A António Guterres omwe ndi mlembi wamkulu wa bungwe la United Nations ananena kuti: “Tikukhala m’dziko lodzaza ndi mavuto.” Kodi inunso mukuona choncho?
Nkhani zimene timamvetsera, kuonera ndi kuwerenga, zimakhala ndi zinthu zambiri zodetsa nkhawa monga:
Matenda ndi miliri
Ngozi za m’chilengedwe
Umphawi ndi njala
Kuonongeka kwa mpweya ndi madzi komanso kutentha kwa dziko