Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 39

Muzilimbikitsa Alongo Mumpingo

Muzilimbikitsa Alongo Mumpingo

“Akazi amene akulengeza uthenga wabwino ndi khamu lalikulu.”​SAL. 68:11.

NYIMBO NA. 137 Akazi Achikhristu Okhulupirika

ZIMENE TIPHUNZIRE *

Alongo athu akhama akuchita zinthu zosiyanasiyana. Ena akuyankha pamisonkhano, kulalikira, kuthandiza nawo ntchito yokonzanso Nyumba ya Ufumu komanso kuthandiza wokhulupirira mnzawo (Onani ndime 1)

1. Kodi alongo amathandiza bwanji gulu la Mulungu, nanga ambiri amakumana ndi mavuto otani? (Onani chithunzi chapachikuto)

TIMASANGALALA kuti tili ndi alongo ambiri mumpingo omwe amagwira ntchito mwakhama. Mwachitsanzo, iwo amayankha komanso kukamba nkhani pamisonkhano, ndiponso amagwira nawo ntchito yolalikira. Ena amathandiza nawo ntchito yokonza Nyumba ya Ufumu, komanso amasonyeza kuti amaganizira abale ndi alongo awo. Komabe alongowa amakumananso ndi mavuto. Ena amasamalira makolo awo okalamba. Ena amatsutsidwa ndi achibale awo. Komanso ena amalera okha ana ndipo amafunika kuti agwire ntchito mwakhama kuti asamalire banja lawo.

2. N’chifukwa chiyani tiyenera kumayesetsa kulimbikitsa alongo mumpingo wathu?

2 N’chifukwa chiyani tiyenera kumalimbikitsa alongo mumpingo? Tiyenera kuchita zimenezi chifukwa anthu m’dzikoli salemekeza akazi. Komanso Baibulo limatilimbikitsa kuti tiziwathandiza. Mwachitsanzo, mtumwi Paulo anauza Akhristu a mumpingo wa Roma kuti alandire mlongo Febe komanso “kumuthandiza pa nkhani iliyonse imene angafune thandizo.” (Aroma 16:1, 2) Paulo ali Mfarisi, nayenso ankakhulupirira kuti akazi ndi otsika ndipo sankawalemekeza. Koma atakhala Mkhristu, iye ankatsanzira Yesu, ndipo ankalemekeza akazi komanso kumachita nawo zinthu mokoma mtima.​—1 Akor. 11:1.

3. Kodi Yesu ankachita bwanji zinthu ndi akazi? Nanga ankaona bwanji akazi amene ankachita chifuniro cha Mulungu?

3 Yesu ankalemekeza akazi onse. (Yoh. 4:27) Iye sankaona akazi ngati mmene atsogoleri a Chiyuda ankachitira. Ndipotu buku lina lofotokozera Baibulo linati: “Yesu sananenepo chilichonse chonyoza akazi.” Koma ankalemekeza kwambiri akazi amene ankachita chifuniro cha Atate wake. N’zochititsa chidwi kuti Yesu ankaona akazi ngati alongo ake. Ndipo ananena kuti akaziwo komanso amuna ena anali mbali ya banja lake lauzimu.​—Mat. 12:50.

4. Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?

4 Nthawi zonse Yesu ankathandiza alongo amene ankatumikira Mulungu. Iye ankawayamikira komanso kuwateteza. Tiyeni tikambirane mmene tingatsanzirire Yesu posonyeza kuti timaganizira alongo athu.

