Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 43

Yehova Akutsogolela Gulu Lake

Yehova Akutsogolela Gulu Lake

“‘Sipakufunika gulu lankhondo, kapena mphamvu, koma mzimu wanga,’ watelo Yehova wa makamu.”—ZEK. 4:6.

NYIMBO 40 Kodi Ndife a Ndani?

ZIMENE TIKAMBILANE *

1. Kodi Akhristu obatizika afunika kupitiliza kucita ciani?

KODI ndimwe wobatizika? Ngati inde, ndiye kuti munalengeza poyela kuti mumakhulupilila Yehova, ndipo ndimwe wofunitsitsa kutumikila m’gulu * lake. Koma cikhulupililo canu mwa Yehova cifunika kupitiliza kukula. Ndipo mufunika kulimbitsa cidalilo canu cakuti Yehova akuseŵenzetsa gulu lake masiku ano.

2-3. Kodi Yehova amatsogolela gulu lake mwa njila yotani masiku ano? Pelekani zitsanzo za makhalidwe ake.

2 Masiku ano, njila imene Yehova amatsogolela gulu lake imaonetsa makhalidwe ake, colinga cake, na miyezo yake. Pa makhalidwe a Yehova, tiyeni tikambilanepo atatu amene amaonekela m’gulu lake.

3 Loyamba, “Mulungu alibe tsankho.” (Mac. 10:34) Cikondi ndico cinalimbikitsa Yehova kupeleka Mwana wake monga “dipo lokwanila ndendende m’malo mwa onse.” (1 Tim. 2:6; Yoh. 3:16) Yehova amaseŵenzetsa anthu ake kulalikila uthenga wabwino kwa onse amene angamvetsele, kuti athandize ambili kupindula na dipo limeneli. Laciŵili, Yehova ni Mulungu wadongosolo komanso wamtendele. (1 Akor. 14:33, 40) Conco, m’pake kuti olambila ake amam’tumikila mwadongosolo komanso mwamtendele. Lacitatu, Yehova ni “Mlangizi . . . Wamkulu.” (Yes. 30:20, 21) Conco, gulu lake limaika patsogolo kuphunzitsa Mawu ake ouzilidwa, ponse paŵili mu mpingo na mu ulaliki. Kodi makhalidwe atatu a Yehova amenewa anali kuonekela bwanji mu mpingo wa Akhristu oyambilila? Nanga amaonekela motani masiku ano? Kodi mzimu woyela ungakuthandizeni bwanji potumikila m’gulu la Yehova masiku ano?

MULUNGU ALIBE TSANKHO

4. Malinga na Machitidwe 1:8, Yesu analamula otsatila ake kucita ciani? Nanga anayembekezela kulandila thandizo lotani?

4 M’nthawi ya Akhristu oyambilila. Uthenga umene Yesu analalikila unapeleka ciyembekezo kwa anthu onse. (Luka 4:43) Analamula otsatila ake kupitiliza nchito imene iye anayambitsa, yocitila umboni “mpaka kumalekezelo a dziko lapansi.” (Ŵelengani Machitidwe 1:8.) Koma iwo sakanakwanitsa kugwila nchitoyo mwa mphamvu zawo. Anafunikila mzimu woyela—“mthandizi” amene Yesu anawalonjeza.—Yoh. 14:26; Zek. 4:6.

5-6. Kodi mzimu woyela unathandiza motani otsatila a Yesu?

5 Otsatila a Yesu analandila mzimu woyelawo pa Pentekosite wa mu 33 C.E. Mothandizidwa na mzimu woyelawo, pamenepo anayamba kulalikila, cakuti m’nthawi yocepa, anthu masauzande analandila uthenga wabwino. (Mac. 2:41; 4:4) Citsutso citabuka, ophunzilawo sanacite mantha ayi. Anatembenukila kwa Mulungu kuti awathandize. Iwo anapemphela kuti: “Lolani kuti akapolo anu apitilize kulankhula mawu anu molimba mtima.” Ndiyeno anadzazidwa na mzimu woyela, na kupitiliza “kulankhula mawu a Mulungu molimba mtima.”—Mac. 4:18-20, 29, 31.

