Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 52

Zimene Tingachite Tikafooka

Zimene Tingachite Tikafooka

“Umutulire Yehova nkhawa zako, ndipo iye adzakuchirikiza.”SAL. 55:22.

NYIMBO NA. 33 Umutulire Yehova Nkhawa Zako

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1. Kodi chingachitike n’chiyani tikafooka?

TSIKU lililonse timakumana ndi mavuto. Koma timayesetsa mmene tingathere kuti tipirire. Mungavomereze kuti zimakhala zovuta kulimbana ndi mavuto tikafooka. Tizikumbukira kuti tikafooka tingayambe kudziona ngati opanda pake komanso zingachititse kuti tisamasangalale. Lemba la Miyambo 24:10, limati: “Ukafooka pa tsiku la masautso, mphamvu zako zidzakhala zochepa.” Choncho tikafooka tingasowe mphamvu zoti tithe kulimbana ndi mavuto athu.

2. Kodi ndi zinthu ziti zimene zingatifooketse, nanga tikambirana chiyani munkhaniyi?

2 Tingathe kufooka chifukwa cha mavuto osiyanasiyana. Mavuto ena angakhale oyambitsidwa ndi ifeyo, ndipo ena angayambe chifukwa cha zinthu zina. Zinthu zimenezi zingakhale zimene timalakwitsa, zimene sitingakwanitse kuchita kapena matenda. Tingathenso kufooka chifukwa sitinapatsidwe utumiki umene timalakalaka m’gulu la Yehova, kapena chifukwa chakuti tikulalikira m’gawo limene anthu ambiri samvetsera uthenga wathu. Munkhaniyi tikambirana zinthu zina zimene tingachite tikafooka.

NGATI TALAKWITSA ZINTHU KOMANSO SITINGAKWANITSE KUCHITA ZINAZAKE

3. Kodi n’chiyani chimene chingatithandize kuti tisamadzione ngati opanda pake chifukwa cha zimene timalakwitsa?

3 N’zosavuta kumadziona ngati wopanda pake komanso kumadziimba mlandu chifukwa cha zinthu zimene talakwitsa. Zimenezi zingapangitse kuti tiziganiza kuti chifukwa cha zimene timalakwitsa Yehova sangafune kuti tikalowe m’dziko latsopano. Maganizo amenewa ndi oopsa kwambiri. Kodi tiyenera kumva bwanji tikalakwitsa zinazake? Baibulo limanena kuti kupatulapo Yesu Khristu yekha, anthu onse ndi “ochimwa.” (Aroma 3:23) Koma Yehova samangoyang’ana zimene timalakwitsa kapena kuyembekezera kuti tizichita zinthu mosalakwitsa chilichonse. M’malomwake Iye ndi atate wachikondi amene amafuna kutithandiza. Komanso ndi woleza mtima. Ndipo akudziwa kuti ambirife tikuyesetsa kuti tizichita zinthu zabwino komanso kuti tisamadzione ngati opanda pake ndipo Iye ndi wokonzeka kutithandiza.​—Aroma 7:18, 19.

Yehova amadziwa zabwino zimene tinachita m’mbuyomu komanso zimene tikuchita panopa (Onani ndime 5) *

4-5. Mogwirizana ndi 1 Yohane 3:19, 20, n’chiyani chinathandiza alongo awiri kuti asafooke?

4 Taganizirani chitsanzo cha Deborah ndi Maria. * Deborah ali mwana, anthu a m’banja lake sankamusonyeza chikondi, ndipo zimenezi zinkamuchititsa kuti aziziona ngati wopanda pake. Nthawi zambiri akachita zabwino sankamuyamikira. Choncho atakula ankangodziona ngati wachabechabe. Ndiye akalakwitsa kanthu ngakhale kakang’ono ankaona kuti palibe chabwino chimene angachite. Maria nayenso anali ndi vuto lomweli. Achibale ake ankamuchititsa manyazi. Zimenezi zinamuchititsa kuti aziziona ngati wachabechabe. Ngakhale pamene anabatizidwa ankaganiza kuti ndi wosayenera kukhala wa Mboni za Yehova.

