alongo ake ngakhale kuti nthawi zina ankamukhumudwitsa. Koma chofunika kwambiri n’choti Paulo anakhalabe wokhulupirika kwa Mulungu kwa moyo wake wonse. (2 Tim. 4:8) Iye anakwanitsa kuchita zimenezi chifukwa sankadalira mphamvu zake koma ankadalira Yehova.

Muzichita zinthu mwaulemu komanso mokoma mtima mukamakambirana ndi anthu amene amatsutsa zimene mumakhulupirira (Onani ndime 15) *

15. Kodi cholinga chathu chiyenera kukhala chiyani, ndipo tingachikwaniritse bwanji?

15 Kodi nanunso mumafunika kupirira mukamanyozedwa kapena kuzunzidwa ndi anzanu akusukulu, omwe mumagwira nawo ntchito kapena achibale anu omwe si Mboni? Kodi munthu wina wa mumpingo anayamba wakuchitirani zinthu zopanda chilungamo? Ngati ndi choncho, musamaiwale chitsanzo cha Davide komanso Paulo. Mukhoza kupitiriza “kugonjetsa choipa mwa kuchita chabwino.” (Aroma 12:21) Anthu ena akamatitsutsa, sitimenyana nawo ngati mmene anachitira Davide pamene ankamenyana ndi Goliati. M’malomwake cholinga chathu ndi choti tizigonjetsa choipa poyesetsa kuthandiza anthu kuphunzira Mawu a Mulungu. Mungakwanitse cholinga chimenechi mukamagwiritsa ntchito Baibulo poyankha mafunso a anthu, mukamalemekeza komanso kusonyeza chifundo anthu amene amakuchitirani zoipa ndiponso mukamachitira zabwino anthu onse, ngakhale adani anu.​—Mat. 5:44; 1 Pet. 3:15-17.

MUZILOLA KUTHANDIZIDWA NDI ENA

16-17. Kodi Paulo sanaiwale chiyani?

16 Mtumwi Paulo asanakhale Mkhristu, anali munthu wachipongwe ndipo ankazunza otsatira a Yesu. (Mac. 7:58; 1 Tim. 1:13) Yesu analetsa Paulo, yemwe pa nthawiyo ankadziwika kuti Saulo, kuti asamazunze mpingo wa Chikhristu. Ali kumwamba, Yesu analankhula ndi Paulo ndipo anamuchititsa khungu. Kuti ayambirenso kuona, Paulo ankafunika kuthandizidwa ndi anthu omwe ankawazunza aja. Iye anadzichepetsa n’kulolera kuthandizidwa ndi Hananiya kuti ayambirenso kuona.​—Mac. 9:3-9, 17, 18.

17 Kenako Paulo anakhala munthu wodziwika bwino mumpingo wa Chikhristu. Koma sanaiwale zimene Yesu anamuphunzitsa panjira yopita ku Damasiko. Paulo anapitiriza kukhala wodzichepetsa ndipo ankalola kuti abale ndi alongo azimuthandiza. Iye ananena za Akhristu anzake ena kuti anamuthandiza komanso kumulimbikitsa.​—Akol. 4:10, 11.

18. N’chiyani chingachititse kuti nthawi zina tizivutika kulola kuti anthu ena atithandize?

18 Kodi tingaphunzire chiyani kuchokera kwa Paulo? Titangoyamba kumene kuphunzira choonadi, tinkafunitsitsa kuti anthu ena azitithandiza chifukwa tinkadziwa kuti sitidziwa zambiri. (1 Akor. 3:1, 2) Nanga bwanji panopa? N’kutheka kuti takhala tikutumikira Yehova kwa zaka zambiri ndipo tikudziwa zinthu zochuluka. Nthawi zina zimenezi zingachititse kuti tizivutika kulola kuti ena atithandize, makamaka ngati munthu amene akutithandizayo wangophunzira kumene choonadi. Komatu nthawi zambiri Yehova amagwiritsa ntchito abale ndi alongo athu kuti atilimbikitse. (Aroma 1:11, 12) Choncho ngati tikufuna kuti Yehova azitipatsa mphamvu, tiyenera kulola kuti abale ndi alongo athu azitithandiza.

19. Kodi n’chiyani chinathandiza Paulo kuti akwanitse kuchita zinthu zambiri?

19 Paulo anakwanitsa kuchita zinthu zambiri atakhala Mkhristu. Kodi n’chiyani chinamuthandiza? Iye anazindikira kuti mphamvu, maphunziro, chuma komanso kumene anachokera sizingathandize munthu kuchita zinthu zabwino. Chofunika kwambiri ndi kudzichepetsa komanso kudalira Yehova. Tiyeni tiziyesetsa kutsanzira Paulo (1) podalira Yehova, (2) kuphunzira kuchokera kwa anthu otchulidwa m’Baibulo komanso (3) polola kuti Akhristu anzathu azitithandiza. Tikatero, Yehova adzatipatsa mphamvu ngakhale zitakhala kuti timadziona kuti ndife ofooka kapena kuti opanda mphamvu.

NYIMBO NA. 71 Ndife Gulu Lankhondo la Yehova

^ ndime 5 Munkhaniyi, tikambirana chitsanzo cha mtumwi Paulo. Tiona kuti tikakhala odzichepetsa, Yehova adzatipatsa mphamvu zomwe zingatithandize kupirira tikamanyozedwa. Adzatipatsanso mphamvu pamene tikuona kuti tafooka.

^ ndime 1 TANTHAUZO LA MAWU ENA: Tikhoza kumadziona kuti ndife ofooka pazifukwa zosiyanasiyana. Mwachitsanzo, tingamadzione chonchi chifukwa ndife anthu ochimwa, osauka, tikudwala kapena sitinapite patali ndi maphunziro. Kuwonjezera pamenepo, adani athu angatichititse kumadziona ngati achabechabe potinyoza kapena kutizunza.

^ ndime 57 MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI: Paulo atayamba kulalikira za Khristu, anasiya zinthu zonse zimene ankagwiritsa ntchito ali Mfarisi. Zinthu zimenezi zikuphatikizapo mipukutu yomwe ankagwiritsa ntchito komanso choikamo mipukutu.

^ ndime 61 MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI: M’bale akukakamizidwa ndi anzake akuntchito kuti achite nawo phwando lokondwerera tsiku lokumbukira kubadwa kwa munthu amene amagwira naye ntchito.