6 Ophunzila a Yesu anakumananso na zovuta zina. Mwacitsanzo, mipukutu ya Malemba inali yocepa. Kunalibe zofalitsa monga masiku ano. Komabe anafunikila kulalikila kwa anthu a vitundu vosiyana-siyana. Ngakhale panali zothetsa nzelu zonsezi, ophunzila okangalikawo anaikwanitsa nchito yooneka monga yosathekayo. Pa zaka pafupi-fupi 30 cabe, anakwanitsa kulalikila uthenga wabwino “m’cilengedwe conse ca pansi pa thambo.”—Akol. 1:6, 23.

7. Zaka zoposa 100 zapitazo, kodi atumiki a Yehova anadziŵa bwanji zimene Mulungu anafuna kuti iwo acite? Nanga iwo anacitapo ciani?

7 M’nthawi zamakono. Yehova akupitilizabe kutsogolela anthu ake na kuwapatsa mphamvu. Amawatsogolela maka-maka kupitila m’Mawu ake ouzilidwa. M’mawu akewo, timaŵelengamo za utumiki wa Yesu komanso lamulo limene anapatsa otsatila ake la kupitiliza nchito imene iye anayambitsa. (Mat. 28:19, 20) Ngakhale kale-kalelo mu July 1881, magazini ino inati: “Sitinaitanidwe kapena kudzozedwa kuti tidzipezele ulemelelo na kudzikundikila cuma ayi, koma kuti tiseŵenzetse zonse zimene tili nazo polalikila uthenga wabwino.” Kabuku kakuti, To Whom the Work Is Entrusted [Kwa Amene Anapatsidwa Nchitoyo] kofalitsidwa mu 1919 kanati: “Nchito imeneyi ioneka yovuta, koma ndi ya Ambuye, ndipo mwa mphamvu zake tidzakwanitsa kuigwila.” Inde, mofanana ndi Akhristu oyambilila, abalewo anadzipeleka molimba mtima pa nchito imeneyi, ali na cidalilo conse kuti mzimu woyela udzawathandiza kulalikila kwa anthu onse, kaya akhale otani. Nafenso tili na cidalilo cimodzi-modzi masiku ano.

Gulu la Yehova limaseŵenzetsa zida zamakono panthawiyo, pofalitsa uthenga wabwino (Onani ndime 8-9)

8-9. Kodi gulu la Yehova laseŵenzetsa njila ziti popititsa patsogolo nchito yolalikila?

8 Gulu la Yehova limaseŵenzetsa zida zamakono za panthawiyo, pofalitsa uthenga wabwino. Zina mwa zidazo ni mabuku opulinta, “Seŵelo la Pakanema la Cilengedwe,” magalamafoni, magalimoto a mikuza mawu, kuulutsa pawailesi, ndipo tsopano pali zipangizo zamakono. Cina, gulu la Mulungu limamasulila zofalitsa m’vitundu vambili kuposa kale lonse! Cifukwa ciani? Kuti anthu olo akhale otani amve uthenga wabwino m’citundu cawo. Yehova alibe tsankho. Iye anakambilatu kuti uthenga wabwino udzalengezedwa “kudziko lililonse, fuko lililonse, cinenelo ciliconse, ndi mtundu uliwonse.” (Chiv. 14:6, 7) Iye afuna kuti anthu onse amve uthenga wa Ufumu.

