Nkhani Yophunzira 46

Limbani Mtima Chifukwa Yehova Akuthandizani

Limbani Mtima Chifukwa Yehova Akuthandizani

“Sindidzakusiyani kapena kukutayani ngakhale pang’ono.”​AHEB. 13:5.

NYIMBO NA. 55 Musawaope!

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1. Kodi n’chiyani chimene chingatilimbikitse ngati tikuona kuti tili tokhatokha kapena sitingakwanitse kupirira mavuto athu? (Salimo 118:5-7)

KODI nthawi zina mumamva kuti muli nokhanokha ndipo palibe amene angakuthandizeni pa mavuto anu? Ambiri amamvanso choncho, kuphatikizapo atumiki okhulupirika a Yehova. (1 Maf. 19:14) Ngati inunso mutayamba kumva choncho, muzikumbukira lonjezo la Yehova lakuti: “Sindidzakusiyani kapena kukutayani ngakhale pang’ono.” Choncho tinganene molimba mtima kuti: “Yehova ndiye mthandizi wanga. Sindidzaopa.” (Aheb. 13:5, 6) Mtumwi Paulo analembera mawu amenewa okhulupirira anzake a ku Yudeya cha m’ma 61 C.E. Mawu akewa akutikumbutsa zimene wolemba masalimo ananena pa Salimo 118:5-7.—Werengani.

2. Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi, nanga n’chifukwa chiyani?

2 Mofanana ndi wolemba masalimoyu, Paulo ankadziwa kuti Yehova angamuthandize chifukwa anamuthandizapo kambirimbiri m’mbuyomu. Mwachitsanzo, zaka zoposa ziwiri asanalembe kalata yake yopita kwa Aheberi, Paulo anapulumuka chimphepo choopsa pamene ankayenda panyanja. (Mac. 27:4, 15, 20) Pa ulendo wonsewu komanso kwa zaka zambiri asananyamuke ulendowu, Yehova anathandiza Paulo m’njira zosiyanasiyana. Munkhaniyi tikambirana njira zitatu. Yehova anamuthandiza pogwiritsa ntchito Yesu ndi angelo, anthu audindo komanso okhulupirira anzake. Kukambirana zimene zinachitika pa moyo wa Paulo kutithandiza kuti tizikhulupirira kwambiri lonjezo la Mulungu lakuti adzatiyankha tikamam’pempha kuti atithandize.

ANATHANDIZIDWA NDI YESU KOMANSO ANGELO

3. Kodi mwina Paulo ankadzifunsa funso lotani, nanga n’chifukwa chiyani?

3 Paulo ankafunika kuthandizidwa. Cha m’ma 56 C.E., khamu la anthu linamukokera kunja kwa kachisi ku Yerusalemu ndipo linkafuna kumupha. Tsiku lotsatira, pamene Paulo anamubweretsa ku Khoti Lalikulu la Ayuda, adani ake anatsala pang’ono kumukhadzulakhadzula. (Mac. 21:30-32; 22:30; 23:6-10) Pa nthawiyi mwina Paulo ankadzifunsa kuti, ‘Kodi ndipirira mavuto amenewa mpaka liti?’

4. Kodi Yehova anagwiritsa ntchito bwanji Yesu kuti athandize Paulo?

4 Kodi Yesu anathandiza bwanji Paulo? Tsiku limene Paulo anamangidwa, usiku “Ambuye” Yesu anaimirira pambali yake ndi kunena kuti: “Limba mtima! Pakuti wandichitira umboni mokwanira mu Yerusalemu, ndipo ukandichitiranso umboni ku Roma.” (Mac. 23:11) Zimenezitu zinalimbikitsa kwambiri Paulo. Yesu anayamikira Paulo chifukwa cha ntchito yochitira umboni imene anagwira ku Yerusalemu. Ndipo analonjeza kuti Paulo akafika bwinobwino ku Roma kuti akapitirize kugwira ntchito yochitira umboni kumeneko. Atamva zimenezi, Paulo anayamba kuona kuti ndi wotetezeka ngati mwana amene ali m’manja mwa bambo ake.

