Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 39

Muziwathandiza Alongo Mumpingo

Muziwathandiza Alongo Mumpingo

“Akazi amene akulengeza uthenga wabwino ndi khamu lalikulu.”—SAL. 68:11.

NYIMBO 137 Azimayi Okhulupilika, Alongo Athu

ZIMENE TIKAMBILANE *

Alongo athu akhama akupeleka ndemanga pa misonkhano, akulalikila, akukonzanso Nyumba za Ufumu, ndiponso akuonetsa kuti amakonda Akhristu anzawo (Onani ndime 1)

1. Kodi alongo amathandiza pa nchito ziti m’gulu la Yehova? Nanga ambili amakumana na mavuto otani? (Onani cithunzi pacikuto.)

N’ZOKONDWELETSA ngako kuti mumpingo tili na alongo ambili amene amatumikila mwakhama! Mwacitsanzo, alongo amapeleka ndemanga pa misonkhano, komanso amatengako mbali pa nchito yolalikila. Ena amagwila nchito yokonzanso Nyumba za Ufumu, ndipo amaonetsa kuti amakonda Akhristu anzawo. Komabe, iwo amakumana na mavuto. Ena amasamalila makolo awo okalamba. Ena amatsutsidwa na a m’banja lawo. Enanso amalela okha ana, ndipo amagwila nchito mwakhama kuti apezele anawo zofunikila.

2. N’cifukwa ciani tifunika kuyesetsa kuthandiza alongo athu?

2 N’cifukwa ciani tifunika kuthandiza alongo athu? Cifukwa cakuti anthu m’dzikoli kambili salemekeza akazi. Kuwonjezela apo, Baibo imatilimbikitsa kuti tiziwathandiza. Mwacitsanzo, mtumwi Paulo analangiza mpingo wa ku Roma kuti ulandile mlongo Febe na ‘kumuthandiza pa nkhani iliyonse imene angafune thandizo lawo.’ (Aroma 16:1, 2) Pamene Paulo anali Mfarisi, anali m’gulu la anthu amene anali kuona kuti akazi ni anthu otsika komanso osafunika. Koma atakhala Mkhristu, anatengela citsanzo ca Yesu, ndipo anayamba kulemekeza akazi na kucita nawo zinthu mokoma mtima. —1 Akor. 11:1.

3. Kodi Yesu anali kucita nawo zinthu motani akazi? Nanga akazi amene anali kucita cifunilo ca Mulungu anali kuwaona bwanji?

3 Yesu anali kucita zinthu mwaulemu ndi akazi onse. (Yoh. 4:27) Iye sanali kuona akazi monga mmene atsogoleli acipembedzo aciyuda anali kuwaonela m’nthawi yake. Ndipo buku lina lofotokoza Baibo limati: “Yesu sanakambepo mawu onyoza kapena opeputsa akazi.” M’malomwake, anali kulemekeza kwambili akazi amene anali kucita cifunilo ca Atate wake. Anali kuwaona monga alongo ake, ndipo anawachula pamodzi na amuna amene iye anali kuwaona kuti ni banja lake lauzimu.—Mat. 12:50.

4. Kodi tikambilana ciani m’nkhani ino?

4 Yesu anali wokonzeka nthawi zonse kuthandiza alongo ake auzimu. Iye anali kuwaona kuti ni ofunika, anali kuwayamikila, ndiponso anali kuwaikila kumbuyo. Tiyeni tikambilane zimene tingacite potengela citsanzo ca Yesu coganizila alongo athu acikhristu.

