Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 51

Yehova Amapulumutsa Anthu Olefuka Mtima

Yehova Amapulumutsa Anthu Olefuka Mtima

“Yehova ali pafupi ndi anthu a mtima wosweka. Ndipo odzimvela cisoni mumtima mwawo amawapulumutsa.”—SAL. 34:18.

NYIMBO 30 Tate Wanga, Mulungu Wanga, Bwenzi Langa

ZIMENE TIKAMBILANE *

1-2. Tikambilane ciani m’nkhani ino?

NTHAWI zina, timaganizila za mfundo yosatsutsika yakuti moyo ni waufupi, komanso ni “wodzaza ndi masautso.” (Yobu 14:1) Conco, m’pomveka kuti nthawi zina timalefuka. Atumiki a Yehova ambili m’nthawi zakale anamvelapo cimodzi-modzi. Ena anali kufuna kuti afe cabe. (1 Maf. 19:2-4; Yobu 3:1-3, 11; 7:15, 16) Koma mobweleza-bweleza, Yehova, Mulungu amene iwo anali kum’dalila anali kuwatonthoza na kuwalimbikitsa. Zocitika za mu umoyo wawo zinalembedwa kuti zititonthoze na kutiphunzitsa.—Aroma 15:4.

2 M’nkhani ino, tikambilane zitsanzo za ena mwa atumiki a Yehova amene anapilila mavuto olefula. Tikambilane za Yosefe mwana wa Yakobo, mkazi wamasiye Naomi na mpongozi wake Rute, Mlevi wina wake amene analemba Salimo 73, komanso mtumwi Petulo. Kodi Yehova anawalimbikitsa bwanji? Nanga aliyense wa ife angaphunzilepo ciani pa zitsanzo zawo? Mayankho pa mafunso amenewa adzatitsimikizila kuti “Yehova ali pafupi ndi anthu a mtima wosweka. Ndipo odzimvela cisoni mumtima mwawo amawapulumutsa.”—Sal. 34:18.

YOSEFE ANAPILILA ZINTHU ZOPANDA CILUNGAMO

3-4. Kodi n’zotani zinacitikila Yosefe ali wacicepele?

3 Yosefe anali na zaka pafupifupi 17 pamene analota maloto aŵili ocokela kwa Mulungu. Maloto amenewa anaonetsa kuti Yosefe tsiku lina adzakhala munthu wolemekezeka m’banja lawo. (Gen. 37:5-10) Koma posapita nthawi Yosefe atalota malotowo, zinthu zinasintha mwadzidzidzi mu umoyo wake. M’malo momulemekeza, abale ake anam’gulitsa monga kapolo. Iye anakakhala kapolo m’nyumba ya nduna ya ku Iguputo dzina lake Potifara. (Gen. 37:21-28) Ndipo m’kanthawi kocepa, Yosefe anacoka pakukhala mwana wokondedwa wa atate ake, n’kukakhala kapolo wamba wa nduna yacikunja ya ku Iguputo.—Gen. 39:1.

4 Tsopano zinthu zinafika povuta kwambili mu umoyo wa Yosefe. Mkazi wa Potifara ananamizila Yosefe kuti anali kufuna kum’gwilila. Ndipo popanda kufufuza nkhani yonseyo, Potifara anaponya Yosefe m’ndende na kum’manga m’maunyolo. (Gen. 39:14-20; Sal. 105:17, 18) Ganizilani cabe mmene wacicepele Yosefe anamvelela atam’namizila kuti anali kufuna kugwilila mkazi wa Potifara. Ndipo ganizilani za citonzo cimene cinabwela pa dzina la Yehova kamba ka cinenezo cimeneco. Conco m’pomveka kuti Yosefe analefuka mtima.

