Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Ika Mtima pa Utumiki Wako!

Ika Mtima pa Utumiki Wako!

KODI mumamvela bwanji mukalandila kalata yocokela kwa mnzanu wabwino? Wophunzila wacikhristu Timoteyo, analandila kalata ngati imeneyo kucokela kwa mtumwi Paulo, ndipo kalatayo tsopano ni buku la m’Baibo la 2 Timoteyo. Mosakaikila, Timoteyo anali wofunitsitsa kupeza malo aphee kuti aŵelenge zimene mnzake wapamtima anamulembela. Mwina Timoteyo anali kuganiza kuti: ‘Kodi Paulo ali bwanji? Kodi ali na malangizo ena ake a mmene niyenela kuonela utumiki wanga? Kodi kalatayi idzanithandiza kucita bwino utumiki wanga wacikhristu na kuthandiza ena?’ Monga tionele, Timoteyo anapeza mayankho pa mafunso amenewa, komanso zina zambili m’kalata yofunika imeneyi. Koma palipano, tiyeni tisumike maganizo pa mfundo zingapo zikulu-kulu zokhala na uphungu wothandiza m’kalatayi.

“NDIKUPILILABE ZINTHU ZONSE”

Timoteyo atangoŵelenga mawu oyambilila m’kalatayo, anaona cikondi cimene Paulo anali naco pa iye. Mokoma mtima, Paulo anachula Timoteyo kuti “mwana wanga wokondedwa.” (2 Tim. 1:2) Ngakhale kuti Timoteyo anali na zaka za m’ma 30 pamene analandila kalatayi, ca mu 65 C.E., anali kale mkulu wacikhristu wacidziŵitso. Iye anali atatumikilapo kale na Paulo kwa zaka zoposa 10 ndipo anaphunzila zambili.

Timoteyo ayenela kuti analimbikitsidwa kwambili atadziŵa kuti Paulo anali kupilila masautso mokhulupilika. Paulo anali m’maunyolo m’ndende ku Roma, ndipo anali kuyembekezela kuphedwa. (2 Tim. 1:15, 16; 4:6-8) Timoteyo anaona kuti Paulo anali wolimba mtima cifukwa Paulo anati: “Ndikupililabe zinthu zonse.” (2 Tim. 2:8-13) Mofanana na Timoteyo, nafenso tingapeze mphamvu pa citsanzo cabwino kwambili ca Paulo pankhani ya kupilila.

‘MPHATSO IMENE UNALANDILA UIKOLEZELE NGATI MOTO’

Paulo analimbikitsa Timoteyo kuona utumiki wake kukhala wofunika kwambili. Paulo anali kufuna kuti Timoteyo ‘aikolezele ngati moto, mphatso ya Mulungu’ imene inali mwa iye. (2 Tim. 1:6) Pa liwu lakuti “mphatso,” Paulo anaseŵenzetsa liwu la Cigiliki lakuti khaʹri·sma. Liwu la Cigiliki limeneli, kweni-kweni limafotokoza za mphatso yaulele yopatsidwa mwa cisomo cabe, popanda kucita zinthu zopangitsa munthu kuyenelela mphatsoyo. Timoteyo analandila mphatsoyi atasankhidwa kutumikila mpingo m’njila yapadela.—1 Tim. 4:14.

Kodi Timoteyo anafunika kucita ciani na mphatso imeneyi? Pamene anaŵelenga mawu akuti “uikolezele ngati moto,” iye ayenela kuti anaganizila za moto woyaka lawilawi, kuti nthawi zina umafika pokhala cabe makala ofiila a moto popanda malawi. Makala amenewo anafunika kukolezedwa kuti atulutse malawi na kuwonjezela kutentha. Dikishonale ina imakamba kuti liwu la Cigiliki (a·na·zo·py·reʹo) limene Paulo anaseŵenzetsa limatanthauza “kuutsanso, kupatsanso mphamvu, kubukitsanso moto,” mophiphilitsa kutanthauza “kukhalanso wofunitsitsa komanso wokangalika pa nchito ina yake.” Conco Paulo anali kulangiza Timoteyo kuti: ‘Ika mtima pa utumiki wako!’ Nafenso masiku ano tiyenela kucita cimodzi-modzi, inde kukangalika pa utumiki wathu.

