NKHANI YOPHUNZIRA 31

Kodi Mukuyembekezera “Mzinda Wokhala ndi Maziko Enieni”?

Kodi Mukuyembekezera “Mzinda Wokhala ndi Maziko Enieni”?

“Anali kuyembekezera mzinda wokhala ndi maziko enieni, mzinda umene Mulungu ndiye anaumanga ndi kuupanga.”​AHEB. 11:10.

NYIMBO NA. 22 Ufumu Umene Ukulamulira Kumwamba Ubwere

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1. Kodi anthu a Mulungu ambiri amadzimana zinthu ziti, ndipo n’chifukwa chiyani amachita zimenezi?

ANTHU a Mulungu ambiri masiku ano ali ndi mtima wodzimana. Abale ndi alongo ambiri anasankha kuti asakhale pabanja ndipo ena omwe ali pabanja anasankha kuti asakhale ndi ana. Palinso mabanja ochuluka omwe amakhala moyo wosalira zambiri. Onsewa anasankha zimenezi chifukwa amafuna kuti azichita zambiri potumikira Yehova. Iwo amakhutira ndi zimene ali nazo komanso amadalira kuti Yehova aziwapatsa zimene akufunikira. Kodi anthuwa angadzanong’oneze bondo ndi zimene anasankhazi? Ayi. Tikudziwa zimenezi chifukwa kale Yehova ankapatsa atumiki ake zofunika pa moyo. Mwachitsanzo, anadalitsa Abulahamu yemwe ndi “tate wa onse . . . okhala ndi chikhulupiriro.”​—Aroma 4:11.

2. (a) Mogwirizana ndi Aheberi 11:8-10, 16, n’chifukwa chiyani Abulahamu analolera kuchoka ku Uri? (b) Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?

2 Abulahamu analolera kusiya moyo wabwino kwambiri umene anali nawo mumzinda wa Uri. N’chifukwa chiyani anachita zimenezi? Chifukwa ankayembekezera “mzinda wokhala ndi maziko enieni.” (Werengani Aheberi 11:8-10, 16.) Kodi “mzinda” umenewu ndi chiyani? Kodi Abulahamu anakumana ndi mavuto otani pamene ankayembekezera kuti mzindawu umangidwe? Nanga tingatsanzire bwanji Abulahamu komanso atumiki ena a masiku ano omwe amatsatira chitsanzo chake?

KODI “MZINDA WOKHALA NDI MAZIKO ENIENI” NDI CHIYANI?

3. Kodi “mzinda” umene Abulahamu ankayembekezera ndi chiyani?

3 Mzinda umene Abulahamu ankayembekezerawu ndi Ufumu wa Mulungu. Yesu Khristu komanso Akhristu odzozedwa okwana 144,000 ndi amene ali olamulira a Ufumuwu. Paulo anatchula Ufumu umenewu kuti ndi “mzinda wa Mulungu wamoyo, Yerusalemu wakumwamba.” (Aheb. 12:22; Chiv. 5:8-10; 14:1) Yesu anaphunzitsa ophunzira ake kuti azipempherera Ufumuwu kuti ubwere kuti chifuniro cha Mulungu chichitike padziko lapansi ngati mmene chikuchitikira kumwamba.​—Mat. 6:10.

4. Mogwirizana ndi Genesis 17:1, 2, 6, kodi Abulahamu ankadziwa zinthu zochuluka bwanji zokhudza mzinda, kapena kuti Ufumu, umene Yehova analonjeza?

4 Kodi Abulahamu ankadziwa mmene Ufumu wa Mulungu udzakhalire? Ayi. Tikutero chifukwa kwa zaka zambiri nkhani yokhudza Ufumu wa Mulungu inali “chinsinsi chopatulika.” (Aef. 1:8-10; Akol. 1:26, 27) Koma Abulahamu ankadziwa kuti ena mwa ana ake adzakhala mafumu chifukwa Yehova anali atamulonjeza kale zimenezi. (Werengani Genesis 17:1, 2, 6.) Abulahamu ankakhulupirira kwambiri zimene Mulungu anamulonjezazi moti ankatha kuona Wodzozedwayo, kapena kuti Mesiya, yemwe anadzakhala Mfumu ya Ufumu wa Mulungu. N’chifukwa chake Yesu anauza Ayuda kuti: “Atate wanu Abulahamu anali wosangalala poyembekezera kuona tsiku langa, ndipo analiona moti anakondwera.” (Yoh. 8:56) N’zoonekeratu kuti Abulahamu ankadziwa kuti ena mwa ana ake adzakhala mafumu mu Ufumu umene Mulungu adzakhazikitse ndipo ankayembekezera kuti Yehova adzakwaniritse zimene anamulonjeza.