5. Kodi Yosefe anapilila bwanji zolefula?

5 Pamene Yosefe anali kapolo komanso mkaidi, analibe ufulu woyenda ndipo palibe zimene akanacita pa vuto lake. Kodi n’ciani cinam’thandiza kuti asataye mtima? M’malo mosumika maganizo ake pa zimene sakanatha kucita, iye anagwila molimbika nchito imene anapatsidwa. Koposa zonse, Yosefe anali kuonabe kuti Yehova ndiye anali wofunika kwambili mu umoyo wake. Ndipo cotulukapo cake n’cakuti Yehova anadalitsa zonse zimene Yosefe anacita.—Gen. 39:21-23.

6. Kodi Yosefe ayenela kuti anatonthozedwa motani na maloto ake?

6 Yosefe ayenela kuti analimbikitsidwanso mwa kuganizila maloto aulosi amene analota poyamba. Malotowo anaonetsa kuti iye adzaonananso na banja lake, ndipo zinthu zidzakhala bwino. Izi n’zimene zinacitikadi. Ndipo pamene Yosefe anali na zaka pafupi-fupi 37, maloto ake aulosi anayamba kukwanilitsidwa mocititsa cidwi kwambili.—Gen. 37:7, 9, 10; 42:6, 9.

7. Malinga na 1 Petulo. 5:10, n’ciani cingatithandize kupilila mayeselo?

7 Zimene tiphunzilapo. Nkhaniyi itikumbutsa kuti dzikoli n’lankhanza, ndipo anthu adzaticitila zinthu zopanda cilungamo. Ngakhale Mkhristu mnzathu angatikhumudwitse. Koma ngati timaona Yehova monga Thanthwe lathu, kapena malo athu othawilapo, sitidzataya mtima kapena kuleka kum’tumikila. (Sal. 62:6, 7; ŵelengani 1 Petulo. 5:10.) Kumbukilaninso kuti Yosefe ayenela kuti anali na zaka pafupifupi 17 pamene Yehova anam’pangitsa kulota maloto. N’zacidziŵikile kuti Yehova amadalilanso atumiki ake acicepele. Masiku ano acicepele ambili ali monga Yosefe. Nawonso ali na cikhulupililo mwa Yehova. Ena mwa iwo amaikidwa m’ndende mopanda cilungamo, cifukwa cofuna kukhalabe okhulupilika kwa Mulungu.—Sal. 110:3.

AZIMAYI AŴILI AMENE ANALI ACISONI KWAMBILI

8. Kodi n’ciani cinacitikila Naomi na Rute?

8 Cifukwa ca njala yaikulu, Naomi na banja lake anacoka kwawo ku Yuda kupita kukakhala ku Moabu ku dziko lacilendo. Kumeneko, mwamuna wa Naomi, Elimeleki, anamwalila na kumusiya na ana aamuna aŵili. Patapita nthawi, anawo anakwatila akazi acimoabu, Rute na Olipa. Pambuyo pa zaka 10, ana a Naomi amenewo anamwalila, ndipo anafa opanda ana. (Rute 1:1-5) Ganizilani za cisoni cacikulu cimene azimayi atatuwo anali naco. Rute na Olipa akanakwatiwanso. Koma kodi ndani akanasamalila Naomi wokalamba? Naomi anapsinjika kwambili maganizo cakuti panthawi ina anati: “Musandichulenso kuti Naomi, muzindichula kuti Mara, cifukwa Wamphamvuyonse wacititsa moyo wanga kukhala wowawa kwambili.” Pambuyo pa mavuto onsewa, Naomi anaganiza zobwelela ku Betelehemu, ndipo Rute anam’tsatila.—Rute 1:7, 18-20.

