Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 50

“Kodi Akufa Adzaukitsidwa Motani?”

“Kodi Akufa Adzaukitsidwa Motani?”

“Imfa iwe, kupambana kwako kuli kuti? Imfawe, mphamvu yako ili kuti?”—1 AKOR. 15:55.

NYIMBO 141 Moyo ni Cozizwitsa

ZIMENE TIKAMBILANE *

1-2. N’cifukwa ciani Akhristu onse ayenela kucita cidwi na kuukitsidwa kwa amene adzapita kumwamba?

ATUMIKI a Yehova ambili ali na ciyembekezo codzakhala na moyo wosatha pano padziko lapansi. Koma Akhristu odzozedwa otsalila amayembekezela kukakhala na moyo kumwamba. Akhristu odzozedwa amenewa amakhala na cidwi cofuna kudziŵa mmene umoyo wawo wa kutsogolo udzakhalile. Nanga bwanji za amene ali na ciyembekezo codzakhala padziko lapansi? Monga mmene tionele, kuuka kopita kumwamba kudzabweletsanso madalitso kwa amene ali na ciyembekezo codzakhala padziko lapansi kwamuyaya. Conco kaya ciyembekezo cathu ni cakumwamba, kapena padziko lapansi tiyenela kucita cidwi na kuukitsidwa kwa amene adzapita kumwamba.

2 Mulungu anauzila ena mwa ophunzila a Yesu a m’nthawi ya Akhristu oyambilila, kulemba za kuuka kopita kumwamba. Mtumwi Yohane anafotokoza kuti: “Tsopano ndife ana a Mulungu, koma padakali pano sizinaonekelebe kuti tidzakhala otani. Tikudziwa kuti akadzaonekela, tidzakhala ngati iyeyo.” (1 Yoh. 3:2) Conco, Akhristu odzozedwa sadziŵa mmene adzakhalile akadzaukitsidwa kukakhala na moyo kumwamba na matupi amzimu. Komabe, iwo adzaona Yehova pamaso-m’pamaso akakalandila mphoto yawo kumwamba. Baibo siifotokoza zonse za ciukililo copita kumwamba. Koma mtumwi Paulo anafotokozapo mfundo zina pa nkhaniyi. Akhristu odzozedwa adzakhala limodzi na Khristu pamene ‘adzathetsa maboma onse, ulamulilo onse, ndi mphamvu zonse,’ kuphatikizapo “imfa . . . mdani womalizila.” Pothela pake, Yesu pamodzi na olamulila anzake adzadzipeleka kukhala pansi pa ulamulilo wa Yehova na kupeleka zinthu zonse kwa iye. (1 Akor. 15:24-28) Imeneyi idzakhala nthawi yokondweletsa ngako! *

3. Malinga na 1 Akorinto 15:30-32, kodi kukhulupilila kuti akufa adzauka kunathandiza Paulo kucita ciani?

3 Kukhulupilila kuti akufa adzauka, kunathandiza Paulo kupilila mayeso ambili. (Ŵelengani 1 Akorinto 15:30-32.) Iye anauza Akhristu a ku Korinto kuti: “Tsiku ndi tsiku ndimakhala pa ngozi yoti ndikhoza kufa.” Paulo anakambanso kuti: “Ndinamenyana ndi zilombo ku Efeso.” Mwina Paulo anatanthauza kumenyana na nyama zenizeni m’bwalo la maseŵela ku Efeso. (2 Akor. 1:8; 4:10; 11:23) Kapena mwina anali kutanthauza Ayuda ankhanza na anthu ena amene anali monga “zilombo.” (Mac. 19:26-34; 1 Akor. 16:9) Kaya Paulo anali kutanthauza ciani, iye anakumana na mavuto aakulu. Ngakhale n’telo, anayang’anabe kutsogolo mwacidalilo.—2 Akor. 4:16-18.

Banja limene likhala m’dziko limene nchito yathu ni yoletsedwa, likupitilizabe kulambila Mulungu, ndipo ali na cikhulupililo conse kuti iye wawasungila zinthu zabwino ngako kutsogolo (Onani ndime 4)

4. Kodi ciyembekezo cakuti akufa adzauka, cimawalimbikitsa motani Akhristu masiku ano? (Onani cithunzi pacikuto.)

4 Tikukhala m’nthawi yovuta kwambili. Ena mwa abale na alongo athu, anacitilidwapo zaupandu. Ena amakhala m’madela mmene mumacitika nkhondo, ndipo miyoyo yawo imakhala paciwopsezo. Enanso amatumikila Yehova m’maiko amene nchito yolalikila ni yoletsedwa, kapena alibe ufulu wokwanila wa kulambila. Komabe, iwo amatumikila Yehova na kum’lambila ngakhale kuti amaika miyoyo yawo na ufulu wawo paciwopsezo. Abale na alongo athu onsewa, ni zitsanzo zabwino kwa ife. Iwo sacita mantha cifukwa adziŵa kuti ngakhale ataye miyoyo yawo pali pano, Yehova wawasungila moyo wabwino ngako kutsogolo.

