Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 31

Kodi Mukuyembekezela “Mzinda Wokhala Ndi Maziko Eni-eni”?

Kodi Mukuyembekezela “Mzinda Wokhala Ndi Maziko Eni-eni”?

“Anali kuyembekezela mzinda wokhala ndi maziko enieni, mzinda umene Mulungu ndiye anaumanga ndi kuupanga.”—AHEB. 11:10.

NYIMBO 22 Ufumu Ulamulila—Ubwele!

ZIMENE TIKAMBILANE *

1. Kodi Akhristu ambili acita zinthu zotani zoonetsa kudzimana? Nanga n’cifukwa ciani acita zimenezo?

MASIKU ano, anthu a Mulungu mamiliyoni amadzimana zinthu zosiyana-siyana. Mwacitsanzo, abale na alongo ambili asankha kusakhala pabanja. Ndipo ena amene ali pabanja asankha kusakhala ndi ana palipano. Komanso mabanja ena asankha kukhala na umoyo wosalila zambili. Pali cifukwa cimodzi cacikulu cimene Akhristu onsewa anapangila zosankha zimenezi. Cifukwa cake n’cakuti afuna kucita zambili potumikila Yehova mmene angathele. Iwo ni osangalala, ndipo amakhulupilila kuti Yehova adzawapatsa zonse zofunikila pa umoyo wawo. Kodi n’zoona kuti Yehova adzawapatsa zofunikila? Inde. N’cifukwa ciani tayankha motsimikiza conco? Cifukwa cimodzi n’cakuti Yehova anadalitsa Abulahamu, “tate wa onse . . . okhala ndi cikhulupililo.”—Aroma 4:11.

2. (a) Malinga na Aheberi 11:8-10, 16, n’cifukwa ciani Abulahamu analolela kusiya mzinda wa Uri? (b) Tikambilana ciani m’nkhani ino?

2 Abulahamu analolela kusiya umoyo wofewa umene anali nawo mu mzinda wa Uri. Cifukwa ciani? Cifukwa anali kuyembekezela “mzinda wokhala ndi maziko enieni.” (Ŵelengani Aheberi 11:8-10, 16.) Kodi “mzinda” umenewo n’ciani? Kodi Abulahamu anakumana na mavuto otani pamene anali kuyembekezela kuti mzindawo umangidwe? Nanga tingatengele bwanji citsanzo ca Abulahamu ndi ca Akhristu ena amakono amene atengela citsanzo cake?

KODI “MZINDA WOKHALA NDI MAZIKO ENIENI” N’CIANI?

3. Kodi mzinda umene Abulahamu anali kuyembekezela n’ciani?

3 Mzinda umene Abulahamu anali kuyembekezela ni Ufumu wa Mulungu. Amene adzalamulila mu Ufumu umenewo ni Yesu Khristu komanso Akhristu odzozedwa okwana 144,000. Paulo anakamba kuti Ufumu umenewo ni “mzinda wa Mulungu wamoyo, Yerusalemu wakumwamba.” (Aheb. 12:22; Chiv. 5:8-10; 14:1) Yesu anaphunzitsa ophunzila ake kuti azipemphela kuti Ufumu umenewo ubwele, n’colinga cakuti cifunilo ca Mulungu cicitike pano padziko lapansi, monga mmene zilili kumwamba.—Mat. 6:10.

4. Kulingana na Genesis 17:1, 2, 6, ni zinthu ziti zimene Abulahamu anali kudziŵa ponena za mzinda, kapena kuti Ufumu umene Mulungu analonjeza?

4 Kodi Abulahamu anali kudziŵa mmene Ufumu wa Mulungu udzakhalila? Iyai. Kwa zaka mahandiledi ambili, nkhani imeneyi inali “cinsinsi copatulika.” (Aef. 1:8-10; Akol. 1:26, 27) Koma Abulahamu anali kudziŵa kuti ena mwa mbadwa zake adzakhala mafumu. N’zimene Yehova anamulonjeza. (Ŵelengani Genesis 17:1, 2, 6.) Abulahamu anali kukhulupilila kwambili malonjezo a Mulungu, moti zinali ngati kuti akuona Wodzozedwa wa Mulungu kapena kuti Mesiya, amene anali kudzakhala Mfumu mu Ufumu wa Mulungu. N’cifukwa cake Yesu anauza Ayuda a m’nthawi yake kuti: “Atate wanu Abulahamu anali wosangalala poyembekezela kuona tsiku langa, ndipo analiona moti anakondwela.” (Yoh. 8:56) Conco, n’zoonekelatu kuti Abulahamu anali kudziŵa kuti mbadwa zake zidzalamulila mu Ufumu umene Yehova adzakhazikitsa. Ndipo anayembekezela lonjezo la Yehova limenelo moleza mtima.