Panyanja patachita mphepo yamkuntho, mngelo anatsimikizira Paulo kuti aliyense amene anali m’ngalawayo apulumuka paulendo woopsawo (Onani ndime 5)

5. Kodi Yehova anathandiza bwanji Paulo pogwiritsa ntchito mngelo? (Onani chithunzi chapachikuto.)

5 Kodi Paulo anakumananso ndi mavuto ena ati? Patadutsa zaka pafupifupi ziwiri kuchokera pa nthawi imene adani anamuukira ku Yerusalemu, Paulo anakwera ngalawa pa ulendo wopita ku Italiya. Ngalawayi inakumana ndi mphepo yamkuntho ndipo oyendetsa komanso anthu amene anali mmenemo ankaganiza kuti afa. Koma Paulo sankachita mantha. Chifukwa chiyani? Iye anauza anthu amene anali m’ngalawayo kuti: “Usiku mngelo wa Mulungu wanga, amene ndikumuchitira utumiki wopatulika, anaima pafupi nane, ndi kunena kuti, ‘Usaope Paulo. Uyenera kukaima pamaso pa Kaisara, ndipo taona! Chifukwa cha iwe, Mulungu mokoma mtima adzapulumutsa onse amene uli nawo pa ulendowu.’” Yehova anagwiritsa ntchito mngelo kuti alimbikitse Paulo ngati mmene anamulimbikitsira m’mbuyomu pogwiritsa ntchito Yesu. Paulo anakafikadi ku Roma monga mmene Yehova anamulonjezera.—Mac. 27:20-25; 28:16.

6. Kodi ndi lonjezo liti la Yesu lomwe lingatilimbikitse, nanga n’chifukwa chiyani?

6 Kodi Yesu amatithandiza bwanji? Yesu adzatithandiza ngati mmene anathandizira Paulo. Mwachitsanzo, Yesu analonjeza otsatira ake onse kuti: “Ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse mpaka m’nyengo ya mapeto a nthawi ino.” (Mat. 28:20) Mawu a Yesuwa ndi olimbikitsa. Chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa chakuti masiku ena timakumana ndi zinthu zovuta kupirira. Mwachitsanzo, munthu amene timam’konda akamwalira timakhala achisoni, osati kwa masiku ochepa, koma mwina kwa zaka zambiri. Enanso amavutika tsiku ndi tsiku chifukwa cha ukalamba. Ndipo ena amavutika chifukwa cha nkhawa. Ngakhale zili choncho, timapeza mphamvu kuti tithe kupirira chifukwa tikudziwa kuti Yesu alinafe “masiku onse” kuphatikizapo nthawi zovuta kwambiri pa moyo wathu.—Mat. 11:28-30.

Angelo amatithandiza komanso kutitsogolera tikamalalikira (Onani ndime 7)

7. Mogwirizana ndi Chivumbulutso 14:6, kodi Yehova amatithandiza bwanji masiku ano?

7 Mawu a Mulungu amatitsimikizira kuti Yehova amatithandiza pogwiritsa ntchito angelo. (Aheb. 1:7, 14) Mwachitsanzo, angelo amatithandiza ndi kutitsogolera tikamalalikira “uthenga wabwino wa Ufumu” kwa anthu ochokera “kudziko lililonse, fuko lililonse, chinenero chilichonse.”—Mat. 24:13, 14; werengani Chivumbulutso 14:6.

ANTHU AUDINDO AMATITHANDIZA

8. Kodi Yehova anathandiza bwanji Paulo pogwiritsa ntchito mkulu wa asilikali?

8 Kodi anthu audindo anathandiza bwanji Paulo? Mu 56 C.E., Yesu anatsimikizira Paulo kuti akafika ku Roma. Komabe Ayuda ena ku Yerusalemu anakonza chiwembu choti aphe Paulo. Mkulu wa asilikali a Chiroma dzina lake Kalaudiyo Lusiya atamva za chiwembu chimenechi anapulumutsa Paulo. Mwamsanga, Kalaudiyo analamula gulu la asilikali kuti ateteze Paulo ndi kum’tenga kupita naye ku Kaisareya, womwe ndi mtunda wa makilomita 105 kuchokera ku Yerusalemu. Ku Kaisareyako Bwanamkubwa Felike analamula kuti Paulo “amusunge m’nyumba ya mfumu Herode ndi kumuyang’anira.” Ayuda amene ankafuna kupha Paulo aja sakanatha kufikako.—Mac. 23:12-35.