Mulungu anaonetsa Naomi na Rute kuti angathandize atumiki ake kugonjetsa zolefula na kuthetsa cisoni. Kodi angacitenso zimenezi kwa inu? (Onani ndime 8-13) *

9. Malinga na Rute 1:16, 17, 22, kodi Rute anam’limbikitsa bwanji Naomi?

9 Cimene cinathandiza Naomi kupilila mavutowo cinali cikondi cokhulupilika. Mwacitsanzo, Rute anaonetsa cikondi cokhulupilika kwa Naomi mwa kukhalabe naye. (Ŵelengani Rute 1:16, 17, 22.) Ku Betelehemu, Rute anali kugwila nchito yokunkha balele wake, komanso wa Naomi. Ndipo cotulukapo cake n’cakuti Rute anakhala na mbili yabwino.—Rute 3:11; 4:15.

10. Kodi Yehova anaonetsa bwanji cifundo kwa anthu ovutika monga Naomi na Rute?

10 Yehova anapatsa Aisiraeli lamulo loonetsa cifundo kwa ovutika, monga Naomi na Rute. Iye anauza anthu ake kuti pokolola, azisiya zokolola m’mbali mwa munda kuti osauka azikunkha. (Lev. 19:9, 10) Conco Naomi na Rute, sanafunike kucita kupempha cakudya. Iwo anali kupeza cakudya m’njila yolemekezeka.

11-12. Kodi Boazi anabweletsa bwanji cimwemwe kwa Naomi na Rute?

11 Mwinimunda umene Rute anali kukunkhamo balele, anali mwamuna wolemela dzina lake Boazi. Rute anali wokhulupilika kwa Naomi, komanso anali kum’konda kwambili. Izi zinam’khudza mtima Boazi cakuti anawombola colowa ca banja lawo na kutenga Rute kukhala mkazi wake. (Rute 4:9-13) Iwo anakhala na mwana dzina lake Obedi, amene anakhala ambuye ake a Mfumu Davide.—Rute 4:17.

12 Ganizilani cabe cimwemwe cimene Naomi anali naco atanyamula Obedi wakhanda m’manja mwake, uku akupeleka pemphelo loyamikila Yehova. Koma kwa Naomi na Rute, nkhani yabwino koposa ili kutsogolo. Iwo akadzaukitsidwa, adzadziŵa kuti Obedi anali mu mzele wobadwila Mesiya wolonjezedwayo, Yesu Khristu.

13. Kodi ni maphunzilo ofunika ati amene tingatengepo pa nkhani ya Naomi na Rute?

13 Zimene tiphunzilapo. Pamene tikumana na mavuto, tingalefuke ngakhale kutaya mtima. Ndipo mwina tingathedwe nzelu na mavutowo. Panthawi ngati zimenezi, tiyenela kudalila kwambili Atate wathu wakumwamba, na kukhalabe paubale wolimba na Akhristu anzathu. Koma mwina Yehova sangaticotsele vutolo, cifukwa ngakhale Naomi sanamuukitsile mwamuna wake na ana ake kwa akufa. Koma adzatithandiza kupilila, mwina mwa kulimbikitsa abale na alongo athu kuticitila zinthu zoonetsa cikondi cokhulupilika.—Miy. 17:17.

MLEVI WINAWAKE AMENE ANATSALA PANG’ONO KUPUNTHWA

Wolemba Salimo 73 anatsala pang’ono kupunthwa cifukwa coona kuti anthu osatumikila Yehova anali kuoneka kuti zinthu zikuwayendela bwino. Zimenezo zingacitikenso kwa ife (Onani ndime 14-16)

14. N’cifukwa ciani Mlevi winawake analefuka kwambili?

14 Amene analemba Salimo 73 anali Mlevi. Conco iye anali na mwayi wapadela wotumikila pamalo a Yehova olambilila. Ngakhale n’conco, iye analefuka panthawi ina mu umoyo wake. Cifukwa ciani? Anayamba kucitila kaduka anthu oipa, komanso odzikuza, osati cifukwa ca zoipa zimene anali kucita, koma cifukwa cakuti anali kuoneka kuti zinthu zikuwayendela bwino. (Sal. 73:2-9, 11-14) Iwo anali kuoneka kuti ali na zonse, cuma, umoyo wabwino, komanso wopanda nkhawa. Zimenezi zinalefula wamasalimo ameneyu cakuti anati: “Ndithudi, ndayeletsa mtima wanga pacabe, Ndipo ndasamba m’manja mwanga pacabe posonyeza kuti ndine wopanda colakwa.” N’zoonekelatu kuti iye anali pangozi yaikulu yauzimu.

