Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 45

Mmene Tingathandizile Ena Kusunga Malamulo a Khristu

Mmene Tingathandizile Ena Kusunga Malamulo a Khristu

“Pitani mukaphunzitse anthu . . . , kuti akhale ophunzila anga . . . , ndi kuwaphunzitsa kusunga zinthu zonse zimene ndinakulamulilani.”—MAT. 28:19, 20.

NYIMBO 89 Mvela Udalitsike

ZIMENE TIKAMBILANE *

1. Malinga na Mateyu 28:18-20, kodi Yesu anapeleka lamulo liti?

YESU ataukitsidwa kwa akufa, anaonekela kwa ophunzila ake amene anasonkhana ku Galileya. Anali kufuna kuwauza nkhani yofunika kwambili. Kodi inali nkhani yanji? Tiipeza pa Mateyu 28:18-20.—Ŵelengani.

2. Kodi tikambilane mafunso ati?

2 Lamulo la Yesu lopanga ophunzila lipitanso kwa atumiki a Mulungu masiku ano. Conco, tiyeni tikambilane mafunso atatu okhudza nchito imene Yesu anatipatsa. Loyamba, kuwonjezela pa kuphunzitsa ophunzila atsopano zimene Mulungu amafuna, kodi tiyenela kucitanso ciani? Laciŵili, kodi ofalitsa onse mu mpingo angathandizile bwanji kuti ophunzila Baibo akule mwauzimu? Lacitatu, kodi tingawathandize bwanji okhulupilila anzathu ozilala kuti ayambenso kugwila nchito yopanga ophunzila?

APHUNZITSENI KUSUNGA MALAMULO A KHRISTU

3. Ni mfundo yofunika iti imene Yesu anachula m’lamulo lake?

3 Malangizo a Yesu ni omveka bwino. Tifunika kuphunzitsa anthu zimene iye analamula. Komabe, sitiyenela kuiŵala mfundo ina yofunika kwambili. Yesu sanangokamba kuti: ‘Aphunzitseni zinthu zonse zimene ndinakulamulilani’. M’malo mwake anati: Aphunzitseni “kusunga zinthu zonse zimene ndinakulamulilani.” Conco, kuti ticite zimenezi pamene tiphunzitsa munthu Baibo, sitiyenela kumangom’phunzitsa cabe, koma kumuonetsanso mmene angaseŵenzetsele zimene akuphunzilazo. N’cifukwa ciani tifunika kucita zimenezi?

4. Kodi kusunga lamulo kumatanthauza ciani? Fotokozani citsanzo.

4 “Kusunga” lamulo kumatanthauza kumvela lamulolo. Kuti timvetse mmene tingaphunzitsile munthu kusunga, kapena kumvela zimene Khristu analamula, tiyeni tiganizile citsanzo ici. Kodi wophunzitsa anthu kuyendetsa motoka, amaphunzitsa bwanji ophunzila ake kusunga malamulo a pa msewu? Coyamba, mphunzitsiyo angaphunzitse ophunzilawo kuwadziŵa bwino malamulo a pa msewu m’kalasi. Koma kuti awaphunzitse mowatsatilila malamulowo, afunikanso kucita cinthu cina. Afunika kukwela m’motoka na wophunzilayo kuti azim’longoza poyendetsa, na kum’thandiza kuseŵenzetsa zimene anaphunzila. Tingaphunzilepo ciani pa citsanzo cimeneci?

5. (a) Malinga na Yohane 14:15 komanso 1 Yohane 2:3, kodi tifunika kuphunzitsa maphunzilo athu a Baibo kucita ciani? (b) Fotokozani mmene tingawathandizile ophunzila athu.

