Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 40

‘Sungani Bwino Cimene Cinaikidwa M’manja Mwanu’

‘Sungani Bwino Cimene Cinaikidwa M’manja Mwanu’

“Timoteyo, sunga bwino cimene cinaikidwa m’manja mwako.” —1 TIM. 6:20.

NYIMBO 29 Tikhala Monga mwa Dzina Lathu

ZIMENE TIKAMBILANE *

1-2. Malinga na 1 Timoteyo 6:20, kodi Timoteyo anafunika kucita ciani?

NTHAWI zambili, timapempha anthu ena kuti atisungileko zinthu zathu za mtengo wapatali. Mwacitsanzo, tingasungitse ndalama zathu ku banki. Tikatelo, timakhala na cidalilo cakuti ndalamazo zidzasungika bwino, ndipo sizidzatayika kapena kubedwa. Tsopano tamvetsa tanthauzo la kusungitsa cinthu cathu ca mtengo wapatali kwa munthu wina.

2 Ŵelengani 1 Timoteyo 6:20. Mtumwi Paulo anakumbutsa Timoteyo kuti analandila cinthu ca mtengo wapatali. Cinthu cimeneco ni cidziŵitso colondola conena za colinga ca Mulungu kwa anthu. Timoteyo anapatsidwanso mwayi ‘wolalikila mawu,’ ndiponso ‘wogwila nchito ya mlaliki.’ (2 Tim. 4:2, 5) Paulo analangiza Timoteyo kuti asunge bwino zinthu zimene zinaikidwa m’manja mwake. Mofanana na Timoteyo, nafenso Mulungu watisungiza zinthu zamtengo wapatali. Kodi ni zinthu zotani zimenezo? Nanga n’cifukwa ciani tifunika kuteteza cuma cimene Yehova watipatsa?

TAPATSIDWA COONADI CA MTENGO WAPATALI

3-4. Chulani zifukwa zina zimene tikambila kuti coonadi ca m’Baibo ni camtengo wapatali.

3 Mokoma mtima, Yehova anatithandiza kumvetsetsa coonadi camtengo wapatali copezeka m’Mawu ake, Baibo. Coonadi ca m’Baibo cimeneci ni camtengo wapatali cifukwa cimatithandiza kudziŵa mmene tingakhalile paubale wabwino na Yehova, komanso mmene tingakhalile na cimwemwe ceni-ceni mu umoyo. Ngati timakhulupilila mfundo za coonadi zimenezi na kuzitsatila, timamasuka ku ziphunzitso zonama na kupewa makhalidwe oipa.—1 Akor. 6:9-11.

4 Palinso cifukwa cina cimene cimapangitsa coonadi ca m’Mawu a Mulungu kukhala camtengo wapatali. Cifukwa cake n’cakuti Yehova amaulula coonadi cimeneci kwa anthu okhawo odzicepetsa amene ali na “maganizo abwino.” (Mac. 13:48) Anthu odzicepetsa amenewa amakhulupilila kuti Yehova amaseŵenzetsa kapolo wokhulupilika ndi wanzelu potiphunzitsa coonadi masiku ano. (Mat. 11:25; 24:45) Pa ife tekha, sitingakwanitse kumvetsetsa coonadi, ndipo palibe cina camtengo wapatali kuposa kumvetsetsa coonadi.—Miy. 3:13, 15.

5. N’ciani cina cimene Yehova watipatsa?

5 Yehova anatipatsanso mwayi wophunzitsako ena coonadi ponena za iye na colinga cake. (Mat. 24:14) Uthenga umene timalalikila ni wamtengo wapatali kwambili cifukwa umathandiza anthu kubwela m’banja la Yehova. Umawapatsanso mwayi wokapeza moyo wosatha. (1 Tim. 4:16) Conco, mosasamala kanthu za kuculuka kwa zimene timakwanitsa kucita mu ulaliki, timathandiza pa nchito yofunika kwambili imene ikucitika masiku ano. (1 Tim. 2:3, 4) Ni mwayi waukulu cotani nanga kukhala anchito anzake a Mulungu!—1 Akor. 3:9.

GWILITSITSANI CIMENE MWAPATSIDWA!

