Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 47

Kodi Mudzakhalabe Okonzeka Kusintha?

Kodi Mudzakhalabe Okonzeka Kusintha?

“Pomalizila abale, ndikuti pitilizani kukondwela, kusintha maganizo anu.”—2 AKOR. 13:11.

NYIMBO 54 “Njila ni Iyi”

ZIMENE TIKAMBILANE *

1. Malinga na Mateyu 7:13, 14, kodi tili paulendo m’lingalilo lotani?

TONSEFE tili paulendo. Kumene talinga, kapena kuti colinga cathu, ni kukakhala m’dziko latsopano pansi pa ulamulilo wacikondi wa Yehova. Tsiku lililonse, timayesetsa kuyenda panjila yopita ku moyo. Koma monga mmene Yesu anakambila, njila imeneyo ni yopanikiza ndipo nthawi zina zimativuta kuyendamo. (Ŵelengani Mateyu 7:13, 14.) Ndife opanda ungwilo, ndipo n’capafupi kupatuka panjila imeneyi.—Agal. 6:1.

2. Tikambilane ciani m’nkhani ino? (Onaninso bokosi lakuti “ Kudzicepetsa Kumatithandiza Kupanga Masinthidwe.”)

2 Kuti tipitilize kuyenda panjila yopanikiza imeneyi ya ku moyo, tiyenela kukhalabe okonzeka kusintha kaganizidwe kathu, kaonedwe kathu ka zinthu, na zocita zathu. Mtumwi Paulo analimbikitsa Akhristu a ku Korinto kupitilizabe “kusintha maganizo” awo. (2 Akor. 13:11) Malangizo amenewa amapitanso kwa ife. M’nkhani ino, tikambilane mmene Baibo ingatithandizile kusintha njila zathu, komanso mmene anzathu okhwima kuuzimu angatithandizile kuyendabe panjila ya ku moyo. Tione zimene zingapangitse kuti nthawi zina cikhale covuta kwa ife kutsatila malangizo amene gulu la Yehova limapeleka. Tionenso mmene kudzicepetsa kungatithandizile kupanga masinthidwe popanda kutaya cimwemwe cathu potumikila Yehova.

LOLANI MAWU A MULUNGU KUKUWONGOLELANI

3. Kodi Mawu a Mulungu angakuthandizeni bwanji?

3 Si capafupi kudzipenda mofikapo kuti tidziŵe maganizo athu komanso mmene timamvelela. Mtima wathu ni wonyenga, ndipo izi zingapangitse kuti zikhale zovuta kudziŵa kumene ukutitsogolela. (Yer. 17:9) N’cosavuta kudzinyenga tokha na “maganizo onama.” (Yak. 1:22) Conco, tiyenela kuseŵenzetsa Mawu a Mulungu podzifufuza. Mawu a Mulungu amavumbula zamkati mwa mtima wathu, ‘zimene timaganiza komanso zolinga za mtima wathu.’ (Aheb. 4:12, 13) Mawu a Mulungu tingawayelekezele na makina a Ekiselo (X-ray), amene amaunika mkati mwa thupi la munthu. Koma kuti tipindule na uphungu wa m’Baibo, komanso wocokela kwa oimilako Mulungu, tiyenela kukhala odzicepetsa.

4. N’ciani cionetsa kuti Mfumu Sauli anakhala munthu wodzikuza?

4 Zimene zinacitikila Mfumu Sauli zionetsa zimene zingatigwele ngati sitili odzicepetsa. Sauli anakhala wodzikuza kwambili cakuti analephela kuvomeleza kuti anafunika kusintha maganizo ake na zocita zake. (Sal. 36:1, 2; Hab. 2:4) Izi zinaonekela pamene Yehova anapatsa Sauli malangizo omveka bwino pa zimene anafunika kucita atagonjetsa Aamaleki. Sauli sanamvele Yehova. Ndipo pamene mneneli Samueli anakamba naye za nkhaniyi, Sauli anakana kuvomeleza colakwa cake. M’malo mwake, iye anadzilungamitsa mwa kupeputsa colakwa cake na kukankhila ena colakwaco. (1 Sam. 15:13-24) Panthawi ina kumbuyoko, Sauli anaonetsanso khalidwe limeneli. (1 Sam. 13:10-14) N’zacisoni kuti analola mtima wake kudzikuza. Cifukwa sanafune kusintha kaganizidwe kake, Yehova anam’dzudzula na kumukana.

