Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 36

Kodi Ndimwe Wokonzeka Kukhala Msodzi wa Anthu?

Kodi Ndimwe Wokonzeka Kukhala Msodzi wa Anthu?

“Usacite mantha. Kuyambila lelo uzisodza anthu amoyo.” —LUKA 5:10.

NYIMBO 73 Tilimbitseni Mtima

ZIMENE TIKAMBILANE *

1. Kodi Yesu anapempha asodzi anayi kuti acite ciani? Nanga iwo anacita ciani?

OPHUNZILA a Yesu Petulo, Andireya, Yakobo, na Yohane anali kugwila nchito ya usodzi. Ganizilani cabe mmene iwo anamvelela Yesu atawaitana n’kuwauza kuti: “Nditsatileni, ndipo ndikusandutsani asodzi a anthu.” * Kodi iwo anacita ciani? Baibo imati: “Nthawi yomweyo iwo anasiya maukonde awo n’kumutsatila.” (Mat. 4:18-22) Cosankha cawo cimeneci cinasinthilatu umoyo wawo. M’malo mosodza nsomba, iwo anakhala ‘asodzi a anthu amoyo.’ (Luka 5:10) Masiku ano, Yesu akuitana anthu oona mtima amene amakonda coonadi kuti nawonso akhale asodzi a anthu. (Mat. 28:19, 20) Kodi imwe munalabadila ciitano ca Yesu cakuti mukhale msodzi wa anthu?

2. N’cifukwa ciani tiyenela kuona kuti kusankha kukhala msodzi wa anthu ni nkhani yaikulu? Nanga n’ciani cingatithandize kupanga cosankha cimeneci?

2 N’kutheka kuti mwakhala mukuphunzila Baibo kwa kanthawi, ndipo mwasintha umoyo wanu. Ndiye lomba, mufuna kupanga cosankha cokhala wofalitsa uthenga wabwino. Ngati mumayopa kukhala wofalitsa, musataye mtima. Kuyopako kungakhale cizindikilo cakuti mumaona kuti cosankha cimeneci n’cacikulu komanso cofunika kwambili. N’zoona kuti Baibo imakamba kuti Yesu ataitana Petulo na anzake, “nthawi yomweyo” iwo anasiya maukonde awo. Koma sikuti Petulo na m’bale wake anapanga cosankha cimeneci mopupuluma. Pamene iwo anali kupanga cosankha cimeneci, n’kuti amudziŵa kale Yesu kwa miyezi 6, ndipo akhulupilila kuti analidi Mesiya. (Yoh. 1:35-42) Mofananamo, mwina na imwe munaphunzila kale zambili za Yehova na Yesu, ndipo mufuna kupita patsogolo kuuzimu. Koma mufunika kuŵelengela mtengo wake coyamba musanapange cosankha cimeneci. Kodi n’ciani cinathandiza Petulo, Andireya, na ena kupanga cosankha cokhala otsatila a Yesu?

3. Ni makhalidwe ati amene angakusonkhezeleni kulabadila ciitano ca Yesu cakuti mukhale msodzi wa anthu?

3 Ophunzila a Yesu oyambilila anali na mtima wofunitsitsa kugwila nchito yawo ya usodzi, anali kuidziŵa bwino, anali olimba mtima, komanso akhama. Mosakayikila, makhalidwewa ndi amenenso anawathandiza kukhala asodzi abwino a anthu. Nkhani ino ifotokoza mmene mungakulitsile makhalidwe amenewa kuti mukhale wophunzila wa Khristu waluso.

KHALANI NA MTIMA WOFUNITSITSA KULALIKILA

Petulo na ena anakhala asodzi a anthu. Nchito yofunika kwambili imeneyi ikupitilizabe masiku ano (Onani ndime 4-5)

4. N’cifukwa ciani Petulo anali kugwila nchito ya usodzi?

4 Petulo anali kugwila nchito yosodza nsomba n’colinga cakuti azisamalila banja lake. Koma cionekanso kuti Petulo anali kuikonda nchito ya usodzi. (Yoh. 21:3, 9-15) Iye anaphunzilanso kukonda nchito yosodza anthu. Ndipo mothandizidwa na Yehova, Petulo anakhala waluso kwambili pa nchitoyo.—Mac. 2:14, 41.