Kodi Abulahamu anaonetsa bwanji kuti anali kukhulupilila malonjezo a Yehova? (Onani ndime 5)

5. Tidziŵa bwanji kuti Abulahamu anali kuyembekezela mzinda wokhazikitsidwa na Mulungu?

5 Kodi Abulahamu anaonetsa bwanji kuti anali kuyembekezela mzinda, kapena kuti Ufumu wokhazikitsidwa na Mulungu? Coyamba, iye sanakhale nzika ya ufumu uliwonse pano padziko lapansi. Abulahamu anali kusamuka-samuka. Anasankha kusakhala pamalo amodzi, ndiponso sanacilikize mfumu iliyonse ya umunthu. Kuwonjezela apo, iye sanayese kukhazikitsa ufumu wake-wake. M’malomwake, anapitiliza kumvela Yehova na kumuyembekezela kuti adzakwanilitsa lonjezo lake. Mwa kucita zimenezi, Abulahamu anaonetsa kuti anali na cikhulupililo cacikulu mwa Yehova. Tsopano, tiyeni tikambilane mavuto ena amene iye anakumana nawo, na kuona zimene tingaphunzilepo pa citsanzo cake.

KODI ABULAHAMU ANAKUMANA NA MAVUTO OTANI?

6. Fotokozani mmene mzinda wa Uri unalili.

6 Abulahamu anasiya mzinda wa Uri, umene unali wotetezeka ndiponso wabwino. Anthu kumeneko anali ophunzila komanso olemela. Mzindawo unali wotetezeka cifukwa unali na mpanda waukulu komanso ngalande yakuya ya madzi kumbali zitatu za mpandawo. Anthu mumzinda wa Uri anali akatswili pa zolemba-lemba na masamu. Zioneka kuti mzinda umenewo unali likulu la zamalonda, cifukwa ofukula za m’matongwe, anapeza makalata ambili a zamalonda pamalo amene panali mzindawo. Nyumba za mumzindawo zinali zanchelwa, zoikidwa pulasta, komanso zopakidwa laimu. Zina mwa nyumbazo zinali na zipinda 13 kapena 14, ndipo payadi pake panali poyalidwa miyala yomangidwa bwino.

7. N’cifukwa ciani Abulahamu anafunika kudalila Yehova kuti adzamuteteza pamodzi na banja lake?

7 Abulahamu anafunika kudalila Yehova kuti adzamuteteza pamodzi na banja lake. Cifukwa ciani? Kumbukilani kuti iye na Sara anasiya nyumba yabwino komanso yotetezeka mu mzinda wa Uri, n’kukakhala ku dela la kumidzi ku Kanani. Kumeneko, Abulahamu na banja lake sanalinso otetezeka cifukwa kunalibe mipanda kapena ngalande zakuya zamadzi. Apa zinali zosavuta adani kuwaukila.

8. Kodi Abulahamu panthawi ina anakumana na vuto lotani?

8 Abulahamu anali kucita cifunilo ca Mulungu. Ngakhale n’conco, pa nthawi ina anasoŵa cakudya copatsa banja lake. Anavutika na njala yoopsa imene inagwa m’dziko la Kanani limene Yehova anamuuza kuti akakhalemo. Njalayo inafika poipa kwambili moti Abulahamu anasamuka pamodzi na banja lake n’kukakhala ku Iguputo kwa kanthawi. Koma ali kumeneko, wolamulila wa dzikolo Farao, anatenga mkazi wa Abulahamu kuti akhale wake. Tangoganizilani nkhawa imene Abulahamu anali nayo. Koma nkhawa imeneyo inatha pamene Yehova analamula Farao kuti abweze Sara kwa Abulahamu.—Gen. 12:10-19.

9. Ni mavuto ati a m’banja amene Abulahamu anakumana nawo?

9 Cinanso, m’banja la Abulahamu munali mavuto. Mkazi wake wokondedwa Sara sanali kubeleka. Kwa zaka zambili, iwo anangolipilila vuto limeneli. Potsilizila pake, Sara anapeleka mdzakazi wake Hagara kwa Abulahamu kuti awabelekele ana. Koma Hagara atakhala na pakati pa Isimaeli, anayamba kupeputsa Sara. Zinthu zinafika povuta kwambili cakuti Sara anathamangitsa Hagara panyumbapo.—Gen. 16:1-6.

