Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 46

Limbani Mtima—Yehova Ndiye Mthandizi Wanu

Limbani Mtima—Yehova Ndiye Mthandizi Wanu

“Sindidzakusiyani kapena kukutayani ngakhale pang’ono.” —AHEB. 13:5.

NYIMBO 55 Musaŵayope!

ZIMENE TIKAMBILANE *

1. Kodi cingatitonthoze n’ciani tikamva monga tili tokha, kapena tikalefuka na mavuto? (Sal. 118:5-7)

KODI munayamba mwamvelapo kuti muli nokha-nokha, wopanda wina aliyense wokuthandizani kulimbana na vuto limene munakumana nalo? Ambili anamvelapo conco, kuphatikizapo atumiki a Yehova okhulupilika. (1 Maf. 19:14) Ngati zimenezi zingakucitikileni, kumbukilani lonjezo la Yehova lakuti: “Sindidzakusiyani kapena kukutayani ngakhale pang’ono.” Conco tingakambe motsimikiza kuti: “Yehova ndiye mthandizi wanga. Sindidzaopa.” (Aheb. 13:5, 6) Mtumwi Paulo analemba mawu amenewa kwa Akhristu anzake a ku Yudeya ca m’ma 61 C.E. Mawu akewo atikumbutsa zolembedwa pa Salimo 118:5-7.—Ŵelengani.

2. Kodi tikambilane ciani m’nkhani ino? Ndipo cifukwa ciani?

2 Mwa zocitika pa umoyo wake, Paulo mofanana na wamasalimo anadziŵa kuti Yehova ndiye Mthandizi wake. Mwacitsanzo, zaka zoposa ziŵili kumbuyoko asanalembe kalata yake kwa Aheberi, Paulo ananyamuka ulendo woopsa wa panyanja yowinduka na cimphepo camkuntho. (Mac. 27:4, 15, 20) Asanyamuke ulendowo komanso mkati mwa ulendowo, Yehova anaonetsa m’njila zambili kuti analidi Mthandizi wa Paulo. M’nkhani ino tikambilane njila zitatu mwa zimenezo. Yehova anam’thandiza kupitila mwa Yesu na angelo, anthu a ulamulilo, komanso Akhristu anzake. Kukambilana zocitikazi mu umoyo wa Paulo, kudzalimbitsa cidalilo cathu m’lonjezo la Mulungu lakuti adzayankha mapemphelo athu opempha thandizo.

THANDIZO LA YESU NA ANGELO

3. Kodi Paulo ayenela kuti anafika podzifunsa ciani? Ndipo cifukwa ciani?

3 Paulo anali kufunikila thandizo. Ca mu 56 C.E., gulu la laciwawa linagwila Paulo na kum’guguzila kunja kwa kacisi ku Yerusalemu kuti akamuphe. Tsiku lotsatila, Paulo atapelekedwa ku Khoti Yapamwamba ya Ayuda, adani ake anatsala pang’ono kum’khadzula-khadzula. (Mac. 21:30-32; 22:30; 23:6-10) Panthawiyo, n’kutheka kuti Paulo anafika podzifunsa kuti, ‘Kodi nidzapilila mavutowa mpaka liti?’

4. Kodi Yehova anam’thandiza bwanji Paulo kupitila mwa Yesu?

4 Kodi Paulo analandila thandizo lotani? Usiku wotsatila Paulo atamangidwa, “Ambuye,” Yesu, anaimilila pambali pake na kumuuza kuti: “Limba mtima! Pakuti wandicitila umboni mokwanila mu Yerusalemu, ndipo ukandicitilanso umboni ku Roma.” (Mac. 23:11) Cinalidi cilimbikitso ca panthawi yake! Yesu anayamikila Paulo cifukwa cocitila umboni mu Yerusalemu. Ndipo analonjeza Paulo kuti adzafika bwino-bwino ku Roma, ndipo akacitilanso umboni kumeneko. Pambuyo polandila cilimbikitso cimeneco, Paulo ayenela anamva kukhala wotetezeka monga mwana wofungatiwa na atate ake.