Kodi Abulahamu anasonyeza bwanji kuti ankakhulupirira malonjezo a Yehova? (Onani ndime 5)

5. Kodi tikudziwa bwanji kuti Abulahamu ankayembekezera “mzinda” womwe Mulungu anakhazikitsa?

5 Kodi Abulahamu anasonyeza bwanji kuti ankayembekezera “mzinda” kapena Ufumu wokhazikitsidwa ndi Mulungu? Iye sanakhale nzika ya ufumu uliwonse wapadziko lapansi komanso ankakhala moyo woyendayenda ndipo sanali mbali ya ufumu uliwonse. Kuwonjezera apo, Abulahamu sanayese kukhazikitsa ufumu wake. M’malomwake anapitiriza kumvera Yehova kwinaku akuyembekezera kuti adzakwaniritse zomwe anamulonjeza. Zimene anachitazi zinasonyeza kuti ankakhulupirira kwambiri Yehova. Tsopano tiyeni tikambirane mavuto amene Abulahamu anakumana nawo komanso zimene tingaphunzire kwa iye.

KODI ABULAHAMU ANAKUMANA NDI MAVUTO OTANI?

6. Kodi mzinda wa Uri unali wotani?

6 Abulahamu anachoka mumzinda wa Uri womwe unali wotetezeka komanso wotukuka ndipo anthu ake anali ophunzira komanso olemera. Mzindawu unkatetezedwa ndi mipanda italiitali komanso ngalande zikuluzikulu zamadzi. Anthu amumzinda wa Uri ankadziwa bwino kulemba komanso masamu. Zikuoneka kuti anthu amumzindawu ankachitanso malonda chifukwa ofufuza zinthu zakale anapeza zikalata zimene ankagwiritsa ntchito pochita malonda. Nyumba za anthu zinali zanjerwa ndipo ankazipanga pulasitala komanso kuzipaka laimu. Nyumba zina zinkakhala ndi zipinda 13 kapena 14 ndipo pakati pake pankakhala bwalo lokonzedwa bwino ndi miyala.

7. N’chifukwa chiyani Abulahamu ankafunika kukhulupirira kuti Yehova adzamuteteza limodzi ndi banja lake?

7 Abulahamu ankafunika kukhulupirira kuti Yehova adzamuteteza limodzi ndi banja lake. Tikutero chifukwa paja iye ndi mkazi wake anachoka mumzinda umene unali wotetezeka komanso anasiya nyumba yabwino n’kumakakhala m’matenti ku Kanani. Iwo sankatetezedwanso ndi mipanda italiitali komanso ngalande zikuluzikulu zamadzi. M’malomwake anali osatetezeka ndipo adani awo akanatha kuwaukira mosavuta.

8. Kodi pa nthawi ina, Abulahamu anakumana ndi mavuto otani?

8 Abulahamu ankachita chifuniro cha Mulungu koma nthawi ina banja lake linalibe chakudya chokwanira. M’dziko limene Yehova anamuuza kuti akakhale munagwa njala yaikulu. Njalayi inavuta kwambiri moti Abulahamu ndi banja lake anaganiza zosamukira ku Iguputo. Koma ali ku Iguputoko, Farao yemwe anali wolamulira wadzikolo, anamulanda mkazi. Taganizirani nkhawa imene Abulahamu anali nayo mpaka pamene Yehova analowererapo n’kuchititsa kuti Farao amubwezere mkazi wakeyo.​—Gen. 12:10-19.

9. Kodi Abulahamu anakumana ndi mavuto otani m’banja mwake?

9 Abulahamu anakumananso ndi mavuto m’banja mwake. Mkazi wake Sara anali wosabereka. Vutoli linachititsa kuti asamasangalale kwa zaka zambiri. Kenako Sara anapereka kapolo wake Hagara kwa Abulahamu kuti awaberekere ana. Koma Hagara ali ndi pakati pa Isimaeli, anayamba kuchitira chipongwe Sara. Zinthu zinafika poipa kwambiri mpaka Sara anathamangitsa Hagara.​—Gen. 16:1-6.