MUZIWAGANIZILA ALONGO ATHU OKONDEDWA

5. N’cifukwa ciani alongo ena cimawavuta kupindula na mayanjano olimbikitsa?

5 Ife tonse kaya ndife abale kapena alongo, timafunikila mayanjano olimbikitsa. Koma nthawi zina alongo cingawavute kupindula na mayanjano aconco. Cifukwa ciani? Onani zimene alongo ena anakamba. Mlongo wina dzina lake Jordan * anati, “Popeza ndine mbeta, nthawi zambili nimadziona monga wosafunikila mumpingo. Nimadzionanso ngati sindili mbali ya mpingo.” Mlongo Kristen amene ni mpainiya, ndipo anawonjezela utumiki wake mwa kusamukila kudela lina anati: “Ukakhala watsopano mumpingo, ungamakhale wosungulumwa.” Abale ena angamvelenso cimodzi-modzi. Akhristu amene a m’banja lawo si Mboni, nthawi zina cingakhale comuvuta kugwilizana ndi a m’banja lakewo, ndipo pa nthawi imodzimodzi angamadzione kuti ni wotalikilana na abale na alongo mumpingo. Alongo ena amakhala osungulumwa cifukwa ni odwala ndipo sangacoke panyumba, kapena cifukwa amasamalila m’bululu wawo wodwala. Mlongo Annette anati: “Abale na alongo akaniitanila kumaceza, zinali zovuta kupezekako cifukwa n’nali na udindo waukulu wosamalila amayi.”

Mofanana na Yesu, timawadela nkhawa mwacikondi alongo athu okhulupilika (Onani ndime 6-9) *

6. Kodi lemba la Luka 10:38-42, lionetsa kuti Yesu anathandiza bwanji Marita na Mariya?

6 Yesu anali kupatula nthawi yoceza na alongo ake auzimu, ndipo anali bwenzi labwino kwa iwo. Ganizilani ubwenzi umene unalipo pakati pa iye na Mariya komanso Marita, alongo amene mwacidziŵikile anali osakwatiwa. (Ŵelengani Luka 10:38-42.) N’zoonekelatu kuti mwa zokamba na zocita zake, Yesu anapangitsa alongowo kukhala omasuka. Mwacitsanzo, Mariya anamasuka kukhala pansi pafupi na iye monga wophunzila wake. * Nayenso Marita ataona kuti Mariya sakumuthandiza nchito, anamasuka kuuza Yesu dandaulo lake. Panthawi ya maceza imeneyo, Yesu anaphunzitsa azimayi aŵiliwa mfundo zofunika zauzimu. Ndipo iye anaonetsa kuti anali kuwakonda azimayiwa pamodzi na mlongo wawo Lazaro, mwa kupita kukawacezela pa nthawi zina. (Yoh. 12:1-3) Conco, n’zosadabwitsa kuti Lazaro atadwala kwambili, Mariya na Marita anamasuka kupempha thandizo kwa Yesu.—Yoh. 11:3, 5.

7. Kodi njila imodzi imene tingalimbikitsile alongo ni iti?

7 Alongo ambili amaona kuti amakhala na mwayi waukulu woceza na olambila anzawo pa nthawi ya misonkhano. Conco, akabwela kumisonkhano tiyenela kuwalandila na manja aŵili, kukamba nawo, na kuwaonetsa kuti timawakonda na kuwaganizila. Mlongo Jordan amene tamuchulapo kale anati, “Nimalimbikitsidwa kwambili ena akayamikila ndemanga zanga, akakonza zakuti tiyendele limodzi mu ulaliki, kapena akanicitila zinthu zina zoonetsa kuti amanikonda.” Tifunika kucita zinthu zoonetsa kuti timaona alongo athu kuti ni ofunika. Mlongo Kia anati, “Ngati sin’napezeke pamisonkhano, nimadziŵa kuti nidzalandila mameseji ocokela kwa abale na alongo ofuna kudziŵa ngati nili bwino. Izi zimanithandiza kutsimikizila kuti iwo amanikonda kwambili.”