Cimphepo camphamvu cili mkati panyanja, mngelo akutsimikizila Paulo kuti onse m’ngalawayo adzapulumuka paulendo wovuta umenewo (Onani ndime 5)

5. Kodi Yehova anam’thandiza bwanji Paulo kupitila mwa mngelo? (Onani cithunzi pacikuto.)

5 Kodi Paulo anakumananso na mavuto ena ati? Patapita zaka pafupi-fupi ziŵili pambuyo pa zocitika za ku Yerusalemu, Paulo ananyamuka ulendo wapamadzi wopita ku Italy. Ali paulendowo, ngalawa imene anakwela inakumana na cimphepo camphamvu, cakuti oyendetsa ngalawayo, komanso okwelamo, onse anaganiza kuti adzafa. Koma Paulo mtima unali m’malo, sanacite mantha. Cifukwa ciani? Iye anauza onse m’ngalawayo kuti: “Pakuti usiku mngelo wa Mulungu wanga, amene ndikumucitila utumiki wopatulika, anaima pafupi nane, ndi kunena kuti, ‘Usaope Paulo. Uyenela kukaima pamaso pa Kaisara, ndipo taona! Cifukwa ca iwe, Mulungu mokoma mtima adzapulumutsa onse amene uli nawo pa ulendowu.’” Yehova anaseŵenzetsa mngelo kubweleza mawu acilimbikitso amene iye anali atauza Paulo poyamba kupitila mwa Yesu. Ndipo Paulo anakafikadi ku Roma.—Mac. 27:20-25; 28:16.

6. Ni lonjezo la Yesu liti limene lingatilimbikitse? Ndipo cifukwa ciani?

6 Kodi timalandila thandizo lotani? Yesu adzaticilikiza monga anacitila kwa Paulo. Mwacitsanzo, amalonjeza otsatila ake onse kuti: “Ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse mpaka m’nyengo ya mapeto a nthawi ino.” (Mat. 28:20) Mawu a Yesu amenewa amatilimbikitsa kwambili. Tikutelo cifukwa ciani? Cifukwa masiku ena amakhala ovuta kucita nawo. Mwacitsanzo, tikataikilidwa wokondedwa wathu, timakhala acisoni osati kwa masiku ocepa ayi, koma mwina kwa zaka zambili. Ndipo cimatiŵaŵa kwambili. Ena amalimbana na masiku ovuta a ukalamba. Ndipo palinso ena amene amakhala okhwethemuka masiku ena cifukwa ca kupsinjika maganizo. Ngakhale n’telo, timapeza mphamvu zokwanitsa kupilila cifukwa tidziŵa kuti Yesu ali nafe “masiku onse,” ngakhale zinthu zitavuta bwanji pa umoyo wathu.—Mat. 11:28-30.

Angelo amaticilikiza na kutitsogolela pamene tikulalikila (Onani ndime 7)

7. Malinga na Chivumbulutso 14:6, kodi Yehova amatithandiza bwanji masiku ano?

7 Mawu a Mulungu amatitsimikizila kuti Yehova adzatithandiza kupitila mwa angelo ake. (Aheb. 1:7, 14) Mwacitsanzo, angelo amaticilikiza na kutitsogolela tikamalalikila ‘uthenga wabwino wa Ufumu,’ kwa anthu “kudziko lililonse, fuko lililonse, [komanso] cinenelo ciliconse.”—Mat. 24:13, 14; Ŵelengani Chivumbulutso 14:6.

THANDIZO LA ANTHU A ULAMULILO

8. Kodi Yehova anam’thandiza bwanji Paulo kupitila mwa mkulu wa asilikali?

8 Kodi Paulo analandila thandizo lotani? Kumbuyoko mu 56 C.E., Yesu analimbikitsa Paulo kuti adzafika ku Roma. Komabe, Ayuda ena anakonza ciwembu cakuti akakhalizile Paulo panjila kuti akamuphe. Koma mkulu wa asilikali aciroma, Kalaudiyo Lusiya, atadziŵa za ciwembuco, anapulumutsa Paulo. Iye mwamsanga analamula gulu la asilikali kuti am’pelekeze Paulo ku Kaisareya, pa mtunda wa makilomita 105 kucokela ku Yerusalemu. Atafika Kaisareya, Bwanamkubwa Felike analamula kuti Paulo “amusunge m’nyumba ya mfumu Herode ndi kumuyang’anila.” Apa lomba aciwembu aja ofuna kupha Paulo palibe zimene akanacita.—Mac. 23:12-35.