10. N’chiyani chinachitikira Isimaeli ndi Isaki chomwe chikanachititsa kuti zikhale zovuta kuti Abulahamu akhulupirire Yehova?

10 Patapita nthawi, Sara anakhala ndi pakati ndipo anabereka mwana wamwamuna yemwe anamupatsa dzina lakuti Isaki. Abulahamu ankakonda ana ake onse awiri, Isimaeli ndi Isaki. Koma chifukwa choti Isimaeli ankazunza Isaki, Abulahamu anakakamizika kuthamangitsa Isimaeli ndi Hagara. (Gen. 21:9-14) Patapita zaka, Yehova anauza Abulahamu kuti apereke nsembe mwana wake Isaki. (Gen. 22:1, 2; Aheb. 11:17-19) Pa zochitika zonsezi Abulahamu ankakhulupirira kuti Yehova adzakwaniritsa zimene analonjeza zokhudza ana ake.

11. N’chifukwa chiyani Abulahamu ankafunika kuyembekezera Yehova moleza mtima?

11 Pa nthawi yonseyi, Abulahamu ankafunika kuyembekezera Yehova moleza mtima. N’kutheka kuti pamene ankachoka ku Uri anali ndi zaka 70. (Gen. 11:31–12:4) Ndipo kwa zaka pafupifupi 100, ankakhala moyo woyendayenda n’kumagona m’matenti m’dziko la Kanani. Abulahamu anamwalira ali ndi zaka 175. (Gen. 25:7) Koma sanaone Yehova akukwaniritsa lonjezo lake loti adzapereka dzikolo kwa ana ake. Ndiponso anamwalira mzinda kapena kuti Ufumu wa Mulungu usanakhazikitsidwe. Ngakhale zili choncho, Baibulo limati Abulahamu anamwalira atakhala ndi “moyo wabwino, wautali ndi wokhutira.” (Gen. 25:8) Abulahamu anafunika kupirira mavuto ambiri koma anapitiriza kukhala ndi chikhulupiriro cholimba ndipo ankasangalala pamene ankayembekezera malonjezo a Yehova. N’chiyani chinamuthandiza kupirira? Anapirira chifukwa Yehova ankamuteteza komanso ankachita naye zinthu ngati mnzake.​—Gen. 15:1; Yes. 41:8; Yak. 2:22, 23.

Potengera chitsanzo cha Abulahamu ndi Sara, kodi atumiki a Mulungu amasonyeza bwanji chikhulupiriro komanso kuleza mtima? (Onani ndime 12) *

12. Kodi tikuyembekezera chiyani, nanga tikambirana chiyani?

12 Mofanana ndi Abulahamu nafenso tikuyembekezera mzinda wokhala ndi maziko enieni. Koma mosiyana ndi Abulahamu, ifeyo sitikuyembekezera kuti mzindawu umangidwe. Tikutero chifukwa Ufumu wa Mulungu unakhazikitsidwa mu 1914 ndipo unayamba kale kulamulira kumwamba. (Chiv. 12:7-10) Tikuyembekezera kuti uyambe kulamulira dziko lonse lapansi. Pamene tikuyembekezera zimenezi, tingafunike kupirira mavuto osiyanasiyana ofanana ndi omwe Abulahamu ndi Sara anakumana nawo. Atumiki a Yehova ambiri masiku ano amatsanzira Abulahamu. Nkhani za mu Nsanja ya Olonda zofotokoza mbiri ya atumiki a Yehova zimasonyeza mmene iwo asonyezera chikhulupiriro komanso kuleza mtima ngati Abulahamu ndi Sara. Tiyeni tikambirane zina mwa nkhanizi ndipo tione zimene tingaphunzirepo.