9. Kodi Bwanamkubwa Fesito anathandiza bwanji Paulo?

9 Zaka ziwiri zinadutsa Paulo adakali m’ndende ku Kaisareya. Felike analowedwa m’malo ndi Fesito amene anakhala bwanamkubwa watsopano. Ayuda anapempha Fesito kuti Paulo apite ku Yerusalemu kuti akamuimbe mlandu, koma Fesito anakana. N’kutheka kuti bwanamkubwayu ankadziwa kuti Ayudawo anakonza chiwembu kuti “amudikirire panjira ndi kumupha.”—Mac. 24:27–25:5.

10. Kodi Bwanamkubwa Fesito anayankha bwanji Paulo atapempha kuti mlandu wake ukaweruzidwe ndi Kaisara?

10 Kenako mlandu wa Paulo unazengedwa ku Kaisareya. Koma Fesito “pofuna kuti Ayudawo amukonde,” anafunsa Paulo kuti: “Kodi ukufuna kupita ku Yerusalemu, kuti nkhani imeneyi ikaweruzidwe kumeneko pamaso panga?” Paulo ankadziwa kuti akapita ku Yerusalemu akhoza kukaphedwa komanso ankadziwa zoyenera kuchita kuti apulumutse moyo wake n’cholinga choti akafike ku Roma ndi kukapitiriza kulalikira. Iye anati: “Ndikupempha kuti ndikaonekere kwa Kaisara!” Atakambirana ndi aphungu ake, Fesito anauza Paulo kuti: “Popeza kuti wapempha kukaonekera kwa Kaisara, udzapitadi kwa Kaisara.” Zimene Fesito anachita posankha kuti amutumize ku Roma zinapulumutsa Paulo kwa adani ake. Posakhalitsa Paulo anafika ku Roma komwe Ayuda amene ankafuna kumupha aja sakanatha kumupeza.—Mac. 25:6-12.

11. Kodi Paulo ayenera kuti ankaganizira mawu olimbikitsa ati amene Yesaya analemba?

11 Pamene Paulo ankayembekezera kunyamuka ulendo wake wopita ku Italiya, ayenera kuti ankaganizira chenjezo limene mouziridwa mneneri Yesaya anauza anthu otsutsana ndi Yehova. Mneneriyu anati: “Konzani zochita, koma zidzalephereka. Nenani zoti anthu achite, koma sizidzachitidwa, chifukwa Mulungu ali nafe.” (Yes. 8:10) Paulo ankadziwa kuti Mulungu amuthandiza ndipo zimenezi zinamulimbikitsa kuti apirire mayesero amene ankayembekezera kukumana nawo m’tsogolo.

Monga mmene anachitira m’mbuyomu, masiku anonso Yehova angagwiritse ntchito anthu audindo poteteza anthu ake (Onani ndime 12)

12. Kodi Yuliyo ankamuchitira zotani Paulo, nanga n’kutheka kuti Pauloyo anazindikira chiyani?

12 Mu 58 C.E., Paulo anayamba ulendo wake wopita ku Italiya. Popeza kuti anali mkaidi, Paulo ankayang’aniridwa ndi msilikali wa Chiroma dzina lake Yuliyo. Pa nthawiyi, Yuliyo anali ndi mphamvu zoti akanatha kumuzunza kapena kumukomera mtima. Koma kodi iye anagwiritsa ntchito bwanji udindo wake? Tsiku lotsatira atafika padoko, “Yuliyo anakomera mtima kwambiri Paulo ndipo anamulola kupita kwa mabwenzi ake.” Pa nthawi ina, Yuliyo anapulumutsa moyo wa Paulo. Kodi anachita bwanji zimenezi? Asilikali ankafuna kupha akaidi onse amene anali m’chingalawacho, koma Yuliyo anawaletsa. N’chifukwa chiyani anawaletsa? Iye “anafunitsitsa kuti Paulo akafike naye ali bwinobwino.” N’kutheka kuti Paulo anazindikira kuti Yehova akugwiritsa ntchito msilikali wokoma mtimayu pomuthandiza komanso kumuteteza.—Mac. 27:1-3, 42-44.