9. Kodi Bwanamkubwa Fesito anam’thandiza bwanji Paulo?

9 Zaka ziŵili zinapitapo ndipo Paulo anali cikhalilebe m’ndende ku Kaisareya. Bwanamkubwa tsopano anali Fesito m’malo mwa Felike. Ayuda anacondelela Fesito kuti Paulo apite ku Yerusalemu kuti mlandu wake ukakambidwe, koma Fesito anakana. Mwina bwanamkubwayo anali kudziŵa za ciwembu cimene anakonzela Paulo kuti “amudikilile panjila ndi kumupha.”—Mac. 24:27–25:5.

10. Kodi Bwanamkubwa Fesito anacita ciani Paulo atapempha kuti akaweluzidwe na Kaisara?

10 Pambuyo pake, mlandu wa Paulo unakambidwila ku Kaisareya. Popeza Fesito ‘anafuna kuti Ayudawo amukonde,’ anafunsa Paulo kuti: “Kodi ukufuna kupita ku Yerusalemu, kuti nkhani imeneyi ikaweluzidwe kumeneko pamaso panga?” Paulo anadziŵa zakuti akapita ku Yerusalemu akhoza kukaphedwa. Anadziŵanso zoyenela kucita kuti apulumutse moyo wake, kupita ku Roma, na kupitiliza utumiki wake. Conco iye anati: “Ndikupempha kuti ndikaonekele kwa Kaisara!” Atakambilana na aphungu ake, Fesito anauza Paulo kuti: “Popeza kuti wapempha kukaonekela kwa Kaisara, udzapitadi kwa Kaisara.” Cigamulo cabwino ca Fesito cinapulumutsa Paulo kwa adani ake. Posapita nthawi, Paulo anafika ku Roma, kutali na Ayuda amene anali kufuna kumupha.—Mac. 25:6-12.

11. N’kutheka kuti Paulo anaganizila mawu olimbikitsa ati olembedwa na Yesaya?

11 Poyembekezela kunyamuka ulendo wake wa pamadzi wopita ku Italy, n’kutheka kuti Paulo anaganizila za cenjezo limene mneneli Yesaya anauzilidwa kulemba ponena za anthu otsutsa Yehova. Iye analemba kuti: “Konzani zocita, koma zidzalepheleka. Nenani zoti anthu acite, koma sizidzacitidwa, cifukwa Mulungu ali nafe.” (Yes. 8:10) Paulo anadziŵa kuti Mulungu adzam’thandiza, ndipo izi ziyenela kuti zinam’limbitsa mtima kuti akayang’anizane na mayeso anali kutsogolo.

Monga anacitila kalelo, Yehova angakhudze mitima ya anthu a ulamulilo masiku ano kuti ateteze atumiki ake (Onani ndime 12)

12. Kodi Yuliyo anacita zinthu motani na Paulo? Nanga Paulo ayenela kuti anazindikila ciani?

12 Mu 58 C.E., Paulo ananyamuka ulendo wake wa pamadzi wopita ku Italy. Pokhala mkaidi, anaikidwa m’manja mwa mkulu wa asilikali aciroma, Yuliyo. Kucokela panthawiyo, Yuliyo anali na mphamvu zokhaulitsa Paulo kapena kum’citila zinthu mokoma mtima. Kodi anaziseŵenzetsa bwanji mphamvu zakezo? Tsiku lotsatila atafika kumtunda, “Yuliyo anakomela mtima kwambili Paulo ndipo anamulola kupita kwa mabwenzi ake.” Ndipo pambuyo pake, Yuliyo anacita ngakhale kuteteza moyo wa Paulo. Motani? Asilikali aja anafuna kupha akaidi onse omwe anali m’ngalawa, koma Yuliyo anawaletsa kucita zimenezo. Cifukwa? Iye “anafunitsitsa kuti Paulo akafike naye ali bwinobwino.” Paulo ayenela kuti anazindikila kuti Yehova ndiye anali kuseŵenzetsa mkulu wa asilikali wokoma mtimayo kuti am’thandize.—Mac. 27:1-3, 42-44.