5. Kulingana na Luka 5:8-11, n’cifukwa ciani Petulo anacita mantha? Nanga n’ciani cingatithandize ife kugonjetsa mantha otelo?

5 Timalalikila cifukwa cakuti timakonda Yehova. Ici ndiye cifukwa cacikulu cimene timagwilila nchitoyi. Kukonda Yehova kumatithandiza kuthetsa mantha alionse amene tingakhale nawo. Yesu ataitana Petulo kuti akhale msodzi wa anthu, anamuuza kuti: “Usacite mantha.” (Ŵelengani Luka 5:8-11.) Sikuti Petulo anali kuyopa zimene zikanamucitikila ngati wakhala wotsatila wa Khristu. Koma anayopa poona kuculuka kwa nsomba zimene Yesu anawathandiza kugwila mozizwitsa, moti anadziona kuti anali wosayenelela kugwila nchito pamodzi na Yesu. Mofanana na Petulo, na imwe mungakhale na mantha. Mwina mumacita mantha mukaganizila zimene mudzafunika kucita mukadzakhala wophunzila wa Khristu. Ngati n’conco, yesetsani kukulitsa cikondi canu pa Yehova, Yesu, komanso pa anansi anu. Mukatelo, mudzakhala wokonzeka kulabadila ciitano ca Yesu cakuti mukhale msodzi wa anthu.—Mat. 22:37, 39; Yoh. 14:15.

6. N’zifukwa zina ziti zimene zimatisonkhezela kugwila nchito yolalikila?

6 Onaninso zifukwa zina zimene zimatisonkhezela kugwila nchito yolalikila. Timafuna kumvela lamulo la Yesu lakuti: “Pitani mukaphunzitse anthu.” (Mat. 28:19, 20) Cifukwa cina n’cakuti anthu ni “onyukanyuka ndi otayika,” ndipo ali na njala yaikulu yofuna kuphunzila coonadi ca Ufumu. (Mat. 9:36) Yehova amafuna kuti anthu a mtundu uliwonse adziŵe coonadi molondola kuti akapulumuke.—1 Tim. 2:4.

7. Kodi lemba la Aroma 10:13-15 lionetsa bwanji kufunika kwa nchito yolalikila?

7 Kudziŵa kuti nchito yolalikila imathandiza anthu kuti akapulumuke, kumatisonkhezela kuyamba kuigwila. Mosiyana na msodzi amene amagwila nsomba n’colinga cakuti azigulitsa kapena kudya, ise timasodza anthu kuti tipulumutse miyoyo yawo.—Ŵelengani Aroma 10:13-15; 1 Tim. 4:16.

IDZIŴENI BWINO NCHITO YOLALIKILA

8-9. Kodi msodzi amafunika kudziŵa ciani? Nanga n’cifukwa ciani?

8 M’nthawi ya Yesu, msodzi waciisiraeli anali kudziŵa mtundu wa nsomba zimene angagwile. (Lev. 11:9-12) Analinso kudziŵa malo kumene angapeze nsomba. Kambili, nsomba zimakhala pa malo amene pali madzi amene zimakonda, komanso pamene zimapeza cakudya cambili. Msodzi afunikanso kuganizila nthawi yoyenela yopita kukapha nsomba. Ponena za nthawi yabwino yopha nsomba, onani zimene m’bale wina ku cisumbu ca Pacific anauza mmishonale atapangana naye kuti akaphe nsomba pamodzi. Mmishonaleyo anati: “Tikakumana maŵa m’maŵa pa 9 awazi.” M’baleyo anayankha kuti: “Aa! 9 awazi, mungokamba cifukwa cosadziŵa. Tifunika kupita kukapha nsomba pa nthawi imene tingazipeze, osati cabe pa nthawi yotikomela.”

9 Mofananamo, asodzi a anthu m’nthawi ya atumwi anali kupita kumalo kumene akanapeza anthu komanso panthawi imene anthuwo akanapezeka. Mwacitsanzo, otsatila a Yesu anali kulalikila ku kacisi na m’masunagoge, kunyumba ndi nyumba, komanso kumisika. (Mac. 5:42; 17:17; 18:4) Nafenso tifunika kudziŵa nthawi yabwino imene tingapeze anthu panyumba, kapena kumalo ena m’gawo lathu. Tifunika kukhala okonzeka kusintha ndandanda yathu kuti tipite kukalalikila panthawi yoyenela komanso kumalo kumene tingapeze anthu.—1 Akor. 9:19-23.