8. Kodi tingatengele citsanzo ca Yesu m’njila zina ziti?

8 Mofanana na Yesu, nafenso tingapatule nthawi yoceza na alongo. Mwina tingawaitanileko kunyumba kwathu kuti tidzadye nawo cakudya kapena kucita nawo zosangalatsa zina. Akabwela, tiyenela kuonetsetsa kuti maceza athu ni olimbikitsa. (Aroma 1:11, 12) Akulu ayenela kukhala na maganizo monga amene Yesu anali nawo. Iye anali kudziŵa kuti kukhala pa umbeta kungakhale kovuta kwa Akhristu ena. Koma mosapita m’mbali, Yesu anafotokoza kuti kukwatiwa kapena kukhala ndi ana sindiye kumene kumabweletsa cimwemwe cokhalitsa. (Luka 11:27, 28) M’malomwake, munthu amakhala na cimwemwe cokhalitsa ngati amaika patsogolo utumiki wake kwa Yehova.—Mat. 19:12.

9. Kodi akulu angacite ciani kuti athandize alongo?

9 Akulu maka-maka ayenela kucita zinthu na akazi acikhristu monga alongo awo komanso amayi awo auzimu. (1 Tim. 5:1, 2) Akulu angacite bwino kumapatulako nthawi yokamba na alongo misonkhano isanayambe ndiponso ikatha. Mlongo Kristen anati: “Mkulu wina anaona kuti n’nali kukhala wotangwanika, ndipo anafuna kudziŵa mmene ndandanda yanga inalili. N’nayamikila kwambili kuona kuti mkuluyo anali kunidela nkhawa.” Ngati akulu nthawi zonse amapatula nthawi yoceza na alongo awo auzimu, amaonetsa kuti amawakonda. * Annette amene tamuchula poyamba paja anafotokoza ubwino wokamba na akulu nthawi zonse. Iye anati: “Kumanipatsa mwayi wowadziŵa bwino, ndipo nawonso amanidziŵa bwino. Ndiyeno nikakumana na vuto lalikulu, nimakhala womasuka kukapempha thandizo kwa iwo.”

MUZIWAYAMIKILA ALONGO

10. Kodi tingawalimbikitse bwanji alongo athu?

10 Tonsefe, kaya ndife amuna kapena akazi, timalimbikitsidwa ngati ena atiyamikila pa zimene timacita bwino komanso pa nchito imene timacita. Koma zimafooketsa ngati anthu satiyamikila pa maluso amene tili nawo kapena pa nchito imene timagwila. Mpainiya wina dzina lake Abigail amene ni mbeta anakamba kuti nthawi zina amaona kuti ena samuŵelengela. Anati: “Nimangodziŵika kuti ndine mlongosi wa m’bale uje kapena mwana wa m’bale uje. Nthawi zina nimaona monga kuti palibe amene amaniŵelengela.” Mosiyana na zimenezi, onani zimene mlongo Pam amene ni mbeta anakamba. Iye anatumikila monga mmishonale kwa zaka zambili. M’kupita kwa nthawi anabwelela kunyumba kukasamalila makolo ake. Pano tikamba ali na zaka za m’ma 70, ndipo akali kucitabe upainiya. Mlongo Pam anati: “Cimene canithandiza kwambili ni mawu amene ena amakamba oniyamikila pa nchito imene nimacita.”

11. Kodi Yesu anaonetsa bwanji kuti anali kuyamikila thandizo la akazi amene anali kuyenda naye pocita utumiki wake?

11 Yesu anayamikila thandizo la akazi oopa Mulungu amene anali kumutumikila “pogwilitsa nchito cuma cawo.” (Luka 8:1-3) Iye anawalola kuti azimutumikila, ndiponso anali kuwauza mfundo zozama za coonadi. Mwacitsanzo, pa nthawi ina anawauza kuti iye adzafa kenako adzaukitsidwa. (Luka 24:5-8) Komanso monga mmene anacitila na atumwi ake, iye anakonzekeletsa akazi amenewo kaamba ka mayeselo amene anali kudzakumana nawo kutsogolo. (Maliko 9:30-32; 10:32-34) N’zocititsa cidwi kuti ngakhale kuti atumwi anamuthaŵa Yesu pa nthawi imene anagwidwa, akazi ena amene anali kumutumikila anali naye pafupi pamene iye anali kufa pa mtengo wozunzikilapo.—Mat. 26:56; Maliko 15:40, 41.

