Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Mungakonzekele palipano kuti mudzakhalemo m’dziko labwino limene lili pafupi

Dziko Latsopano la Paradaiso Limene Lili Pafupi!

Dziko Latsopano la Paradaiso Limene Lili Pafupi!

Mulungu analenga dziko lapansi n’colinga cakuti anthu olungama akhalemo kwamuyaya. (Salimo 37:29) Iye anaika mwamuna na mkazi oyambilila, Adamu na Hava m’munda wokongola wochedwa Edeni. Ndipo anthuwo pamodzi na ana awo anawapatsa udindo wolima nthaka na kusamalila dziko lapansi.—Genesis 1:28; 2:15.

Masiku ano, dziko lapansi si Paradaiso monga mmene Mulungu anali kufunila. Koma Mulungu sanasinthe maganizo ake. Kodi iye adzakwanilitsa bwanji colinga cake capoyamba? Monga taonela m’nkhani zapita, Mulungu sadzawononga dziko lapansili. M’malomwake, adzalola anthu okhulupilika kukhalamo. Kodi zinthu zidzakhala bwanji padziko lapansi Mulungu akadzakwanilitsa malonjezo ake?

Boma limodzi lidzalamulila dziko lonse lapansi

Posacedwa, boma latsopano lakumwamba la Mulungu lidzayamba kulamulila mtundu wonse wa anthu. Zikadzatelo, dziko lapansi lidzakhala malo osangalatsa, mmene anthu adzakhala ogwilizana, ndipo azidzagwila nchito yabwino komanso yokhutilitsa. Mulungu anasankha Yesu Khristu kuti adzalamulile dziko lapansi. Mosiyana na olamulila ambili a masiku ano, Yesu nthawi zonse adzaticitila zabwino. Iye adzalamulila mwacikondi, ndipo adzakhala mfumu yokoma mtima, yacifundo, komanso yacilungamo.—Yesaya 11:4.

Anthu onse padziko lapansi adzakhala ogwilizana

Anthu padziko lapansi sadzakhala ogaŵanika cifukwa cosiyana mitundu kapena maiko amene akhala. Mtundu wonse wa anthu udzakhala wogwilizana. (Chivumbulutso 7:9, 10) Anthu onse okhala padziko lapansi adzakhala okonda Mulungu komanso okonda anzawo. Iwo adzagwila nchito mwamtendele komanso mogwilizana kuti akwanilitse colinga ca Mulungu capoyamba cakuti asamalile dziko lapansi, malo awo okhala.—Salimo 115:16.

Anthu sadzawononganso cilengedwe

Ufumu wa Mulungu ukadzayamba kulamulila, Mlengi adzalamulila zinthu zonse m’cilengedwe kuti nyengo iziyenda bwino. (Salimo 24:1, 2) Pamene Yesu analetsa cimphepo coopsa ali padziko lapansi, anaonetsa zimene adzakwanitsa kucita cifukwa ca mphamvu zimene Mulungu anam’patsa. (Maliko 4:39, 41) Mu ulamulilo wa Khristu, palibe munthu amene adzaopa matsoka a zacilengedwe. Ufumu wa Mulungu ukadzayamba kulamulila, anthu adzakhala mwamtendele na zinyama, komanso sadzawononga cilengedwe.—Hoseya 2:18.

Thanzi labwino na cakudya coculuka

Munthu aliyense adzakhala na thanzi labwino. Palibe amene adzadwala, kukalamba, kapena kufa. (Yesaya 35:5, 6) Anthu adzakondwela kukhala m’dziko lokongola ndi laukhondo ngati munda wa Edeni, malo amene mwamuna na mkazi oyambilila anali kukhala. Monga zinalili mu Edeni, m’dziko latsopano nthaka idzapeleka zakudya zoculuka. Ndipo anthu padziko lapansi adzakhala na cakudya camwanaalilenji. (Genesis 2:9) Mofanana na mtundu wa Mulungu wa Aisiraeli akale, aliyense m’Paradaiso adzadya ‘mkate wake ndi kukhuta.’—Levitiko 26:4, 5

Mtendele weni-weni na citetezo

M’boma la Mulungu limene lidzalamulila dziko lonse, anthu onse adzakhala mwamtendele, ndipo adzacitilana zinthu mokoma mtima komanso mwacilungamo. Sikudzakhala nkhondo, kuseŵenzetsa ulamulilo molakwika, ndiponso sikudzakhala kuvutika kusakila zofunikila paumoyo. Baibo imakamba kuti: “Aliyense adzakhala pansi pa mtengo wake wa mpesa ndi mtengo wake wa mkuyu ndipo sipadzakhala wowaopsa.”—Mika 4:3, 4.

Nyumba zokwanila na nchito yokhutilitsa

Banja lililonse lidzakhala na nyumba popanda kuopa kuti mwina adzacotsedwamo. Ndipo nchito iliyonse imene tidzagwila idzakhala yopindulitsa. Monga mmene Baibo imakambila, anthu amene adzakhala m’dziko latsopano la Mulungu, “sadzagwila nchito pacabe” kapena kuti popanda kupeza phindu.—Yesaya 65:21-23.

Maphunzilo abwino

Baibo imakamba kuti: “Dziko lapansi lidzadzaza ndi anthu odziwa Yehova.” (Yesaya 11:9.) Anthu amene adzakhala m’dziko lolamulidwa na Ufumu wa Mulungu, adzaphunzila zambili kwa Mlengi wawo Yehova, amene ali na nzelu zopanda malile. Adzaphunzilanso zambili zokhudza zinthu zokongola zimene iye analenga. Iwo sadzaseŵenzetsa nzelu zawo kuti apange zida zomenyela nkhondo kapena kuti avulaze anzawo. (Yesaya 2:4) M’malomwake, adzaphunzila mmene angakhalile mwamtendele na ena, komanso mmene angasamalile dziko lapansi.—Salimo 37:11.

Moyo wosatha

Mulungu analikonza bwino kwambili dziko lapansi n’colinga cakuti tizisangalala na umoyo tsiku lililonse. Iye amafuna kuti anthufe tidzakhale na moyo kwamuyaya padziko lapansi. (Salimo 37:29; Yesaya 45:18) Pofuna kukwanilitsa colinga cake cimeneci, Mulungu “adzameza imfa kwamuyaya.” (Yesaya 25:8) “Imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulila, kapena kubuula, ngakhale kupweteka,” imatelo Baibo. (Chivumbulutso 21:4) Mulungu adzapeleka mwayi wokhala na moyo wosatha kwa anthu amene adzawapulumutsa pamene adzawononga dziko loipali. Adzapelekanso mwayi umenewo kwa anthu osaŵelengeka amene adzawaukitsa kwa akufa m’dziko latsopano limene likubwela.—Yohane 5:28, 29; Machitidwe 24:15.

Pano tikamba, anthu mamiliyoni akukonzekela kudzakhala m’dziko lolamulidwa na Ufumu wa Mulungu limene lili pafupi kwambili. Ngakhale kuti ni opanda ungwilo, iwo akuyesetsa kukhala mtundu wa anthu amene Mulungu amafuna kuti adzakhale m’dziko latsopano. Kodi iwo akucita motani zimenezi? Mwa kuphunzila za Yehova Mulungu komanso za Yesu Khristu amene iye anamutuma.—Yohane 17:3.

Dziŵani zambili za mmene mungapulumukile mapeto a dzikoli na kudzakhala m’dziko labwino limene likubwela. Phunzilani Baibo kwaulele na wa Mboni za Yehova, pogwilitsa nchito buku la Kondwelani na Moyo Kwamuyaya!