ASODZI ALUSO . . . 1. amapita kumene kumakonda kupezeka nsomba, komanso pa nthawi imene angazipeze (Onani ndime 8-9)

10. Ni zida ziti zimene gulu la Yehova latipatsa?

10 Msodzi wa nsomba amafunika kukhala na zida zoyenelela zophela nsomba, komanso amafunika kudziŵa moziseŵenzetsela. Nafenso tiyenela kukhala na zida zoyenelela zogwilila nchito yathu yolalikila. Tiyenelanso kudziŵa bwino moseŵenzetsela zida zimenezo. Yesu anapeleka malangizo omveka bwino kwa ophunzila ake a mmene akanagwilila nchito yosodza anthu. Anawauza zofunika kunyamula, malo kumene anafunika kukalalikila, ndiponso zimene anafunika kukamba. (Mat. 10:5-7; Luka 10:1-11) Masiku ano, Gulu la Yehova latipatsa Thuboksi imene ili na zida zothandiza kwambili polalikila. * Ndipo timaphunzitsidwa mmene tingaseŵenzetsele zida zimenezo. Zimene timaphunzilazo zimatithandiza kusacita mantha polalikila komanso kukulitsa luso pa nchitoyi.—2 Tim. 2:15.

ASODZI ALUSO . . . 2. amaphunzila kuseŵenzetsa zida zoyenela (Onani ndime 10)

KHALANI OLIMBA MTIMA

11. N’cifukwa ciani asodzi a anthu afunika kukhala olimba mtima?

11 Asodzi a nsomba amafunika kukhala olimba mtima cifukwa nthawi zina angakumane na cimphepo camkuntho mosayembekezeleka pa nyanja. Kuwonjezela apo, nthawi zambili amaseŵenza usiku. Nawonso asodzi a anthu amafunika kukhala olimba mtima. Tikayamba kugwila nchito yolalikila na kudziŵika kuti lomba ndife Mboni za Yehova, tingakumane na mavuto amene ali ngati “cimphepo camkuntho.” Tingayambe kutsutsidwa na a m’banja lathu komanso anzathu, ndiponso tingakumane ndi anthu okana kumvetsela uthenga wathu. Koma tikakumana na zimenezi sitidabwa. Yesu anauza otsatila ake kuti akuwatumiza kukalalikila uthenga wabwino pakati pa anthu otsutsa.—Mat. 10:16.

12. Mogwilizana na Yoswa 1:7-9, n’ciani cingatithandize kukhala olimba mtima?

12 Kodi mungacite ciani kuti mukhale olimba mtima? Coyamba, mufunika kukhulupilila kuti Yesu, amene tsopano ali kumwamba, akupitiliza kutsogolela pa nchito yolalikila. (Yoh. 16:33; Chiv. 14:14-16) Caciŵili, muzikhulupilila kwambili lonjezo la Yehova lakuti adzakusamalilani. (Mat. 6:32-34) Mukakhala na cikhulupililo colimba, m’pamenenso mudzakhala wolimba mtima kwambili. Petulo na anzake anaonetsa cikhulupililo cacikulu pamene anasiya nchito yawo ya usodzi na kutsatila Yesu. Na imwe munaonetsa cikhulupililo cacikulu pamene munadziŵitsa anzanu na a m’banja lanu kuti mwayamba kuphunzila Baibo na Mboni za Yehova ndiponso kupezeka pamisonkhano yawo. Ndipo mosakayikila mwasintha kwambili khalidwe lanu na zinthu zambili mu umoyo wanu n’colinga cakuti muzitsatila mfundo zolungama za Yehova. Kuti mukwanitse kucita zimenezi, panafunikanso cikhulupililo na kulimba mtima. Pamene mupitiliza kukulitsa khalidwe la kulimba mtima, mungakhale na cidalilo cakuti ‘Yehova Mulungu wanu ali namwe kulikonse kumene mupiteko.’—Ŵelengani Yoswa 1:7-9.