Onani ndime 13

13. Kodi Yehova angagwiritse ntchito bwanji anthu a udindo pothandiza anthu ake?

13 Kodi anthu a udindo angatithandize bwanji? Yehova akhoza kugwiritsa ntchito mzimu wake woyera womwe ndi wamphamvu kwambiri, kuchititsa anthu amene ali ndi udindo kuti achite zimene iyeyo akufuna ngati zinthuzo n’zogwirizana ndi chifuniro chake. Mfumu Solomo analemba kuti: “Mtima wa mfumu uli ngati mitsinje yamadzi m’dzanja la Yehova. Amautembenuzira kulikonse kumene iye akufuna.” (Miy. 21:1) Kodi mwambi umenewu ukutanthauza chiyani? Anthu angakumbe ngalande kuti apatutse madzi a mumtsinje n’cholinga chakuti azipita kumene iwowo akufuna. Mofanana ndi zimenezi Yehova angagwiritse ntchito mzimu wake posintha maganizo a olamulira kuti achite zinthu zimene zingakwaniritse cholinga chake. Zikatero anthu olamulira amatha kusankha zinthu zimene zingathandize anthu a Mulungu.—Yerekezerani ndi Ezara 7:21, 25, 26.

14. Mogwirizana ndi Machitidwe 12:5, kodi tingapemphererenso ndani?

14 Kodi ifeyo tiyenera kuchita chiyani? Tingathe kupempherera ‘mafumu ndi anthu onse apamwamba,’ pamene akusankha zinthu zimene zingakhudze kulambira kwathu. (1 Tim. 2:1, 2; Neh. 1:11) Mofanana ndi Akhristu a m’nthawi ya atumwi, ifenso timapempherera mosalekeza abale ndi alongo athu amene ali m’ndende. (Werengani Machitidwe 12:5; Aheb. 13:3) Kuwonjezera apo tingapemphererenso asilikali a kundende amene akuyang’anira abale ndi alongo anthu. Tingapemphe Yehova kuti achititse anthu amenewa kukhala ndi maganizo ofanana ndi Yuliyo kuti ‘azikomera mtima’ abale ndi alongo athu amene ali m’ndende.—Mac. 27:3.

OKHULUPIRIRA ANZATHU AMATITHANDIZA

15-16. Kodi Yehova anathandiza bwanji Paulo pogwiritsa ntchito Alisitako ndi Luka?

15 Kodi Paulo anathandizidwa bwanji ndi okhulupirira anzake? Pa ulendo wake wopita ku Roma, kawirikawiri Paulo ankathandizidwa ndi Yehova kudzera mwa okhulupirira anzake. Tiyeni tione zitsanzo zingapo.

16 Anzake awiri a Paulo okhulupirika omwe ndi Alisitako ndi Luka, anaganiza zopita naye limodzi ku Roma. * Zikuoneka kuti Yesu sanatsimikizire amuna awiri amenewa kuti akafika bwinobwino ku Roma. Komabe mofunitsitsa iwo anaika moyo wawo pangozi kuti apite limodzi ndi Paulo. Zoti apulumuka anazidziwa mkati mwa ulendo wawo pamene anakumana ndi mphepo yamkuntho. Choncho pamene Alisitako ndi Luka anakwera ngalawa ku Kaisareya, Paulo ayenera kuti anapereka pemphero lochokera pansi pamtima kwa Yehova kumuthokoza chifukwa chomuthandiza kudzera mwa okhulupirira anzake olimba mtimawa.—Mac. 27:1, 2, 20-25

17. Kodi Yehova anathandiza bwanji Paulo pogwiritsa ntchito okhulupirira anzake?

17 Pa ulendo wake Paulo anathandizidwapo kangapo ndi okhulupirira anzake. Mwachitsanzo, atafika padoko ku Sidoni, Yuliyo analola Paulo “kupita kwa mabwenzi ake kuti akamusamalire.” Pambuyo pake atafika mumzinda wa Potiyolo, Paulo ndi anzakewo ‘anapeza abale ndipo anawachonderera kuti akhale nawo masiku 7.’ Pamene abalewo ankasamalira Paulo ndi anzakewo, mosakayikira Paulo ayenera kuti ankasangalatsa abalewo powafotokozera nkhani zolimbikitsa. (Yerekezerani ndi Mac. 15:2, 3) Atalimbikitsidwa Paulo ndi anzakewo ayenera kuti anapitiriza ulendo wawo.—Mac. 27:3; 28:13, 14.

