Nkhani Yophunzira 47

Kodi Ndinu Ofunitsitsa Kupitiriza Kutsatira Malangizo?

Kodi Ndinu Ofunitsitsa Kupitiriza Kutsatira Malangizo?

“Pomalizira abale, ndikuti pitirizani kukondwera, kusintha maganizo anu.”2 AKOR. 13:11.

NYIMBO NA. 54 “Njira Ndi Iyi”

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1. Mogwirizana ndi Mateyu 7:13, 14, n’chifukwa chiyani tinganene kuti tili pa ulendo?

TONSEFE tili pa ulendo. Ulendo wake ndi wopita m’dziko latsopano lolamulidwa ndi Yehova, yemwe ndi wolamulira wachikondi. Tsiku lililonse timayesetsa kuyenda panjira imene ingatitsogolere ku moyo. Koma monga mmene Yesu ananenera, njira ya ku moyoyi ndi yopanikiza ndipo nthawi zina imakhala yovuta kuyendamo. (Werengani Mateyu 7:13, 14.) Popeza si ife angwiro, n’zosavuta kuchoka panjirayi.—Agal. 6:1.

2. Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi? (Onaninso bokosi lakuti “ Kudzichepetsa Kumatithandiza Kuti Tisinthe.”)

2 Kuti tipitirize kuyenda panjira yopanikiza ya ku moyo, tiyenera kukhala ofunitsitsa kusintha mmene timaganizira komanso zochita zathu. Mtumwi Paulo analimbikitsa Akhristu omwe ankakhala ku Korinto kuti apitirize “kusintha maganizo” awo. (2 Akor. 13:11) Malangizo amenewa ndi ofunikanso kwa ife. Munkhaniyi, tikambirana mmene Baibulo lingatithandizire kuti tisinthe komanso mmene Akhristu anzathu achitsanzo chabwino angatithandizire kuti tipitirize kuyenda panjira ya ku moyo. Tikambirananso zimene zingachititse kuti zikhale zovuta kutsatira malangizo amene gulu la Yehova latipatsa. Tionanso mmene kudzichepetsa kungatithandizire kuti tisinthe n’kumapitirizabe kutumikira Yehova mosangalala.

MUZILOLA KUTI MAWU A MULUNGU AZIKUTHANDIZANI KUSINTHA

3. Kodi Mawu a Mulungu angatithandize bwanji?

3 Nthawi zambiri zimativuta kufufuza maganizo athu komanso mmene timamvera. Izi zili choncho chifukwa choti mtima wathu ndi wonyenga ndipo zimenezi zingachititse kuti kukhale kovuta kudziwa zomwe mtimawu ungatilimbikitse kuchita. (Yer. 17:9) N’zosavuta kuti tizidzipusitsa ndi “maganizo onama.” (Yak. 1:22) Choncho, tikamadzifufuza tiyenera kugwiritsa ntchito Mawu a Mulungu. Mawu a Mulunguwa amatithandiza kudziwa mmene tilili chifukwa amatha kuzindikira “zimene munthu akuganiza komanso zolinga za mtima wake.” (Aheb. 4:12, 13) Pamenepa Mawu a Mulungu tingawayerekezere ndi mashini a X-ray, omwe amatithandiza kuona zinthu zamkati zimene sitikanatha kuziona. Koma tiyenera kukhala odzichepetsa kuti titsatire malangizo ochokera m’Baibulo kapena omwe Akhristu anzathu angatipatse.

4. Kodi n’chiyani chikusonyeza kuti Mfumu Sauli anayamba kunyada?

4 Chitsanzo cha Mfumu Sauli chikusonyeza zimene zingachitike ngati si ife odzichepetsa. Sauli anayamba kunyada ndipo anakana kuvomereza kuti ankafunika kusintha maganizo komanso zochita zake. (Sal. 36:1, 2; Hab. 2:4) Zimenezi zinaonekera pamene Yehova anamupatsa malangizo omveka bwino okhudza zomwe ankayenera kuchita atagonjetsa Aamaleki. Koma Sauli sanamvere Yehova. Ndipo pamene mneneri Samueli ankamufunsa za nkhaniyi, Sauli anakana kuvomereza zimene analakwitsa. M’malomwake, iye anayesa kudziikira kumbuyo ponena kuti sinali nkhani yaikulu komanso ananena kuti anthu ena ndi omwe anamukakamiza kuchita zimene anachitazo. (1 Sam. 15:13-24) M’mbuyomu, Sauli anali atachitanso zofanana ndi zimenezi. (1 Sam. 13:10-14) N’zomvetsa chisoni kuti anayamba kukhala ndi mtima wodzikuza. Iye sanasinthe maganizo ake ndipo Yehova anamudzudzula komanso anamukana.