ANTHU ENA OMWE ANATSANZIRA ABULAHAMU

M’bale Walden analolera kudzimana zinthu zina ndipo Yehova anamudalitsa

13. Kodi tikuphunzira chiyani pa chitsanzo cha M’bale Bill Walden?

13 Tiyenera kukhala ndi mtima wodzimana. Kuti tiike mzinda wa Mulungu kapena kuti Ufumu pamalo oyamba ngati mmene Abulahamu anachitira, tiyenera kulolera kusiya zinthu zina kuti tisangalatse Mulungu. (Mat. 6:33; Maliko 10:28-30) Chitsanzo ndi m’bale wina dzina lake Bill Walden. * Mu 1942, m’baleyu anali atatsala pang’ono kumaliza maphunziro ake akuyunivesite kuti atenge digiri ya zomangamanga. Pa nthawiyi anakumana ndi a Mboni za Yehova ndipo anayamba kuphunzira Baibulo. Mmodzi mwa aphunzitsi ake akuyunivesite anamupezera ntchito yoti akayambe akamaliza maphunziro, koma Bill anakana. Iye ananena kuti anasankha kuti azichita zambiri potumikira Mulungu m’malo mogwira ntchito yamalipiro ambiri. Patangopita ka nthawi, boma linamulamula kuti akalowe usilikali. Iye anakana mwaulemu ndipo izi zinachititsa kuti alipiritsidwe ndalama zokwana madola 10,000 a ku America komanso kuti akakhale m’ndende kwa zaka 5. M’baleyu anatulutsidwa m’ndende patatha zaka zitatu. Kenako anaitanidwa kuti akalowe Sukulu ya Giliyadi ndipo anatumizidwa ku Africa kumene ankatumikira ngati mmishonale. M’bale Bill anakwatira Mlongo Eva ndipo ankatumikira limodzi ku Africa. Pamenepa onse awiri ankafunika kukhala ndi mtima wodzimana. Patadutsa zaka zingapo, anabwerera ku United States kuti akasamalire mayi a M’bale Bill. Pofotokoza mwachidule mbiri ya moyo wake, iye anati: “Ndimasangalala kwambiri ndikaganizira mwayi umene ndakhala nawo wogwiritsidwa ntchito ndi Yehova kwa zaka zoposa 70. Ndimamuthokoza chifukwa chondilola kumutumikira kwa moyo wanga wonse.” Kodi nanunso mumafuna kuchita utumiki wa nthawi zonse kwa moyo wanu wonse?

M’bale ndi Mlongo Apostolidis ankaona kuti Yehova ankawalimbikitsa

14-15. Kodi tikuphunzira chiyani pa chitsanzo cha M’bale ndi Mlongo Apostolidis?

14 Tisamaganize kuti sitizikumana ndi mavuto. Chitsanzo cha Abulahamu chikutiphunzitsa kuti anthu amene adzipereka kutumikira Yehova kwa moyo wawo wonse amakumananso ndi mavuto. (Yak. 1:2; 1 Pet. 5:9) Nkhani ya M’bale Aristotelis Apostolidis * ingatithandize kumvetsa zimenezi. M’baleyu anabatizidwa ku Greece mu 1946. Mu 1952, anayamba chibwenzi ndi mlongo wina dzina lake Eleni, ndipo onse ankafuna kuchita zambiri potumikira Yehova. Koma Mlongo Eleni anayamba kudwala ndipo anamupeza ndi chotupa muubongo. Anamuchita opaleshoni n’kuchichotsa koma patapita zaka zochepa atangokwatirana, chotupa chija chinayambiranso. Anamuchitanso opaleshoni ina koma pa nthawiyi anafa ziwalo zina ndipo sankatha kulankhula bwinobwino. Koma mlongoyu anapitirizabe kulalikira mwakhama ngakhale kuti ankadwala komanso pa nthawiyo boma linkazunza a Mboni.

15 M’bale Apostolidis anasamalira mkazi wake kwa zaka 30. Pa nthawiyi, m’baleyu anali mkulu, ankatumikira m’makomiti a msonkhano komanso ankathandiza pa ntchito yomanga Malo a Msonkhano. Mu 1987, Mlongo Eleni anavulala pamene ankalalikira. Anakhala chikomokere kwa zaka zitatu kenako anamwalira. Pofotokoza mwachidule mbiri ya moyo wake, M’bale Apostolidis anati: “Kwa zaka zonsezi, ndakhala ndikukumana ndi mavuto ndipo ena anali a mwadzidzidzi komanso osayembekezereka. Choncho ndinkafunika kupirira kuti ndisafooke. Komabe, nthawi zonse Yehova wakhala akundipatsa mphamvu zimene ndinkafunikira kuti ndithane ndi mavutowa.” (Sal. 94:18, 19) Yehova amakonda kwambiri atumiki ake omwe amachita zonse zomwe angathe pomutumikira ngakhale akukumana ndi mavuto.