TIZISONYEZA KUTI TIMAGANIZIRA ALONGO ATHU

5. N’chifukwa chiyani alongo ena zingawavute kupeza anzawo abwino ocheza nawo?

5 Tonsefe, kaya ndife abale kapena alongo, timafuna kukhala ndi anzathu abwino ocheza nawo. Koma nthawi zina alongo angavutike kupeza anzawo abwino ocheza nawo. N’chifukwa chiyani tikutero? Taonani zimene alongo ena ananena. Mlongo wina dzina lake Jordan * anati: “Chifukwa chakuti ndine wosakwatiwa, nthawi zambiri ndimaona kuti ndine wosafunika mumpingo komanso ndimamva ngati sindiwerengeredwa.” Mlongo winanso dzina lake Kristen, yemwe ndi mpainiya, anasamukira kudera limene kunkafunika ofalitsa ambiri. Iye anati: “Ukasamukira mumpingo watsopano, ungamamve ngati uli wekhawekha.” Abale enanso angamve chimodzimodzi. Enanso amene akukhala m’banja loti ena si a Mboni, zingawavute kuti azigwirizana kwambiri ndi anthu a m’banja lawo. Komanso angamadzimve kuti ali kutali ndi abale ndi alongo mumpingo. Alongo ena angamadzimve kuti ali okhaokha chifukwa chakuti akudwala ndipo sangachoke pakhomo pawo, kapena chifukwa chakuti akusamalira achibale awo amene akudwala. Mlongo wina dzina lake Annette ananena kuti: “Sindinkatha kupita kukacheza abale ndi alongo akandiitana chifukwa ndinkasamalira amayi anga.”

Mofanana ndi Yesu tingasonyeze kuti timakonda komanso kuganizira alongo athu okhulupirika (Onani ndime 6-9) *

6. Malinga ndi Luka 10:38-42, kodi Yesu anathandiza bwanji Malita ndi Mariya?

6 Yesu ankapeza nthawi yocheza ndi alongo ndipo anali mnzawo weniweni. Iye ankacheza ndi Mariya komanso Malita, omwe anali alongo osakwatiwa. (Werengani Luka 10:38-42.) Zimene ankalankhula komanso kuchita zinkapangitsa alongowa kuti azimasuka naye. Mwachitsanzo, Mariya anamasuka kukhala pamapazi a Yesu monga wophunzira wake. * Komanso Malita, yemwe anakhumudwa chifukwa chakuti Mariya sankamuthandiza ntchito, anali womasuka kuuza Yesu zimene zinali m’maganizo mwake. Pa nthawiyi, Yesu anaphunzitsa alongo awiriwa mfundo zofunika. Anasonyezanso kuti ankawaganizira alongowa komanso mchimwene wawo Lazaro, chifukwa ankawayendera nthawi zina. (Yoh. 12:1-3.) N’zosadabwitsa kuti Lazaro atadwala kwambiri Mariya ndi Malita ankadziwa kuti akhoza kupempha thandizo kwa Yesu.​—Yoh. 11:3, 5.

7. Kodi ndi njira ina iti yomwe tingalimbikitsire alongo athu?

7 Kwa alongo ena, misonkhano imawapatsa mwayi wokhala ndi Akhristu anzawo. Choncho akabwera pamisonkhano tiyenera kuwalandira bwino, kulankhula nawo komanso kuwathandiza kudziwa kuti timawaganizira. Mlongo Jordan amene tamutchula kale uja anati: “Zimandilimbikitsa kwambiri anthu ena akandiyamikira chifukwa cha ndemanga imene ndapereka pamisonkhano, akandiuza kuti akufuna kuti alowe nane mu utumiki kapena akachita zinazake zosonyeza kuti amandiganizira.” Alongo ayenera kudziwa kuti timawaona kuti ndi ofunika kwambiri. Mlongo wina dzina lake Kia anati: “Ndikakhala kuti sindinapite kumisonkhano, ndimadziwa kuti abale ndi alongo andilembera mameseji kuti adziwe ngati ndili bwino. Zimenezi zimasonyeza kuti amandikonda kwambiri.”

