Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 51

Yehova Amapulumutsa Anthu a Mtima Wosweka

Yehova Amapulumutsa Anthu a Mtima Wosweka

“Yehova ali pafupi ndi anthu a mtima wosweka. Ndipo odzimvera chisoni mumtima mwawo amawapulumutsa.”​SAL. 34:18.

NYIMBO NA. 30 Atate Wanga, Mulungu Wanga Ndiponso Bwenzi Langa

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1-2. Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?

MOYO wathu ndi waufupi komanso “wodzadza ndi masautso.” (Yobu 14:1) Zimenezi nthawi zina zimachititsa kuti tikhale osweka mtima. Atumiki ena a Yehova m’mbuyomu zimenezi zinawachitikirapo, moti ena anafika poona kuti bola angofa. (1 Maf. 19:2-4; Yobu 3:1-3, 11; 7:15, 16) Koma nthawi zonse Yehova amene ankamukhulupirira ankawalimbikitsa komanso kuwapatsa mphamvu. Nkhani za anthu amenewa zinalembedwa kuti zizitilimbikitsa komanso kutilangiza.​—Aroma 15:4.

2 Munkhaniyi, tikambirana za atumiki ena a Yehova omwe anapirira mayesero osiyanasiyana. Anthu ake ndi Yosefe yemwe anali mwana wa Yakobo, Naomi yemwe anali mkazi wamasiye ndi mpongozi wake Rute, Mlevi yemwe analemba buku la Salimo 73 komanso mtumwi Petulo. Kodi Yehova analimbikitsa bwanji atumiki ake amenewa? Nanga tingaphunzirepo chiyani pa zimene zinawachitikira? Mayankho a mafunso amenewa amatitsimikizira kuti “Yehova ali pafupi ndi anthu a mtima wosweka ndipo odzimvera chisoni mumtima mwawo amawapulumutsa.”​—Sal. 34:18.

YOSEFE ANAPIRIRA ZINTHU ZANKHANZA KOMANSO ZOPANDA CHILUNGAMO

3-4. Kodi Yosefe ali wachinyamata anakumana ndi zotani?

3 Yosefe anali ndi zaka 17 pamene analota maloto awiri ochokera kwa Mulungu. Malotowo anasonyeza kuti tsiku lina Yosefe adzakhala ndi udindo waukulu ndipo anthu a m’banja lake adzamulemekeza. (Gen. 37:5-10) Koma pasanapite nthawi kuchokera pamene analota malotowa, zinthu zinasintha mwadzidzidzi pa moyo wake. M’malo momulemekeza, abale ake anamugulitsa ndipo anakhala kapolo wa Potifara, yemwe anali nduna ya panyumba ya Farao. (Gen. 37:21-28) M’kanthawi kochepa moyo wa Yosefe unasintha kwambiri, kuchoka pa mwana wokondedwa ndi bambo ake n’kukhala kapolo wa Mwiguputo yemwe sankalambira Yehova.​—Gen. 39:1.

4 Koma zinthu zinafika poipa kwambiri pa moyo wa Yosefe. Mkazi wa Potifara ananamizira Yosefe kuti ankafuna kumugwiririra. Potifara sanafufuze kuti adziwe zoona, m’malomwake anangolamula kuti Yosefe amangidwe unyolo ndipo amuike m’ndende. (Gen. 39:14-20; Sal. 105:17, 18) Tangoganizani mmene Yosefe anamvera pamene anamunamizira mlandu wogwiririra. Taganiziraninso mmene zimenezi zikananyozetsera dzina la Yehova. Kunena zoona, izi zinachititsa kuti Yosefe akhale wosweka mtima.

