Kodi Dzikoli Lidzatha?

Kodi Dzikoli Lidzatha?

Mwina mukudziwa kuti Baibulo limanena za mapeto a dzikoli. (1 Yohane 2:17) Kodi zimenezi zikutanthauza kuti padzikoli sipadzakhalanso anthu? Kodi dzikoli lidzakhala lopanda chamoyo chilichonse kapenanso lidzawonongedwa?

BAIBULO LIMAYANKHA KUTI AYI MAFUNSO AWIRI ONSEWA

Ndi zinthu ziti zimene sizidzatha?

ANTHU

Zimene Baibulo limanena: Mulungu ‘sanalenge [dzikoli] popanda cholinga, koma analiumba kuti anthu akhalemo.’—YESAYA 45:18.

DZIKO LAPANSI

Zimene Baibulo limanena: “M’badwo umapita ndipo m’badwo wina umabwera, koma dziko lapansi lidzakhalapobe mpaka kalekale.”—MLALIKI 1:4.

KODI ZIMENEZI ZIKUTANTHAUZA CHIYANI? Mogwirizana ndi zimene Baibulo limanena dzikoli silidzawonongedwa ndipo zamoyo zidzakhalamobe mpaka kalekale. Ndiye kodi tikamanena za mapeto a dzikoli timatanthauza chiyani?

TAGANIZIRANI IZI: Baibulo limayerekezera mapeto a dzikoli ndi zimene zinachitika m’masiku a Nowa. Pa nthawiyo dziko lapansi ‘linadzaza ndi chiwawa.’ (Genesis 6:13) Komabe Nowa anali munthu wolungama. Choncho Mulungu anapulumutsa Nowa ndi banja lake koma anawononga anthu onse oipa pogwiritsa ntchito madzi osefukira. Baibulo likamafotokoza zomwe zinachitika pa nthawiyo limanena kuti: “Dziko la pa nthawiyo linawonongedwa pamene linamizidwa ndi madzi.” (2 Petulo 3:6) Amenewa anali mapeto a dziko la pa nthawiyo. Ndiye kodi n’chiyani chimene chinawonongedwa? Anthu oipa ndi amene anawonongedwa osati dziko lapansili. Ndiye Baibulo likamanena za mapeto a dzikoli silinena za kuwonongedwa kwa dziko lenilenili. Koma limanena za kuwonongedwa kwa anthu oipa amene ali padzikoli ndi maboma onse amene anawakhazikitsa.

Ndi zinthu ziti zimene zidzatha?

MAVUTO KOMANSO ZINTHU ZOIPA

Zimene Baibulo limanena: “Patsala kanthawi kochepa, woipa sadzakhalakonso. Udzayang’ana pamene anali kukhala, ndipo sadzapezekapo. Koma anthu ofatsa adzalandira dziko lapansi, ndipo adzasangalala ndi mtendere wochuluka.”​—SALIMO 37:10, 11.

KODI ZIMENEZI ZIKUTANTHAUZA CHIYANI? Chigumula cha nthawi ya Nowa sichinathetseretu zoipa zonse. Pambuyo pa chigumulachi, anthu oipa anayamba kuchita zinthu zoipa zomwe zinkasowetsa mtendere anthu ena. Posachedwapa Mulungu athetsa zoipa zonse. Mogwirizana ndi zimene wolemba masalimo ananena: “Woipa sadzakhalakonso.” Mulungu adzathetsa zoipa zonse pogwiritsa ntchito Ufumu wake. Ufumuwu ndi boma lomwe lili kumwamba ndipo udzalamulira anthu omvera Mulungu padzikoli.

TAGANIZIRANI IZI: Kodi anthu amene akulamulira dzikoli panopa adzasangalala kuti Ufumu wa Mulungu uyambe kulamulira? Baibulo limasonyeza kuti sadzasangalala. Iwo adzachita zinthu mopanda nzeru polimbana ndi Ufumu wa Mulungu. (Salimo 2:2) Ndiye kodi zotsatira zake zidzakhala zotani? Ufumu wa Mulungu udzalowa m’malo mwa maboma onse a anthu “ndipo udzakhalapo mpaka kalekale.” (Danieli 2:44) Koma n’chifukwa chiyani ulamuliro wa anthu ukufunikira kutha?

Ulamuliro wa Anthu Ukufunikira Kutha

Zimene Baibulo limanena: “Munthu amene akuyenda alibe ulamuliro wowongolera mapazi ake.”​—YEREMIYA 10:23.

KODI ZIMENEZI ZIKUTANTHAUZA CHIYANI? Anthu sanalengedwe kuti azidzilamulira. Iwo salamulira bwino anzawo ndipo amalephera kuthetsa mavuto awo.

TAGANIZIRANI IZI: Malinga ndi zimene zinalembedwa pamalo ena ofufuzira nkhani, “zikuoneka kuti maboma a anthu alephera kuthetsa mavuto apadziko lonse monga umphawi, njala, matenda, ngozi za m’chilengedwe, nkhondo kapenanso zachiwawa. Anthu ena amakhulupirira kuti mavuto onse amene ali padzikoli angatheretu patakhala boma limodzi lokha lolamulira dziko lonse lapansi.” (Britannica Academic) Komabe, ngakhale maboma onse apadzikoli atapanga mgwirizano, olamulira dzikoli angakhalebe anthu ochimwa omwewo, amene sangathetse mavuto onse amene tawatchulawa. Ufumu wa Mulungu ndi boma lokhalo limene lili ndi mphamvu yothetseratu mavuto onse amene akuchitika padzikoli.

Mogwirizana ndi zimene Baibulo limanena anthu abwino sakufunikira kuchita mantha akaganizira za mapeto a dzikoli, kapena kuti maulamuliro a anthu amene alipowa. M’malomwake tiziyembekezera mwachidwi nthawi imeneyi chifukwa dziko loipa lakaleli lidzalowedwa m’malo ndi dziko latsopano la Mulungu lomwe ndi labwino kwambiri.

Kodi zimenezi zidzachitika liti? Baibulo liyankha funso limeneli munkhani yotsatira.