10. Ni zocitika ziti zokhudza Isimaeli na Isaki zimene zikanapangitsa kuti cikhale covuta kwa Abulahamu kukhulupilila Yehova?

10 Pamapeto pake, Sara anakhala na pakati, ndipo anabelekela Abulahamu mwana wamwamuna amene anamucha Isaki. Abulahamu anali kuwakonda ana ake onse aŵili, Isimaeli na Isaki. Koma cifukwa cakuti Isimaeli anali kucitila nkhanza Isaki, Abulahamu anakakamizika kucotsa Isimaeli na Hagara panyumbapo. (Gen. 21:9-14) Patapita zaka zambili, Yehova analamula Abulahamu kuti amupeleke nsembe Isaki. (Gen. 22:1, 2; Aheb. 11:17-19) Pa zocitika zonsezi, Abulahamu anali kukhulupilila kuti Yehova adzakwanilitsa zimene analonjeza zokhudza ana ake.

11. N’cifukwa ciani Abulahamu anafunika kuyembekezela Yehova moleza mtima?

11 Panthawi yonseyi, Abulahamu anaphunzila kuyembekezela Yehova moleza mtima. Iye ayenela kuti anali na zaka zoposa 70 pamene anacoka mumzinda wa Uri pamodzi na banja lake. (Gen. 11:31–12:4) Ndipo kwa zaka pafupi-fupi 100, anali kukhala m’matenti m’madela osiyana-siyana a dziko la Kanani. Abulahamu anamwalila ali na zaka 175. (Gen. 25:7) Koma iye sanaone kukwanilitsidwa kwa lonjezo la Yehova lakuti adzapeleka dziko limene anayendamo kwa mbadwa zake. Ndipo anafa asanaone mzinda kapena kuti Ufumu umene Mulungu anakhazikitsa. Ngakhale n’conco, Malemba amati Abulahamu anamwalila ali “wokalamba, . . . ndi wokhutila.” (Gen. 25:8) Ngakhale kuti iye anakumana na mavuto ambili, anakhalabe na cikhulupililo colimba ndiponso anayembekezela Yehova mwacimwemwe. Kodi anakwanitsa bwanji kupilila? Anakwanitsa cifukwa pa umoyo wake wonse, Yehova anali kumuteteza na kumusamalila monga bwenzi lake.—Gen. 15:1; Yes. 41:8; Yak. 2:22, 23.

Mofanana na Abulahamu na Sara, kodi atumiki a Mulungu amaonetsa bwanji cikhulupililo na kuleza mtima? (Onani ndime 12) *

12. Kodi tikuyembekezela ciani? Nanga tikambilana ciani tsopano?

12 Mofanana na Abulahamu, nafenso tikuyembekezela mzinda wokhala na maziko eni-eni. Komabe, sitikuyembekezela kumangidwa kwa mzindawo cifukwa Ufumu wa Mulungu unakhazikitsidwa kale mu 1914, ndipo pano tikamba ukulamulila kumwamba. (Chiv. 12:7-10) Cimene tikuyembekezela n’cakuti uyambe kulamulila pano padziko lapansi. Koma pamene tikuyembekezela zimenezi, pali mavuto osiyana-siyana amene tifunika kuwapilila, ofanana na amene Abulahamu na Sara anakumana nawo. Masiku ano, atumiki a Yehova osiyana-siyana akwanitsa kutengela citsanzo ca Abulahamu. Nkhani za mutu wakuti “Mbili Yanga” za mu Nsanja ya Mlonda zionetsa kuti mofanana na Abulahamu na Sara, masiku ano atumiki a Yehova ambili aonetsa cikhulupililo na kuleza mtima poyembekezela Yehova. Lomba tiyeni tikambilaneko zina mwa nkhani zimenezi na kuona zimene tingaphunzilepo.

