Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Muzichita Khama pa Utumiki Wanu

Muzichita Khama pa Utumiki Wanu

KODI mumamva bwanji mukalandira kalata yolimbikitsa kuchokera kwa mnzanu wapamtima? Timoteyo analandira kalata ngati imeneyi kuchokera kwa mtumwi Paulo, ndipo ndi imene imadziwika monga buku la m’Baibulo la 2 Timoteyo. Mosakayikira Timoteyo anafunafuna malo opanda phokoso n’cholinga choti awerenge kalata imene mnzake wapamtimayu anamulembera. N’kutheka kuti Timoteyo ankaganiza kuti, ‘Kodi Paulo ali bwanji? Kodi wandilembera malangizo alionse amene angandithandize pa utumiki wanga? Kodi malangizo a m’kalatayi angathandize ena komanso ineyo kuti ndizitha kulalikira komanso kuphunzitsa bwino?’ Monga mmene tionere, Timoteyo anapeza mayankho a mafunso amenewa komanso ena ambiri m’kalata yofunikayi. Koma mu nkhaniyi tikambirana mfundo zingapo zothandiza zimene zikupezeka m’kalatayi.

“NDIKUPIRIRABE ZINTHU ZONSE”

Timoteyo atangoyamba kuwerenga kalatayi ayenera anazindikira kuti Paulo ankamukonda kwambiri. Tikutero chifukwa chakuti mwachikondi Paulo anamutchula kuti “mwana wanga wokondedwa.” (2 Tim. 1:2) Timoteyo analandira kalatayi cha m’ma 65 C.E. Panthawiyi iye anali ndi zaka zoposa 30, ndipo n’kuti atakhala mkulu kwa nthawi ndithu. Komanso anali atagwira ntchito ndi Paulo kwa zaka zoposa 10 ndipo anaphunzira zinthu zambiri.

Timoteyo ayenera kuti analimbikitsidwa kwambiri atadziwa kuti Paulo akupitirizabe kupirira masautso amene akukumana nawo ndipo akupitirizabe kukhala wokhulupirika. Panthawiyi Paulo anali mu ndende ku Roma ndipo anali atatsala pang’ono kuphedwa. (2 Tim. 1:15, 16; 4:6-8) Timoteyo anaona kuti mtumwiyu ndi wolimba mtima chifukwa cha mawu amene ananena akuti, “ndikupirirabe zinthu zonse.” (2 Tim. 2:8-13) Mofanana ndi Timoteyo, ifenso tingalimbikitsidwe ndi chitsanzo chabwino cha Paulo yemwe anapitirizabe kupirira.

“MPHATSO . . . UIKOLEZERE NGATI MOTO”

Paulo analimbikitsa Timoteyo kuti aziona zimene ankachita potumikira Mulungu monga chinthu chamtengo wapatali. Iye ankafuna kuti Timoteyo ‘akolezere mphatso ya Mulungu imene inali mwa iye ngati moto.’ (2 Tim. 1:6) Apa Paulo anagwiritsa ntchito mawu a Chigiriki akuti khaʹri·sma ponena za “mphatso.” Mawu a Chigirikiwa angatanthauzenso mphatso yaulere, kapena imene sumayenera kupatsidwa. Choncho Timoteyo anapatsidwa mphatso imeneyi pamene anasankhidwa kutumikira mumpingo wa Chikhristu m’njira yapadera.​—1 Tim. 4:14.

Kodi pamenepa Paulo ankalimbikitsa Timoteyo kuchita chiyani ndi mphatsoyi? Pamene anawerenga mawu akuti “uikolezere ngati moto,” Timoteyo ayenera kuti anakumbukira kuti anthu ena m’nyumba zawo amagwiritsa ntchito moto wamakala, ndipo munthu ankafunika kupitirizabe kukolezera motowo n’cholinga choti upitirizebe kuyaka. Buku lina limanena kuti verebu ya Chigiriki imene Paulo anagwiritsa ntchito ponena za kukolezera ingatanthauzenso, “kuyatsanso, kapena kupepelera kuti uyake kwambiri.” Choncho Timoteyo ayenera anazindikira kuti zimenezi zikutanthauza “kuyambiranso kuchita changu pantchito inayake.” Apa tingati Paulo amamulangiza Timoteyo kuti: ‘Uzichita khama pa utumiki wako.’ Amenewatu ndi malangizo abwino kwa ifenso masiku ano, tiyenera kupitirizabe kuchita khama pa utumiki wathu.