5. Kodi n’chiyani chinathandiza Yosefe kuti aziona zinthu moyenera?

5 Pamene Yosefe anali kapolo komanso pamene anali m’ndende, sakanatha kuchita chilichonse kuti asinthe mmene zinthu zinalili pa moyo wake. Ndiye kodi n’chiyani chimene chinamuthandiza kuti aziona zinthu moyenera? M’malo momangoganizira zinthu zimene sakanatha kuchita, ankadzipereka kwambiri kugwira ntchito iliyonse imene wapatsidwa. Komanso chofunika kwambiri n’chakuti Yosefe nthawi zonse ankaona kuti Yehova ndi wofunika kwambiri pa moyo wake. Chifukwa cha zimenezi, Yehova anadalitsa chilichonse chimene Yosefe ankachita.​—Gen. 39:21-23.

6. Kodi Yosefe ankalimbikitsidwa bwanji akaganizira maloto ake?

6 Yosefe ayeneranso kuti ankalimbikitsidwa akaganizira maloto amene analota aja. Malotowo ankasonyeza kuti zinthu pa moyo wake zidzasintha ndipo adzaonananso ndi achibale ake. Ndipo zimenezi ndi zomwe zinachitikadi. Yosefe ali ndi zaka pafupifupi 37, maloto ake aja anayamba kukwaniritsidwa modabwitsa kwambiri.​—Gen. 37:7, 9, 10; 42:6, 9.

7. Mogwirizana ndi 1 Petulo 5:10, kodi n’chiyani chingatithandize kupirira mayesero?

7 Zimene tikuphunzirapo. Nkhani ya Yosefe imatikumbutsa kuti anthu m’dzikoli ndi ankhanza ndipo angatichitire zinthu zopanda chilungamo. Ngakhale abale ndi alongo akhoza kutichitira zinthu zimene zingatikhumudwitse. Koma tikamaona Yehova ngati thanthwe lathu kapena malo athu othawirapo, sitingataye mtima kapena kusiya kumutumikira. (Sal. 62:6, 7; werengani 1 Petulo 5:10.) Tizikumbukiranso kuti Yosefe anali ndi zaka 17 pamene Yehova anamulotetsa maloto ake aja. Choncho zimenezi zikusonyeza kuti Yehova amadaliranso atumiki ake achinyamata. Masiku ano pali achinyamata ambiri amene ali ngati Yosefe, nawonso amakhulupirira kwambiri Yehova. Ena mwa achinyamata amenewa afika mpaka pomangidwa chifukwa sanafune kusiya kukhala okhulupirika kwa Mulungu.​—Sal. 110:3.

AZIMAYI AWIRI OMWE ANALI NDI CHISONI CHACHIKULU

8. Kodi Naomi ndi Rute anakumana ndi zotani?

8 Naomi ndi anthu a m’banja lake anachoka kwawo ku Yuda n’kukakhala alendo ku Mowabu chifukwa m’dziko lawo munali njala yaikulu. Ali kumeneko, mwamuna wake wa Naomi dzina lake Elimeleki anamwalira n’kumusiya ndi ana ake awiri aamuna. Patapita nthawi ana akewo anakwatira akazi a Chimowabu, omwe mayina awo ndi Rute ndi Olipa. Patapita zaka pafupifupi 10, ana a Naomi aja nawonso anamwalira koma sanasiye ana. (Rute 1:1-5) Taganizirani chisoni chimene azimayi atatuwa anali nacho. N’zoona kuti Rute ndi Olipa akanatha kukwatiwanso. Koma nanga kodi ndani amene akanasamalira Naomi yemwe anali wachikulire? Naomi anasweka mtima kwambiri moti ananena kuti: “Musanditchulenso kuti Naomi, muzinditchula kuti Mara, chifukwa Wamphamvuyonse wachititsa moyo wanga kukhala wowawa kwambiri.” (Rute 1:20) Pambuyo pa mavuto onsewa, Naomi anaganiza zobwerera kwawo ku Betelehemu ndipo Rute anapita naye limodzi.​—Rute 1:7, 18-20.