9 Nanga bwanji za awo amene n’zovuta kuwalalikila, mwina cifukwa cakuti amakhala m’malo acitetezo cokhwima? Pofuna kulalikila anthu ambili, gulu la Yehova laganizilapo njila zosiyana-siyana za ulaliki wapoyela. Mwacitsanzo, mu 2001, Bungwe Lolamulila linavomeleza kuseŵenzetsa tumasitandi na mathebulo a ulaliki ku France, ndiyeno pambuyo pake ku maiko ena. Panakhala zotulukapo zabwino. Mu 2011, anayamba njila ina yatsopano ku United States, mu mzinda wa anthu ambili wa New York. M’caka coyamba, anagaŵila mabuku 102,129 komanso magazini 68,911. Ndipo anthu okwana 4,701 anapempha kuti aziphunzila Baibo! Mwacionekele, mzimu woyela unali kucilikiza nchitoyi. Conco, Bungwe Lolamulila linavomeleza kuseŵenzetsa njila za ulaliki wapoyela zimenezi padziko lonse.

10. Kodi tiyenela kucita ciani kuti tizicita bwino mu ulaliki?

10 Zimene muyenela kucita. Tengelani mwayi maphunzilo amene Yehova amapeleka pa misonkhano yacikhristu. Muzipita mu ulaliki na kagulu kanu nthawi zonse. Mukamatelo, mudzathandizidwa m’mbali zosiyana-siyana, ndipo mudzalimbikitsidwa na citsanzo cabwino ca ena. Muzipilila mukakumana na zovuta mu ulaliki. Lemba limene pazikidwa nkhani yathu, litikumbutsa kuti tingathe kucita cifunilo ca Mulungu, osati mwa mphamvu zathu, koma mwa mzimu woyela. (Zek. 4:6) Ndi iko komwe, nchito imene tikugwila ni ya Mulungu.

YEHOVA NI MULUNGU WADONGOSOLO KOMANSO WAMTENDELE

11. Kodi zinatheka bwanji kuti bungwe lolamulila lakalelo litumikile mogwilizana, na kusungitsa dongosolo na mtendele pakati pa anthu a Mulungu?

11 M’nthawi ya Akhristu oyambilila. Bungwe Lolamulila ku Yerusalemu linali kutumikila mogwilizana kuti pakati pa anthu a Mulungu pakhale dongosolo na mtendele. (Mac. 2:42) Mwacitsanzo, nkhani ya mdulidwe itafika povuta ca m’ma 49 C.E., bungwe lolamulila, motsogoleledwa na mzimu woyela linasamalila nkhaniyo. Mpingowo ukanakhalabe wogaŵikana pa nkhaniyi, nchito yolalikila sikanayenda bwino. Ngakhale kuti atumwiwo komanso amuna acikulile anali Ayuda, iwo sanasonkhezeledwe na miyambo yaciyuda kapena aja olimbikitsa miyamboyo. M’malomwake, anadalila Mawu a Mulungu na mzimu woyela kuti uwatsogolele. (Mac. 15:1, 2, 5-20, 28) Zotulukapo? Yehova anadalitsa cigamulo cawo, cakuti mu mpingo munakhala mtendele na mgwilizano, ndipo nchito yolalikila inapitabe patsogolo.—Mac. 15:30, 31; 16:4, 5.

12. N’ciani cimaonetsa kuti m’gulu la Yehova muli dongosolo na mtendele?

12 M’nthawi zamakono. Gulu la Yehova lacita zonse zotheka kuti pakhale dongosolo na mtendele pakati pa anthu a Yehova. Ngakhale kale-kalelo mu 1895, magazini yakuti Zion’s Watch Tower and Herald of Christ’s Presence ya November 15, inali na nkhani yakuti: “Mwadongosolo ndi Moyenela,” yozikidwa pa 1 Akorinto 14:40. Nkhaniyo inati: “Atumwiwo analembela Chalichi coyambilila zambili zokhudza dongosolo . . . N’kofunika kuti tizilabadilabe ‘zinthu zimene zinalembedwa kalekalelo kuti zitilangize.’” (Aroma 15:4) Inde, monga zinalili m’nthawi ya Akhristu oyambilila, gulu la Yehova masiku anonso limayesetsa kusungitsa dongosolo na mtendele. Mwacitsanzo, ngati mungapezeke pa Phunzilo la Nsanja ya Mlonda ku mpingo wina, ngakhale ku dziko lina, mungadziŵiletu mmene phunzilolo licitikile, ngakhalenso nkhani imene muphunzile. Panthawi yomweyo mudzakhala womasuka! Ndithudi, palibenso cina cingatheketse mgwilizano wotelewu, kupatulapo mzimu wa Mulungu!—Zef. 3:9.