“CHUMA CHAPADERA . . . UCHISUNGE”

Popitiriza kuwerenga kalata yochokera kwa mnzake wapamtimayu, Timoteyo anapezanso mawu ena omwe Paulo analemba, amene akanamuthandiza kuti zinthu zimuyendere bwino pa utumiki wake. Paulo analemba kuti: “Chuma chapadera chimene anachiika m’manja mwakochi, uchisunge mothandizidwa ndi mzimu woyera umene uli mwa ife.” (2 Tim. 1:14) Kodi chuma chapadera chimenechi chinali chiyani? Malinga ndi vesi la m’mbuyo, Paulo asananene mawuwa anali atanena za “mawu olondola,” omwe ndi choonadi chomwe chimapezeka m’Malemba. (2 Tim. 1:13) Monga mtumiki wa Chikhristu, Timoteyo ankayenera kulengeza choonadi mu mpingo komanso kwa anthu ena. (2 Tim. 4:1-5) Komanso iye anali atasankhidwa kukhala mkulu kuti awete nkhosa za Mulungu. (1 Pet. 5:2) Choncho Timoteyo akanasunga chuma chimenechi, chomwe ndi choonadi chomwe amayenera kuuza ena, popitirizabe kudalira mzimu woyera wa Mulungu komanso Mawu ake.​—2 Tim. 3:14-17.

Ifenso masiku ano tinapatsidwa choonadi chimene timauza ena mu utumiki wathu wa Chikhristu. (Mat. 28:19, 20) Choncho tingasonyeze kuti timayamikira kwambiri chuma chapadera chimenechi popitirizabe kupemphera, komanso kukhala ndi chizolowezi chowerenga Mawu a Mulungu. (Aroma 12:11, 12; 1 Tim. 4:13, 15, 16) Mwina ifenso tingaikidwe kuti tikhale mkulu, kapena kuchita utumiki winawake wanthawi zonse. Tiziona zimenezo monga chuma, ndipo zizitithandiza kukhala odzichepetsa, komanso kupitirizabe kudalira Mulungu kuti azitithandiza. Choncho tiyenera kusunga kapena kuti kuteteza chuma chimenechi popitirizabe kuchiona monga chinthu chamtengo wapatali, komanso kudalira Yehova kuti azitithandiza kusamalira chumacho.

“ZIMENEZO UZIPHUNZITSE KWA ANTHU OKHULUPIRIKA”

Utumiki umene Timoteyo anapatsidwa si kuti unkakhudza iye yekha, unkakhudzanso anthu ena. N’chifukwa chake Paulo analimbikitsa Timoteyo kuti: “Zinthu zimene unazimva kwa ine . . . uziphunzitse kwa anthu okhulupirika, amene nawonso adzakhala oyenerera bwino kuphunzitsa ena.” (2 Tim. 2:2) Choncho apa Paulo anakumbutsa Timoteyo kuti zinthu zimene anaphunzira kwa abale ena a Chikhristu, ankayenera kuphunzitsanso anthu ena. Ndizofunika kuti oyang’anira a Chikhristu masiku anonso azichita zimenezi. Woyang’anira wabwino sachita nsanje n’kumalephera kuphunzitsa ena ntchito inayake. M’malomwake amayesetsa kuwaphunzitsa n’cholinga choti agwire bwino ntchitoyo. Iye saopa kuti anthu enawo angadziwe zambiri kapena kugwira bwino ntchitoyo kuposa mmene iyeyo akanaigwirira. Choncho si kuti amangowaphunzitsa zinthu zochepa zokhudza ntchitoyo. M’malomwake amafunitsitsa kuthandiza anthu amene akuwaphunzitsawo kuti akhale ndi luso mpaka kufika pokhala Akhristu odalirika. Zikatero, “anthu okhulupirika” amene iye wawaphunzitsa amathandiza kuti zinthu ziziyenda bwino mumpingo.

Sitikukayikira kuti Timoteyo anasangalala kwambiri ndi kalata yolimbikitsa imene analandira kwa Paulo. N’kutheka kuti iye ankawerenga mobwerezabwereza malangizo othandiza a m’kalatayi n’kumaganizira mmene angawagwiritsire ntchito pa utumiki wake.

Ifenso tiyenera kumagwiritsa ntchito malangizo amenewa. Kodi tingachite bwanji zimenezi? Tingatero popitirizabe kusunga mphatso imene tapatsidwa, yomwe ndi chuma chapadera chimene tili nacho komanso kuphunzitsa ena zonse zomwe tikudziwa ndiponso luso lathu. Tikatero, monga mmene Paulo anauzira Timoteyo, ‘tidzakwaniritsa mbali zonse za utumiki wathu.’​—2 Tim. 4:5.