NKHANI YOPHUNZIRA 42

Muzithandiza Ophunzira Baibulo Anu Kuti Afike Pobatizidwa​—Gawo 2

Muzithandiza Ophunzira Baibulo Anu Kuti Afike Pobatizidwa​—Gawo 2

“Uzisamala ndi zimene umachita komanso zimene umaphunzitsa.”​—1 TIM. 4:16.

NYIMBO NA. 77 Kuwala M’dziko Lamdima

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1. N’chifukwa chiyani tinganene kuti kuphunzitsa anthu kuti akhale ophunzira a Yesu ndi ntchito yopulumutsa miyoyo?

KUPHUNZITSA anthu kuti akhale ophunzira a Yesu ndi ntchito yopulumutsa miyoyo. N’chifukwa chiyani tikutero? Tikutero chifukwa Yesu popereka lamulo lopezeka pa Mateyu 28:19, 20, ananena kuti: “Pitani mukaphunzitse anthu . . . kuti akhale ophunzira anga. Muziwabatiza.” Kodi kubatizidwa n’kofunika bwanji? Munthu kuti adzapeze moyo wosatha ayenera kubatizidwa. Munthu amene akufuna kubatizidwa ayenera kukhulupirira kuti adzapeza moyo wosatha chifukwa chakuti Yesu anatifera ndipo anaukitsidwa. N’chifukwa chake mtumwi Petulo anauza Akhristu anzake kuti: ‘Ubatizo ukupulumutsanso inuyo tsopano mwa kuukitsidwa kwa Yesu Khristu.’ (1 Pet. 3:21) Choncho munthu akabatizidwa, amayembekezera kudzakhala ndi moyo wosatha.

2. Kodi lemba la 2 Timoteyo 4:1, 2 limatilimbikitsa kuti tiyenera kukhala aphunzitsi otani?

2 Kuti tithandize anthu kukhala ophunzira a Yesu tiyenera kukhala ndi “luso la kuphunzitsa.” (Werengani 2 Timoteyo 4:1, 2.) N’chifukwa chiyani timafunika kukhala ndi luso? Chifukwa chakuti Yesu anatilamula kuti: “Pitani mukaphunzitse anthu . . . kuti akhale ophunzira anga, . . . ndi kuwaphunzitsa kusunga zinthu zonse.” Mtumwi Paulo anauza Timoteyo kuti “pitiriza” kugwira ntchito imeneyi, “chifukwa ukatero udzadzipulumutsa wekha komanso anthu okumvera.” Choncho m’pomveka kuti Paulo ananena kuti: “Nthawi zonse uzisamala ndi . . . zimene umaphunzitsa.” (1 Tim. 4:16) Popeza timafunika kuphunzitsa anthu kuti akhale ophunzira a Yesu, tiyenera kuyesetsa kuti tikhale aphunzitsi aluso.

3. Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi chokhudza kuchititsa maphunziro a Baibulo?

3 Timaphunzira Baibulo ndi anthu mamiliyoni ambiri padziko lonse. Koma monga mmene tinaonera munkhani yapita ija, tiyenera kudziwa zimene tingachite kuti tithandize anthu amenewo kufika pobatizidwa n’kukhala ophunzira a Yesu Khristu. Munkhaniyi tiona zinthu zinanso 5 zimene mphunzitsi aliyense ayenera kuchita kuti athandize wophunzira wake kuti abatizidwe.

MUZIGWIRITSA NTCHITO BAIBULO MUKAMAPHUNZITSA

Muzipempha aphunzitsi aluso kuti akuthandizeni kuti muzitha kugwiritsa ntchito bwino Baibulo pophunzitsa (Onani ndime 4-6) *