5. Tingaphunzilepo ciani pa citsanzo coipa ca Sauli?

5 Kuti titengepo cenjezo pa citsanzo coipa ca Sauli, tingacite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi nikaŵelenga uphungu wonikhudza m’Mawu a Mulungu nimayesa kudzilungamitsa? Kodi nimayesa kupeputsa zotulukapo zake? Kodi nimakankhila kwa wina mlandu wa zocita zanga?’ Ngati yankho ni inde pa iliyonse ya mafunsowa, tifunika kusintha kaganizidwe kathu na kaonedwe kathu ka zinthu. Apo ayi, tidzakhala wodzikuza kwambili cakuti Yehova adzatikana kuti tisakhalenso bwenzi lake.—Yak. 4:6.

6. Fotokozani kusiyana pakati pa Mfumu Sauli na Mfumu Davide.

6 Onani kusiyana pakati pa Mfumu Sauli na Mfumu Davide amene anam’loŵa m’malo, munthu wokonda “cilamulo ca Yehova.” (Sal. 1:1-3) Davide anali kudziŵa kuti Yehova amapulumutsa anthu odzicepetsa, koma amatsutsa odzikuza. (2 Sam. 22:28) Conco Davide analola cilamulo ca Mulungu kuwongolela kaganizidwe kake. Iye analemba kuti: “Ndidzatamanda Yehova amene wandipatsa malangizo. Ndithudi, usiku impso zanga zandiwongolela.”—Sal. 16:7.

MAWU A MULUNGU

Mawu a Mulungu amaticenjeza tikayamba kupatuka panjila. Ngati ndife odzicepetsa, tidzalola Mawu a Mulungu kuwongolela maganizo athu olakwika (Onani ndime 7))

7. Kodi tidzacita ciani ngati tili odzicepetsa?

7 Ngati ndife odzicepetsa, tidzalola Mawu a Mulungu kuwongolela maganizo athu olakwika tisanacite coipa. Mawu a Mulungu adzakhala ngati mawu amene akutiuza kuti: “Njila ndi iyi. Yendani mmenemu.” Adzaticenjeza tikayamba kupatukila kumanzele kapena kulamanja. (Yes. 30:21) Tikamamvela Yehova, tidzapindula m’njila zambili. (Yes. 48:17) Mwacitsanzo, tidzapewa kucititsidwa manyazi cifukwa cowongoleledwa na munthu wina. Ndipo tidzamuyandikila kwambili Yehova, podziŵa kuti amacita nafe monga ana ake okondeka.—Aheb. 12:7.

8. Malinga na Yakobo 1:22-25, kodi tingaseŵenzetse bwanji Mawu a Mulungu monga galasi?

8 Mawu a Mulungu ali monga galasi kwa ife. (Ŵelengani Yakobo 1:22-25.) Ambili a ife timayang’ana pa galasi m’mawa uliwonse tisanacoke pa nyumba. Kucita izi, kumatithandiza kuti tidzikonze bwino tisanaonekele kwa anthu. Mofananamo, tikamaŵelenga Baibo tsiku lililonse, tidzaona mbali zofunika kusintha pa kaganizidwe kanthu na kaonedwe kathu ka zinthu. Ambili amakonda kuŵelenga lemba la tsiku m’mawa uliwonse asanacoke panyumba. Amafuna kuti zimene aŵelenga zikhale m’maganizo awo. Ndiyeno tsiku lonselo, amayesa kupeza mipata yoseŵenzetsa uphungu wa m’Mawu a Mulungu. Kuwonjezela apo, tiyenelanso kukhala na pulogilamu yophunzila Baibo, yophatikizapo kuŵelenga na kusinkha-sinkha Mawu a Mulungu tsiku lililonse. Iyi ingaoneke kuti ni mbali yocepa, koma ni yofunika kwambili kuti tipitilizebe kuyenda panjila yopanikiza ya ku moyo.

