Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Mawu opezeka pa mwala: “Utembeleledwe na Yahweh Sabaot, iwe Hagaf mwana wa Hagav.”

Kodi Mudziŵa?

Kodi Mudziŵa?

Kodi zolemba zamakedzana zimacilikiza bwanji zimene Baibo imakamba?

M’MIZIYAMU ya ku Yerusalemu yochedwa Bible Lands Museum, muli mwala umene uli na zolemba zimene zinalembedwa kale-kale pakati pa zaka za mu 700 na 600 B.C.E. Mwalawo anaupeza m’phanga la manda kufupi na mzinda wa Hebron ku Israel. Zolembazo zinali na mawu akuti: “Utembeleledwe na Yahweh Sabaot, iwe Hagaf mwana wa Hagav.” Kodi mawuwa acilikiza bwanji zimene Baibo imakamba? Mawuwa aonetsa kuti dzina la Mulungu lakuti Yehova, lolembedwa na zilembo za YHWH m’Ciheberi cakale, linali lodziŵika bwino ndipo anthu anali kulichula mu umoyo wawo wa tsiku na tsiku m’nthawi za m’Baibo. Zolemba zina zopezeka m’mapanga a manda amenewo, zionetsa kuti anthu anali kuseŵenzetsa mapanga monga malo okumanako, komanso obisalako. Ndipo nthawi zambili iwo anali kulemba dzina la Mulungu pa zipupa pamodzi na maina a anthu okhala na dzina la Mulungu.

Pokamba za zolemba zimenezi, katswili wina, Dr. Rachel Nabulsi wa pa Yunivesiti ya ku Georgia anakamba kuti: “Kuseŵenzetsedwa kwa dzina lakuti YHWH mobweleza-bweleza n’kofunika kwambili. . . . Zolemba zimenezi zionetsa kuti Aisiraeli na Ayuda anali kuona kufunika kwa mwini dzina lakuti YHWH mu umoyo wawo.” Izi zimagwilizana na Baibo, cifukwa dzina la Mulungu lolembedwa kuti YHWH m’Ciheberi, limapezeka maulendo masauzande m’Baibo. Ndipo nthawi zambili, maina a anthu anali kukhala na dzina la Mulungu.

Mawu akuti “Yahweh Sabaot,” opezeka pa mwala uja, atanthauza “Yehova wa makamu.” Izi zionetsa kuti dzina la Mulungu komanso mawu akuti “Yehova wa makamu” anali kuseŵenzetsedwa kaŵili-kaŵili m’nthawi za m’Baibo. Izi zigwilizana na Baibo pa kuseŵenzetsa mawu akuti “Yehova wa makamu,” amene amapezeka maulendo oposa 250 m’Malemba a Ciheberi, makamaka m’buku la Yesaya, Yeremiya, komanso Zekariya.