5 Komabe alongo awiriwa sanasiye kutumikira Yehova. Chifukwa chiyani? Chifukwa chimodzi n’chakuti ankapemphera kwa Yehova n’kumuuza mmene ankamvera. (Sal. 55:22) Anazindikira kuti Atate wathu wachikondi amadziwa kuti zinthu zoipa zimene zinatichitikira zingatichititse kuti tizidziona ngati opanda pake. Anazindikiranso kuti Mulungu amaona makhalidwe abwino amene tili nawo ngakhale kuti patokha sitiona kuti tili ndi makhalidwe amenewa.​—Werengani 1 Yohane 3:19, 20.

6. Kodi munthu angatani ngati atabwerezanso kuchita tchimo linalake?

6 Munthu wina angakhale kuti amayesetsa kuti asiye kuchita makhalidwe oipa koma angapezeke kuti wachitanso, ndipo zimenezi zingamukhumudwitse. N’zoona kuti mwachibadwa timadziimba mlandu tikalakwitsa zinazake. (2 Akor. 7:10) Koma sitikuyenera kudziimba mlandu mopitirira malire n’kumaganiza kuti: ‘Ndine wachabechabe ndipo Yehova sangandikhululukire.’ Maganizo amenewa ndi olakwika ndipo angapangitse kuti tisiye kutumikira Yehova. Kumbukirani kuti pa Miyambo 24:10, tinawerenga kuti tikafooka mphamvu zathu zimachepa. M’malomwake muyenera kupemphera kwa Yehova kuti akukhululukireni n’cholinga choti mukhalenso pa ubwenzi wabwino ndi Iye. (Yes. 1:18) Iye akaona kuti mwalapa kuchokera pansi pamtima angakukhululukireni. Kuwonjezera pamenepo muyenera kukauzanso akulu. Iwo angakuthandizeni moleza mtima kuti mukhalenso pa ubwenzi ndi Yehova.​—Yak. 5:14, 15.

7. N’chifukwa chiyani sitiyenera kufooka ngati tikuvutika kusiya khalidwe linalake loipa?

7 Mkulu wina ku France dzina lake Jean-Luc, anauza anthu amene akuyesetsa kuti asiye khalidwe linalake loipa kuti: “Yehova amaona kuti munthu ndi wolungama osati chifukwa choti salakwitsa zinthu, koma chifukwa choti akalakwitsa zinthu amadzimvera chisoni n’kulapa.” (Aroma 7:21-25) Choncho ngati mukuvutika kuti musiye khalidwe linalake loipa musadzione ngati wachabechabe. Popeza kuti tonsefe timalakwitsa zinthu timafuna kuti Yehova azitisonyeza kukoma mtima kwake kwakukulu, ndipo zimenezi zimatheka chifukwa cha nsembe ya Yesu.​—Aef. 1:7; 1 Yoh. 4:10.

8. Kodi tingapite kwa ndani kuti atithandize tikafooka?

8 Abale ndi alongo athu mumpingo angatilimbikitse. Iwo angamvetsere pamene tikuwafotokozera mavuto athu ndipo angatilimbikitse. (Miy. 12:25; 1 Ates. 5:14) Mlongo wina wa ku Nigeria dzina lake Joy amene wakhala akulimbana ndi zinthu zina zimene zinkamufooketsa ananena kuti: “Sindikanatha kupirira zikanakhala kuti abale ndi alongo sanandithandize. Zimene iwo ankachita pondilimbikitsa ndi umboni wakuti Yehova amayankha mapemphero anga. Abale ndi alongowa andiphunzitsanso mmene ndingalimbikitsire anthu ena amene ali pa mavuto.” Komabe tizikumbukira kuti si nthawi zonse pamene abale ndi alongo athu angadziwe kuti tikufunika kulimbikitsidwa. Choncho tingafunike kupita kwa m’bale kapena mlongo wolimba mwauzimu n’kumufotokozera mavuto athu.

NGATI TIKUDWALA

9. Kodi lemba la Salimo 41:3 ndi 94:19, lingatilimbikitse bwanji?

9 Tizipempha Yehova kuti atithandize. Tikamadwala, makamaka ngati matendawo atenga nthawi yaitali, mwina zingamativute kuti tiziona zinthu moyenera. N’zoona kuti Yehova sangatichiritse modabwitsa panopa, koma amatilimbikitsa ndi kutipatsa mphamvu kuti tithe kupirira. (Werengani Salimo 41:3; 94:19.) Mwachitsanzo, angalimbikitse abale ndi alongo athu kuti atithandize ntchito zapakhomo kapena kukatigulira zinthu. Iye angalimbikitsenso abale athu kuti apemphere nafe limodzi kapenanso angatikumbutse mfundo zolimbikitsa zopezeka m’Mawu ake. Angatikumbutse zinthu zabwino zimene tikuyembekezera m’dziko latsopano monga moyo wabwino wopanda matenda kapena zopweteka zilizonse.​—Aroma 15:4.