5 Tikamaphunzitsa anthu Baibo, timawaphunzitsa zimene Mulungu afuna kwa ife. Koma tiyenela kucita zoposa pamenepo. Tiyenelanso kuwaphunzitsa kuseŵenzetsa pa umoyo wawo zimene akuphunzila. (Ŵelengani Yohane 14:15; 1 Yohane 2:3.) Mwacitsanzo cathu, tingathandize ophunzila athu kuona mmene angaseŵenzetsele mfundo zikulu-zikulu za m’Malemba kusukulu, kunchito, kapena panthawi yosangalala. Tingawafotokozeleko cocitika mu umoyo wathu cowaonetsa mmene kuseŵenzetsa malangizo a m’Baibo kunatitetezela ku zoipa, kapena mmene malangizowo anatithandizila kupanga cosankha canzelu. Pamaso pa wophunzila wathu, tingapemphele kwa Yehova kuti mzimu woyela uzimutsogolela.—Yoh. 16:13.

6. Kodi kuphunzitsa ena kusunga malamulo a Yesu kumaphatikizapo ciani?

6 Kodi kuphunzitsa ena kusunga malamulo a Yesu kumaphatikizapo ciani? Tifunika kuthandiza maphunzilo athu a Baibo kukhala na cikhumbo ca kupanga ophunzila. Ophunzila Baibo ena angamacite nayo mantha nchito yolalikila. Tifunika kukhala oleza mtima pamene tithandiza ophunzila athu kumvetsa mfundo za m’Baibo zimene zingawafike pamtima, na kuwalimbikitsa kucitapo kanthu. Kodi tingaseŵenzetse njila iti pothandiza ophunzila athu kukhala na cikhumbo ca kulalikila uthenga wabwino?

7. Tingam’thandize bwanji wophunzila kukhala na cikhumbo ca kulalikila uthenga wabwino?

7 Tingafunse wophunzila Baibo wathu mafunso monga aya: “Kodi mwapindula bwanji cifukwa coseŵenzetsa mfundo za m’Baibo? Kodi muganiza kuti ena afunika kumvela uthenga umenewu? Mungacite ciani kuti muwathandize?” (Miy. 3:27; Mat. 9:37, 38) Onetsani wophunzila wanu mathirakiti a mu Thuboksi yathu na kumuuza kuti asankhe kathilakiti kamene aona kuti kangakhale kothandiza kwa abululu ŵake, mabwenzi ake, kapena anzake a kunchito. M’patseni mathilakiti angapo. Ndiyeno yesezani kuti mum’thandize mmene angagaŵile kathilakiti mwaluso. Ndipo ngakhale wophunzila wathu atayenelezedwa kukhala wofalitsa wosabatizika, tiyenela kupitilizabe kum’thandiza mwa kulalikila naye.—Mlal. 4:9, 10; Luka 6:40.

MMENE MPINGO UNGATHANDIZILE MAPHUNZILO A BAIBO KUPITA PATSOGOLO

8. N’cifukwa ciani kuli kofunika kuti ophunzila athu akhale na cikondi cacikulu pa Mulungu komanso pa mnansi? (Onaninso bokosi lakuti “ Mmene Tingathandizile Maphunzilo Athu a Baibo Kukulitsa Cikondi pa Mulungu.”)

8 Kumbukilani kuti Yesu anatilangiza kuphunzitsa anthu “kusunga zinthu zonsezimene analamula. Mosakaikila, izi ziphatikizapo malamulo aŵili aakulu koposa—kukonda Mulungu na kukonda mnansi wathu. Malamulo onse aŵiliwa amakhudza nchito yolalikila na kupanga ophunzila. (Mat. 22:37-39) Motani? Cikondi cathu pa Mulungu na mnansi, ndiye cimene cimatilimbikitsa kulalikila uthenga wabwino. Komabe, ophunzila Baibo ena angacite mantha kutengako mbali mu nchito yolalikila. Koma tingatsimikizile ophunzilawo kuti mwa thandizo la Yehova, pang’ono-mpang’ono angathetse mantha awo oopa anthu. (Sal. 18:1-3; Miy. 29:25) Bokosi lili m’nkhani ino lifotokoza masitepu amene tingatenge kuti tithandize wophunzila wathu kukulitsa cikondi cake pa Mulungu. Kuwonjezela apo, kodi mpingo ungacite ciani kuti uthandize ophunzila atsopano kukulitsa cikondi cawo?