Timoteyo anakhalabe m’coonadi pamene ena anasankha kusiya coonadi (Onani ndime 6)

6. N’ciani cinacitika kwa anthu amene analephela kugwilitsitsa zinthu zimene anapatsidwa?

6 M’nthawi ya Timoteyo, Akhristu ena analephela kuyamikila mwayi wokhala anchito anzake a Mulungu. Mwacitsanzo, cifukwa cokonda zinthu za m’dzikoli, Dema anataya mwayi wake wotumikila pamodzi na Paulo. (2 Tim. 4:10) Ndipo zioneka kuti Fugelo na Heremogene anasiya utumiki wawo cifukwa coopa kuzunzidwa mmene Paulo anazunzidwila. (2 Tim. 1:15) Hemenayo, Fileto, ndi Alekizanda, anakhala a mpatuko ndipo anasiya coonadi. (1 Tim. 1:19, 20; 2 Tim. 2:16-18) Mwacionekele, anthu onsewa poyamba anali olimba mwauzimu, koma analeka kuona kuti zinthu zimene Mulungu anawapatsa zinali zamtengo wapatali.

7. Ni zinthu ziti zimene Satana amacita pofuna kutisonkhezela kucita zofuna zake?

7 Kodi Satana amacita zotani pofuna kutipangitsa kutaya cuma camtengo wapatali cimene Yehova watipatsa? Onani zina zimene iye amacita. Amaseŵenzetsa zosangalatsa komanso nkhani zimene timamvetsela pa TV, pa wailesi, kapena pa intaneti pofuna kutipangitsa kuyamba kuganiza na kucita zinthu zimene pang’ono-mpang’ono, zingaticititse kuleka kukonda Yehova kapena kumvela malamulo ake. Iye amasonkhezela anthu kuti azitiopseza kapena kutizunza n’colinga cakuti tileke kulalikila. Ndiponso pofuna kutisiyitsa coonadi, iye amayesa kutikopa kuti timvetsele nkhani za anthu ampatuko “zimene ena monama amati ndiye ‘kudziŵa zinthu.’”—1 Tim. 6:20, 21.

8. Kodi taphunzilapo ciani pa citsanzo ca m’bale Daniel?

8 Ngati sitingasamale, pang’ono-mpang’ono tingasiye coonadi. Ganizilani citsanzo ca Daniel, * amene anali kukonda maseŵela a pa kompyuta. Iye anati: “N’nayamba kucita maseŵela a pa kompyuta nili na zaka 10. Poyamba, n’nali kucita maseŵela abwino-bwino. Koma pang’ono-mpang’ono, n’nayamba kucita maseŵela a zaciwawa komanso a zamizimu.” M’kupita kwa nthawi, m’baleyu anayamba kucita maseŵelawo kwa maola pafupi-fupi 15 tsiku lililonse. Daniel anakambanso kuti: “Mumtima, n’nali kudziŵa kuti maseŵela amene n’nali kucita ndiponso nthawi imene n’nali kuthela pocita maseŵelawo, zinali kunipangitsa kutalikilana na Yehova. Koma mtima wanga unali utauma moti n’nali kuona kuti mfundo za m’Baibo sizinali kunikhudza.” Conco ngati sitisamala, kukonda zosangalatsa kungatilepheletse kugwilitsitsa coonadi. Ndipo zotulukapo zake n’zakuti tingataye zinthu zamtengo wapatali zimene Yehova watipatsa.

ZIMENE ZINGATITHANDIZE KUGWILITSITSA COONADI

9. Kulingana na 1 Timoteyo 1:18, 19, kodi Paulo anayelekezela Timoteyo na ndani?

9 Ŵelengani 1 Timoteyo 1:18, 19. Paulo anayelekezela Timoteyo na msilikali, ndipo anamulangiza kuti ‘apitilize kumenya nkhondo yabwino.’ Apa Paulo sanali kutanthauza nkhondo yeni-yeni yakuthupi, koma anali kutanthauza nkhondo yauzimu. Kodi Akhristu afanana bwanji na asilikali amene ali pa nkhondo? Monga asilikali a Khristu, ni makhalidwe ati amene tifunika kukulitsa? Tiyeni lomba tikambilane mfundo 5 zimene tingaphunzile pa mawu a Paulo amenewa oyelekezela Mkhristu na msilikali. Mfundo zimenezo zingatithandize kugwilitsitsa coonadi.

10. Kodi kudzipeleka kwa Mulungu kutanthauza ciani? Nanga n’cifukwa ciani timafunika kukhala na khalidwe limeneli?

10 Khalani odzipeleka kwa Mulungu. Msilikali wabwino amakhala wokhulupilika. Iye amamenya nkhondo zolimba kuti ateteze munthu amene amamukonda kapena cinthu cimene amaciona kuti n’camtengo wapatali. Paulo analimbikitsa Timoteyo kukulitsa khalidwe la kudzipeleka kwa Mulungu, kutanthauza kukhala na cikondi cokhulupilika pa Mulungu. (1 Tim. 4:7) Tikamakonda kwambili Mulungu na kukhala odzipeleka kwambili kwa iye, timakhala ofunitsitsa kucigwila mwamphamvu coonadi.—1 Tim. 4:8-10; 6:6.

