Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Mafunso Ocokela kwa Oŵelenga

Mafunso Ocokela kwa Oŵelenga

Kodi lemba la Mlaliki 5:8 limakamba cabe za olamulila aumunthu kapena limaphatikizaponso Yehova?

Lemba locititsa cidwi limeneli limati: “Ukaona munthu wosauka akupondelezedwa ndiponso zinthu zaciwawa ndi zopanda cilungamo zikucitika m’cigawo ca dziko, usadabwe nazo. Pakuti wamkulu kuposa amene akucita zimenezoyo akuona, ndipo pamwamba pa akuluakuluwo palinso ena akuluakulu kuposa iwowo.”—Mlal. 5:8.

Mkaonedwe kathu ka umunthu, tingaone monga lembali likamba cabe za anthu olamulila m’boma. Koma tikaliganizila mozama, tiona kuti likambanso mfundo inayake yokhudza Yehova, imene ni yotonthoza komanso yolimbikitsa.

Lemba la Mlaliki 5:8 limakamba za wolamulila amene amapondeleza anthu osauka na kuwacitila zinthu zopanda cilungamo. Wolamulilayo afunika kukumbukila kuti winawake amene ali na malo apamwamba kapena kuti ulamulilo waukulu kuposa iye, akuona zimene akucita. Ndipo pangakhale anthu ena amene ali na ulamulilo waukulu kuposa onsewo. Koma n’zacisoni kuti m’maboma a anthu, olamulila onse nthawi zina amakhala opanda cilungamo, ndipo anthu wamba amavutika cifukwa ca kupanda cilungamo kwawo.

Koma olo zinthu zivute bwanji, tingapeze citonthozo podziŵa kuti Yehova akuyang’ana ngakhale olamulila akulu-akulu m’maboma a anthu. Tingapemphe thandizo kwa Mulungu na kumutulila nkhawa zathu. (Sal. 55:22; Afil. 4:6, 7) Tidziŵa kuti “maso a Yehova akuyenda-yenda padziko lonse lapansi kuti aonetse mphamvu zake kwa anthu amene mtima wawo uli wathunthu kwa iye.” —2 Mbiri 16:9.

Conco, lemba la Mlaliki 5:8 limatikumbutsa mmene zinthu zilili m’maboma a anthu kuti nthawi zonse pamakhala winawake wa ulamulilo waukulu kuposa ena. Koma cofunika kwambili n’cakuti lembali limatithandiza kukumbukila mfundo yakuti Yehova ndiye Wolamulila Wamkulu kuposa onse. Palipano, iye akulamulila kupitila mwa Mwana wake Yesu Khristu, amene ni Mfumu ya Ufumu wake. Yehova Wamphamvuzonse ameneyo, akuona zonse zimene zikucitika, ndipo ni wacilungamo nthawi zonse. Umu ni mmenenso Mwana wake alili.