ANTHU ENA AMENE ANATENGELA CITSANZO CA ABULAHAMU

M’bale Bill Walden anadzimana zinthu zina, ndipo Yehova anam’dalitsa

13. Kodi mwaphunzilapo ciani pa citsanzo ca M’bale Walden?

13 Khalani okonzeka kudzimana zinthu zina. Kuti tiike mzinda wa Mulungu, kapena kuti Ufumu wake patsogolo mu umoyo wathu, tifunika kukhala monga Abulahamu, amene anadzimana zinthu zina popanda kudandaula kuti akondweletse Mulungu. (Mat. 6:33; Maliko 10:28-30) Ganizilani citsanzo ici ca m’bale Bill Walden. * Mu 1942, iye atatsala pang’ono kutenga digiri yake ya maphunzilo a zomanga-manga pa yunivesite inayake ku America, anayamba kuphunzila Baibo na Mboni za Yehova. Panthawiyo, mmodzi wa aphunzitsi ake pa yunivesiteyo anamupezela nchito ya malipilo apamwamba yoti azikagwila akatsiliza maphunzilo ake, koma iye anakana. Bill anakamba kuti anakana nchitoyo n’colinga cakuti acite zambili potumikila Mulungu. Pasanapite nthawi yaitali, boma linam’lamula kuti aloŵe usilikali. Mwaulemu iye anakana, ndipo pa cifukwa cimeneci anamuweluza kuti apeleke ndalama zokwana madola 10,000, ndiponso kuti akapike jele zaka zisanu. Koma patapita zaka zitatu, anatulutsidwa m’ndendemo. Patapita nthawi, anaitanidwa ku Sukulu ya Giliyadi, ndipo pambuyo pake anatumikila monga mmishonale mu Africa. Bill anakwatila mlongo Eva, ndipo anatumikila limodzi mu Africa. Pocita utumiki wawo, iwo anali kudzimana zinthu zina. M’kupita kwa nthawi, anabwelela ku America kukasamalila amayi ake a Bill. Potsiliza kufotokoza mbili ya moyo wake, Bill anati: “Nimasangalala kwambili nikaganizila mwayi umene nakhala nawo wogwilitsidwa nchito na Yehova kwa zaka zoposa 70. Nimamuthokoza cifukwa conilola kumutumikila kwa moyo wanga wonse.” Kodi mungadzipeleke kucita utumiki wa nthawi zonse monga nchito yaikulu pa umoyo wanu?

Eleni na Aristotelis Apostolidis anaona kuti Yehova anali kuwapatsa mphamvu

14-15. Mwaphunzilapo ciani pa citsanzo ca M’bale na Mlongo Apostolidis?

14 Musayembekezele kukhala na umoyo wopanda mavuto. Pa citsanzo ca Abulahamu tiphunzilapo kuti ngakhale anthu amene atumikila Yehova kwa moyo wawo wonse amakumananso na mavuto. (Yak. 1:2; 1 Pet. 5:9) Mwacitsanzo, ganizilani zimene zinacitikila m’bale Aristotelis Apostolidis. * Iye anabatizika mu 1946 ku Greece, ndipo mu 1952 anatomela mlongo Eleni, amene anali na zolinga zofanana na zake. Komabe, Eleni anadwala, ndipo anamupeza na cotupa mu ubongo. Cotupaco anacicotsa, koma patangopita zaka zocepa kucokela pamene anakwatilana, cinamelanso. Madokotala anamucitanso opaleshoni. Koma izi zinacititsa kuti ziwalo zake zina zileke kugwila nchito bwino, moti anali kulephela kukamba bwino-bwino. Mosasamala kanthu za matenda komanso cizunzo cimene cinalipo panthawiyo, mlongo Eleni anakhalabe wacangu pa nchito yolalikila.

15 M’bale Aristotelis anasamalila mkazi wakeyo kwa zaka 30. Panthawi imeneyi, iye anali kutumikila monga mkulu, komanso anatumikilapo m’komiti yoyang’anila misonkhano yacigawo. Anagwilakonso nchito yomanga Bwalo la Misonkhano. Ndiyeno, mu 1987, Eleni anavulala pa ngozi pamene anali kulalikila. Iye anakhala cikomokele kwa zaka zitatu, ndipo pambuyo pake anamwalila. Kumapeto kwa nkhani yofotokoza mbili yake, M’bale Aristotelis anati: “Kwa zaka zonsezi, mavuto na zocitika zadzidzidzi zinafuna kupilila na kulimbikila kwambili. Komabe, nthaŵi zonse Yehova wakhala akunipatsa mphamvu zimene n’nafunikila kuti nithane na mavuto amenewa.” (Sal. 94:18, 19) Ndithudi! Yehova amakonda atumiki ake amene amacita zonse zimene angathe pom’tumikila, olo kuti akukumana na mavuto.