Mlongo Audrey Hyde ankasangalala chifukwa ankaganizira madalitso am’tsogolo

16. Kodi M’bale Knorr anapereka malangizo otani kwa mkazi wake?

16 Tiziganizira zam’tsogolo. Abulahamu ankaganizira madalitso amene Yehova adzamupatse ndipo zimenezi zinamuthandiza kupirira mavuto omwe anakumana nawo. Mlongo Audrey Hyde ankaganiziranso zimene ankayembekezera m’tsogolo ngakhale ankakumana ndi mavuto. Mwamuna wake woyamba yemwe anali M’bale Nathan H. Knorr anamwalira ndi matenda a khansa ndipo mwamuna wake wachiwiri, Glenn Hyde anadwala kwambiri. * Mlongoyu ananena kuti chomwe chinamuthandiza kupirira ndi mawu amene mwamuna wake woyamba anamuuza patangotsala milungu yochepa kuti amwalire. Iye anati: “Nathan anandiuza kuti: ‘Tikamwalira, chiyembekezo chathu sichikhalanso chokayikitsa, ndipo zikatere ndiye kuti sitidzamvanso ululu ayi.’ Kenako anandilimbikitsa kuti: ‘Uziganizira zam’tsogolo chifukwa mphoto yako ili m’tsogolo.’ . . . Ndiye anawonjezera kuti: “Uzionetsetsa kuti uli ndi chochita nthawi zonse, uziyesetsa kugwiritsira ntchito moyo wako kuthandiza anthu ena. Zimenezi zidzakuthandiza kuti uzisangalala.’” Malangizowa ndi othandiza kwambiri chifukwa timafunikadi kumayesetsa kuchitira ena zabwino komanso ‘kukondwera ndi chiyembekezo.’​—Aroma 12:12.

17. (a) N’chifukwa chiyani tinganene kuti tili ndi zifukwa zambiri zotichititsa kuganizira zam’tsogolo? (b) Kodi kutsatira malangizo a pa Mika 7:7, kungatithandize bwanji kuti tidzasangalale ndi madalitso am’tsogolo?

17 Masiku ano, tili ndi zifukwa zambiri zotichititsa kuganizira zam’tsogolo. Zinthu zimene zikuchitika m’dzikoli zikusonyeza kuti panopo tili kumapeto kwa masiku otsiriza. Posachedwapa sitidzafunikanso kuyembekezera kuti mzinda wokhala ndi maziko enieni uyambe kulamulira dziko lonse lapansi. Pali madalitso ambiri amene tidzasangalale nawo. Limodzi mwa madalitsowa ndi loti anzathu komanso achibale athu amene anamwalira adzaukitsidwa. Pa nthawiyi, Yehova adzadalitsa Abulahamu chifukwa cha kukhulupirika komanso kuleza mtima kwake, pomuukitsa limodzi ndi banja lake. Kodi inuyo mudzapezekapo kuti mudzawalandire? Zimenezi zingadzatheke ngati nanunso, mofanana ndi Abulahamu, mumalolera kudzimana zinthu zina chifukwa cha Ufumu wa Mulungu, ngati mumakhulupirirabe Mulungu ngakhale mukumane ndi mavuto komanso ngati mumayembekezera moleza mtima malonjezo a Yehova.​—Werengani Mika 7:7.

NYIMBO NA. 74 Tiyeni Tiimbire Limodzi Nyimbo ya Ufumu

^ ndime 5 Pamene tikuyembekezera kuti malonjezo a Yehova akwaniritsidwe, tikhoza kutopa kapena chikhulupiriro chathu chingayambe kuchepa. Kodi tingaphunzire chiyani kwa Abulahamu pa nkhani ya kuyembekezera moleza mtima kukwaniritsidwa kwa malonjezo a Yehova? Nanga tingaphunzire chiyani kwa atumiki a Yehova ena a masiku ano?

^ ndime 13 Mbiri ya moyo wa M’bale Walden ili mu Nsanja ya Olonda ya December 1, 2013, tsamba 8-10.

^ ndime 14 Mbiri ya moyo wa M’bale Apostolidis ili mu Nsanja ya Olonda ya February 1, 2002, tsamba 24-28.

^ ndime 16 Mbiri ya moyo wa Mlongo Hyde ili mu Nsanja ya Olonda ya July 1, 2004, tsamba 23-29.

^ ndime 56 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI Tsamba 5: Banja lachikulire likutumikirabe Yehova mokhulupirika ngakhale likukumana ndi mavuto. Iwo amakhalabe ndi chikhulupiriro cholimba chifukwa amaganizira malonjezo a Yehova am’tsogolo.