12. Ni nchito ziti zimene Yesu anapatsa akazi?

12 Yesu anapatsa akazi nchito yofunika. Mwacitsanzo, akazi oopa Mulungu ndiwo anali oyamba kudziŵa kuti Yesu waukitsidwa. Ndipo iye anawatuma kuti akauze atumwi kuti iye waukitsidwa kwa akufa. (Mat. 28:5, 9, 10) Komanso, akazi ayenela kuti analipo pa Pentekosite wa mu 33 C.E., pamene ophunzila a Khristu anadzozedwa na mzimu woyela. Ngati zinalidi conco, ndiye kuti alongo odzozedwa catsopanowo analandilako mphamvu yozizwitsa yokamba zinenelo zosiyana-siyana, ndipo anali kuuzako ena “zinthu zazikulu za Mulungu.”—Mac. 1:14; 2:2-4, 11.

13. Kodi alongo amacita nchito zotani masiku ano? Nanga imwe muganiza kuti tingaonetse bwanji kuti timayamikila zimene amacita?

13 Alongo athu tifunika kuwayamikila kwambili pa zonse zimene amacita mu utumiki wa Yehova. Nchito zina zimene amacita ni monga kumanga na kukonzanso nyumba zolambililamo, kuthandizila tumagulu tokamba citundu cina, komanso kudzipeleka kukathandizila nchito pa Beteli. Enanso amathandiza pa nchito yopeleka thandizo pakagwa masoka a zacilengedwe, kumasulila mabuku athu, komanso kutumikila monga apainiya ndiponso amishonale. Mofanana na abale, alongo nawonso amangena sukulu ya apainiya, Sukulu ya Alengezi a Ufumu, na Sukulu ya Giliyadi. Kuwonjezela apo, akazi amathandiza amuna awo kusamalila maudindo aakulu mumpingo ndi nchito zina m’gulu la Yehova. Popanda kuthandizidwa na akazi awo, abale apaudindo amenewa sangakwanitse kutumikila mokwanila pa udindo wawo monga “mphatso za amuna.” (Aef. 4:8) Kodi imwe muganiza kuti tingawathandize bwanji alongo athu pa nchito zimene amacita?

14. Kodi lemba la Salimo 68:11, limakamba ciani za alongo? Nanga akulu anzelu amacita ciani?

14 Akulu anzelu amazindikila kuti alongo ni “khamu lalikulu” la anchito odzipeleka, ndipo nthawi zambili amakhala aluso kwambili pa nchito yolalikila uthenga wabwino. (Ŵelengani Salimo 68:11.) Conco akulu amayesetsa kupeza mipata yophunzilako zinthu zina kwa alongo. Abigail amene tam’chulapo kale m’nkhani ino, amalimbikitsidwa ngati abale amufunsa kuti afotokoze njila zimene waona kuti n’zothandiza kwambili poyambitsa makambilano ndi anthu a m’gawo la mpingo wawo. Iye anati: “Izi zimanithandiza kuona kuti Yehova amaona kuti ndine wofunika m’gulu lake.” Kuwonjezela apo, akulu amadziŵa kuti alongo acikulile okhulupilika amadziŵa bwino kuthandiza alongo acicepele polimbana na mavuto. (Tito 2:3-5) Kukamba zoona, timafunika kuwayamikila kwambili alongo athu amenewa!

MUZIWAIKILAKO KUMBUYO ALONGO NA KUWATHANDIZA

15. Ni panthawi iti pamene alongo angafunikile wina wowakambilako?

15 Nthawi zina, alongo angafunikile munthu wina wowaikilako kumbuyo kapena kuti kuwakambilako pa zovuta zimene angakumane nazo. (Yes. 1:17) Mwacitsanzo, mlongo wamasiye kapena amene anasudzulidwa na mwamuna wake, angafunikile wina womukambilako pa nkhani zina, komanso kumuthandiza pa nchito zina zimene mwamuna wake anali kucita. Komanso mlongo wacikulile angafunikile munthu wina womuthandiza pokamba na madokotala. Nthawi zinanso, mlongo mpainiya amene amagwila nchito zina za m’gulu angafunikile wina womuikilako kumbuyo ngati ena akumunena kuti sacita zambili mu ulaliki monga mmene apainiya ena amacitila. Kodi ni zinthu ziti zina zimene tingacite kuti tithandize alongo athu? Tiyeni tikambilanenso citsanzo ca Yesu.