9. Pa citsanzo ca wophunzitsa kuyendetsa motoka, kodi wophunzilayo angatengepo maphunzilo ofunika m’njila ziti?

9 Ganizilaninso citsanzo ca munthu amene akuphunzila kuyendetsa motoka. Pamene akuyendetsa motoka ali na mphunzitsi wake, kodi amaphunzilanso motani? Mwa kumvetsela kwa mphunzitsi wake na kuyang’ana mmene madilaiva ena osamala akucitila zinthu pa msewu. Mwacitsanzo, mphunzitsi wake angamulatile dilaiva wina amene mokoma mtima wapeleka mpata kuti dilaiva winanso apite patsogolo pake. Kapena angamuonetse dilaiva wina amene mokoma mtima wacepetsa kuwala kwa malaiti a motoka yake kuti asatoŵe m’maso madilaiva ena. Wophunzilayo angatengepo maphunzilo pa zitsanzo zimenezi, amene angaseŵenzetse poyendetsa.

10. N’ciani cidzathandiza wophunzila Baibo kupita patsogolo mwauzimu?

10 Mofananamo, wophunzila Baibo amene wayamba kuyenda pa msewu wopita ku moyo, samangophunzila cabe kwa mphunzitsi wake. Amaphunzilanso kwa atumiki ena a Yehova acitsanzo cabwino. Conco, n’ciani maka-maka cingathandize maphunzilo a Baibo kupita patsogolo mwauzimu? Kupezeka ku misonkhano yathu. Cifukwa ciani? Malangizo a m’Malemba amene amapelekedwa ku misonkhano adzawathandiza kuti cidziŵitso cawo cikule, adzalimbitsa cikhulupililo cawo, na kuwathandiza kukulitsa cikondi cawo pa Mulungu. (Mac. 15:30-32) Kuwonjezela apo, mphunzitsi angadziŵikitse wophunzila wake kwa abale na alongo amene amafanana naye m’njila zambili. Wophunzila adzaona mmene abale na alongo amaonetselana cikondi cacikhristu mu mpingo. Ganizilani zitsanzo izi.

11. Ni zitsanzo zotani zimene wophunzila angaone mu mpingo, nanga zingam’limbikitse bwanji?

11 Wophunzila Baibo amene amalela yekha ana akuona mlongo wina amene nayenso amalela yekha ana. Izi zamukhudza mtima kwambili wophunzilayo kuona mmene mlongoyo amayesetsela kufika pa Nyumba ya Ufumu na ana ake aang’ono. Wophunzila amene akuvutika kuleka fodya, wadziŵana na wofalitsa wina amene anali na vuto limenelo koma analithetsa. Wofalitsayo akuuza wophunzilayo mmene kukulitsa cikondi cake pa Yehova kunam’limbikitsila kumvela malamulo a Mulungu. (2 Akor. 7:1; Afil. 4:13) Pambuyo pomvetsela mmene wofalitsayo analekela fodya, wophunzilayo walimbikitsidwa kwambili pamene wofalitsayo amutsimikizila kuti, “Na iwe ungakwanitse kuleka.” Mtsikana amene akuphunzila Baibo waona mlongo wacitsikana amene amanyadila kukhala Mboni ya Yehova. Wophunzilayo waona kuti mlongo wacitsikanayo amaoneka wacimwemwe, ndipo akufunitsitsa kudziŵa cimene cimapangitsa mlongoyo kumaoneka wacimwemwe nthawi zonse.