4. N’chifukwa chiyani tiyenera kupewa kulankhula kwambiri tikamachititsa phunziro la Baibulo? (Onani mawu a m’munsi.)

4 Timakonda kwambiri zimene timaphunzitsa kuchokera m’Mawu a Mulungu. Choncho mwina tikhoza kumalankhula kwambiri tikamaphunzitsa anthu Baibulo. Komabe, kaya tikuchititsa Phunziro la Nsanja ya Olonda, Phunziro la Baibulo la Mpingo kapena phunziro la Baibulo lapanyumba, tizikumbukira kuti sitiyenera kumalankhula kwambiri. Kuti tizigwiritsa ntchito Baibulo pophunzitsa, tiyenera kukhala odziletsa ndipo tiziyesetsa kupewa kufotokoza zinthu zonse zimene tikudziwa zokhudza lemba kapena nkhani inayake. * (Yoh. 16:12) Yerekezerani zimene munkadziwa zokhudza Baibulo pa nthawi imene munkabatizidwa ndi zimene mukudziwa panopa. N’kutheka kuti pa nthawiyo munkangodziwa ziphunzitso zoyambirira za m’Baibulo. (Aheb. 6:1) Panopa mukudziwa zochuluka chifukwa mwakhala mukuphunzira Baibulo kwa zaka zambiri. Choncho tizipewa kuphunzitsa wophunzira wathu zinthu zonse zimene tikudziwa nthawi imodzi.

5. (a) Mogwirizana ndi lemba la 1 Atesalonika 2:13, kodi tiyenera kuthandiza wophunzira wathu kuzindikira chiyani? (b) Kodi tingalimbikitse bwanji wophunzira kuti azifotokoza zimene akuphunzira?

5 Timafuna kuti wophunzira wathu azidziwa kuti zimene akuphunzirazo zikuchokera m’Mawu a Mulungu. (Werengani 1 Atesalonika 2:13.) Kodi tingamuthandize bwanji kudziwa zimenezi? Muzilimbikitsa wophunzirayo kuti azifotokoza zimene akuphunzira. M’malo moti nthawi zonse tizimufotokozera malemba, nthawi zina tizimupempha kuti atifotokozere malemba ena. Muzimuthandiza kuona mmene Mawu a Mulungu angamuthandizire pa moyo wake. Muzimufunsa mafunso amene angamuthandize kuti afotokoze mmene akuganizira komanso mmene akumvera pa malemba amene wawerengawo. (Luka 10:25-28) Mwachitsanzo, mungamufunse kuti: “Kodi palembali mwaonapo khalidwe liti limene Yehova ali nalo?” “Kodi mukuona kuti zinthu zimene mwaphunzira kuchokera m’Baibulozi zingakuthandizeni bwanji?” “Kodi mukumva bwanji ndi zimene mwaphunzirazi?” (Miy. 20:5) Tizikumbukira kuti chofunika kwambiri si kuchuluka kwa zimene wophunzirayo akudziwa, koma kuti azikonda ndi kugwiritsa ntchito zimene akudziwazo.

6. N’chifukwa chiyani zingakhale bwino kupita ndi wofalitsa wina waluso kuphunziro lathu la Baibulo?

6 Kodi nthawi zina mumapita ndi ofalitsa ena aluso kuphunziro lanu la Baibulo? Ngati ndi choncho, mungawafunse kuti akufotokozereni zimene aona zokhudza mmene mumachititsira phunziro, komanso ngati mumagwiritsa ntchito bwino Baibulo pamene mumaphunzitsa. Zimenezi n’zofunika chifukwa kuti mukhale mphunzitsi wabwino, muyenera kukhala wodzichepetsa. (Yerekezerani ndi Machitidwe 18:24-26) Mungafunsenso wofalitsayo kuti afotokoze ngati akuona kuti wophunzirayo akumvetsa zimene akuphunzira. Mungathenso kumupempha kuti azikaphunzira ndi munthuyo mukachokapo kwa mlungu umodzi kapena iwiri. Zimenezi zingathandize kuti phunzirolo lisaime komanso wophunzirayo aziona kufunika kwa zimene akuphunzira. Musamakhale ndi maganizo akuti ndi phunziro “langa,” ndiye sindingalole kuti wina azilichititsa. Pajatu timafunira wophunzira wathuyo zabwino, ndipo timafunitsitsa kuti apitirize kuphunzira zambiri zokhudza choonadi.

MUZISONYEZA KUTI MUMAKONDA KOMANSO KUKHULUPIRIRA ZIMENE MUMAPHUNZITSA

Muzifotokozera wophunzira wanu za anthu ena amene anasintha moyo wawo kuti zimuthandize kuona mmene angagwiritsire ntchito zimene akuphunzira (Onani ndime 7-9) *

7. Kodi n’chiyani chingathandize wophunzira kuti azikonda zimene akuphunzira?

7 Wophunzira wanu aziona kuti mumakonda komanso kukhulupirira zimene Baibulo limaphunzitsa. (1 Ates. 1:5) Zimenezi zingamuthandize kuti nayenso azikonda kwambiri zimene akuphunzira. Mwinanso mungamufotokozere mmene mfundo za m’Baibulo zakuthandizirani pa moyo wanu. Mukamachita zimenezi, wophunzirayo angayambe kuzindikira kuti m’Baibulo muli malangizo abwino amene angamuthandize.