5. Kodi ni maganizo owopsa ati amene angafooketse cikhulupililo cathu cakuti akufa adzauka?

5 Paulo anacenjeza abale ake za kuwopsa kwa maganizo akuti: “Ngati akufa sadzauka, ‘tiyeni tidye ndi kumwa,’ pakuti mawa tifa.’” Ngakhale Paulo asanakhaleko anthu enanso anali na maganizo amenewa. Mwina iye anagwila mawu Yesaya 22:13, imene ionetsa maganizo amene Aisiraeli anali nawo. M’malo moyandikila kwa Mulungu, iwo anali kufuna kukhala umoyo wodzikondweletsa okha. Maganizo a Aisiraeli amenewo anali akuti, ‘tiyeni tikondwele lelo, pakuti mawa tifa,’ ndipo maganizo amenewa ni ofala ngakhale masiku ano. Komabe, Baibo imatifotokozela mavuto amene mtundu wa Isiraeli unakumana nawo cifukwa cokhala na maganizo amenewa.—2 Mbiri 36:15-20.

6. Kodi ciyembekezo cathu cakuti akufa adzauka ciyenela kukhudza bwanji nkhani yosankha mabwenzi?

6 Timadziŵa kuti Yehova adzaukitsa akufa. Conco tiyenela kukhala osamala na anthu amene timasankha kuti akhale mabwenzi athu. Abale a ku Korinto anafunika kupewa kuceza na anthu amene sanali kukhulupilila kuti akufa adzauka. Pamenepa pali phunzilo kwa ife. Sipangakhale zotulukapo zabwino ngati timaceza na anthu amene zakutsogolo alibe nazo nchito, amene amangokhalila zalelo. Kuceza na anthu otelo kungawononge makhalidwe abwino a Mkhristu woona na kusintha kaonedwe kake ka zinthu. Ndipo anthuwo angam’pangitse kuyamba kucita zinthu zoipa zimene Mulungu sakondwela nazo. N’cifukwa cake mtumwi Paulo anakamba mwamphamvu kuti: “Dzukani ku tulo tanu kuti mukhale olungama ndipo musamacite chimo.”—1 Akor. 15:33, 34.

KODI ADZAUKITSIDWA NA THUPI LOTANI?

7. Malinga na 1 Akorinto 15:35-38, kodi ni funso liti limene mwina ena anali nalo pankhani ya kuuka kwa akufa?

7 Ŵelengani 1 Akorinto 15:35-38. Munthu amene anali kufuna kupangitsa ena kukayikila zakuti akufa adzauka, mwina anali kufunsa kuti: “Kodi akufa adzaukitsidwa motani?” Tingacite bwino kuganizila yankho ya Paulo cifukwa cakuti anthu ambili masiku ano ali na maganizo osiyana-siyana pankhani ya zimene zimacitika munthu akamwalila. Koma kodi Baibo imaphunzitsa ciani?

Mwakuseŵenzetsa fanizo la mbewu na comela, Paulo anaonetsa kuti Mulungu angapeleke thupi loyenelela kwa amene adzaukitsidwa (Onani ndime 8)

8. Kodi ni fanizo liti limene lingatithandize kumvetsa za ciukililo copita kumwamba?

8 Munthu akamwalila thupi lake limawola. Koma amene analenga cilengedwe angaukitse munthuyo na kum’patsa thupi loyenelela. (Gen. 1:1; 2:7) Paulo anaseŵenzetsa fanizo loonetsa kuti Mulungu sadzaukitsa munthu na thupi limene anali nalo asanamwalile. Ganizilani za “mbewu.” Mbewu ikabyalidwa m’nthaka, imamela kenako n’kukhala comela catsopano. Comelaco cimakhala cosiyana na kambewu. Paulo anaseŵenzetsa fanizo limeneli poonetsa kuti Mlengi wathu angapeleke ‘thupi monga mwakufuna kwake.’

