Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Malangizo Odalirika Okhudza Tsogolo Labwino Tingawapeze Kuti?

Kodi Malangizo Odalirika Okhudza Tsogolo Labwino Tingawapeze Kuti?

Monga mmene taonera munkhani zapitazi, anthu akhala akuganiza kuti zinthu monga kukhulupirira mwayi, maphunziro, chuma komanso kungokhala munthu wabwino n’zimene zingawathandize kukhala ndi tsogolo labwino. Kugwiritsa ntchito njira zimenezi kuli ngati kupita kumalo amene sitikuwadziwa pogwiritsa ntchito mapu olakwika. Kodi zimenezi zikutanthauza kuti palibe malangizo odalirika otithandiza kudziwa za tsogolo lathu? Tiyeni tione.

KUMENE TINGAPEZE MALANGIZO ODALIRIKA

Tikamafuna kusankha zochita pa nkhani inayake, nthawi zambiri timafunsira nzeru kwa munthu wamkulu komanso wanzeru kuposa ifeyo. Mofananamo, tingapeze malangizo odalirika okhudza tsogolo lathu kuchokera kwa winawake yemwe ndi wamkulu komanso wanzeru kuposa ifeyo. Malangizo amenewa tingawapeze m’buku lomwe linayamba kulembedwa zaka 3,500 zapitazo. Buku limeneli limatchedwa Baibulo.

Kodi Baibulo ndi lodalirika chifukwa chiyani? Baibulo ndi buku lodalirika chifukwa amene analilemba ndi wamkulu komanso wanzeru kwambiri m’chilengedwe chonse. Iye amatchedwa “Wamasiku Ambiri” ndipo wakhalapo “kuyambira kalekale mpaka kalekale.” (Danieli 7:9; Salimo 90:2) Iye ndi “Mlengi wa kumwamba, Mulungu woona, amene anaumba dziko lapansi.” (Yesaya 45:18) Kudzera m’buku lakeli, amatiuza kuti dzina lake ndi Yehova.​—Salimo 83:18.

Baibulo silinena kuti chikhalidwe kapena mtundu winawake wa anthu ndi wabwino kuposa mitundu ina. Zili choncho chifukwa tinalengedwa ndi Mulungu yemwe analenga anthu onse. Malangizo ake ndi othandiza nthawi zonse ndipo athandiza kwambiri anthu m’mayiko onse. Baibulo limapezeka m’zinenero zambiri ndipo lafalitsidwa kwambiri kuposa buku lina lililonse. * Choncho munthu wina aliyense akhoza kuliwerenga n’kupindula ndi malangizo ake. Zimenezi zikugwirizana ndi zimene Baibulo limanena. Limati:

“Mulungu alibe tsankho. Iye amalandira munthu wochokera mu mtundu uliwonse, amene amamuopa ndi kuchita chilungamo.”—MACHITIDWE 10:34, 35.

Mofanana ndi kholo limene limakonda komanso kupereka malangizo kwa ana ake, Yehova Mulungu yemwe ndi atate wachikondi amatipatsa malangizo kudzera m’Mawu ake Baibulo. (2 Timoteyo 3:16) Choncho mungakhulupirire Mawu ake chifukwa chakuti iyeyo ndi amene anatilenga ndipo amadziwa bwino zinthu zimene zingatithandize kuti tizisangalala.

Kodi mungatani kuti mudzalandire nawo madalitso amenewa? Werengani nkhani yotsatira kuti muone zimene mungachite.

^ ndime 6 Kuti mudziwe zambiri pa nkhani ya kumasulira komanso kufalitsidwa kwa Baibulo, pitani pa www.pr418.com pamene palembedwa kuti ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA > MBIRI KOMANSO BAIBULO.

^ ndime 16 Kuti mudziwe zambiri, onani mutu 9 wa buku lakuti, Baibulo​—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova. Bukuli likupezeka pawebusaiti yathu ya www.pr418.com pamene alemba kuti LAIBULALE > MABUKU.