10. N’chiyani chinathandiza Isang kuti asapitirize kumadzimvera chisoni atachita ngozi?

10 Isang yemwe amakhala ku Nigeria, anachita ngozi yomwe inachititsa kuti afe ziwalo. Dokotala wake anamuuza kuti sadzathanso kuyenda. Iye anati: “Ndinakhumudwa kwambiri komanso kudzimvera chisoni.” Koma kodi anapitirizabe kudzimvera chisoni? Ayi. N’chiyani chinamuthandiza? Iye anafotokoza kuti: “Ine ndi mkazi wanga sitinasiye kupemphera kwa Yehova komanso kuphunzira Mawu ake. Komanso tinapitiriza kuyamikira zinthu zabwino zimene tili nazo kuphatikizapo chiyembekezo cha moyo wosatha m’dziko limene Mulungu watilonjeza.”

Ngakhale anthu amene sangathe kuchita zambiri muutumiki chifukwa cha matenda kapena uchikulire, akhoza kupeza njira zolalikirira n’kumasangalala (Onani ndime 11-13)

11. Kodi n’chiyani chinathandiza Cindy kuti akhalebe wosangalala pamene ankadwala kwambiri?

11 Cindy amene amakhala ku Mexico, anauzidwa ndi dokotala wake kuti ali ndi matenda amene angathe kufa nawo. Kodi anachita chiyani kuti apirire? Ali m’chipatala ankaonetsetsa kuti tsiku lililonse azilalikira. Iye analemba kuti: “Zimenezi zinandithandiza kuti ndiziganizira anthu ena m’malo momangoganizira za opaleshoni yanga, ululu umene ndinkamva kapenanso matenda anga. Zimene ndinkachita ndi izi: Ndikamakambirana ndi madokotala kapena manesi ndinkawafunsa za mabanja awo. Kenako ndinkawafunsa chifukwa chake anasankha ntchito yovutayi. Ndikatero zinali zosavuta kusankha nkhani imene ingawafike pamtima. Ambiri ananena kuti kawirikawiri wodwala samawafunsa za moyo wawo ndipo ankandiyamikira chifukwa chowaganizira, moti ena anandipatsa ma adiresi kapena manambala awo a foni. Choncho panthawi yovutayi ndinkadziwa kuti Yehova andithandiza kuti ndipirire. Koma ndinadabwanso ndi mmene anandithandizira kuti ndikhale wosangalala kwambiri.”​—Miy. 15:15.

12-13. Kodi anthu ena amene akudwala komanso achikulire amachita zotani kuti azilalikira, nanga zotsatira zake n’zotani?

12 Anthu amene akudwala kapena achikulire angakhumudwe chifukwa sangathe kuchita zambiri muutumiki. Komabe ambiri amapeza njira zolalikirira. Mwachitsanzo, mlongo wina wa ku United States, dzina lake Laurel anakhala m’mashini omuthandiza kupuma kwa zaka 37. Mlongoyu anapezekanso ndi khansa, matenda a pa khungu komanso anachitidwa maopaleshoni ambiri. Koma mavuto amenewa sanamulepheretse kulalikira. Iye ankalalikira kwa manesi komanso anthu ena amene ankabwera kunyumba kwake. Kodi zotsatira zake zinali zotani? Mlongoyo anathandiza anthu pafupifupi 17 kuti aphunzire za Yehova. *

13 Mkulu wina wa ku France dzina lake Richard, anafotokoza zimene zingathandize anthu amene sangathe kuchoka panyumba kapena amene akukhala ku nyumba zosungira anthu okalamba. Iye anati: “Ndimaona kuti n’zothandiza ngati atamaika mabuku ndi magazini pamalo oti anthu aziwaona. Zimenezi zimathandiza kuti anthu akhale ndi chidwi komanso kuti ayambe kukambirana nawo mosavuta. Kukambirana ndi anthu m’njira imeneyi kungalimbikitse abale ndi alongo athu amene sangathe kukalalikira kunyumba ndi nyumba.” Abale ndi alongo amenewa angathenso kulalikira polemba makalata kapena kuimba mafoni.

