Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

N’ciani Cingatithandize Kukhala na Tsogolo Labwino?

N’ciani Cingatithandize Kukhala na Tsogolo Labwino?

Monga taonela m’nkhani zapita, anthu amayesa kudzikonzela tsogolo labwino mwa kukhulupilila zinthu monga mphamvu inayake imene amati ndiyo imayendetsa zocitika pa umoyo wawo, maphunzilo, cuma, komanso kukhala munthu wabwino. Koma kucita zinthu zimenezi kuli ngati kuseŵenzetsa mapu yolakwika imene ingasoceletse munthu paulendo. Kodi izi zitanthauza kuti palibe malangizo odalilika amene angatithandize kukhala na tsogolo labwino? Iyai!

MALANGIZO OCOKELA KWA WINAWAKE WANZELU KWAMBILI

Popanga zisankho, nthawi zambili timafunsila malangizo kwa munthu wamkulu komanso wanzelu kuposa ife. Mofananamo, tingapeze malangizo odalilika otithandiza kukhala na tsogolo labwino kucokela kwa Winawake wamkulu komanso wanzelu kwambili kuposa ife. Malangizo ake tingawapeze m’buku limene linayamba kulembedwa zaka pafupifupi 3,500 zapitazo. Buku limenelo limachedwa Baibo.

N’cifukwa ciani muyenela kuikhulupilila Baibo? Cifukwa Mlembi wake ni wamkulu ndiponso wanzelu kwambili m’cilengedwe conse. Iye amachedwa “Wamasiku Ambili,” amene wakhalapo “kuyambila kalekale mpaka kalekale.” (Danieli 7:9; Salimo 90:2) Ni “Mlengi wa kumwamba, Mulungu woona, amene anaumba dziko lapansi ndi kulipanga.” (Yesaya 45:18) Iye amatiuza kuti dzina lake ni Yehova.—Salimo 83:18.

Cifukwa cakuti Baibo ni yocokela kwa Mlengi wa anthu onse, sionetsa kuti anthu a mtundu wina kapena a cikhalidwe cina ni apamwamba kuposa ena. Malangizo ake amathandiza nthawi zonse, ndipo apindulitsa anthu kulikonse padzikoli. Baibo imapezeka m’zinenelo zambili, ndipo yafalitsidwa kwambili kuposa buku lina lililonse. * Conco anthu kulikonse angathe kuiŵelenga na kupeza malangizo amene angawathandize pa umoyo wawo. Izi zigwilizana na zimene Baibo imakamba zakuti:

“Mulungu alibe tsankho. Iye amalandila munthu wocokela mu mtundu uliwonse, amene amamuopa ndi kucita cilungamo.”—MACHITIDWE 10:34, 35.

Mofanana na kholo limene limapeleka malangizo kwa ana ake, Yehova Mulungu ni Tate wacikondi amene amatithandiza kupitila m’Mawu ake Baibo. (2 Timoteyo 3:16) Tingadalile Mawu ake cifukwa iye ndiye anatilenga, ndipo amadziŵa zimene zingatithandize kukhala na umoyo wabwino.

Kodi mungacite ciani kuti mukhale na tsogolo labwino conco? Ŵelengani nkhani yotsatila.

^ ndime 6 Kuti mudziŵe zambili zokhudza nchito yomasulila Baibo na kufalitsidwa kwake, pitani pa www.pr418.com na kuona pa ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA > MBILI KOMANSO BAIBULO.

^ ndime 16 Kuti mudziŵe zambili, onani mutu 9 m’buku lakuti Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu? lofalitsidwa na Mboni za Yehova. Bukuli lipezekanso pa webusaiti yathu ya www.pr418.com. Pitani ku Chichewa pa LAIBULALE > MABUKU NDI ZINTHU ZINA.