15. Malinga na Salimo 73:16-19, 22-25, kodi Mlevi amene analemba Salimoyi anagonjetsa bwanji zolefula?

15 Ŵelengani Salimo 73:16-19, 22-25. Mleviyo ‘analowa m’malo opatulika a Mulungu.’ Mmenemo, mwina ali pakati pa alambili anzake, anatha kupenda bwino-bwino mkhalidwe wake, modekha, moganiza bwino, komanso mwapemphelo. Izi zinam’thandiza kuona kuti anayamba kuganiza mopusa. Ndipo anali atayamba kuyenda panjila yowopsa imene ikanam’patutsa kwa Yehova. Iye anazindikilanso kuti anthu oipa ali “pamalo otelela” ndipo mapeto awo adzakhala owopsa. Kuti athetse kaduka na kuleka kudzimva wolefuka, Mlevi wamasalimo ameneyu, anayenela kuona zinthu mmene Yehova amazionela. Mwakucita zimenezi, anakhala pamtendele ndipo anakhalanso wacimwemwe. Iye anati: “Palibe wina wondisangalatsa padziko lapansi koma inu nokha [Yehova].”

16. Kodi tiphunzilapo ciani pa citsanzo ca Mlevi?

16 Zimene tiphunzilapo. Tisamacitile kaduka anthu oipa amene angaoneke kuti zinthu zikuwayendela mu umoyo. Cimwemwe cawo si ceni-ceni, ndipo n’cakanthawi. Iwo sadzakhalapo kwamuyaya. (Mlal. 8:12, 13) Kuwacitila kaduka kungatilefule, ndipo kungativulaze mwauzimu. Conco, ngati mwazindikila kuti mwayamba kucitila kaduka anthu oipa amene akuoneka kuti zinthu zikuwayendela, citani zimene Mlevi uja anacita. Mvelani malangizo a Mulungu acikondi na kugwilizana na anthu amene amacita cifunilo ca Mulungu. Ngati mumam’konda kwambili Yehova kuposa cina ciliconse, mudzapeza cimwemwe ceni-ceni. Ndipo mudzakhalabe panjila ya ku “moyo weniweniwo.”—1 Tim. 6:19.

ZOFOOKA ZAKE PETULO ZINAM’LEFULA

Tingathandizidwe kapena tingathandize ena mwa kuganizila mmene Petulo anapitilizila kutumikila Mulungu pambuyo polefuka (Onani ndime 17-19)

17. Kodi ni zifukwa ziti zikanapangitsa Petulo kulefuka?

17 Mtumwi Petulo anali munthu wokangalika. Koma nthawi zina anali kucita zinthu mopupuluma, ndipo sanali kudekha pofotokoza maganizo ake. Cifukwa ca zimenezi, iye nthawi zina anakamba kapena kucita zinthu zimene anadziimba nazo mlandu pambuyo pake. Yesu atauza atumwi ake kuti adzavutika na kufa, Petulo anadzudzula Yesu kuti: “Dzikomeleni mtima Ambuye. Musalole kuti zimenezi zikucitikileni ngakhale pang’ono.” (Mat. 16:21-23) Yesu anam’patsa uphungu Petulo. Cigulu ca anthu citabwela kudzagwila Yesu, Petulo anacita zinthu mopupuluma, anadula khutu la kapolo wa mkulu wansembe. (Yoh. 18:10, 11) Apanso Yesu anam’patsa uphungu mtumwiyo. Kuwonjezela apo, Petulo modzikuza anakamba kuti ngakhale atumwi ena onse atamusiya Yesu, iye sangacite zimenezo ngakhale pang’ono. (Mat. 26:33) Koma kudzidalila kwambili kumeneko kunapangitsa kuti Petulo akane Mbuye wake katatu cifukwa cowopa anthu. Ali wolefuka kwambili maganizo, Petulo “anatuluka panja n’kuyamba kulila mopwetekedwa mtima kwambili.” (Mat. 26:69-75) Iye ayenela kuti anakaikila ngati Yesu adzam’khululukila.