8. Kodi tingatsanzire Yesu m’njira zinanso ziti?

8 Mofanana ndi Yesu, nafenso tingachite bwino kumapeza nthawi yocheza ndi alongo. Mwachitsanzo, tingawaitanire kunyumba kuti tidzadye nawo chakudya, kapena kuti tidzangocheza. Tikamachita zimenezi, tizionetsetsa kuti tikukambirana nkhani zolimbikitsa. (Aroma 1:11, 12) Akulu angachite bwino kukhala ndi maganizo ofanana ndi a Yesu. Yesu ankadziwa kuti n’zovuta kwa ena kumakhala okha. Koma iye anafotokoza momveka bwino kuti, kuti munthu akhale wosangalala sizimadalira kuti akhale pabanja kapena kuti akhale ndi ana. (Luka 11:27, 28) M’malo mwake tingapeze chimwemwe chenicheni ngati timaona kuti kutumikira Yehova n’kofunika kwambiri pa moyo wathu.​—Mat. 19:12.

9. Kodi akulu angatani kuti azithandiza alongo?

9 Makamaka akulu ayenera kumaona akazi a Chikhristu monga alongo awo komanso amayi awo. (1 Tim. 5:1, 2) Akulu ayenera kumapeza nthawi yocheza ndi alongo misonkhano isanayambe kapena ikatha. Mlongo Kristen anati: “Mkulu wina anaona kuti ndinkakhala otanganidwa kwambiri ndipo ankafuna kudziwa mmene ndimachitira zinthu. Ndinayamikira kwambiri chifukwa ndinaona kuti amandiganizira.” Nthawi zonse akulu akamapeza nthawi yocheza ndi alongo, zimasonyeza kuti amawaganizira kwambiri. * Annette yemwe tamutchula kale uja, anafotokoza kufunika koti azilankhula ndi akulu nthawi zonse. Iye anati: “Ndinayamba kuwadziwa bwino kwambiri ndipo iwonso anayamba kundidziwa bwino. Ndiyeno ndikakumana ndi mavuto, ndimamasuka kuwapempha kuti andithandize.”

MUZIYAMIKIRA ZIMENE ALONGO AMACHITA

10. N’chiyani chingathandize kuti alongo anthu azisangalala?

10 Tonse kaya ndife amuna kapena akazi, timasangalala kwambiri anthu akatiuza kuti amayamikira ntchito imene timagwira. Koma tikaona kuti anthu ena sakuyamikira zimene timachita, tingayambe kufooka. Mpainiya wina yemwe sali pabanja dzina lake Abigail, ananena kuti amaona kuti anthu ena sachita naye chidwi. Iye anati: “Abale ndi alongo ena amangodziwa kuti ndine m’bale wake wa wakutiwakuti komanso mwana wa auje. Nthawi zina ndimangodziona ngati wopanda ntchito.” Koma taonani zimene mlongo wina dzina lake Pam ananena. Mlongoyu sali pabanja ndipo anatumikira monga mmishonale kwa zaka zambiri. Kenako anabwerera kwawo kuti akasamalire makolo ake. Panopa ali ndi zaka za m’ma 70 ndipo akupitirizabe kuchita upainiya. Pam ananena kuti: “Chomwe chandithandiza kwambiri n’kuona kuti abale ndi alongo amayamikira zimene ndimachita.”

11. Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti ankaona kuti akazi amene ankatumikira naye limodzi ndi ofunika?

11 Yesu ankayamikira kwambiri zimene akazi okonda Mulungu ankachita pomutumikira ndi “chuma chawo.” (Luka 8:1-3) Iye anawalola kuti azimutumikira komanso ankawaphunzitsa choonadi chokhudza cholinga cha Mulungu. Mwachitsanzo, anawauza kuti adzaphedwa kenako adzaukitsidwa. (Luka 24:5-8) Iye anawauza akaziwa monganso mmene anachitira ndi atumwi, kuti adzakumana ndi mayesero. (Maliko 9:30-32; 10:32-34) N’zochititsa chidwi kuti atumwi ena atathawa pamene Yesu ankagwidwa, ena mwa akazi omwe ankamutumikirawa anali pambali pake ndipo anamuona akufa mozunzika pamtengo.​—Mat. 26:56; Maliko 15:40, 41.