NGATI SITINAPATSIDWE UTUMIKI UMENE TIMALAKALAKA

14. Kodi Mfumu Davide anapereka chitsanzo chotani?

14 Pali zifukwa zambiri zimene zingachititse kuti tisapatsidwe utumiki umene timalakalaka m’gulu la Yehova. Mwachitsanzo, mwina chifukwa cha uchikulire, matenda kapena chifukwa cha zinthu zina. Ngati zinthu zili choncho pa moyo wathu tingaphunzire zambiri kuchokera kwa Mfumu Davide. Davide ankafunitsitsa kuti agwire ntchito yomanga kachisi koma atauzidwa kuti Mulungu sanamusankhe kuti agwire ntchitoyi, anathandiza ndi mtima wonse munthu amene Mulungu anamusankha kuti agwire ntchitoyo. Iye anapereka golide ndi siliva wambiri kuti agwiritsidwe ntchito pomanga kachisiyo. Chimenechitu ndi chitsanzo chabwino kwambiri kwa ife.​—2 Sam. 7:12, 13; 1 Mbiri 29:1, 3-5.

15. Kodi M’bale Hugues anachita chiyani kuti asafooke?

15 Chifukwa cha matenda, m’bale wina wa ku France dzina lake Hugues, anasiya kutumikira ngati mkulu komanso sankatha ngakhale kugwira ntchito zing’onozing’ono zapakhomo. Iye analemba kuti: “Poyamba ndinakhumudwa kwambiri ndipo ndinkangodziona ngati wachabechabe. Patapita nthawi ndinaona kuti ndi bwino kuti ndisamadandaule chifukwa cha zinthu zimene sindinkakwanitsa kuchita. Nditatero ndinayamba kusangalala ndi zimene ndinkakwanitsa kuchita potumikira Yehova. Ndatsimikiza mtima kuti ndisabwerere m’mbuyo. Mofanana ndi Gidiyoni ndi amuna 300 omwe anali otopa, ndipitirizabe kumenya nkhondo.”​—Ower. 8:4.

16. Kodi tingaphunzire chiyani kuchokera kwa angelo?

16 Angelo okhulupirika amatipatsa chitsanzo chabwino. Mwachitsanzo nthawi ina Yehova anafunsa angelo kuti apereke maganizo awo pa mmene angapusitsire Mfumu Ahabu yemwe anali woipa. Angelo angapo anapereka maganizo awo. Koma Mulungu anasankha mngelo mmodzi n’kumuuza kuti maganizo ake ndi omwe angathandize. (1 Maf. 22:19-22) Kodi angelo ena okhulupirikawo anafooka n’kumaganiza kuti, ‘Ndangotaya nthawi kupereka maganizo anga?’ Ayi sichoncho. Tikutero chifukwa angelo ndi odzichepetsa kwambiri ndipo amafuna kuti ulemerero wonse uzipita kwa Yehova.​—Ower. 13:16-18; Chiv. 19:10.

17. Kodi tiyenera kuchita chiyani ngati takhumudwa chifukwa choti sitinapatsidwe utumiki umene timalakalaka?

17 Tizikumbukira kuti tili ndi mwayi wodziwika ndi dzina la Mulungu komanso wolalikira za Ufumu wake. Tikhoza kupatsidwa utumiki wina wake komanso utumikiwo ukhoza kutha. Choncho utumiki umene timachita si umene umapangitsa kuti tikhale amtengo wapatali kwa Mulungu. Chimene chingachititse kuti tikhale amtengo wapatali kwa Yehova komanso kwa abale ndi alongo athu ndi kudzichepetsa. Ndiye tizipempha Yehova kuti atithandize kukhalabe odzichepetsa. Tiziganizira zitsanzo za atumiki odzichepetsa a Yehova zopezeka m’Baibulo. Tizikhala ofunitsitsa kutumikira abale athu mmene tingathere.​—Sal. 138:6; 1 Pet. 5:5.

NGATI ANTHU A M’GAWO LATHU SACHITA CHIDWI NDI UTHENGA WATHU

18-19. Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tizisangalalabe ngakhale pamene anthu a m’gawo lathu sachita chidwi ndi uthenga wathu?