12. N’cifukwa ciani tinganene kuti aliyense mu mpingo ali na udindo wothandiza maphunzilo a Baibo?

12 Wophunzila akadziŵa ofalitsa okhulupilika osiyana-siyana, angaphunzile pa zitsanzo zawo zabwino, ndipo angamvetse tanthauzo la kusunga lamulo la Khristu lokonda Mulungu na mnansi. (Yoh. 13:35; 1 Tim. 4:12) Cina, monga taonela kale, wophunzila Baibo angaphunzile kwa ofalitsa ena amene ali na mavuto amene iyenso akukumana nawo. Akaona zitsanzo zotelo, amazindikila kuti n’zotheka kupanga masinthidwe ofunikila kuti akhale wophunzila wa Khristu. (Deut. 30:11) Aliyense mu mpingo angathandizile m’njila zambili kuti ophunzila Baibo apite patsogolo. (Mat. 5:16) Kodi imwe pacanu mumacita ciani kuti mulimbikitse ophunzila Baibo amene amabwela ku misonkhano?

KUTHANDIZA OZILALA KUYAMBANSO KULALIKILA

13-14. Kodi Yesu anacita nawo motani atumwi ake amene anafooka panthawi ina?

13 Timafuna kuthandiza abale na alongo athu amene anazilala kuyambanso kulalikila, kuti nawonso azikwanilitsa lamulo la Khristu la kupanga ophunzila. Mmene Yesu anacitila zinthu na atumwi ake atafooka, zitionetsa zimene ifenso tingacite masiku ano.

14 Kumapeto kwa utumiki wa Yesu padziko lapansi, atatsala pang’ono kuphedwa, atumwi ake “onse anathawa ndi kumusiya yekha.” (Maliko 14:50; Yoh. 16:32) Kodi Yesu anacita zinthu motani na atumwi ake amene anafooka panthawi ina? Ataukitsidwa, iye anauza ena mwa otsatila ake kuti: “Musaope! Pitani, kauzeni abale anga [kuti n’naukitsidwa].” (Mat. 28:10a) Yesu sanawakane atumwi ake. Ngakhale kuti iwo anamusiya panthawi ina, anawachabe “abale anga.” Mofanana na Yehova, Yesu anali wacifundo komanso wokhululuka.—2 Maf. 13:23.

15. Kodi timamvela bwanji tikaganizila za amene analeka kulalikila?

15 Mofananamo, timawadela nkhawa kwambili amene analeka kulalikila. Iwo ni abale na alongo athu, ndipo timawakonda! Timakumbukilabe nchito zoonetsa cikondi zimene abale athu amenewa anacita kumbuyoko—ena kwa zaka zambili. (Aheb. 6:10) Timawayewa kwambili! (Luka 15:4-7) Potengela citsanzo ca Yesu, ni m’njila ziti zimene tingaonetsele kuti timawadela nkhawa?

16. Kodi tingaonetse motani kuti timawadela nkhawa abale na alongo athu ozilala?

16 Aitanileni ku misonkhano. Njila imodzi imene Yesu analimbikitsila atumwi ake amene anakhwethemuka ni kuwaitanila ku msonkhano. (Mat. 28:10b; 1 Akor. 15:6) Mofananamo, masiku ano tingalimbilikitse ozilala kuyambanso kupezeka ku misonkhano ya mpingo. Tidziŵa kuti tingafunike kuwaitanila maulendo angapo asanayambe kubwela. Paja amati kanthu n’khama. Mosakaika konse, Yesu anakondwela ngako kuti ophunzila ake analandila ciitano cake.—Yelekezelani na Mateyu 28:16 komanso Luka 15:6.

17. Kodi mudzacita bwanji wozilala akabwela ku misonkhano?

17 Alandileni na manja aŵili. Yesu anapangitsa ophunzila ake kumva omasuka atakumana nawo. Iye ndiye anayamba kukambilana nawo. (Mat. 28:18) Kodi mudzacita bwanji wozilala akabwela ku Nyumba ya Ufumu? Tiyenela kukhala patsogolo kum’landila na manja aŵili. Poyamba, mwina tingadodome kuti tidzawauza ciani. Koma m’malo momucititsa manyazi, tingamuuze kuti ndife okondwa kumuona.