Mofanana ndi Paulo, ifenso Yehova amatithandiza pogwiritsa ntchito okhulupirira anzathu (Onani ndime 18)

18. N’chifukwa chiyani Paulo anayamika Mulungu komanso kulimba mtima?

18 Pamene Paulo ankayandikira mzinda wa Roma ayenera kuti ankaganizira zimene analembera mpingo wa kumeneko zaka zitatu m’mbuyomo kuti: “Kwa zaka zambiri ndakhala ndikulakalaka kufika kwanuko.” (Aroma 15:23) Koma sankayembekezera kuti adzafika mumzindamo ngati mkaidi. Iye ayenera kuti analimbikitsidwa kwambiri kuona abale a ku Roma akumudikirira panjira kuti amupatse moni. “Paulo atawaona, anayamika Mulungu, ndipo analimba mtima.” (Mac. 28:15) Onani kuti Paulo anayamika Mulungu abalewa atabwera kudzakumana naye. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti Paulo anaona kuti apanso Yehova wamuthandiza pogwiritsa ntchito okhulupirira anzake.

Onani ndime 19

19. Malinga ndi zimene lemba la 1 Petulo 4:10 likunena, kodi Yehova angatigwiritsire ntchito bwanji kuti athandize anthu amene akufunika thandizo?

19 Kodi tingathandize bwanji okhulupirira anzathu? Kodi mukudziwa abale kapena alongo mumpingo mwanu amene akuvutika chifukwa cha matenda kapena chifukwa chakuti akukumana ndi mavuto ena? Kapena mwina ali ndi chisoni chifukwa chakuti wachibale wawo anamwalira? Tikadziwa kuti munthu wina akufunika thandizo, tingapemphe Yehova kuti atithandize kuti timuuze mawu olimbikitsa kapena kumuchitira zinthu zabwino. N’kutheka kuti zimene tingalankhule kapena kuchita ndi zimene zingalimbikitse m’bale kapena mlongo wathuyo. (Werengani 1 Petulo 4:10) * Ngati titawathandiza angayambe kukhulupirira kwambiri kuti lonjezo la Yehova lakuti, “Sindidzakusiyani kapena kukutayani ngakhale pang’ono,” likukwaniritsidwa pa iwo. Zimenezi zingakupangitseni kukhala osangalala.

20. N’chifukwa chiyani tinganene molimba mtima kuti “Yehova ndiye mthandizi wanga”?

20 Monga zinalili kwa Paulo ndi anzake, ifenso tingakumane ndi mavuto ambiri pamoyo wathu. Koma tingalimbe mtima chifukwa tikudziwa kuti Yehova ali nafe. Amatithandiza pogwiritsa ntchito Yesu komanso angelo. Ndipo ngati zikugwirizana ndi chifuniro chake, Yehova angatithandize pogwiritsa ntchito anthu audindo. Komanso malinga ndi zimene zachitikira ambirife, taona kuti Yehova amagwiritsa ntchito mzimu wake woyera polimbikitsa atumiki ake kuti athandize Akhristu anzawo. Mofanana ndi Paulo, tili ndi zifukwa zabwino zonenera molimba mtima kuti: “Yehova ndiye mthandizi wanga. Sindidzaopa. Munthu angandichite chiyani?”—Aheb. 13:6.

NYIMBO NA. 38 Mulungu Adzakulimbitsa

^ ndime 5 Munkhaniyi tikambirana njira zitatu zimene Yehova anathandizira mtumwi Paulo kuti apirire mavuto amene anakumana nawo. Kukambirana mmene Yehova anathandizira atumiki ake ena m’mbuyomu, kutithandiza kuti tizikhulupirira kwambiri kuti Yehova azitithandizanso masiku ano tikamakumana ndi mavuto.

^ ndime 16 Alisitako ndi Luka anali atayamba kale kuyenda ndi Paulo. Amuna okhulupirika amenewa anakhalanso ndi Paulo pamene anali m’ndende ku Roma.—Mac. 16:10-12; 20:4; Akol. 4:10, 14.

^ ndime 19 Onani Nsanja ya Olonda ya January 15, 2009, tsamba 13-14, ndime 5-9