18. Kodi Yesu anam’thandiza bwanji Petulo kugonjetsa zolefula?

18 Komabe, Petulo sanalole kuti zinthu zofooketsa zimulefule. Iye atapunthwa anapitilizabe kutumikila Yehova pamodzi na atumwi ena. (Yoh. 21:1-3; Mac. 1:15, 16) Kodi cinam’thandiza n’ciani? Anakumbukila kuti Yesu anali atam’pemphelela kuti cikhulupililo cake cisazime. Ndipo Yesu analimbikitsa Petulo kubwelela kwa abale ake kukawalimbikitsa. Yehova anayankha pemphelo locokela pansi pamtima limeneli. Patapita nthawi Yesu anaonekela kwa Petulo, ndipo mosakaika konse anam’limbikitsa. (Luka 22:32; 24:33, 34; 1 Akor. 15:5) Atumwi atacezela usiku wonse osagwilako nsomba, Yesu anaonekela kwa iwo. Panthawiyi Yesu anapatsanso Petulo mwayi wotsimikizila kuti amam’kondadi. Yesu anakhululukila mnzake wokondeka ameneyu na kum’patsa zocita zambili.—Yoh. 21:15-17.

19. Kodi Salimo 103:13, 14 itithandiza bwanji kuona zolakwa zathu mmene Yehova amazionela?

19 Zimene tiphunzilapo. Mmene Yesu anacitila zinthu na Petulo zimaonetsa cifundo ca Yesu, ndipo Yesu amaonetsa bwino makhalidwe a Atate ake. Conco ngati talakwitsa zinthu tisamadziweluze kuti Yehova sangatikhululukile. Tisaiwale kuti Satana amafuna kuti tiziganiza mwa njila imeneyi. M’malomwake, tiziyesetsa kudziona mmene Atate wathu wacifundo komanso wacikondi amationela. Ndipo tizionanso anthu amene amatilakwila mmene iye amawaonela.—Ŵelengani Salimo 103:13, 14.

20. Kodi tidzakambilana ciani m’nkhani yotsatila?

20 Zitsanzo za Yosefe, Naomi na Rute, Mlevi, komanso Petulo zititsimikizila kuti “Yehova ali pafupi ndi anthu a mtima wosweka.” (Sal. 34:18) Iye amalola kuti tikumane na mayeso komanso kuti tilefuke nthawi zina. Ngakhale n’telo, tikapilila mayeselo na thandizo la Yehova, cikhulupililo cathu cimalimba. (1 Pet. 1:6, 7) M’nkhani yotsatila, tidzaonanso mmene Yehova amacilikizila atumiki ake okhulupilika amene ni olefuka, mwina cifukwa ca zophophonya zawo kapena cifukwa ca mikhalidwe yovuta.

NYIMBO 7 Yehova Ndiye Mphamvu Zathu

^ ndime 5 Yosefe, Naomi na Rute, Mlevi wina wake, komanso mtumwi Petulo anakumana na mavuto olefula. M’nkhani ino, tiona mmene Yehova anawatonthozela na kuwalimbikitsa. Tionenso zimene tingaphunzilepo pa zitsanzo zawo, komanso mmene Mulungu anacitila nawo zinthu mwacifundo.

^ ndime 56 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Naomi, Rute na Olipa anali na cisoni komanso analefuka cifukwa ca imfa ya amuna awo. Pambuyo pake Rute na Naomi anasangalala pamodzi na Boazi, Obedi atabadwa.