MVELANI KWA ANZANU OKHWIMA KUUZIMU

ANZATHU OKHWIMA KUUZIMU

Mkhristu mnzathu wokhwima kuuzimu angaticenjeze mokoma mtima. Kodi timayamikila kuti mnzathu analimba mtima kukamba nafe?(Onani ndime 9)

9. Ni panthawi iti pamene mnzathu angafunike kutiwongolela?

9 Kodi zinacitikapo kuti mwayamba kuloŵela ku njila yokupatutsani kwa Yehova? (Sal. 73:2, 3) Ngati mnzanu wokhwima mwauzimu analimba mtima na kukuwongolelani, kodi munamumvela na kutsatila uphungu wake? Ngati munatelo, munacita cinthu canzelu. Paja amati wakutsina khutu ndi mnansi. Ndipo mosakaikila mumayamikila kuti mnzanuyo anakucenjezani.—Miy. 1:5.

10. Kodi muyenela kucita bwanji mnzanu akakuwongolelani?

10 Mawu a Mulungu amatikumbutsa kuti: “Zilonda zovulazidwa ndi munthu wokukonda zimakhala zokhulupilika.” (Miy. 27:6) Kodi mawuwa ni oona m’lingalilo lotani? Ganizilani citsanzo ici: Yelekezani kuti mufuna kulumpha msewu wa mamotoka ambili, koma mwaika nzelu zanu ku foni. Ndiyeno mwayamba kuloŵa pa msewu cosayang’ana. Pamenepo, mnzanu akukugwilani padzanja mwamphamvu na kukukokelani kumbali. Wakugwilani mwamphamvu kwambili cakuti dzanja lanu likupweteka, koma wakupulumutsani ku ngozi ya motoka. Ngakhale kuti dzanja lanulo lingapwetekebe kwa masiku angapo, kodi mungakhumudwe na zimene mnzanuyo anacita? Simungatelo ayi! M’malo mwake mudzamuyamikila pa thandizo lake. Mofananamo, ngati mnzanu wakucenjezani kuti zokamba kapena zocita zanu zikusemphana na miyezo ya Mulungu yolungama, mungakhumudwe poyamba. Koma musakane uphungu wake kapena kukhumudwa naye. Kuteloko kungakhale kupusa. (Mlal. 7:9) M’malomwake, yamikilani kuti mnzanuyo walimba mtima kuti akambe namwe.

11. N’ciani cingapangitse munthu kukana uphungu wabwino wocokela kwa mnzake?

11 Kodi n’ciani cingapangitse munthu kukana uphungu wabwino wocokela kwa mnzake wacikondi? Kunyada. Anthu onyada amakonda “zowakomela m’khutu.” Iwo ‘amasiya kumvetsela coonadi.’ (2 Tim. 4:3, 4) Pokhala odzitukumula amadziona kuti amadziŵa zonse. Koma mtumwi Paulo analemba kuti: “Ngati wina akudziona kuti ndi wofunika pamene si wotelo, akudzinyenga.” (Agal. 6:3) Mfumu Solomo anafotokoza mfundoyi momveka bwino. Iye analemba kuti: “Mwana wosauka koma wanzelu ali bwino kuposa mfumu yokalamba koma yopusa, imene sionanso kufunika kocenjezedwa.”—Mlal. 4:13.

12. Tiphunzilapo ciani pa citsanzo ca mtumwi Petulo, copezeka pa Agalatiya 2:11-14?

12 Onani citsanzo ca mtumwi Petulo, pamene anapatsidwa uphungu na mtumwi Paulo pamaso pa anthu. (Ŵelengani Agalatiya 2:11-14) Petulo akanakhumudwa nawo uphungu wa Paulo, akanaika maganizo pa kapelekedwe ka uphunguwo, komanso malo pamene anaupelekela. Koma Petulo anacita mwanzelu. Analandila uphunguwo, ndipo sanasungile Paulo cakukhosi. M’malomwake, patapita nthawi iye anachula Paulo kuti ‘m’bale wokondedwa.’—2 Pet. 3:15.