12. Kodi Yesu anapereka ntchito zotani kwa akazi?

12 Yesu anapereka ntchito zina zofunika kwambiri kwa akazi. Mwachitsanzo, akazi ndi amene anayamba kudziwa kuti iye waukitsidwa. Kenako anatuma akaziwo kuti akauze atumwi kuti waukitsidwa. (Mat. 28:5, 9, 10) Komanso zikuoneka kuti pa Pentekosite mu 33 C.E., akazi ena analipo pamene Mulungu ankapereka mzimu woyera. Ngati ndi choncho akazi amene anadzozedwawa, ayenera kuti anapatsidwa mphatso yolankhula zinenero zina ndipo ankauza ena “zinthu zazikulu za Mulungu.”​—Mac. 1:14; 2:2-4, 11.

13. Kodi akazi a Chikhristu amachita zotani masiku ano, nanga tingasonyeze bwanji kuti timawayamikira?

13 Tiyenera kumayamikira alongo athu chifukwa cha zonse zimene amachita potumikira Yehova. Zinthu zimenezi zikuphatikizapo kumanga komanso kukonza malo olambirira, kulalikira ndi magulu a zinenero za m’mayiko ena komanso kudzipereka kuti atumikire pabeteli. Enanso amagwira nawo ntchito zothandiza ena pakagwa ngozi zachilengedwe, amathandiza kumasulira nawo mabuku, komanso kutumikira ngati apainiya komanso amishonale. Mofanana ndi abale, alongonso amalowa sukulu ya apainiya, Sukulu ya Akhristu Olalikira za Ufumu komanso Sukulu ya Giliyadi. Kuonjezera pamenepa akazi amathandiza amuna awo, kuti akwanitse maudindo awo mumpingo komanso m’gulu la Yehova. Abale amenewa ndi “mphatso za amuna” ndipo amachita zambiri pothandiza ena. Komabe zikanakhala zovuta kwambiri kuti azikwanitsa kuchita zimenezi zikanakhala kuti akazi awo sawathandiza. (Aef. 4:8) Kodi mukuona kuti pali zimene mungachite kuti muzithandiza alongowa pa ntchito yawo?

14. Mogwirizana ndi zimene lemba la Salimo 68:11 limanena, kodi akulu ozindikira amachita chiyani?

14  Akulu ozindikira amaona kuti alongo “ndi khamu lalikulu” la anthu odzipereka ndipo nthawi zambiri ndi amene amachita bwino kwambiri pogwira ntchito yolalikira. (Werengani Salimo 68:11.) Choncho akulu angaphunzirenso zinthu zina kuchokera kwa alongo. Abigail yemwe tamutchula kale uja, ananena kuti zimamulimbikitsa kwambiri akulu akamufunsa kuti afotokoze njira zothandiza zimene amagwiritsa ntchito akamayamba kukambirana ndi anthu. Iye anati: “Zimenezi zimandithandiza kuona kuti ndine ofunika kwambiri m’gulu la Yehova.” Komanso akulu amazindikira kuti alongo olimba mwauzimu amakhala ndi luso lothandiza alongo achitsikana akamakumana ndi mavuto. (Tito 2:3-5) Apatu n’zoonekeratu kuti tiyenera kumayamikira alongo mumpingo.

MUZITETEZA KOMANSO KUTHANDIZA ALONGO MUMPINGO

15. Kodi ndi nthawi ziti pamene alongo angafune kuti munthu wina awathandize?

15 Nthawi zina, alongo amafuna kuti munthu wina awateteze akamakumana ndi mavuto ena ake. (Yes. 1:17) Mwachitsanzo mlongo amene ndi wamasiye kapena amene banja lake linatha, angafune munthu wina kuti azimulankhulira kapena kumuthandiza kuchita zinthu zina zimene mwamuna wake ankachita. Mlongo wina wachikulire angafune kuti munthu wina amuthandize kulankhulana ndi madokotala. Komanso mlongo yemwe ndi mpainiya, amene amagwira ntchito zina m’gulu la Yehova, angafunike munthu womuteteza anthu ena akamamunena kuti salowalowa muutumiki ngati mmene apainiya ena amachitira. Ndiye kodi ndi njira zina ziti zimene tingathandizire alongo athu? Tiyeni tikambiranenso chitsanzo cha Yesu.