5. Kodi tikuphunzira chiyani pa chitsanzo cha Sauli?

5 Palibe amene angafune kukhala ngati Sauli. Choncho tingachite bwino kudzifunsa mafunso awa: ‘Ndikawerenga malangizo a m’Mawu a Mulungu, kodi ndimadziikira kumbuyo kapena kupeza zifukwa zondichititsa kuti ndisatsatire malangizowo? Kodi ndimaganiza kuti zimene ndikuchita si zoipa kwenikweni? Kodi ndimaimba ena mlandu chifukwa cha zimene ndikuchita?’ Ngati yankho ndi loti inde pa lililonse la mafunsowa, ndiye kuti tiyenera kusintha maganizo athu. Ngati sitingatero, tingayambe kukhala ndi mtima wodzikuza ndipo Yehova angatikane kuti tisakhalenso anzake.—Yak. 4:6.

6. Kodi Mfumu Sauli anali wosiyana bwanji ndi Mfumu Davide?

6 Koma Mfumu Sauli anali wosiyana ndi Mfumu Davide, yemwe ankakonda “chilamulo cha Yehova.” (Sal. 1:1-3) Davide ankadziwa kuti Yehova amapulumutsa anthu odzichepetsa koma amatsutsa odzikweza. (2 Sam. 22:28) Choncho Davide analola kuti malamulo a Yehova amuthandize kusintha maganizo ake. Iye analemba kuti: “Ndidzatamanda Yehova amene wandipatsa malangizo. Ndithudi, usiku impso zanga zandiwongolera.”—Sal. 16:7.

MAWU A MULUNGU

Mawu a Mulungu amatichenjeza tikayamba kuyenda panjira yolakwika. Ngati ndife odzichepetsa timalola kuti Mawu a Mulungu azitithandiza kusintha maganizo athu olakwika (Onani ndime 7)

7. Ngati ndife odzichepetsa, kodi tidzachita chiyani?

7 Ngati ndife odzichepetsa, tidzalola kuti Mawu a Mulungu atithandize kusintha maganizo athu olakwika tisanachite zoipa. Zingakhale ngati tikumva Mawu a Mulungu akutiuza kuti: “Njira ndi iyi. Yendani mmenemu.” Mawu a Mulunguwa angatichenjeze tikayamba kuchoka panjirayi kulowera kudzanja lamanzere kapena lamanja. (Yes. 30:21) Kumvera Yehova kumatithandiza m’njira zambiri. (Yes. 48:17) Mwachitsanzo, kumatithandiza kupewa kuchita zinthu zimene zingapangitse kuti wina atipatse uphungu, zomwe n’zochititsa manyazi. Ndiponso kumatithandiza kukhala pa ubwenzi ndi Yehova chifukwa timadziwa kuti amatisamalira monga mwana wake wokondedwa.—Aheb. 12:7.

8. Mogwirizana ndi Yakobo 1:22-25, kodi tingagwiritse ntchito bwanji Mawu a Mulungu ngati galasi lathu?

8 Mawu a Mulungu angakhale ngati galasi lathu. (Werengani Yakobo 1:22-25.) Ambirife timadziyang’anira pagalasi m’mawa uliwonse tisanachoke panyumba. Zimenezi zimatithandiza kuti tikonze pofunika kukonza anthu ena asanaone. Mofanana ndi zimenezi, tikamawerenga Baibulo tsiku lililonse zidzatithandiza kusintha mmene timaganizira komanso mmene timaonera zinthu. Ambiri amaona kuti n’zothandiza kuwerenga lemba latsiku m’mawa uliwonse asanachoke panyumba. Amalola kuti zimene awerengazo zizikhudza mmene amaganizira. Ndiyeno tsiku lonse, amayesetsa kupeza njira zimene angagwiritsire ntchito malangizo a m’Mawu a Mulungu. Kuwonjezera pamenepo, tsiku lililonse tiyenera kukhala ndi chizolowezi chophunzira, zomwe zikuphatikizapo kuwerenga komanso kuganizira mozama Mawu a Mulungu. Zimenezi zingaoneke ngati zosavuta koma n’zofunika kwambiri kuti tipitirize kuyenda panjira yopanikiza yopita ku moyo.