Tikalema pambuyo poseŵenza tsiku lonse, tingafunike kudzikakamiza kupita ku misonkhano. Koma tikapezekapo, timapindula kwambili. (Onani ndime 11)

11. N’cifukwa ciani timafunika khama na kudziletsa?

11 Phunzilani kucita zinthu mwakhama komanso modziletsa. Msilikali amafunika kukhala wakhama komanso wodziletsa kuti akhale wokonzeka kumenya nkhondo. Timoteyo anakhalabe wolimba mwauzimu cifukwa anatsatila malangizo a Paulo akuti athaŵe zilakolako zoipa, ayesetse kukhala na makhalidwe abwino, komanso akuti aziyanjana na Akhristu anzake. (2 Tim. 2:22) Kuti akwanitse kucita zimenezi anafunika kudziletsa komanso khama. Nafenso timafunika khama na kudziletsa kuti tipambane pa nkhondo yolimbana na zilakolako zathupi. (Aroma 7:21-25) Kuwonjezela apo, timafunika khama na kudziletsa kuti tipitilize kuvula umunthu wakale na kuvala umunthu watsopano. (Aef. 4:22, 24) Ndipo tikalema pambuyo poseŵenza tsiku lonse, tingafunike kudzikakamiza kupita ku misonkhano.—Aheb. 10:24, 25.

12. Kodi luso lathu loseŵenzetsa bwino Baibo pophunzitsa tingalikulitse bwanji?

12 Msilikali amafunika kuyeseza mmene angaseŵenzetsele zida zake zankhondo. Kuti akhale waluso poseŵenzetsa zidazo, amafunika kuyeseza nthawi zonse. Nafenso tifunika kukhala aluso kwambili poseŵenzetsa Mawu a Mulungu. (2 Tim. 2:15) Tingaphunzile ena mwa maluso amenewa pamisonkhano yathu. Koma kuti tikwanitse kuthandiza ena kukhulupilila kuti mfundo za coonadi ca m’Baibo n’zamtengo wapatali, tifunika kumaiŵelenga nthawi zonse. Timafunika kuphunzila Mawu a Mulungu kuti tilimbitse cikhulupililo cathu. Kucita izi kumafuna zambili osati kungoŵelenga cabe Baibo. Timafunikanso kusinkha-sinkha pa zimene taŵelenga na kufufuza m’mabuku athu, n’colinga cakuti timvetsetse na kuwaseŵenzetsa bwino Malemba. (1 Tim. 4:13-15) Tikatelo, tidzakwanitsa kuseŵenzetsa Mawu a Mulungu pophunzitsa ena. Kucita izi kumafunanso zambili osati kungoŵelengela munthu Baibo. Timafunika kuthandiza omvela athu kumvetsetsa vesi imene taŵelenga. Timafunanso kuwathandiza kuona mmene igwilila nchito pa iwo. Mwa kutsatila ndandanda yathu ya kuŵelenga Baibo nthawi zonse, tingakulitse luso lathu loseŵenzetsa bwino Mawu ouzilidwa a Mulungu pophunzitsa ena.—2 Tim. 3:16, 17.

13. Mogwilizana na Aheberi 5:14, n’cifukwa ciani timafunika kukhala ozindikila?

13 Khalani ozindikila. Msilikali amafunika kuonelatu ngozi imene angakumane nayo na kuipewa. Nafenso timafunika kudziŵilatu zocitika zimene zingatigwetsele m’mavuto na kucitapo kanthu kuti tipewe mavuto. (Miy. 22:3; ŵelengani Aheberi 5:14.) Mwacitsanzo, timafunika kusankha zosangalatsa mwanzelu. Nthawi zambili mapulogilamu a pa TV komanso mafilimu amaonetsa makhalidwe oipa. Makhalidwe otelo amakhumudwitsa Mulungu, ndipo amawononga. Motelo timapewa zosangalatsa zoipa cifukwa pang’ono-mpang’ono zingatipangitse kuleka kukonda Yehova.—Aef. 5:5, 6.

14. Kodi kukhala wozindikila kunamuthandiza bwanji Daniel?

14 Daniel amene tamuchulapo kale, anazindikila kuti n’kulakwa kucita maseŵela a zaciwawa komanso zamizimu. Iye anafufuza pa Watchtower Laibulale kuti apeze nkhani zimene zikanamuthandiza kuthetsa vuto lake. Kodi kucita izi kunamuthandiza bwanji? Iye analeka kucita maseŵela oipawo. Analekanso kuyanjana na anzake amene anali kucita nawo maseŵelawo. Daniel anati, “M’malo mocita maseŵela a pa kompyuta, n’nayamba kutayila nthawi pocita zinthu zina kapena kupita kukaceza na anzanga mu mpingo.” Daniel manje ni mpainiya komanso mkulu.