18 Kodi munayamba mwafookapo chifukwa chakuti anthu a m’gawo lanu sachita chidwi ndi uthenga wanu, kapena chifukwa choti simuwapeza panyumba mukamalalikira? Zikatere, kodi tingatani kuti tipitirizebe kukhala osangalala? Tingapeze mfundo zina zothandiza m’bokosi lakuti “ Zimene Mungachite Kuti Muzisangalala Ndi Utumiki Wanu.” M’pofunikanso kuti tiziona moyenera ntchito yolalikira. Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani?

19 Tizikumbukira kuti timalalikira n’cholinga chothandiza anthu kudziwa dzina la Mulungu komanso kuwauza za Ufumu wake. Yesu ananena momveka bwino kuti ndi anthu ochepa omwe adzamutsatire. (Mat. 7:13, 14) Tikakhala muutumiki timakhala ndi mwayi wogwira ntchito ndi Yehova, Yesu komanso angelo. (Mat. 28:19, 20; 1 Akor. 3:9; Chiv. 14:6, 7) Yehova amakoka anthu omwe akufuna kumutumikira. (Yoh. 6:44) Choncho ngati munthu sanamvetsere uthenga wathu panthawiyi tingayembekezere kuti adzamvetsera nthawi ina.

20. Kodi lemba la Yeremiya 20:8, 9, likutiphunzitsa kuti n’chiyani chingatithandize kuti tisafooke?

20 Tingaphunzire zambiri kuchokera kwa mneneri Yeremiya. Gawo limene iye anauzidwa kuti azikalalikira linali lovuta kwambiri. Anthu ankamunyoza komanso kumuseka “tsiku lonse.” (Werengani Yeremiya 20:8, 9.) Moti nthawi ina anafooka mpaka kufika pofuna kusiya kulalikira. Komabe sanasiye. N’chiyani chinamuthandiza? “Mawu a Yehova” anali ngati moto mumtima mwa Yeremiya, choncho sakanatha kungokhala osamalalikira. Zimenezinso ndi zomwe zingachitike kwa ife ngati timaphunzira Mawu a Mulungu tsiku lililonse komanso kuganizira mozama zimene timaphunzira. Tikamachita zimenezi, tingakhale osangalala ndi utumiki wathu komanso anthu ambiri angayambe kumvetsera uthenga wathu.​—Yer. 15:16.

21. Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tipitirizebe kutumikira Mulungu ngakhale tikukumana ndi zinthu zimene zingatifooketse?

21 Deborah yemwe tamutchula kale uja anati: “Satana amayesetsa kutifooketsa n’cholinga choti atigonjetse.” Koma Yehova Mulungu ndi wamphamvu kwambiri kuposa Satana. Choncho mukaona kuti mwafooka chifukwa cha zinthu zosiyanasiyana muzipempha Yehova kuti akuthandizeni. Iye angatithandize kuti tisamadziimbe kwambiri mlandu chifukwa cha zinthu zimene timalakwitsa komanso zimene sitingakwanitse kuchita. Angatithandizenso pamene tikudwala. Angatithandize kuti tiziona moyenera utumiki umene tikuchita ndiponso kuti tizisangalala tikamagwira ntchito yolalikira. Choncho muzipemphera kwa Atate wanu wakumwamba n’kumufotokozera mmene mukumvera. Iye adzakuthandizani kuti mupitirizebe kumutumikira ngakhale mukukumana ndi zinthu zimene zingakufooketseni.

NYIMBO NA. 41 Mulungu Imvani Pemphero Langa

^ ndime 5 Nthawi zina tonsefe timafooka. Munkhaniyi, tikambirana zimene tingachite tikafooka komanso tiona mmene Yehova angatithandizire.

^ ndime 4 Mayina ena asinthidwa.

^ ndime 12 Mungawerenge mbiri ya moyo wa Laurel Nisbet mu Galamukani! yachingelezi ya January 22, 1993.

^ ndime 69 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Mlongo amene anafooka kwa kanthawi akuganizira zimene wakhala akuchita m’mbuyomu potumikira Mulungu ndipo kenako akupemphera kwa Yehova. Sakukayikira kuti Mulungu akukumbukira zimene iye anachita m’mbuyomu komanso zimene akuchita panopa.