MUZIMVERA MALANGIZO OCHOKERA KWA ANZANU OLIMBA MWAUZIMU

ANZATHU OLIMBA MWAUZIMU

Mkhristu mnzathu wolimba mwauzimu angathe kutichenjeza mokoma mtima. Kodi timayamikira kuti mnzathuyo analimba mtima n’kutichenjeza? (Onani ndime 9)

9. Kodi ndi pa nthawi iti pamene mnzanu angakupatseni malangizo?

9 Kodi munayamba mwayendapo panjira imene ikanakupangitsani kuti mutalikirane ndi Yehova? (Sal. 73:2, 3) Ngati mnzanu wolimba mwauzimu analimba mtima n’kukupatsani malangizo, kodi munamvera ndi kuwatsatira? Ngati munamvera munachita zinthu zoyenera ndipo sitikukayikira kuti mumayamikira kuti mnzanuyo anakuchenjezani.—Miy. 1:5.

10. Kodi muyenera kutani mnzanu akakupatsani malangizo?

10 Mawu a Mulungu amatikumbutsa kuti: “Zilonda zovulazidwa ndi munthu wokukonda zimakhala zokhulupirika.” (Miy. 27:6) Kodi mawu amenewa akutanthauza chiyani? Taganizirani chitsanzo ichi: Yerekezerani kuti mukufuna kudumpha msewu umene mukudutsa magalimoto ambiri koma maso anu ali pafoni. Ndipo mukulowa mumsewuwo osayang’ana ngati kukubwera galimoto. Nthawi yomweyo mnzanu akukugwirani mkono n’kukukokerani kumbali. Mnzanuyo anakugwirani mwamphamvu moti mkono wanu wavulala koma zimene anachitazo zathandiza kuti musagundidwe ndi galimoto. Ngakhale kuti mungamve ululu kwa masiku angapo, kodi mungakhumudwe kuti mnzanuyo anakukokani? Ayi, simungakhumudwe. Mungayamikire kuti anakuthandizani. Mofanana ndi zimenezi, mnzanu atakuchenjezani kuti zolankhula kapena zochita zanu sizikugwirizana ndi mfundo zolungama za Mulungu, poyamba mungamve ululu. Koma simuyenera kukwiya kapena kukhumudwa chifukwa choti wakupatsani malangizo. Kuchita zimenezo kungakhale kupusa. (Mlal. 7:9) M’malomwake, muyenera kuyamikira kuti mnzanuyo analimba mtima n’kukupatsani malangizowo.

11. Kodi n’chiyani chingachititse munthu kukana malangizo abwino amene mnzake wamupatsa?

11 Kodi n’chiyani chingachititse munthu kukana malangizo abwino amene mnzake wamupatsa? Chimene chingachititse ndi kunyada. Anthu onyada amakonda kumva zinthu “zowakomera m’khutu.” Iwo safuna “kumvetsera choonadi.” (2 Tim. 4:3, 4) Anthuwa amaganiza kuti sakufunikira malangizo chifukwa amadziona kuti ndi anzeru komanso ofunika kuposa ena. Koma mtumwi Paulo analemba kuti: “Ngati wina akudziona kuti ndi wofunika pamene si wotero, akudzinyenga.” (Agal. 6:3) Mfumu Solomo anafotokozanso bwino mfundo imeneyi. Iye analemba kuti: “Mwana wosauka koma wanzeru ali bwino kuposa mfumu yokalamba koma yopusa, imene sionanso kufunika kochenjezedwa.”—Mlal. 4:13.