15. N’cifukwa ciani nkhani zabodza n’zoopsa?

15 Mofanana na Timoteyo, na ife tifunika kuzindikila kuopsa kwa nkhani zimene ampatuko amafalitsa. (1 Tim. 4:1, 7; 2 Tim. 2:16) Mwacitsanzo, iwo angafalitse nkhani zabodza ponena za abale athu, kapena zotipangitsa kuyamba kukayikila gulu la Yehova. Nkhani zabodza zimenezo, zingafooketse cikhulupililo cathu. Sitiyenela kuzikhulupilila. Cifukwa ciani? Cifukwa nkhani zimenezo zimafalitsidwa ndi “anthu opotoka maganizo ndi osadziŵa coonadi.” Iwo amangofuna “kukangana ndi anthu ndiponso kutsutsana pa mawu.” (1 Tim. 6:4, 5) Amafuna kuti tizikhulupilila mabodza awo na kuyamba kukayikila abale athu.

16. Ni zinthu zoceutsa ziti zimene tifunika kupewa?

16 Sumikani maganizo pa nchito yolalikila. “Monga msilikali wabwino wa Khristu Yesu,” Timoteyo anasumikabe maganizo ake pa utumiki. Sanalole kuti mtima wofuna-funa zinthu zakuthupi kapena zinthu zina zimulepheletse kucita utumiki wake. (2 Tim. 2:3, 4) Mofanana na Timoteyo, tiyenela kupewa kukhala na mtima wofuna kudziunjikila zinthu zakuthupi. Apo ayi, “cinyengo camphamvu ca cuma” cingapangitse kuti tileke kukonda Yehova, kuyamikila Mawu ake, ndiponso kuuzako ena mawuwo. (Mat. 13:22) Tifunika kukhala na umoyo wosalila zambili na kuseŵenzetsa nthawi na mphamvu zathu ‘popitiliza kufuna-funa Ufumu coyamba.’—Mat. 6:22-25, 33.

17-18. Tingacite ciani kuti tidziteteze ku zinthu zimene zingatiwononge mwauzimu?

17 Khalani okonzeka kucitapo kanthu mwamsanga. Msilikali amafunika kudziŵilatu zimene angacite kuti adziteteze. Kuti nafenso titeteze zinthu zimene Yehova anatipatsa, tifunika kucitapo kanthu mwamsanga tikaona kuti cinacake cifuna kutitayitsa zinthu zimenezo. N’ciani cingatithandize kucitapo kanthu mwamsanga? Tiyenela kudziŵilatu zimene tingacite ngati takumana na zoopsa.

18 Mwacitsanzo, m’madela ena, anthu akapezeka pa cocitika cinacake, nthawi zambili cocitikaco cisanayambe, amapemphedwa kuti adziŵiletu khomo lapafupi limene angatulukile. Cifukwa ciani? Cifukwa ngati pangacitike ngozi kapena vuto lina lalikulu anthuwo angakwanitse kutuluka mwamsanga. Mofananamo, tingaganiziletu pasadakhale zimene tingacite ngati mwadzidzidzi taona zinthu zosayenela, zaciwawa, kapena nkhani za ampatuko poseŵenzetsa intaneti, potamba filimu, kapena potamba pulogilamu inayake pa TV. Ngati takonzekela pasadakhale, tingacitepo kanthu mwamsanga kuti tidziteteze ku zinthu zimene zingatiwononge mwauzimu. Izi zidzatithandiza kukhalabe oyela pamaso pa Yehova.—Sal. 101:3; 1 Tim. 4:12.

19. Kodi tidzapeza madalitso anji ngati tisunga bwino zinthu zamtengo wapatali zimene Yehova watipatsa?

19 Timafunika kusunga bwino zinthu zamtengo wapatali zimene Yehova watipatsa, zomwe ni coonadi camtengo wapatali ca m’Baibo komanso mwayi wophunzitsako ena coonadico. Tikatelo, tidzakhala na cikumbumtima coyela, umoyo waphindu, na cimwemwe cimene cimabwela cifukwa cothandiza ena kudziŵa Yehova. Mwa thandizo lake, tidzakwanitsa kusunga bwino zinthu zamtengo wapatali zimene iye watipatsa.—1 Tim. 6:12, 19.

NYIMBO 127 Mtundu wa Munthu Amene Niyenela Kukhala

^ ndime 5 Tili na mwayi waukulu wodziŵa coonadi komanso wophunzitsako ena coonadi cimeneci. Nkhani ino itithandiza kugwilitsitsa coonadi cimeneco na kusacitaya.

^ ndime 8 Dzina lasinthidwa.