16. Malinga na mawu a pa Maliko 14:3-9, kodi Yesu anamuikila bwanji kumbuyo Mariya?

16 Yesu anali kuwaikila kumbuyo mwamsanga alongo ake auzimu ngati anthu ena akuwakambila zoipa. Mwacitsanzo, anaikila kumbuyo Mariya pamene Marita anamuimba mlandu. (Luka 10:38-42) Panthawi inanso, Yesu anaikila kumbuyo Mariya pamene ena anali kumudzudzula poganiza kuti zimene anacita zinali zolakwika. (Ŵelengani Maliko 14:3-9.) Yesu anadziŵa cimene cinasonkhezela Mariya kucita zimenezo, ndipo anamuyamikila. Yesu anati: “Iyetu wandicitila zinthu zabwino. . . . Mayiyu wacita zimene angathe.” Iye anafika ngakhale polosela kuti zimene anacitazo zidzalengezedwa “kulikonse kumene uthenga wabwino udzalalikidwe m’dziko lonse,” monga mmene nkhani ino ikucitila. N’zocititsa cidwi kuti potamanda Mariya cifukwa ca cikondi cake copanda dyela, Yesu anakamba kuti zimene iye anacitazo zidzadziŵika kulikonse kumene uthenga wabwino udzalalikidwa padziko lapansi. Ndithudi, mawu a Yesu amenewa ayenela kuti anamulimbikitsa kwambili Mariya pamene ena anali kumunena kuti zimene wacita n’zolakwika!

17. Ni panthawi iti pamene tingafunike kumuikila kumbuyo mlongo? Fotokozani citsanzo.

17 Kodi mumawakambilako alongo anu auzimu pakakhala pofunikila? Mwacitsanzo, ganizilani cocitika ici congoyelekezela. Tinene kuti ofalitsa ena amaona kuti mlongo wina amene mwamuna wake si Mboni, amakonda kufika mocedwa pamisonkhano, ndiponso amacoka mwamsanga misonkhano ikatha. Komanso amaona kuti nthawi zambili satenga ana ake pobwela ku misonkhano. Conco, iwo akumunena kuti sayesetsa kupempha mwamuna wake kuti azimulola kutenga ana pobwela ku misonkhano. Koma zoona zake n’zakuti mlongoyo akucita zonse zimene angathe. Iye alibe ufulu wokwanila wosankha nthawi yocita zinthu. Ndiponso alibe mphamvu yolamula zimene ana afunika kucita. Kodi imwe mungacite ciani mukamvela ena akunena mlongoyo mwanjila imeneyo? Mungacite bwino kumuyamikila mlongoyo na kufotokozela ofalitsa enawo zimene iye amacita bwino. Mukatelo, mungathandize kuti ofalitsa enawo aleke kumukambila zoipa.

18. Kodi alongo athu tingawathandize m’njila zina ziti?

18 Tingaonetse kuti timawakonda kwambili alongo athu mwa kudzipeleka kuwathandiza pa zinthu zina. (1 Yoh. 3:18) Mlongo Annette amene anali kusamalila amayi ake odwala anati: “Abale na alongo ena anali kubwela kunyumba kudzanithandizako kusamalila amayi kuti nikhale na nthawi yocita zinthu zina. Nthawi zina anali kungobweletsa zakudya. Izi zinali kunipangitsa kuona kuti iwo amanikonda. Zinanipangitsanso kudziona kuti nili mbali ya mpingo.” Nayenso mlongo Jordan analandilapo thandizo. M’bale wina anamuphunzitsa mmene angasamalile na kukonza motoka yake. Iye anati: “N’zokondweletsa kudziŵa kuti abale na alongo amanidela nkhawa, ndipo amafuna kuti nizikhala wotetezeka pamene niyendetsa motoka.”