Onani ndime 13

13. Kodi Yehova angaseŵenzetse bwanji mphamvu zake?

13 Kodi timalandila thandizo lotani? Ngati n’zogwilizana na colinga cake, Yehova angaseŵenzetse mzimu wake woyela wamphamvu kupangitsa anthu a ulamulilo kucita zimene iye akufuna. Mfumu Solomo analemba kuti: “Mtima wa mfumu uli ngati mitsinje yamadzi m’dzanja la Yehova. Amautembenuzila kulikonse kumene iye akufuna.” (Miy. 21:1) Kodi mwambiwu utanthauzanji? Anthu angakumbe mfolo wopatutsila madzi kumene iwo akufuna. Mofananamo, Yehova angaseŵenzetse mzimu wake woyela kupatutsa maganizo a olamulila kuti acite zinthu mogwilizana na cifunilo cake. Izi zikacitika, anthu a ulamulilo amakhala na mtima wopanga zigamulo zokomela anthu a Mulungu.—Yelekezelani na Ezara 7:21, 25, 26.

14. Malinga na Machitidwe 12:5, kodi tiyenela kupemphelelanso ndani?

14 Kodi tiyenela kucita ciani? Tingapemphelele anthu a ulamulilo pamene akupeleka zigamulo zokhudza umoyo na utumiki wathu. (1 Tim. 2:1, 2; Neh. 1:11) Mofanana na Akhristu oyambilila, timawapemphelela kwambili abale na alongo athu amene ali m’ndende. (Ŵelengani Machitidwe 12:5; Aheb. 13:3) Kuwonjezela apo, tingapemphelelenso oyang’anila akaidi. Tingacondelele Yehova kuti akhudze maganizo awo kuti azicita zinthu monga Yuliyo, na ‘kukomela mtima’ abale na alongo athu amene ali m’ndende.

THANDIZO LA AKHRISTU ANZATHU

15-16. Kodi Yehova anam’thandiza bwanji Paulo kupitila mwa Arisitako na Luka?

15 Kodi Paulo analandila thandizo lotani? Pa ulendo wake wa ku Roma, Paulo mobweleza-bweleza analandila thandizo limene Yehova anapeleka kupitila mwa Akhristu anzake. Tiyeni tione zitsanzo zina.

16 Anzake a Paulo aŵili okhulupilika, Arisitako na Luka, anadzipeleka kuti apita naye limodzi ku Roma. * Iwo anaika miyoyo yawo paciwopsezo kuti apelekeze Paulo, ngakhale kuti Baibo si ionetsa kuti Yesu nawonso anawapatsa citsimikizo cakuti adzafika bwino ku Roma. Pambuyo pake ali pa ulendo wowopsawo m’pamene anadziŵa kuti miyoyo yawo idzatetezeka. Conco, Luka na Arisitako atakwela ngalawayo ku Kaisareya, Paulo ayenela kuti anapeleka pemphelo locokela pansi pamtima kwa Yehova, kumuyamikila pom’patsa thandizo la Akhristu anzake aŵili olimba mtima.—Mac. 27:1, 2, 20-25.

17. Kodi Yehova anam’thandiza bwanji Paulo kupitila mwa Akhristu abale?

17 Kangapo konse, Paulo anathandizidwa na Akhristu anzake pa ulendo wakewo. Mwacitsanzo, mu mzinda wa Sidoni, Yuliyo analola Paulo “kupita kwa mabwenzi ake kuti akamusamalile.” Ndipo atafika mu mzinda wa Potiyolo, Paulo na anzake ‘anapeza abale ndipo anawacondelela kuti akhale nawo masiku 7.’ Abale na alongo m’madela amenewo anasamalila Paulo na anzake pa zosoŵa zakuthupi. Ndipo omucelezawo ayenela kuti anakondwela kwambili, iye atawafotokozela zocitika zolimbikitsa. (Yelekezelani na Machitidwe 15:2, 3.) Atalimbikitsidwa, Paulo na anzake anapitiliza ulendo wawo.—Mac. 27:3; 28:13, 14.