9. Kodi 1 Akorinto 15:39-41 imakamba za kusiyana kotani pakati pa matupi?

9 Ŵelengani 1 Akorinto 15:39-41. Paulo anafotokoza kuti Mulungu analenga zinthu za m’cilengedwe mosiyana-siyana. Mwacitsanzo, pali matupi osiyana-siyana monga a ng’ombe, mbalame, komanso nsomba. Iye anakamba kuti kumwamba timaona kusiyana pakati pa dzuŵa na mwezi. Ndipo anakamba kuti “ulemelelo wa nyenyezi ina, umasiyana ndi ulemelelo wa inzake.” Inde, ngakhale kuti sitingazione na maso athu, asayansi amakamba kuti pali nyenyezi zikulu-zikulu zofiila, zing’ono-zing’ono zoyela, komanso zacikasu monga dzuŵa. Paulo anakambanso kuti, “palinso matupi akumwamba, ndi matupi apadziko lapansi.” Motani? Padzikoli pali matupi anyama, koma kumwamba kuli matupi amzimu, monga amene angelo ali nawo.

10. Kodi oukitsidwa kukakhala kumwamba adzakhala na matupi otani?

10 Onani mfundo yotsatila imene Paulo anakamba: “Ndi mmenenso zilili ndi kuuka kwa akufa.Thupi limafesedwa lili lokhoza kuwonongeka, limaukitsidwa losakhoza kuwonongeka.” Tidziŵa kuti munthu akamwalila, thupi lake limawola, ndipo amabwelela ku fumbi. (Gen. 3:19) Ndiyeno kodi zingatheke bwanji kuti thupilo, ‘liukitsidwe losakhoza kuwonongeka?’ Paulo sanali kukamba za anthu oukitsidwa kukhala na moyo padziko lapansi, monga amene anaukitsidwa na Eliya, Elisa, komanso Yesu. Paulo anali kukamba za munthu woukitsidwa na thupi la kumwamba, kutanthauza kuti “thupi lauzimu.”—1 Akor. 15:42-44.

11-12. Kodi n’ciani cinasintha, Yesu ataukitsidwa? Nanga cimasinthanso n’ciani kwa Akhristu odzozedwa?

11 Pamene Yesu anali padziko lapansi, anali na thupi lanyama. Koma ataukitsidwa “anakhala mzimu wopatsa moyo,” ndipo anabwelela kumwamba. Mofananamo, Akhristu odzozedwa amaukitsidwa na moyo wamzimu. Paulo anafotokoza kuti: “Monga tilili m’cifanizilo ca wopangidwa ndi fumbi uja, tidzakhalanso m’cifanizilo ca wakumwambayo.”—1 Akor. 15:45-49.

12 Tsopano Paulo anayamba kufotokoza mfundo zikulu-zikulu pa nkhani ya kuuka kwa akufa. Mfundo yofunika kudziŵa ni yakuti Yesu sanaukitsidwe na thupi lanyama. Paulo anakamba momveka bwino kuti: “Mnofu ndi magazi sizingalowe ufumu wa Mulungu” wakumwamba. (1 Akor. 15:50) Atumwi komanso Akhristu anzawo odzozedwasadzaukitsidwa kupita kumwamba na matupi okhoza kuwonongeka a mnofu ndi magazi. Kodi adzaukitsidwa liti? Paulo anagogomeza kuti kuuka kumeneku kunali kudzacitika kutsogolo. Izi zinaonetsa kuti Akhristu odzozedwa panthawiyo sanali kuukitsidwa akangomwalila. Panthawi imene Paulo analemba 1 Akorinto, ena mwa ophunzila anali ‘atagona kale mu imfa,’ mwacitsanzo, mtumwi Yakobo. (Mac. 12:1, 2) Atumwi ena na odzozedwa anali ‘kudzagona mu imfa.’—1 Akor. 15:6.

KUGONJETSA IMFA

13. Kodi cizindikilo ca “kukhalapo” kwa Yesu cinali kudzakhala ciani?

13 Yesu na Paulo onse anakamba za nthawi yapadela m’mbili ya anthu ya kukhalapo kwa Khristu. Cizindikilo ca kukhalapo kumeneko cinali kudzakhala nkhondo, zivomezi, milili, na mavuto ena okhudza dziko lonse. Taona kukwanilitsidwa kwa ulosi wa m’Baibo umenewu kuyambila mu 1914. Palinso mbali ina yofunika kwambili ya cizindikilo cimeneci. Yesu anakamba kuti uthenga wabwino wokamba za Ufumu wa Mulungu kuti ukulamulila, udzalalikidwa “padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni ku mitundu yonse, kenako mapeto adzafika.” (Mat. 24:3, 7-14) Paulo anakamba kuti “nthawi ya kukhalapo kwa Ambuye,” idzakhalanso nthawi ya kuukitsidwa kwa Akhristu odzozedwa amene ‘anagona mu imfa.’—1 Ates. 4:14-16; 1 Akor. 15:23.