16. Mogwirizana ndi lemba la Maliko 14:3-9, kodi Yesu anateteza bwanji Mariya?

16 Yesu ankalankhulapo mwamsanga pofuna kuteteza alongo ake pamene anthu ena sankawamvetsa. Mwachitsanzo anateteza Mariya pamene Marita ankamuimba mlandu. (Luka 10:38-42) Anatetezanso Mariya ulendo wina pamene anthu ena ankaona kuti wachita zinthu mosaganiza bwino. (Werengani Maliko 14:3-9.) Yesu ankaona kuti Mariya anachita zimenezi ndi cholinga chabwino ndipo anamuyamikira ponena kuti: “Wandichitira zinthu zabwino. . . . Mayiyu wachita zimene angathe.” Iye analoseranso kuti zabwino zimene mayiyu anachita, zidzadziwika “kulikonse kumene uthenga wabwino udzalalikidwe m’dziko lonse.” Ndipo zimene Yesu analoserazi zikugwirizana ndi zomwe tikukambirana munkhaniyi. N’zochititsa chidwi kuti Yesu ananena kuti uthenga wabwino udzalalikidwa padziko lonse lapansi, pamene ankayamikira zimene Mariya anachita. Mawu amenewatu ayenera kuti analimbikitsa kwambiri Mariya pamene anthu ena ankamunena kuti sanachite bwino.

17. Kodi tingafunike kuteteza mlongo wathu pa zochitika ngati ziti?

17 Kodi nanunso mumathandiza alongo anu pakafunika kuti muwateteze? Mwachitsanzo, taganizirani zinthu zotsatirazi. Ofalitsa ena amaona kuti mlongo wina yemwe mwamuna wake si wa Mboni, amafika mochedwa pamisonkhano komanso amachoka ikangotha. Amaonanso kuti sakonda kubwera ndi ana ake. Choncho amamunena kuti bwanji sakakamiza mwamuna wakeyo kuti azimulola kutenga ana popita kumisonkhano. Komabe chomwe anthuwo sakudziwa n’chakuti mlongoyo amayesetsa kuchita zomwe angathe. Mlongoyu amafika mochedwa kumisonkhano chifukwa amatanganidwa kwambiri komanso mwamuna wake ndi amene ali ndi mphamvu posankha zochita zokhudza ana awo. Kodi inuyo mungatani mutamva anthu ena akumunena mlongoyo? Ngati mutanena zomuyamikira komanso kuwauza anthuwo zinthu zimene mlongoyo amachita bwino, akhoza kusiya kumunena.

18. Kodi tingathandize alongo athu m’njira zinanso ziti?

18 Tingasonyeze kuti timakonda alongo athu powathandiza kuchita zinthu zina. (1 Yoh. 3:18) Annette, yemwe ankasamalira mayi ake omwe ankadwala anati: “Abale ndi alongo ena ankabwera kunyumba kwathu kudzasamalira mayi anga kuti nanenso ndipeze mpata wochita zinthu zina, enanso ankatibweretsera chakudya. Zimenezi zinandithandiza kuona kuti amandikonda komanso kuti ndine wofunika mumpingo.” Mlongo Jordan nayenso anathandizidwa ndi ena. Mwachitsanzo, m’bale wina anamuthandiza kudziwa mmene angamakonzere galimoto yake. Iye anati: “Ndinasangalala kuona kuti abale ndi alongo anga amandikonda ndipo amafuna kuti ndizikhala wotetezeka ndikamayendetsa galimoto yanga.”