Mofanana na Paulo, timalandila thandizo la Yehova kupitila mwa Akhristu anzathu (Onani ndime 18)

18. N’ciani cinalimbikitsa Paulo kuyamikila Mulungu na kukhala wolimba mtima?

18 Pamene Paulo anali kuyandikila mzinda wa Roma, ayenela kuti anakumbukila zimene analembela mpingo wa mu mzindawo zaka zitatu kumbuyoko kuti: “Kwa zaka zambili ndakhala ndikulakalaka kufika kwanuko.” (Aroma 15:23) Koma sanayembekezele zakuti adzafika kumeneko ali mkaidi. Paulo ayenela kuti analimbikitsidwa kwambili atapeza kuti abale ocokela mu mzinda wa Roma akum’cingamila kunjila kuti amulandile. Baibo imati: “Paulo atawaona, anayamika Mulungu, ndipo analimba mtima.” (Mac. 28:15) Onani kuti Paulo anayamika Mulungu cifukwa cakuti abale a kumeneko anali naye. Cifukwa ciani? Paulo anaonanso kuti Yehova akum’thandiza kupitila mwa Akhristu anzake.

Onani ndime 19

19. Malinga na 1 Petulo 4:10, kodi Yehova angatiseŵenzetse bwanji popeleka thandizo lake kwa ofunikila thandizo?

19 Kodi tiyenela kucita ciani? Kodi mudziŵako abale kapena alongo mu mpingo mwanu amene ni opsinjika maganizo cifukwa ca matenda, kapena mikhalidwe ina yovuta kucita nayo? Kapena mwina anataikilidwa okondedwa awo. Tikadziŵa kuti wina akufunikila thandizo, tingapemphe Yehova kuti atithandize kukamba mawu kapena kum’citila cinthu coonetsa kuti timam’konda munthuyo. Mwina mawu athu na zimene tingam’citile m’bale kapena mlongo wathu, ndiye cilimbikitso cimene akufunikila panthawiyo. (Ŵelengani 1 Petulo 4:10) * Amene tingathandizewo angapezenso cidalilo cakuti lonjezo la Yehova lakuti, “Sindidzakusiyani kapena kukutayani ngakhale pang’ono,” ligwilanso nchito kwa iwo. Kodi izi sizingakupatseni cimwemwe codzaza tsaya?

20. N’cifukwa ciani tingakambe mwacidalilo kuti: “Yehova ndiye mthandizi wanga”?

20 Monga zinalili kwa Paulo na anzake, nafenso timakumana na mavuto amene ali ngati zimphepo zamkuntho pa ulendo wathu wopita ku moyo. Panthawi imodzi-modzi, timadziŵa kuti tingakhale olimba mtima cifukwa Yehova ali nafe. Iye amatithandiza kupitila mwa Yesu na angelo. Ndiponso ngati n’zogwilizana na cifunilo cake, Yehova angatithandize kupitila mwa anthu a ulamulilo. Ndipo ambili a ife taonapo mmene Yehova amaseŵenzetsela mzimu wake woyela kukhudza mitima ya abale na alongo kuti atithandize. Conco, monga Paulo, ifenso tingakambe mwacidalilo kuti: “Yehova ndiye mthandizi wanga. Sindidzaopa. Munthu angandicite ciyani?”—Aheb. 13:6.

NYIMBO 38 Adzakulimbitsa

^ ndime 5 M’nkhani ino tikambilane njila zitatu zimene Yehova anaseŵenzetsa pothandiza mtumwi Paulo kulimbana na mavuto. Kuphunzila mmene Yehova anakhalila Mthandizi kumbuyoko, kudzalimbitsa cikhulupililo cathu cakuti Yehova adzatithandizanso masiku ano pamene tikulimbana na mavuto.

^ ndime 16 Arisitako na Luka anali atayendapo kale na Paulo. Amuna odalilika amenewa anakhalabe na Paulo pamene anali m’ndende ku Roma.—Mac. 16:10-12; 20:4; Akol. 4:10, 14.