14. Kodi cimacitika n’ciani kwa odzozedwa amene amamwalila m’nthawi ya kukhalapo kwa Khristu?

14 Akhristu odzozedwa akangotsiliza moyo wawo wa padziko lapansi masiku ano, nthawi yomweyo amaukitsidwa kukakhala na moyo kumwamba. Mawu a Paulo apa 1 Akorinto 15:51, 52 amatsimikizila zimenezi. Iye anati: “Si tonse amene tidzagona mu imfa, koma tonse tidzasandulika, m’kamphindi, m’kuphethila kwa diso, pa kulila kwa lipenga lomaliza.” Mawu a Paulo amenewa akukwanilitsidwa masiku ano. Abale a Khristu amenewa akangoukitsidwa, amakhala na cimwemwe cacikulu. Iwo ‘azikakhala na Ambuye nthawi zonse.’—1 Ates. 4:17.

Amene adzasandulika “m’kuphethila kwa diso” adzamenya nkhondo limodzi ndi Yesu kucotsapo zoipa zonse padzikoli (Onani ndime 15)

15. Kodi amene adzasandulika “m’kuphethila kwa diso” adzagwila nchito yanji?

15 Baibo imatiuza nchito imene adzagwila kumwamba, awo amene adzasandulika “m’kuphethila kwa diso.” Ponena za iwo Yesu akuti: “Amene wapambana pa nkhondo ndi kutsatila zocita zanga kufikila mapeto, ndidzamupatsa ulamulilo pa mitundu ya anthu. Iyeyo adzakusa anthu ndi ndodo yacitsulo, ngati imenenso ine ndailandila kwa Atate wanga. Anthuwo adzaphwanyidwaphwanyidwa ngati mbiya zadothi.”(Chiv. 2:26, 27) Iwo adzatsatila Yesu poweta mtundu wa anthu monga abusa ndi ndodo yacitsulo.—Chiv. 19:11-15.

16. Kodi anthu ambili adzaigonjetsa motani imfa?

16 Mwacionekele, odzozedwa adzagonjetsa imfa. (1 Akor. 15:54-57) Kuukitsidwa kwawo kudzawapatsa mwayi wotengako mbali pa kugonjetsa kuipa konse kwa padziko lapansi, panthawi ya nkhondo imene ikubwela ya Aramagedo. Akhristu ena mamiliyoni ambili ‘adzatuluka m’cisautso cacikulu’ ndipo adzapulumuka na kuloŵa m’dziko latsopano. (Chiv. 7:14) Oukitsidwawo adzakhala mboni zoona ndi maso, kugonjetsedwa kwina kwa imfa. Inde, kuukitsidwa kwa anthu mabiliyoni amene anafa. Ganizilani za cimwemwe cimene tidzakhala naco zimenezi zikadzacitika! (Mac. 24:15) Ndipo onse amene amatumikila Yehova mokhulupilika na mtima onse, adzagonjetsa imfa yobadwa nayo. Iwo adzakhala na moyo kwamuyaya.

17. Tili na 1 Akorinto 15:58 m’maganizo, kodi tiyenela kucita ciani pali pano?

17 Mkhristu aliyense, ayenela kukhala woyamikila pa mawu olimbikitsa amene Paulo analembela Akhristu a ku Korinto ponena za kuuka kwa akufa. Tili na zifukwa zambili zomvela malangizo a Paulo otilimbikitsa kukhala otangwanika kwambili “mu nchito ya Ambuye.” (Ŵelengani 1 Akorinto 15:58.) Ngati timayesetsa kugwila nchito imeneyi, tingayembekezele kudzasangalala na madalitso a kutsogolo. Tsogolo limenelo lidzakhala labwino kwambili kuposa cina ciliconse cimene tingaganizile. Mmene moyo udzakhalile kutsogolo udzakhala umboni wakuti zonse zimene tinacita m’nchito ya Ambuye, sizinapite pacabe.

NYIMBO 140 Moyo Wosatha Watheka!

^ ndime 5 Mbali yaciŵili ya 1 Akorinto caputa 15, imafotokoza za kuuka kwa akufa, maka-maka kuuka kwa Akhristu odzozedwa. Komabe, zimene mtumwi Paulo analemba zimakhudzanso a nkhosa zina. Nkhani ino itionetsa mmene ciyembekezo cathu cakuti akufa adzauka ciyenela kukhudzila umoyo wathu pali pano, na kutithandiza kuyembekezela za kutsogolo mwacidwi.

^ ndime 2 Mbali ya “Mafunso Ocokela kwa Oŵelenga” m’magazini ino, ifotokoza zimene mtumwi Paulo anakamba pa 1 Akorinto 15:29.