13. Tizikumbukila mfundo ziti popeleka uphungu?

13 Ngati muona kuti mufunika kupatsa uphungu mnzanu, muyenela kukumbukila ciani? Musanam’fikile mnzanuyo, dzifunseni kuti, ‘Kodi nakhala “wolungama mopitilila muyezo”?’ (Mlal. 7:16) Munthu wolungama mopitilila muyezo amaweluza ena pa miyezo yake osati ya Yehova, ndipo nthawi zambili sakhala wacifundo. Ngati pambuyo podziunika, muona kuti mufunika ndithu kukambilana naye mnzanuyo, kam’thandizeni kuliona bwino-bwino vutolo, na kum’funsa mafunso aulemu amene angam’thandize kuzindikila colakwa cake. Onetsetsani kuti zimene mukukamba n’zozikidwa pa Malemba, pokumbukilanso kuti mnzanuyo adzayankha mlandu osati kwa imwe koma kwa Yehova. (Aroma 14:10) Popeleka uphungu kwa wina, dalilani nzelu zopezeka m’Mawu a Mulungu, na kutengela citsanzo ca Yesu pokhala wacifundo. (Miy. 3:5; Mat. 12:20) Cifukwa ciani? Cifukwa Yehova adzacita nafe monga mmene ifenso timacitila na ena.—Yak. 2:13.

TSATILANI MALANGIZO OPELEKEDWA NA GULU LA MULUNGU

GULU LA MULUNGU

Gulu la Mulungu limapeleka mavidiyo, zofalitsa, na misonkhano imene imathandiza tonsefe kuseŵenzetsa malangizo opezeka m’Mawu a Mulungu. Nthawi zina, Bungwe Lolamulila limapanga masinthidwe okhudza mmene nchito iyenela kuyendela (Onani ndime 14)

14. Kodi gulu la Mulungu limatipatsa ciani?

14 Yehova amatitsogolela panjila ya ku moyo kupitila m’gawo la padziko lapansi la gulu lake, limene limapeleka mavidiyo, zofalitsa, na misonkhano imene imathandiza tonsefe kuseŵenzetsa malangizo opezeka m’Mawu a Mulungu. Zonsezi maphunzilo ake amacokela m’Malemba. Bungwe Lolamulila limadalila mzimu woyela popanga zigamulo zokhudza njila zabwino koposa zogwilila nchito yolalikila. Ngakhale n’telo, nthawi na nthawi, Bungwe Lolamulila limabwelelamo m’zigamulo zake na kuona ngati pangafunike masinthidwe. Cifukwa ciani? Cifukwa “zocitika za padzikoli zikusintha,” ndipo gulu la Mulungu limafunika kusintha zinthu zina kuti zigwilizane na mikhalidwe yatsopano.—1 Akor. 7:31.