12. Mogwirizana ndi Agalatiya 2:11-14, kodi tikuphunzira chiyani kwa mtumwi Petulo?

12 Taganizirani zimene mtumwi Petulo anachita mtumwi Paulo atamudzudzula pamaso pa anthu ena. (Werengani Agalatiya 2:11-14.) Petulo akanatha kumukwiyira Paulo chifukwa cha mmene anamulankhulira komanso chifukwa choti panali pagulu. Koma Petulo anachita zinthu mwanzeru ndipo anamvera malangizowo komanso sanamusungire Paulo chakukhosi. M’malomwake, patapita nthawi anamutchula Paulo kuti “m’bale wathu wokondedwa.”—2 Pet. 3:15.

13. Kodi tiyenera kukumbukira mfundo ziti tisanapereke malangizo kwa munthu?

13 Kodi ndi mfundo ziti zimene muyenera kukumbukira ngati mukufuna kupereka malangizo kwa mnzanu? Musanalankhule ndi mnzanuyo, mungadzifunse kuti, ‘Kodi ndikufuna kuchita zinthu ngati munthu “wolungama mopitirira muyezo”?’ (Mlal. 7:16) Munthu wolungama mopitirira muyezo amaweruza ena pogwiritsa ntchito mfundo zake osati za Yehova ndipo sachita zinthu mwachifundo. Mutaiganizira nkhaniyo ndipo mukuonabe kuti mukuyenera kukalankhula ndi mnzanuyo, muyenera kumufotokozera momveka bwino zimene walakwitsa komanso mungagwiritse ntchito mafunso pomuthandiza kumvetsa zimene walakwitsazo. Muzionetsetsa kuti zimene mukunena n’zochokera m’Malemba ndipo muzikumbukira kuti si udindo wanu kumuweruza koma kungomuthandiza kuona mmene Yehova akumvera ndi zochita zakezo. (Aroma 14:10) Muzigwiritsa ntchito nzeru zopezeka m’Mawu a Mulungu ndipo popereka malangizo muzikhala achifundo potsanzira Yesu. (Miy. 3:5; Mat. 12:20) N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa choti zimene timachitira ena Yehova adzatichitiranso zomwezo.—Yak. 2:13.

MUZITSATIRA MALANGIZO AMENE GULU LA MULUNGU LIMAPEREKA

GULU LA MULUNGU

Gulu la Mulungu limatipatsa mabuku, mavidiyo komanso misonkhano zimene zimatithandiza kuti tizitsatira malangizo opezeka m’Mawu a Mulungu. Nthawi zina Bungwe Lolamulira limasintha zinthu zina zokhudza mmene ntchito yathu ikuyendera (Onani ndime 14)

14. Kodi gulu la Mulungu limatipatsa zinthu ziti?

14 Yehova amatitsogolera panjira yopita ku moyo pogwiritsa ntchito mbali yapadziko lapansi ya gulu lake. Gululi limatipatsa mavidiyo, mabuku ndi misonkhano imene imatithandiza kuti tizigwiritsa ntchito malangizo opezeka m’Mawu a Mulungu. Malangizo amenewa ndi odalirika chifukwa amachokera m’Malemba. Abale a m’Bungwe Lolamulira akamasankha njira yabwino yolalikirira, amadalira mzimu woyera. Komabe nthawi ndi nthawi abalewa amakambirananso zimene anasankha kuti aone ngati pakufunika kusintha. N’chifukwa chiyani amachita zimenezi? Chifukwa choti “zochitika za padzikoli zikusintha” ndipo gulu la Mulungu limayenera kusintha zinthu kuti zigwirizane ndi mmene zilili pa nthawiyo.—1 Akor. 7:31.