8. Kodi n’chiyaninso chimene tingachite kuti tithandize wophunzira Baibulo wathu, nanga n’chifukwa chiyani tiyenera kuchita zimenezi?

8 Tikamaphunzira Baibulo tingafotokozere wophunzira za abale ndi alongo amene anakumananso ndi mavuto ofanana ndi ake ndiponso zimene anachita kuti athane nawo. Tikhozanso kupita kuphunzirolo ndi m’bale kapena mlongo ngati ameneyu n’cholinga choti akalimbikitse wophunzirayo. Komanso tingapeze nkhani zolimbikitsa pa jw.org munkhani zakuti “Baibulo Limasintha Anthu.” * Nkhani ngati zimenezi komanso mavidiyo zingathandize wophunzirayo kuona kuti ndi nzeru kutsatira mfundo za m’Baibulo pa moyo wake.

9. Kodi mungalimbikitse bwanji wophunzira wanu kuti aziuza achibale komanso anzake zimene akuphunzira?

9 Ngati wophunzirayo ali pabanja, kodi mwamuna kapena mkazi wake amaphunzira nawo? Ngati si choncho, mungamupemphe kuti azikhala nawo paphunzirolo. Muzilimbikitsa wophunzirayo kuti aziuza achibale komanso anzake zimene akuphunzira. (Yoh. 1:40-45) Mungachite bwanji zimenezi? Mukhoza kumufunsa kuti: “Kodi mungafotokozere bwanji achibale anu mfundo imeneyi” kapena “Kodi ndi lemba liti limene mungagwiritse ntchito pothandiza anzanu kuti amvetse mfundo imeneyi?” Mukamachita zimenezi ndiye kuti mukumuphunzitsa kuti akhale mphunzitsi. Ndiyeno akayenerera kukhala wofalitsa, angayambe kulalikira limodzi ndi mpingo. Mungafunse wophunzirayo ngati akudziwa aliyense amene akufuna kuphunzira Baibulo. Ngati alipo mungalankhule naye nthawi yomweyo n’kumupempha kuti muziphunzira naye. Mungamuonetse vidiyo yakuti Kodi Phunziro la Baibulo Limachitika Bwanji? *

MUZILIMBIKITSA WOPHUNZIRA KUTI APEZE ANZAKE MUMPINGO

Muzilimbikitsa ophunzira kuti akhale ndi anzawo mumpingo (Onani ndime 10-11) *

10. Mogwirizana ndi 1 Atesalonika 2:7, 8, kodi mphunzitsi angatengere bwanji chitsanzo cha Paulo?

10 Monga aphunzitsi, tizisonyeza kuti timakonda ophunzira athu. Tiziwaona kuti posachedwa akhoza kudzakhala abale ndi alongo athu mumpingo. (Werengani 1 Atesalonika 2:7, 8.) Tiyenera kudziwa kuti si zophweka kuti asiye kucheza ndi anzawo a poyamba komanso kuti asinthe zinthu zina pa moyo wawo n’kuyamba kutumikira Yehova. Choncho tiyenera kuwathandiza kuti apeze anzawo abwino mumpingo. Ophunzira anuwo ayenera kukhala anzanu. Muzipeza nthawi yocheza nawo, osati kumangocheza nawo pa nthawi imene mukuphunzira yokha. Mungasonyeze kuti mumawaganizira powaimbira foni, kuwatumizira meseji kapena kupita kukawaona.

11. Kodi tingathandize bwanji ophunzira athu kuti apeze anzawo mumpingo, nanga n’chifukwa chiyani kuchita zimenezi n’kofunika?