15. Kodi cakhala covuta kwa ofalitsa ena n’ciani?

15 Mosakaikila, timatsatila mosavuta kamvedwe katsopano ka coonadi, kapena mfundo zokhudza makhalidwe. Koma kodi timacita bwanji gulu la Mulungu likapanga masinthidwe okhudza umoyo wathu mwacindunji? Mwacitsanzo, m’zaka zaposacedwapa, mitengo yogulila zomangila kapena kukonza Nyumba za Ufumu yakwela kwambili. Conco, Bungwe Lolamulila linagamula kuti Nyumba za Ufumu ziziseŵenzetsedwa mokwanila. Mwa ici, mipingo ina yaphatikizidwa n’kukhala mpingo umodzi, ndipo Nyumba za Ufumu zina zagulitsidwa. Ndalamazo zimakathandiza kumanga Nyumba za Ufumu kumadela amene n’zosowekela kwambili. Ngati mukhala m’dela limene Nyumba za Ufumu zikugulitsidwa ndipo mipingo ikuphatikizidwa pamodzi, zingakhale zovuta kwa inu kuyamikila makonzedwe atsopano amenewa. Ofalitsa ena lomba amafunika kuyenda mtunda wotalikilapo kuti akasonkhane. Abale na alongo ena amene anagwila nchito molimbika kumanga kapena kukonza Nyumba ya Ufumu, sangamvetse cifukwa cake holoyo akuigulitsa. Angaone monga anangotaya nthawi na mphamvu zawo pacabe. Ngakhale n’telo, iwo amagwilizana na makonzedwe atsopano amenewa, ndipo tiwayamikila kwambili.

16. Kodi kuseŵenzetsa uphungu wa pa Akolose 3:23, 24 kungatithandize bwanji kukhalabe acimwemwe?

16 Koma tidzasungabe cimwemwe cathu ngati tikumbukila kuti amene tikumuseŵenzela ni Yehova, ndipo ni amene akutsogolela gulu lake. (Ŵelengani Akolose 3:23, 24.) Mfumu Davide anapeleka citsanzo cabwino pocita zopeleka zomangila kacisi. Iye anati: “Ndine ndani ine, ndipo anthu anga ndani kuti tithe kupeleka nsembe zaufulu ngati zimenezi? Pakuti ciliconse n’cocokela kwa inu, ndipo tapeleka kwa inu zocokela m’dzanja lanu.” (1 Mbiri 29:14) Tikacita zopeleka, nafenso tikupatsa Yehova zocokelanso kwa iye. Ngakhale n’conco, Yehova amayamikila nthawi yathu, mphamvu zathu, komanso cuma cathu cimene timapeleka pocilikiza nchito imene afuna kuti icitike.—2 Akor. 9:7.

PITILIZANI KUYENDA PANJILA YOPANIKIZA

17. N’cifukwa ciani simuyenela kugwa ulesi mukaona kuti mufunika kuwongolela pa mbali zina?

17 Kuti tipitilizebe kuyenda panjila ya ku moyo, tonse tifunika kutsatila mapazi a Yesu mosamalitsa. (1 Pet. 2:21) Mukaona kuti mufunika kuwongolela pa mbali zina, musagwe ulesi. Cingakhale cizindikilo cabwino, ndipo zingaonetse kuti mumafuna kutsatila malangizo a Yehova. Kumbukilani kuti Yehova sayembekezela kuti anthu opanda ungwilofe tingatsatile citsanzo ca Yesu mwangwilo pali pano ayi.

18. Kodi tiyenela kucita ciani kuti tikafike kumene talinga?

18 Tiyeni tonsefe tiike maganizo athu kutsogolo na kukhalabe wokonzeka kusintha kaganizidwe kathu, kaonedwe kathu ka zinthu, na zocita zathu. (Miy. 4:25; Luka 9:62) Tiyeni tikhalebe odzicepetsa, komanso ‘kupitiliza kukondwela, na kusintha maganizo athu.’ (2 Akor. 13:11) Tikacita zimenezi, “Mulungu wacikondi ndi wamtendele adzakhala [nafe].” Ndipo tidzasangalala na ulendo wathu, mpaka tidzafika kumene talinga.

NYIMBO 34 N’dzayenda mu Umphumphu Wanga

^ ndime 5 Kwa enafe n’covuta kusintha kaganizidwe kathu, kaonedwe kathu ka zinthu, na zocita zathu. M’nkhani ino, tikambilane cifukwa cake tonsefe tifunika kupanga masinthidwe, komanso mmene tingakhalilebe acimwemwe pocita zimenezi.

^ ndime 76 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Pamene m’bale wacinyamata akufotokoza zimene zinam’citikila atapanga cosankha colakwika, m’bale wacikulile (kulamanja) akumvetsela modekha kuti aone ngati afunika kupelekapo uphungu wothandiza.