Mulungu anasonyeza Naomi ndi Rute kuti amathandiza anthu amene amamulambira akafooka komanso akakhala ndi chisoni. Ndipo angachitenso zimenezi kwa ife (Onani ndime 8-13) *

9. Mogwirizana ndi Rute 1:16, 17, 22, kodi Rute analimbikitsa bwanji Naomi?

9 Chikondi chokhulupirika chomwe Rute anasonyeza ndi chomwe chinathandiza Naomi. Mwachitsanzo, Rute anasonyeza chikondi kwa Naomi popitiriza kukhala naye limodzi. (Werengani Rute 1:16, 17, 22.) Ali ku Betelehemu, Rute ankagwira ntchito mwakhama yokunkha balere kuti apeze chakudya cha iyeyo ndi Naomi. Chifukwa cha zimenezi aliyense ankaona kuti Rute anali mkazi wabwino komanso wolimbikira ntchito.​—Rute 3:11; 4:15.

10. Kodi Yehova anasonyeza bwanji kuti ankakonda anthu osauka ngati mmene analili Naomi ndi Rute?

10 Yehova anapereka lamulo kwa Aisiraeli lomwe linkasonyeza chifundo chake kwa anthu osauka ngati mmene analili Naomi ndi Rute. Iye anauza anthu ake kuti akamakolola asamachotseretu mbewu zonse za mphepete mwa minda yawo, kuti anthu osauka azikunkha. (Lev. 19:9, 10) Choncho Naomi ndi Rute sankafunika kupemphetsa kuti apeze chakudya.

11-12. Kodi Boazi anathandiza bwanji Naomi ndi Rute kuti akhale osangalala?

11 Munda umene Rute ankakakunkha balere unali wa munthu wina wolemera dzina lake Boazi. Iye anachita chidwi chifukwa cha kukhulupirika komanso chikondi chimene Rute ankasonyeza kwa apongozi ake a Naomi. Choncho Boazi anakwatira Rute ndipo anagula malo omwe anali a banja la Naomi amene ana a Rute ankayenera kulandira ngati cholowa chawo. (Rute 4:9-13) Boazi ndi Rute anabereka mwana dzina lake Obedi, yemwe anadzakhala agogo ake a Mfumu Davide.​—Rute 4:17.

12 Taganizirani mmene Naomi anasangalalira atanyamula Obedi ali mwana, uku akupereka pemphero loyamikira kwa Yehova. Palinso zinthu zina zosangalatsa zimene Naomi ndi Rute adzasangalale nazo. Iwo akadzaukitsidwa adzasangalala kudziwa kuti Obedi anali mumzera wa makolo a Mesiya amene Mulungu analonjeza, kapena kuti Yesu Khristu.

13. Kodi ndi mfundo zofunika ziti zimene tingaphunzire pankhani ya Naomi ndi Rute?

13 Zimene tikuphunzirapo. Tikakumana ndi mayesero tikhoza kufooka komanso kusweka mtima. Mwina tingamaone kuti mavuto athuwo sangathe. Pa nthawi ngati imeneyi tingachite bwino kukhulupirira kwambiri Atate wathu wakumwamba komanso kukhala pafupi ndi abale ndi alongo athu. N’zoona kuti mwina Yehova sangatithetsere vuto lathulo. Mwachitsanzo, taona kuti iye sanaukitse mwamuna wa Naomi komanso ana ake. Koma angatithandize kupirira pogwiritsa ntchito abale ndi alongo athu omwe angatisonyeze chikondi chokhulupirika.​—Miy. 17:17.

MLEVI AMENE ANATSALA PANG’ONO KUSIYA KUTUMIKIRA YEHOVA

Wolemba Salimo 73 anatsala pang’ono kusiya kutumikira Yehova chifukwa chosirira anthu osalambira Yehova omwe ankaoneka ngati zinthu zikuwayendera bwino. Zimenezi zingatichitikirenso ifeyo (Onani ndime 14-16)

14. Kodi n’chiyani chinachititsa kuti Mlevi wina afooke?

14 Munthu amene analemba Salimo 73 anali Mlevi. Choncho anali ndi mwayi wapadera wotumikira pamalo olambirira Yehova. Ngakhale zili choncho, pa nthawi ina iye anafooka. Kodi n’chiyani chinachititsa kuti iye afooke? Iye anayamba kusirira anthu oipa ndi odzitukumula, osati chifukwa choti ankafuna kuchita zoipa koma ankaona ngati anthu amenewo zinthu zinkawayendera bwino. (Sal. 73:2-9, 11-14) Ankaoneka ngati anali ndi chilichonse, chuma, moyo wabwino komanso analibe nkhawa. Mleviyo ataona zimenezi anakhumudwa kwambiri moti ananena kuti: “Ndithudi, ndayeretsa mtima wanga pachabe, ndipo ndasamba m’manja mwanga pachabe posonyeza kuti ndine wopanda cholakwa.” Zimenezi zikanachititsa kuti asiye kutumikira Yehova.