11 Pali mawu akuti: “Udindo wolera mwana ndi wa mudzi wonse.” Mofanana ndi zimenezi, tinganenenso kuti: “Ndi udindo wa mpingo wonse kuthandiza munthu kuti akhale wophunzira wa Yesu.” Choncho aphunzitsi abwino a Baibulo amathandiza ophunzira awo kuti adziwane ndi anthu ena mumpingo. Anthu amenewa angathandize ophunzirawo kuti akhale pa ubwenzi ndi Yehova. Zotsatira zake, ophunzirawo angasangalale kumagwirizana ndi anthu a Mulungu omwe angamawalimbikitse akakumana ndi mavuto. Muzithandiza ophunzirawo kuti aziona kuti ndi ofunika mumpingo ndiponso kuti ndi mbali ya banja lathu lauzimu. Tikufuna kuti wophunzira aliyense azisangalala kukhala m’banja la abale ndi alongo amene amakondana. Ndiyeno zingakhale zosavuta kuti wophunzirayo asiye kucheza ndi anthu amene sangamuthandize kuti azikonda Yehova. (Miy. 13:20) Ngati anthu amene ankacheza nawo poyamba atayamba kumusala, angadziwe kuti akhoza kupeza anzake abwino m’gulu la Yehova.​—Maliko 10:29, 30; 1 Pet. 4:4.

MUZIWAFOTOKOZERA KUFUNIKA KODZIPEREKA KOMANSO KUBATIZIDWA

Pali zambiri zimene wophunzira Baibulo ayenera kuchita kuti afike pobatizidwa (Onani ndime 12-13)

12. N’chifukwa chiyani tiyenera kufotokozera ophunzira athu kufunika kodzipereka komanso kubatizidwa?

12 Muzikambirana pafupipafupi ndi ophunzira anu kufunika kodzipereka kwa Yehova ndi kubatizidwa. Pajatu cholinga chathu tikamaphunzira Baibulo ndi anthu n’choti abatizidwe komanso azitumikira Yehova. Munthu akaphunzira Baibulo kwa miyezi ingapo, makamaka akayamba kufika pamisonkhano, ayenera kudziwa kuti cholinga chathu n’choti timuthandize kuti akhale wa Mboni za Yehova.

13. Kodi wophunzira ayenera kuchita chiyani kuti afike pobatizidwa?

13 Pali zambiri zimene wophunzira Baibulo ayenera kuchita kuti afike pobatizidwa. Choyamba, ayenera kudziwa Yehova, kumukonda komanso kumukhulupirira. (Yoh. 3:16; 17:3) Kenako wophunzirayo amayamba kukhala pa ubwenzi ndi Yehova komanso abale ndi alongo mumpingo. (Aheb. 10:24, 25; Yak. 4:8) Pakapita nthawi, amasiya makhalidwe oipa amene ankachita n’kulapa machimo ake. (Mac. 3:19) Komanso amayamba kuuza ena zimene amakhulupirira. (2 Akor. 4:13) Kenako amadzipereka kwa Yehova n’kubatizidwa. (1 Pet. 3:21; 4:2) Limenelitu limakhala tsiku losangalatsa kwambiri kwa aliyense. Wophunzira akamayesetsa kuchita zinthu zimene akuyenera kuchita kuti abatizidwe, tizimuyamikira kuchokera pansi pa mtima ndipo tizimulimbikitsa kuti apitirize kuchita zimenezo.

NTHAWI NDI NTHAWI MUZIONA NGATI WOPHUNZIRA WANU AKUSINTHA

14. Kodi mphunzitsi angatani kuti adziwe ngati wophunzira wake akusintha?

14 Tiyenera kukhala oleza mtima tikamathandiza ophunzira Baibulo kuti afike podzipereka n’kubatizidwa. Koma pa nthawi ina tingafunike kufufuza kuti tidziwe ngati wophunzirayo akufunadi kutumikira Yehova Mulungu. Kodi amasonyeza kuti akuyesetsa kumvera malamulo a Yesu? Kapena kodi amangosangalala ndi kuphunzira Baibulo basi?

15. Kodi mphunzitsi angadziwe bwanji ngati wophunzira wake ali wokonzeka kubatizidwa?

15 Nthawi ndi nthawi muziona zimene wophunzira wanu akuchita posonyeza kuti akusintha. Mwachitsanzo, kodi wophunzira wanu amasonyeza kuti amakonda Yehova? Kodi amapemphera kwa Yehova? (Sal. 116:1, 2) Kodi amakonda kuwerenga Baibulo? (Sal. 119:97) Kodi amafika pamisonkhano nthawi zonse? (Sal. 22:22) Kodi wasintha zinthu zina pa moyo wake posonyeza kuti akutsatira zimene akuphunzira? (Sal. 119:112) Kodi wayamba kuuza achibale ndi anzake zimene akuphunzira? (Sal. 9:1) Koposa zonse, kodi akufuna kukhala wa Mboni za Yehova? (Sal. 40:8) Ngati wophunzirayo sakusintha, tiyenera kufufuza mosamala chifukwa chake, kenako tingakambirane naye nkhaniyo mokoma mtima komanso mosapita m’mbali. *