13. Malinga na Yakobo 3:17, kodi tiyenela kudzifunsa mafunso ati?

13 Zimene muyenela kucita. Yehova amafuna kuti ife anthu ake ‘tizisunga umodzi wathu mwa mzimu na mwamtendele monga comangila cotigwilizanitsa.’ (Aef. 4:1-3) Conco dzifunseni kuti: ‘Kodi nimalimbikitsa mgwilizano na mtendele mu mpingo? Kodi nimagonjela kwa amene amatsogolela? Kodi ena mu mpingo anganidalile, maka-maka nikapatsidwa mbali zakuti nisamalile? Kodi nimasunga nthawi, kuthandiza ena, komanso kufunitsitsa kutumikila?’ (Ŵelengani Yakobo 3:17.) Ngati muona kuti pali mbali zimene mufunika kuwongolela, pemphani mzimu woyela. Mukamalola mzimu woyela kuti ukuumbeni na kukutsogolelani pa zocita zanu, abale na alongo anu adzakukondani kwambili. Adzakuonani kuti ndimwe wofunika.

YEHOVA AMATIPHUNZITSA NA KUTIPATSA ZOFUNIKILA

14. Malinga na Akolose 1:9, 10, kodi Yehova anaphunzitsa motani anthu ake m’nthawi ya Akhristu oyambilila?

14 M’nthawi ya Akhristu oyambilila. Yehova amakondwela kwambili kuphunzitsa anthu ake. (Sal. 32:8) Amafuna kuti iwo am’dziŵe bwino, azim’konda, komanso kuti akhale kwamuyaya monga ana ake okondeka. Zonsezi sizikanatheka popanda maphunzilo amene iye amapeleka. (Yoh. 17:3) Yehova anaseŵenzetsa mpingo wa Akhristu oyambilila kuphunzitsa anthu ake. (Ŵelengani Akolose 1:9, 10) Ndipo mzimu woyela—“mthandizi” amene Yesu analonjeza—unaŵathandiza kwakukulu. (Yoh. 14:16) Unawathandiza ophunzilawo kumvetsetsa Mawu a Mulungu, ndipo unawakumbutsa zambili zimene Yesu anakamba na kucita, zimene pambuyo pake zinalembedwa m’mabuku a Uthenga Wabwino. Cidziŵitso cimeneci, cinalimbitsa cikhulupililo ca Akristu oyambilila, komanso kukulitsa cikondi cawo pa Mulungu, Mwana wake, komanso kwa wina na mnzake.

15. Kodi imwe pacanu, mwaona kuti Yehova akukwanilitsa motani lonjezo lake la pa Yesaya 2:2, 3?

15 M’nthawi zamakono. Yehova ananenelatu kuti “m’masiku otsiliza,” anthu a mitundu yonse adzakhamukila ku phili lake lophiphilitsila kuti akaphunzitsidwe njila zake. (Ŵelengani Yesaya 2:2, 3.) Ulosiwu ukukwanilitsidwa m’maso mwathu. Inde, kulambila koona kwakwezeka pamwamba kwambili kuposa kulambila konyenga kulikonse. Kunena zoona, Yehova akutipatsa cakudya cauzimu ca mwana alilenji! (Yes. 25:6) Mwa “kapolo wokhulupilika ndi wanzelu,” Yehova satipatsa cabe cakudya coculuka cauzimu ayi, amatipatsa cakasintha-sintha, monga mabuku, nkhani za onse, mavidiyo atukadoli, mavidiyo ena, na zina zambili. (Mat. 24:45) Timamvela mmene Elihu mnzake wa Yobu anamvelela. Iye anati: “Kodi mphunzitsi winanso ndani wofanana [ndi Mulungu]?”—Yobu 36:22.