15. Mogwirizana ndi Salimo 73:16-19, 22-25, kodi Mlevi amene analemba salimoli anachita chiyani kuti asapitirize kukhala wofooka?

15 Werengani Salimo 73:16-19, 22-25. Mleviyu ‘analowa m’malo opatulika aulemerero a Mulungu.’ Mmenemo, ali pakati pa okhulupirira anzake, anayamba kuganizira mofatsa mmene zinthu zinalili pa moyo wake komanso kupemphera. Zimenezi zinamuthandiza kuti adziwe kuti maganizo ake sanali anzeru ndipo akanatha kumuchititsa kuti asakhalenso pa ubwenzi ndi Yehova. Iye anazindikiranso kuti anthu oipa anali “pamalo oterera” ndiponso kuti “afika pamapeto awo ndipo atha chifukwa cha masoka owagwera modzidzimutsa.” Mleviyu anafunika kumaona zinthu monga mmene Yehova amazionera kuti asafooke komanso asiye kusirira anthu oipa. Atachita zimenezi anakhalanso ndi mtendere ndipo ankasangalala. Iye anati: “Palibe wina wondisangalatsa padziko lapansi koma inu nokha [Yehova].”

16. Kodi tingaphunzire chiyani kuchokera pa zimene zinachitikira Mlevi wina?

16 Zimene tikuphunzirapo. Tisamasirire anthu oipa omwe akuoneka ngati zinthu zikuwayendera bwino. Chimwemwe chawo ndi chakanthawi ndipo sadzakhala ndi moyo wosatha. (Mlal. 8:12, 13) Tikamawasirira tingathe kufooka ndiponso tingawononge ubwenzi wathu ndi Yehova. Choncho mukayamba kuona kuti mwayamba kusirira anthu oipa, muzichita zimene Mleviyu anachita. Muzimvera malamulo a Mulungu komanso muzikhala pafupi ndi anthu amene amachita zimene Yehova amafuna. Ndipotu mungakhale osangalala kwambiri mukamakonda Yehova kuposa china chilichonse. Komanso mungapitirizebe kuyenda panjira ya ‘kumoyo weniweniwo.’​—1 Tim. 6:19.

PETULO ANAFOOKA CHIFUKWA CHA ZIMENE ANALAKWITSA

Tikafooka, kuganizira zimene zinathandiza Petulo kuti ayambirenso kutumikira Yehova kungatithandize ifeyo komanso anthu ena (Onani ndime 17-19)

17. Kodi n’chiyani chinachititsa kuti Petulo afooke?

17 Mtumwi Petulo anali wolimba mtima, komabe nthawi zina ankachita zinthu mopupuluma ndipo ankafulumira kunena maganizo ake. Zotsatira zake, panthawi ina ananena komanso kuchita zinthu zimene ananong’oneza nazo bondo. Mwachitsanzo, pamene Yesu ankauza atumwi ake kuti ayenera kuzunzidwa komanso kuphedwa, Petulo anamutsutsa ponena kuti: “Musalole kuti zimenezi zikuchitikireni ngakhale pang’ono.” (Mat. 16:21-23) Koma Yesu anamudzudzula. Pamene gulu la anthu linabwera kudzagwira Yesu, Petulo anachita zinthu mopupuluma. Iye anadula khutu la kapolo wa mkulu wa ansembe. (Yoh. 18:10, 11) Apanso Yesu anadzudzula mtumwiyu. Kuwonjezera pamenepo, Petulo anadzitama kuti ngakhale atumwi onse atathawa n’kumusiya Yesu, iyeyo sangachite zimenezo. (Mat. 26:33) Koma Petulo sanali wolimba mtima ngati mmene ankaganizira chifukwa usiku womwewo anachita mantha kwambiri moti anakana katatu kuti sankamudziwa Yesu. Petulo anakhumudwa kwambiri “ndipo anatuluka panja n’kuyamba kulira mopwetekedwa mtima kwambiri.” (Mat. 26:69-75) N’kutheka kuti iye ankaganiza kuti mwina Yesu sangamukhululukire.