19. Kodi akulu angathandize alongo m’njira zinanso ziti?

19 Nawonso akulu amayesetsa kuthandiza alongo. Iwo amadziwa kuti Yehova amafuna kuti alongo azisamalidwa bwino. (Yak. 1:27) Choncho akulu amayesetsa kutengera chitsanzo cha Yesu ndipo amachita zinthu moganiza bwino. Iwo amachita zimenezi popewa kumangopanga malamulo pa nthawi yomwe zingakhale bwino kuchita zinthu mwachifundo komanso kumvetsa mavuto amene alongo amakumana nawo. (Mat. 15:22-28) Akulu akamayesetsa kuchita zimenezi, amathandiza alongo kudziwa kuti Yehova komanso gulu lake amawakonda. Woyang’anira kagulu ka utumiki kamene mlongo Kia ankalalikira, atadziwa kuti akusamukira kunyumba ina, anakonza zoti amuthandize. Mlongoyu anati: “Zimenezi zinachepetsa nkhawa yomwe ndinali nayo. Chifukwa choti anandilimbikitsa komanso kundithandiza, akuluwo anasonyeza kuti amandiona kukhala wofunika mumpingo ndiponso kuti ndisamadzione kuti ndili ndekha ndikakumana ndi mavuto.”

ALONGO ONSE MUMPINGO AMAFUNA THANDIZO LATHU

20-21. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timakonda alongo athu onse mumpingo?

20 M’mipingo yathu masiku ano muli alongo ambiri akhama omwe amafunika thandizo lathu. Monga mmene taonera chitsanzo cha Yesu, tingathandize alongo athu tikamapeza mpata wocheza nawo, n’cholinga choti tiwadziwe bwino. Tingawayamikirenso chifukwa cha zimene amachita potumikira Mulungu. Komanso tiyenera kumawateteza pakafunikira kutero.

21 Kumapeto kwa kalata yake yopita kwa Akhristu a ku Roma, mtumwi Paulo anatchula mayina alongo 9. (Aroma 16:1, 3, 6, 12, 13, 15) N’zosakayikitsa kuti alongowa analimbikitsidwa kwambiri kumva Paulo akuwapatsa moni komanso kuwayamikira. Nafenso tiyenera kumathandiza alongo athu mumpingo. Tikamachita zimenezi timasonyeza kuti timawakonda komanso kuti ndi anthu am’banja lathu.

NYIMBO NA. 136 Yehova “Akufupe Mokwanira”

^ ndime 5 Alongo athu amakumana ndi mavuto ambiri. Munkhaniyi tiona mmene tingalimbikitsire alongo athuwa potsanzira Yesu. Tionanso kuti Yesu ankapeza nthawi yocheza ndi akazi, kuwayamikira komanso kuwateteza.

^ ndime 5 Mayina ena asinthidwa.

^ ndime 6 Buku lina limati: “Ophunzira ankakhala pamapazi a aphunzitsi awo. Iwo ankachita zimenezi pokonzekera kudzakhalanso aphunzitsi, koma akazi sankaloledwa kukhala aphunzitsi. . . . Choncho amuna ambiri a Chiyuda akanadabwa kwambiri kuona Mariya atakhala pamapazi a Yesu n’kumamumvetsera mwachidwi.”

^ ndime 9 Akulu ayenera kuchita zinthu mosamala akamathandiza alongo. Mwachitsanzo, ayenera kupewa kupita okha ngati akukathandiza mlongo.

^ ndime 65 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: M’bale akusonyeza kuti amatsanzira chitsanzo cha Yesu posonyeza kuti amaganizira alongo okhulupirika, m’bale akuthandiza alongo awiri kusintha tayala la galimoto yawo, m’bale wina wapita kukaona mlongo wachikulire, ndipo m’bale winanso wapita ndi mkazi wake kunyumba ya mlongo wina ndi mwana wake kuti akachite kulambira kwa pabanja.