15. Kodi ofalitsa ena akumana ndi vuto lotani?

15 Mosakayikira gulu la Yehova likatifotokozera kuti pali kusintha pa mfundo zina za m’Baibulo zimene timakhulupirira poyamba kapena malangizo okhudza makhalidwe, timavomereza ndipo timatsatira. Koma kodi timatani gulu la Yehova likasintha zinthu zina zimene zikukhudza moyo wathu? Mwachitsanzo, m’zaka zaposachedwapa mtengo wogulira zipangizo zomangira komanso kukonzera malo olambirira wakwera kwambiri. Choncho Bungwe Lolamulira linapereka malangizo akuti Nyumba za Ufumu zizigwiritsidwa ntchito mokwanira. Zimenezi zapangitsa kuti mipingo ina iphatikizidwe komanso Nyumba za Ufumu zina zigulitsidwe. Ndipo ndalamazo zikugwiritsidwa ntchito pomanga Nyumba za Ufumu kumadera kumene kulibe nyumbazi. Ngati mukukhala kudera kumene Nyumba za Ufumu zikugulitsidwa ndipo mipingo ikuphatikizidwa, mwina zingakuvuteni kuzolowera zimenezi. Mwachitsanzo, tsopano ofalitsa ena angafunike kuyenda mtunda wautali kuti akapezeke kumisonkhano. Enanso amene anagwira nawo ntchito mwakhama pomanga komanso kukonza Nyumba ya Ufumuyo sangamvetse chifukwa chake ikugulitsidwa. Mwina angamaone ngati anangowononga nthawi komanso mphamvu zawo. Komabe, iwo akugwirizana ndi kusintha kumeneku ndipo tiyenera kuwayamikira.

16. Kodi kugwiritsa ntchito malangizo opezeka pa Akolose 3:23, 24, kungatithandize bwanji kuti tikhalebe osangalala?

16 Tidzakhalabe osangalala tikamakumbukira kuti ntchito yomwe tikugwirayi ndi ya Yehova komanso kuti ndi amene akutsogolera gulu lake. (Werengani Akolose 3:23, 24.) Mfumu Davide anapereka chitsanzo chabwino pamene ankapereka ndalama zomangira kachisi. Iye anati: “Ndine ndani ine, ndipo anthu anga ndani kuti tithe kupereka nsembe zaufulu ngati zimenezi? Pakuti chilichonse n’chochokera kwa inu, ndipo tapereka kwa inu zochokera m’dzanja lanu.” (1 Mbiri 29:14) Tikamapereka zopereka ifenso timakhala tikum’patsa Yehova zinthu zimene watipatsa. Komabe iye amayamikira kwambiri tikamagwiritsa ntchito nthawi, mphamvu komanso ndalama zathu pothandizira pa ntchito yake.—2 Akor. 9:7.

PITIRIZANI KUYENDA PANJIRA YOPANIKIZA

17. N’chifukwa chiyani simuyenera kutaya mtima ngati mwaona kuti mukufunika kusintha zinthu zina?

17 Kuti tipitirize kuyenda panjira yopanikiza yopita ku moyo, tonsefe tiyenera kutsatira mapazi a Yesu mosamala kwambiri. (1 Pet. 2:21) Ngati mukuona kuti pali zinthu zina zimene mukufunika kusintha, musataye mtima. Kuzindikira zimenezi ndi umboni woti mukufunitsitsa kutsatira malangizo a Yehova. Musaiwale kuti Yehova akudziwa kuti si ife angwiro. Choncho tikamatsatira chitsanzo cha Yesu, sayembekezera kuti tizichita zinthu mosalakwitsa chilichonse.

18. Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tidzapeze madalitso m’tsogolo?

18 Tiyeni tonse tiziganizira za madalitso amene tidzapeze m’tsogolo ndipo tikhale ofunitsitsa kusintha mmene timaganizira, mmene timaonera zinthu komanso zochita zathu. (Miy. 4:25; Luka 9:62) Tiyeni tipitirize kukhala odzichepetsa, ‘kukondwera ndi kusintha maganizo athu.’ (2 Akor. 13:11) Tikamachita zimenezi, “Mulungu wachikondi ndi wamtendere adzakhala [nafe].” Ndipo adzatithandiza kuti tikhale osangalala panopa komanso adzatipatsa moyo m’dziko latsopano.

NYIMBO NA. 34 Kuyenda ndi Mtima Wosagawanika

^ ndime 5 Ena a ife mwina zingamativute kusintha mmene timaganizira komanso zochita zathu. Munkhaniyi tikambirana chifukwa chake tonsefe tiyenera kusintha komanso zimene tingachite kuti tizisangalalabe pamene tikuyesetsa kusintha.

^ ndime 76 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: M’bale wachinyamata akufotokoza zimene zinamuchitikira atasankha zinthu mosaganiza bwino ndipo m’bale wachikulire akumvetsera modekha kuti aone ngati akufunika kumupatsa malangizo.