16. Kodi tingadziwe bwanji ngati tikufunika kusiya kuphunzira ndi munthu?

16 Nthawi ndi nthawi muzifufuza kuti muone ngati mukufunika kupitiriza kuphunzira ndi munthu. Muzidzifunsa kuti: ‘Kodi wophunzirayu sakonzekera phunziro? Kodi safuna kubwera kumisonkhano? Kodi sanasiye makhalidwe ake oipa? Kodi amapitabe kuchipembedzo chonyenga?’ Ngati yankho ndi lakuti inde, kupitiriza kuphunzira ndi munthu woteroyo kungakhale ngati kuphunzitsa kusambira, munthu amene sakufuna kunyowa. Ndiye ngati wophunzira sakonda kwenikweni zimene akuphunzirazo komanso sakufuna kusintha, kodi pali chifukwa chilichonse chopitirizira kuphunzira naye?

17. Mogwirizana ndi 1 Timoteyo 4:16 kodi aphunzitsi onse a Baibulo ayenera kuchita chiyani?

17 Timaona kuti udindo wathu wophunzitsa anthu ndi wofunika kwambiri, ndipo timafuna kuthandiza ophunzira Baibulo kuti abatizidwe. N’chifukwa chake timagwiritsa ntchito Baibulo pophunzitsa komanso timasonyeza kuti timakonda ndi kukhulupirira zimene tikuwaphunzitsazo. Timalimbikitsa ophunzira kuti akhale ndi anzawo mumpingo. Komanso timawafotokozera kufunika kodzipereka kwa Yehova ndi kubatizidwa. Nthawi ndi nthawi timafufuza kuti tione ngati wophunzirayo akusintha. (Onani bokosi lakuti “ Zimene Aphunzitsi Angachite Kuti Athandize Ophunzira Kuti Abatizidwe.”) Tikusangalala kugwira nawo ntchito yopulumutsa moyoyi. Choncho tiyeni tiyesetse kuchita zonse zimene tingathe kuti tithandize amene timaphunzira nawo Baibulo kuti abatizidwe.

NYIMBO NA. 79 Athandizeni Kukhala Olimba

^ ndime 5 Tikamaphunzira Baibulo ndi anthu, timakhala ndi mwayi woti tiwathandize kuti ayambe kuganiza komanso kuchita zinthu m’njira imene Yehova amafuna. Nkhaniyi ikufotokoza zinthu zinanso zimene zingatithandize kuti tikhale aphunzitsi aluso.

^ ndime 4 Onani nkhani yakuti “Zinthu Zimene Tiyenera Kupewa Tikamachititsa Phunziro la Baibulo” mu Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu ya September 2016.

^ ndime 8 Pitani pamene alemba kuti ZOKHUDZA IFEYO > ZOCHITIKA PA MOYO WA A MBONI ZA YEHOVA.

^ ndime 9 Pa JW Library®, pitani pamene alemba kuti MEDIA > OUR MEETINGS AND MINISTRY > TOOLS FOR THE MINISTRY.

^ ndime 15 Onani nkhani yakuti “Munthu Amabatizidwa Chifukwa Chokonda Yehova Komanso Kumuyamikira” komanso yakuti “Kodi Ndinu Okonzeka Kubatizidwa?” mu Nsanja ya Olonda ya March 2020.

^ ndime 77 MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI: Pambuyo pochititsa phunziro, mlongo waluso akuthandiza mlongo amene amachititsa phunzirolo kuona kufunika koti asamalankhule kwambiri akamaphunzitsa.

^ ndime 79 MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI: Paphunziro la Baibulo, wophunzira waphunzira zimene angachite kuti akhale mkazi wabwino. Kenako akufotokozera mwamuna wake zimene waphunzira.

^ ndime 81 MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI: Wophunzira ndi mwamuna wake akusangalala kucheza kwa anzawo amene anakumana nawo ku Nyumba ya Ufumu.