Kodi Kupemphera Kungakuthandizeni Bwanji?

Kodi Kupemphera Kungakuthandizeni Bwanji?

Munthu wina dzina lake Pamela anadwala kwambiri ndipo anapita kuchipatala. Koma anapempheranso kwa Mulungu kuti amupatse mphamvu yomuthandiza kupirira vutoli. Kodi kupempherako kunamuthandiza?

Pamela anapezeka ndi khansa ndipo anati: “Nthawi zambiri ndinkachita mantha ndikamalandira mankhwala a khansa. Koma ndikapemphera kwa Yehova Mulungu mtima unkakhala m’malo ndipo ndinkatha kuganiza bwino. Ndimavutikabe ndi ululu koma pemphero limandithandiza kuona zinthu moyenera. Anthu akandifunsa kuti, ‘Muli bwanji?’ ndimayankha kuti, ‘Sindikupeza bwino koma ndikusangalala.’”

Koma sitiyenera kudikira mpaka titakumana ndi vuto lalikulu kuti tipemphere. Tonsefe timakumana ndi mavuto, kaya aakulu kapena aang’ono, ndipo timafunika kuthandizidwa kuti tilimbane ndi mavutowo. Koma kodi kupemphera kungathandizedi?

Baibulo limanena kuti: “Umutulire Yehova nkhawa zako, ndipo iye adzakuchirikiza. Sadzalola kuti wolungama agwedezeke.” (Salimo 55:22) Lembali ndi lolimbikitsa kwambiri. Koma kodi kupemphera kungakuthandizeni bwanji? Mukamapemphera kwa Mulungu m’njira yovomerezeka, iye adzakupatsani zinthu zimene zingakuthandizeni kulimbana ndi mavuto anu.​—Onani bokosi lakuti “ Zimene Mungapeze Chifukwa Chopemphera.”