ASODZI ALUSO . . . 3. amagwila nchito yawo molimba mtima ngakhale pamene nyengo siili bwino (Onani ndime 11-12)

13. Kodi kusinkha-sinkha na kupemphela kungakuthandizeni bwanji kukulitsa khalidwe la kulimba mtima?

13 N’ciani cina cimene mungacite kuti mukulitse khalidwe la kulimba mtima? Pemphelani kwa Yehova kuti akuthandizeni kukhala wolimba mtima. (Mac. 4:29, 31) Yehova adzayankha mapemphelo anu ndipo sadzakusiyani olo pang’ono. Iye ni wokonzeka nthawi zonse kukuthandizani. Komanso, muyenela kusinkha-sinkha za mmene Yehova anapulumutsila anthu ena kumbuyoko. Muyenelanso kuganizila mmene iye anakuthandizilani kulimbana na mavuto enaake ndiponso mmene anakuthandizilani kusintha khalidwe lanu. Musakayikile kuti Mulungu, amene anapulumutsa anthu ake pa Nyanja Yofiila angakuthandizeni kukhala wophunzila wa Khristu. (Eks. 14:13) Khalani na cikhulupililo monga cimene wamasalimo wina anali naco. Iye anati: “Yehova ali kumbali yanga, sindidzaopa. Munthu wocokela kufumbi angandicite ciani?”—Sal. 118:6.

14. Kodi mwaphunzila ciani pa citsanzo ca mlongo Masae na mlongo Tomoyo?

14 Cinanso cimene cingakuthandizeni kukulitsa khalidwe la kulimba mtima ni kuphunzila mmene Yehova anathandizila anthu ena amene ni amanyazi mwacibadwa, koma anaphunzila kukhala olimba mtima. Ganizilani citsanzo ca mlongo wina dzina lake Masae. Iye anali wamanyazi kwambili moti anali kuona kuti sangakwanitse kulalikila. Mlongoyu anali kuona kuti kukamba ndi anthu osawadziŵa n’kovuta kwambili ngati mmene zimakhalila zovuta kukwela mpanda wautali. Conco anali kuona kuti sangakwanitse kugwila nchito yolalikila. Koma anacitapo kanthu mwakhama kuti akulitse cikondi cake pa Mulungu komanso pa anansi ake. Anayamba kuganizila za kufunika kogwila mwamsanga nchito yolalikila, ndiponso anapemphela kwa Mulungu kuti amuthandize kukhala na mtima wofunitsitsa kulalikila. Zotulukapo zake n’zakuti, mantha ake anatha, ndipo anakwanitsa ngakhale kutengako upainiya wanthawi zonse. Yehova angathandizenso ofalitsa atsopano ‘kukhala olimba mtima.’ Ganizilaninso citsanzo ca mlongo Tomoyo. Atafika pa nyumba yoyamba patsiku limene anayamba kulalikila ku nyumba na nyumba, mwininyumba anamukalipila amvekele: “Sinifuna kukamba na a Mboni za Yehova!” Kenako anatseka citseko mwamphamvu. Tomoyo sanaope, koma anauza mlongo amene anali naye kuti: “Mwamvela zimene akamba? Sin’nakambe ciliconse, koma adziŵa kuti ndine Mboni ya Yehova. Namvela bwino ngako!” Tsopano mlongo Tomoyo akutumikila monga mpainiya wanthawi zonse.

PHUNZILANI KUCITA ZINTHU MWAKHAMA

15. Ngati zimativuta kugwila nchito yolalikila, kodi tingatengele bwanji citsanzo ca asodzi? Nanga n’cifukwa ciani kucita zimenezi n’kofunika kwa Akhristu?

15 Asodzi amene usodzi umawayendela bwino ni aja amene amacita zinthu mwakhama. Mwacitsanzo, amauka m’mamaŵa kupita ku nchito yawo, ndipo amapitiliza kugwila nchitoyo olo kuti nyengo siili bwino. Na ife timafunika khama kuti tipilile pa nchito yathu mpaka kuitsiliza.—Mat. 10:22.

16. N’ciani cimene cingatithandize kucita zinthu zimene tiona kuti n’zovuta?

16 Khama siticita kubadwa nalo. Mwacibadwa, timakonda kucita zinthu zimene tiona kuti n’zosavuta. Pamafunika kudziletsa kuti munthu azicita zinthu mwakhama. Conco, timafunika thandizo kuti tiphunzile kucita zinthu zimene timaona kuti n’zovuta. Yehova amatipatsa thandizo limenelo kupitila mwa mzimu wake woyela.—Agal. 5:22, 23.