18. Kodi tingawalimbikitse bwanji ofalitsa ozilala?

18 Alimbikitseni moona mtima. Ophunzila a Yesu ayenela kuti anaona nchito imene anapatsidwa ya kulalikila padziko lonse lapansi, kukhala cinchito cosatheka. Koma Yesu analimbikitsa otsatila ake powauza kuti: “Ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse.” (Mat. 28:20) Kodi izi zinathandiza ophunzila ake? Ngako! Posapita nthawi, iwo anali yakali-yakali “kuphunzitsa ndi kulengeza uthenga wabwino.” (Mac. 5:42) Ofalitsa ozilala nawonso amafunika cilimbikitso. Iwo angacite mantha akaganizila za kuyambanso kulalikila. Tingawalimbikitse kuti sadzayamba kulalikila okha. Akakhala okonzeka, tingalalikile nawo limodzi. Mosakaikila, adzayamikila kwambili thandizo lathu pamene akuyambanso kulalikila uthenga wabwino. Ngati timaona ozilala monga abale na alongo athu, zotulukapo zake zidzakondweletsa mpingo wonse. Kumbukilani kuti dzedzele-dzedzele si kugwa.

TIMAFUNA KUTSILIZA NCHITO IMENE YESU ANATIPATSA

19. Kodi cokhumba ca mtima wathu n’cotani? Nanga cifukwa ciani?

19 Kodi tiyenela kugwila nchito yopanga ophunzila mpaka liti? Mpaka kumapeto a dongosolo lino la zinthu. (Mat. 28:20) Koma kodi tidzakwanitsadi kugwila nchitoyi mpaka kumapeto? Tilidi otsimikiza mtima kucita zimenezi! Timakondwela kwambili kuseŵenzetsa nthawi yathu, mphamvu zathu, na cuma cathu kuti tipeze anthu amene ‘ali ndi maganizo abwino amene angawathandize kukapeza moyo wosatha.’ (Mac. 13:48) Pocita zimenezi, timatengela citsanzo ca Yesu. Iye anati: “Cakudya canga ndico kucita cifunilo ca amene anandituma ndi kutsiliza nchito yake.” (Yoh. 4:34; 17:4) Nafenso ndiye cokhumba ca mtima wathu. Timafuna tikatsilize nchito imene tinapatsidwa. (Yoh. 20:21) Timafunanso kuti ena, kuphatikizapo ozilala, agwile nafe nchitoyi mopilila.—Mat. 24:13.

20. Mogwilizana na Afilipi 4:13, n’cifukwa ciani tingakwanitse kuitsiliza nchito imene Yesu anatilamula?

20 Kukamba zoona, nchito imene Yesu anatipatsa si yopepuka. Koma si ili pamapewa pathu tokha. Yesu analonjeza kuti adzakhala nafe. Timagwila nchitoyi ya kupanga ophunzila monga “anchito anzake a Mulungu,” komanso pamodzi na “Khristu.” (1 Akor. 3:9; 2 Akor. 2:17) Conco, tingakwanitse kuitsiliza nchitoyi. Ni mwayi wokondweletsa kugwila nchito imeneyi na kuthandiza ena kucitanso cimodzi-modzi.—Ŵelengani Afilipi 4:13.

NYIMBO 79 Aphunzitseni Kucilimika

^ ndime 5 Yesu analamula otsatila ake kupanga ophunzila na kuwaphunzitsa kusunga zinthu zonse zimene iye anawalamula. M’nkhani ino, tiphunzila mmene tingatsatilile malangizo a Yesu. Mfundo zina m’nkhani ino zacokela mu Nsanja ya Olonda ya July 1, 2004, mapeji 14-19.

^ ndime 66 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Potsogoza phunzilo la Baibo, mlongoyu akufotokozela wophunzila wake masitepu amene angatenge kuti akulitse cikondi cake pa Mulungu. Pambuyo pake, wophunzilayo akuseŵenzetsa masitepu atatu amene waphunzila.