19. Kodi akulu angathandize alongo m’njila zina ziti?

19 Akulu amayesetsanso kusamalila zosoŵa za alongo. Amadziŵa kuti Yehova amafuna kuti alongo azisamalidwa bwino. (Yak. 1:27) Conco, amacita zinthu mokoma mtima monga Yesu, ndipo saika malamulo pamene sipafunikila malamulo. (Mat. 15:22-28) Ngati akulu ayesetsa kuthandiza alongo, alongowo amaona kuti Yehova na gulu lake amawakonda. Mwacitsanzo, woyang’anila kagulu atamvela kuti mlongo Kia akukukila ku nyumba ina, nthawi yomweyo anakonza zakuti amuthandize. Kia anati: “Zimenezi zinanicepetsela nkhawa kwambili. Mawu olimbikitsa amene akulu ananiuza na zimene anacita ponithandiza, zinaonetselatu kuti amaniona kuti ndine wofunika mumpingo, komanso kuti ni okonzeka kunithandiza panthawi ya mavuto.”

ALONGO ATHU ONSE AUZIMU AMAFUNIKILA THANDIZO LATHU

20-21. Kodi tingaonetse bwanji kuti alongo athu onse timawakonda?

20 Masiku ano, tikayang’ana m’mipingo tipeza kuti muli akazi acikhristu ambili ofunika kuwathandiza amene amatumikila mwakhama. Monga taphunzilila pa citsanzo ca Yesu, tingawathandize mwa kupatula nthawi yoceza nawo na kuwadziŵa bwino. Tiyenela kuwayamikila pa zimene amacita potumikila Mulungu. Ndipo tingawakambileko pakakhala pofunikila.

21 Cakumapeto kwa kalata yake imene analembela Akhristu a ku Roma, mtumwi Paulo anachula maina 9 a akazi acikhristu. (Aroma 16:1, 3, 6, 12, 13, 15) Mosakayikila, akazi amenewo analimbikitsidwa ngako kumvela kuti Paulo wawapatsa moni na kuwayamikila. Na ife tiyeni tizithandiza alongo onse mumpingo mwathu. Tikatelo, tidzaonetsa kuti timawakonda alongo athu amene ali mbali ya banja lathu lauzimu.

NYIMBO 136 Yehova “Akufupe Mokwanila”

^ ndime 5 Alongo amakumana na mavuto ambili. M’nkhani ino, tikambilana mmene tingathandizile alongo mumpingo potengela citsanzo ca Yesu. Iye anali kupatula nthawi yoceza na akazi, kuwaonetsa kuti anali ofunika, komanso kuwaikila kumbuyo. Tiona zimene tingaphunzile kwa iye pa mbali zimenezi.

^ ndime 5 Maina ena asinthidwa.

^ ndime 6 Buku lina limati: “Ophunzila anali kukhala pafupi na mphunzitsi wawo. Ophunzila akhama, anali kukonzekela kuti akaphunzila akakhale aphunzitsi—nchito imene akazi sanali kuloledwa kugwila. . . . Conco amuna ambili aciyuda akanadabwa kuona Mariya atakhala pansi pafupi na Yesu ali na mtima wofuna kuphunzitsidwa na iye.”

^ ndime 9 Akulu ayenela kukhala osamala pothandiza alongo. Mwacitsanzo, ayenela kupewa kupita kukacezela mlongo ali okha.

^ ndime 65 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Potengela citsanzo ca Yesu cokonda akazi okhulupilika, m’bale akuthandiza alongo aŵili kusintha wilo ku motoka yawo, m’bale wina wapita kukacezela mlongo wodwala, ndipo m’bale winanso na mkazi wake wapita kukacita nawo kulambila kwa pabanja ku nyumba kwa mlongo wina na mwana wake.