17. Malinga na 1 Akorinto 9:25-27, kodi mtumwi Paulo anaonetsa bwanji kuti anali wakhama?

17 Mtumwi Paulo anali munthu wakhama. Olo zinali telo, iye anakamba kuti anafunikabe “kumenya” thupi lake kuti akwanitse kucita zoyenela. (Ŵelengani 1 Akorinto 9:25-27.) Paulo analimbikitsa ena kukhala akhama na kucita zinthu zonse “moyenela ndi mwadongosolo.” (1 Akor. 14:40) Timafunika khama kuti tipitilize kutsatila pulogilamu yathu ya zauzimu, imene imaphatikizapo kugwila nawo nthawi zonse nchito yolalikila na kuphunzitsa uthenga wabwino.—Mac. 2:46.

MUSAZENGELEZE

18. Kodi tiyenela kucita ciani kuti Yehova aziona kuti tikucita bwino pa nchito yathu yolalikila?

18 Msodzi amaona kuti nchito yamuyendela bwino ngati wagwila nsomba zambili. Koma ife sitiona kuti nchito yathu yatiyendela bwino mwa kuŵelenga anthu amene tawathandiza kubwela m’gulu la Mulungu. (Luka 8:11-15) Cofunika kwambili ni kupitiliza kulalikila uthenga wabwino na kuphunzitsa anthu. Tikatelo, Yehova amationa kuti tikucita bwino pa nchito yathu. N’cifukwa ciani takamba conco? Cifukwa kucita zimenezi kumaonetsa kuti timamvela Mulungu na Mwana wake.—Maliko 13:10; Mac. 5:28, 29.

19-20. Kodi tili na cifukwa capadela citi cogwilila nchito yolalikila masiku ano?

19 M’maiko ena, pali miyezi yoikika imene asodzi amaloledwa kupha nsomba. M’maiko amenewo, asodzi amacita khama kwambili kupha nsomba miyeziyo ikatsala pang’ono kutha. Monga asodzi a anthu, tili na cifukwa cina cogwilila nchito yolalikila masiku ano. Cifukwa cake n’cakuti mapeto a dzikoli ali pafupi kwambili. Nthawi imene yatsala kuti tigwile nchitoyi yacepa kwambili. Conco, musazengeleze kapena kuyembekezela kuti zinthu zikhaliletu bwino kuti muyambe kugwila nawo nchito yofunika kwambili imeneyi.—Mlal. 11:4.

20 Ino ndiyo nthawi yofunika kukulitsa mtima wofuna kugwila nchito yolalikila, yophunzila zambili za m’Baibo, yokulitsa khalidwe la kulimba mtima, ndiponso yophunzila kucita zinthu mwakhama. Loŵani m’gulu la asodzi oposa 8 miliyoni, ndipo mudzapeza cimwemwe cimene Yehova amapeleka. (Neh. 8:10) Tsimikizani mtima kugwila nawo nchito yolalikila za Ufumu mmene mungathele, na kupitiliza kuigwila mpaka pamene Yehova adzanene kuti yatha. M’nkhani yotsatila, tidzakambilana zinthu zitatu zimene zingatithandize kutsimikiza mtima kupitiliza kugwila nchitoyi monga asodzi a anthu.

NYIMBO 66 Lengezani Uthenga Wabwino

^ ndime 5 Yesu anaitana asodzi odzicepetsa komanso akhama kuti akhale ophunzila ake. Masiku anonso, iye akupitiliza kuitana anthu amene ali na makhalidwe amenewa kuti akhale asodzi a anthu. M’nkhani ino, tikambilana zimene ophunzila Baibo amene amazengeleza kulabadila ciitano ca Yesu ayenela kucita.

^ ndime 1 KUFOTOKOZELA MAWU ENA: Mawu akuti “asodzi a anthu” atanthauza anthu onse amene amalalikila uthenga wabwino na kuphunzitsa ena kuti akhale ophunzila a Khristu.

^ ndime 10 Onani nkhani yakuti “Kuphunzitsa Coonadi” mu Nsanja ya Mlonda ya October 2018, mape. 11-16.