18. Kodi Yesu anathandiza bwanji Petulo pamene anafooka?

18 Komabe Petulo sanafooke kwambiri mpaka kufika posiya kutumikira Yehova. Pambuyo pake anapitirizabe kutumikira Yehova limodzi ndi atumwi enawo. (Yoh. 21:1-3; Mac. 1:15, 16) Kodi n’chiyani chinamuthandiza? Iye anakumbukira kuti Yesu anali atamupempherera kale kuti chikhulupiriro chake chisathe komanso anauza Petulo kuti akabwerera akalimbikitse abale ake. Yehova anayankha pemphero la Yesu lochokera pansi pamtimali. Kenako Yesu anaonekera kwa Petulo kuti amulimbikitse. (Luka 22:32; 24:33, 34; 1 Akor. 15:5) Yesu anaonekeranso kwa atumwi onse atagwira ntchito usiku wonse koma osapha nsomba. Panthawiyi Yesu anamupatsa Petulo mwayi winanso womusonyeza mmene amamukondera. Yesu anakhululukira mnzake wapamtimayu ndipo anamupatsa ntchito yambiri.​—Yoh. 21:15-17.

19. Kodi lemba la Salimo 103:13, 14, limatithandiza bwanji kudziwa mmene Yehova amationera tikachimwa?

19 Zimene tikuphunzirapo. Mmene Yesu anachitira zinthu ndi Petulo zimasonyeza kuti iye ndi wachifundo kwambiri ngati Atate wake. Choncho tikalakwitsa zinazake, tisamaganize kuti Yehova sangatikhululukire. Tizikumbukira kuti Satana ndi amene amafuna kuti tiziganiza choncho. M’malomwake tizikumbukira kuti Yehova amatikonda komanso amatimvetsa ndipo ndi wokonzeka kutikhululukira. Choncho tiyenera kumutsanzira, anthu ena akachita zinthu zotikhumudwitsa.​—Werengani Salimo 103:13, 14.

20. Kodi tidzakambirana chiyani munkhani yotsatira?

20 Zitsanzo za Yosefe, Naomi, Rute, Mlevi komanso Petulo zikutitsimikizira kuti “Yehova ali pafupi ndi anthu a mtima wosweka.” (Sal. 34:18) Iye nthawi zina angalole kuti tikumane ndi mayesero komanso kusweka mtima. Komabe Yehova akatithandiza kupirira mayeserowo chikhulupiriro chathu chimalimba. (1 Pet. 1:6, 7) Munkhani yotsatira, tionanso mmene Yehova amathandizira atumiki ake okhulupirika omwe afooka mwina chifukwa chakuti si angwiro kapena chifukwa cha mavuto ena.

NYIMBO NA. 7 Yehova Ndiye Mphamvu Zathu

^ ndime 5 Yosefe, Naomi, Rute, Mlevi wina komanso mtumwi Petulo anakumana ndi zinthu zimene zinachititsa kuti mitima yawo isweke. Munkhaniyi, tiona mmene Yehova anawalimbikitsira komanso kuwapatsa mphamvu. Tionanso zimene tikuphunzira kuchokera kwa anthu amenewa komanso mmene Yehova anawathandizira mwachikondi.

^ ndime 56 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Naomi, Rute ndi Olipa anakhumudwa kwambiri ndi imfa ya amuna awo. Kenako Rute, Naomi komanso Boazi anasangalala Obedi atabadwa.