Audrey Hyde sanataye ciyembekezo cifukwa anasumika maganizo ake pa madalitso akutsogolo

16. Ni malangizo ati othandiza amene M’bale Knorr anapatsa mkazi wake?

16 Muziika maganizo anu pa madalitso akutsogolo. Abulahamu anasumika maganizo pa madalitso akutsogolo amene Yehova anamulonjeza. Izi zinamuthandiza kupilila mavuto amene anali kukumana nawo. Mofanana na Abulahamu, Mlongo Audrey Hyde * anayesetsa kusumika maganizo ake pa madalitso akutsogolo. Sanataye ciyembekezo olo kuti mwamuna wake woyamba, M’bale Nathan H. Knorr, anamwalila na matenda a khansa, ndipo mwamuna wake waciŵili, Glenn Hyde, anadwala matenda enaake oopsa a mu ubongo. Iye anakamba kuti cimene cinamulimbikitsa ni mawu amene M’bale Knorr anamuuza kutatsala mawiki angapo kuti amwalile. Mlongoyu anati: “Nathan ananiuza kuti: ‘Tikamwalila, ciyembekezo cathu sicikhalanso cokayikitsa, ndipo zikatelo ndiye kuti sitidzamvanso ululu ayi.’ Kenako ananilimbikitsa kuti: ‘Uziganizila za m’tsogolo cifukwa mphoto yako ili m’tsogolo.’ . . . Ndiye anawonjezela kuti: ‘Uzionetsetsa kuti uli ndi cocita nthaŵi zonse, uziyesetsa kugwilitsila nchito moyo wako kuthandiza anthu ena. Zimenezi zidzakuthandiza kusangalala na moyo.’” Kukamba zoona, malangizo akuti tiyenela kuyesetsa kucitila ena zabwino na ‘kukondwela ndi ciyembekezo’ ni othandiza kwambili.—Aroma 12:12.

17. (a) Kodi tili na cifukwa canji comveka cosumikila maganizo athu pa madalitso akutsogolo? (b) Kodi kutengela citsanzo ca pa Mika 7:7 kungatithandize bwanji kuti tidzalandile madalitso akutsogolo?

17 Kuposa kale lonse, masiku ano tili na cifukwa comveka cosumikila maganizo athu pa madalitso akutsogolo. Zocitika padzikoli zionetselatu kuti tili kumapeto kweni-kweni kwa masiku otsiliza a dziko loipali. Posacedwapa, mzinda wokhala na maziko eni-eni, kapena kuti Ufumu wa Mulungu, udzayamba kulamulila dziko lonse lapansi. Limodzi mwa madalitso amene tidzasangalala nawo panthawiyo, ni kuona okondedwa athu akuukitsidwa. Panthawiyo, Yehova adzadalitsa Abulahamu cifukwa ca cikhulupililo cake na kuleza mtima kwake, mwa kumuukitsa pamodzi na banja lake kuti akhale na moyo pano padziko lapansi. Kodi mudzakhalamo kuti mukawalandile? Mudzakhalamo ngati mofanana na Abulahamu, ndimwe okonzeka kudzimana zinthu zina kaamba ka Ufumu wa Mulungu, ngati mukhalabe na cikhulupililo olo kuti mukumana na mavuto, komanso ngati muyesetsa kuyembekezela Yehova moleza mtima.—Ŵelengani Mika 7:7.

NYIMBO 74 Imbani Nafe Nyimbo ya Ufumu!

^ ndime 5 Kuyembekezela kukwanilitsika kwa malonjezo a Mulungu kungayese kuleza mtima kwathu, ngakhalenso cikhulupililo cathu. Kodi ni mfundo zotani zimene tingaphunzile pa citsanzo ca Abulahamu, zimene zingatithandize kuti tiziyembekezela moleza mtima malonjezo a Yehova? Nanga tingaphunzile ciani pa zitsanzo zabwino za atumiki a Yehova amakono?

^ ndime 13 Nkhani yofotokoza mbili ya M’bale Walden inafalitsidwa mu Nsanja ya Olonda ya December 1, 2013, mape. 8-10.

^ ndime 14 Nkhani yofotokoza mbili ya M’bale Apostolidis inafalitsidwa mu Nsanja ya Olonda ya February 1, 2002, mape. 24-28.

^ ndime 16 Nkhani yofotokoza mbili ya Mlongo Hyde inafalitsidwa mu Nsanja ya Mlonda ya July 1, 2004, mape. 23-29.

^ ndime 56 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: M’bale na mkazi wake, amene ni okalamba, akupitiliza kutumikila Yehova mokhulupilika olo kuti amakumana na mavuto. Amalimbitsa cikhulupililo cawo mwa kusumika maganizo awo pa malonjezo a Yehova.