“CUMA CAPADELA CIMENE ANACIIKA M’MANJA MWAKOCI, UCISUNGE”

Pamene Timoteyo anapitiliza kuŵelenga kalata yocokela kwa mnzake wapamtima imeneyo, anapeza mawu amene akanam’thandiza kucita bwino utumiki wake. Paulo analemba kuti: “Cuma capadela cimene anaciika m’manja mwakoci, ucisunge mothandizidwa ndi mzimu woyela umene uli mwa ife.” (2 Tim. 1:14) Kodi cuma cimeneco cinali ciani? Kodi ni cinthu cofunika kwambili citi cimene Timoteyo anapatsidwa? Mu vesi ya pambuyo, Paulo anakamba za “mawu olondola,” kutanthauza coonadi ca m’Malemba. (2 Tim. 1:13) Monga mtumiki wacikhristu, Timoteyo anafunika kulalikila coonadi mkati na kunja kwa mpingo. (2 Tim. 4:1-5) Komanso, Timoteyo anaikidwa kukhala mkulu kuti aŵete nkhosa za Mulungu. (1 Pet. 5:2) Timoteyo anafunika kusunga kapena kuti kuteteza cuma cake capadela—coonadi cimene anafunika kuphunzitsa—mwa kudalila mzimu woyela wa Yehova na Mawu ake.—2 Tim. 3:14-17.

Masiku ano, nafenso tinapatsidwa coonadi cimene timalengeza kwa ena. (Mat. 28:19, 20) Tingakhalebe oyamikila cuma cabwino cimeneci mwa kulimbikila kupemphela na kukulitsa cizoloŵezi ca kuphunzila Mawu a Mulungu. (Aroma 12:11, 12; 1 Tim. 4:13, 15, 16) Mwina tingakhalenso na mwayi wina wautumiki monga kukhala mkulu kapena kukhala mu utumiki wanthawi zonse. Kukhala na mwayi wocita utumiki wofunika ngati umenewo kuyenela kutipangitsa kukhala odzicepetsa, na kutilimbikitsa kudalila Mulungu. Conco tingasunge, kapena kuteteza cuma cathu cimeneci mwa kuuona kukhala wofunika utumikiwo na kudalila thandizo la Yehova kuti tiucite bwino.

‘ZIMENEZO UZIPHUNZITSE KWA AMUNA OKHULUPILIKA’

Utumiki umene Timoteyo anapatsidwa sunakhudze iye cabe. Unali kukhudzanso ena. Ndiye cifukwa cake Paulo analimbikitsa Timoteyo kuti: ‘Zinthu zimene unazimva kwa ine uziphunzitse kwa amuna okhulupilika amene nawonso, adzakhala oyenelela bwino kuphunzitsa ena.’ (2 Tim. 2:2) Inde, Timoteyo anafunika kuphunzitsa ena zimene anaphunzila kwa Akhristu ena. M’pofunika kwambili kuti woyang’anila aliyense mu mpingo wacikhristu aziyesetsa kucita zimenezi. Woyang’anila wabwino sacita nsanje na kubisa zimene amadziŵa kuti ena asadziŵe mocitila utumiki wina wake. M’malo mwake, amaphunzitsa ena kuti athe kuigwila bwino nchitoyo. Iye sawopa kuti mwina anthuwo adzam’posa mwa kukhala na cidziŵitso cacikulu kapena kuonetsa luso kuposa iye pa nchitoyo. Conco, woyang’anilayo saphunzitsa ena mwa patali-patali mocitila utumiki wina wake ayi. Iye amayesetsa kuthandiza amene akuwaphunzitsa kukulitsa luso la kupanga zosankha zoyenela, komanso kukhala wozindikila—kukula mwauzimu. Kucita zimenezi kudzathandiza kuti ‘amuna okhulupilika’ amene awaphunzitsawo akhale opindulitsa kwambili mu mpingo.

Mosakaikila, Timoteyo anaona kalata imene analandila kwa Paulo kukhala yofunika kwambili. N’zosakaikitsa kuti Timoteyo anaŵelenga uphungu wothandiza wa m’kalatayo mobweleza-bweleza, na kusinkha-sinkha mmene angauseŵenzetsele mu utumiki wake.

Nafenso tiyenela kuseŵenzetsa malangizo amenewa. Motani? Tingayesetse kukolezela mphatso yathu ngati moto, kusunga kapena kuti kuteteza cuma cathu capadela, komanso kugaŵilako ena cidziŵitso cimene tingakhale naco. Tikacita zimenezi, monga mmene Paulo anauzila Timoteyo, ‘tingakwanilitse mbali zonse za utumiki wathu.’—2 Tim. 4:5.