Khomelezani coonadi mu mtima mwanu na kuseŵenzetsa mfundo zake mu umoyo wanu (Onani ndime 16) *

16. Kodi muyenela kucita ciani kuti mukule mwauzimu?

16 Zimene muyenela kucita. Mzimu wa Mulungu udzakuthandizani kuseŵenzetsa zimene mumaŵelenga na kuphunzila m’Mawu ake. Pemphelani mmene wamasalimo anacitila kuti: “Inu Yehova, ndilangizeni za njila yanu. Ndidzayenda m’coonadi canu. Ndipatseni mtima wosagawanika kuti ndiope dzina lanu.” (Sal. 86:11) Conco, pitilizani kudya cakudya cauzimu cimene Yehova amapeleka kupitilila m’Mawu ake na gulu lake. Koma colinga canu sikungopeza cidziŵitso cabe ayi. Muyenela kukhomeleza coonadi pamtima panu na kuseŵenzetsa mfundo zake mu umoyo wanu. Mzimu wa Yehova ungakuthandizeni kucita zimenezi. Muyenelanso kulimbikitsa abale na alongo anu. (Aheb. 10:24, 25) Cifukwa ciani? Cifukwa ni banja lanu lauzimu. Pemphani mzimu wa Mulungu kuti uzikuthandizani kupeleka ndemanga zogwila mtima pa misonkhano, komanso kuti muzisamalila bwino mbali zanu papulogilamu. Mukatelo, mudzaonetsa Yehova na mwana wake kuti mumakonda “nkhosa” zawo za mtengo wapatali.—Yoh. 21:15-17.

17. Kodi mungaonetse bwanji kuti mumacilikiza gulu la Yehova mokhulupilika?

17 Posacedwa, gulu lotsogoleledwa na mzimu wa Mulungu ndilo lokha lidzatsala padziko lapansi. Conco, tumikilani molimbika na gulu la Yehova. Onetsani anthu cikondi ca Mulungu copanda tsankho, mwa kulengeza uthenga wabwino kwa onse amene mwapeza mu ulaliki. Tengelani Yehova pankhani yokonda dongosolo na mtendele, mwa kulimbikitsa mgwilizano mu mpingo. Ndipo mvetselani kwa Mlangizi wanu Wamkulu mwa kupindula mokwanila na cakudya cauzimu coculuka cimene iye amapeleka. Mukatelo, pamene dziko la Satanali likufika kumapeto, simudzacita mantha. M’malomwake mudzaima nji, pamodzi na aja otumikila na gulu la Yehova mokhulupilika.

NYIMBO 3 Ndimwe Mphamvu Zathu, Ciyembekezo, na Cidalilo Cathu

^ ndime 5 Kodi mumakhulupililadi kuti Yehova akutsogolela gulu lake masiku ano? M’nkhani ino, tikambilane mmene Yehova anatsogolela mpingo woyambilila wacikhristu, komanso mmene akupitilizila kutsogolela anthu ake masiku ano.

^ ndime 1 KUFOTOKOZELA MAWU ENA: Gulu la Yehova lili na gawo lakumwamba komanso gawo la padziko lapansi. M’nkhani ino, tikamati “gulu” la Mulungu titanthauza gawo la padziko lapansi.

^ ndime 52 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Pambuyo potamba mavidiyo oonetsa ena otumikila ku maiko amene kuli kusowa, mlongo mpainiya walimbikitsidwa kutengela citsanzo cawo. Kenako, wakwanilitsa colinga cake cokatumikila kugawo losowa.