Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 4

Pitilizani Kuonetsana Cikondi Ceni-ceni

Pitilizani Kuonetsana Cikondi Ceni-ceni

“Pokonda abale, khalani ndi cikondi ceniceni pakati panu.” —AROMA 12:10

NYIMBO 109 Tizikondana ndi Mtima Wonse

ZIMENE TIKAMBILANE *

1. N’ciani cionetsa kuti anthu m’mabanja ambili sakondana masiku ano?

BAIBO inanenelatu kuti m’masiku otsiliza anthu adzakhala “osakonda acibale awo.” (2 Tim. 3:1, 3) Masiku ano timakuona kukwanilitsidwa kwa ulosi umenewu. Mwacitsanzo, mabanja mamiliyoni ambili amasokonezeka cifukwa cosudzulana. Cikwati cikatha, makolowo amakhala okwiilana kwambili, ndipo ana amaona kuti sakondedwa. Ngakhale anthu a m’banja limodzi amene amakhala m’nyumba imodzi zingatheke kuti sagwilizana kweni-kweni. Mlangizi wina wa za mabanja anati: “Amayi, atate, komanso ana, kaŵili-kaŵili sacitila zinthu pamodzi. M’malomwake, amatangwanika kwambili na kompyuta, tabuleti, foni, kapena maseŵela a pa kompyuta. Ngakhale kuti anthu amenewa amakhala m’nyumba imodzi, sadziŵana bwino.”

2-3. (a) Malinga na Aroma 12:10, kodi tiyenela kuonetsa ndani cikondi ceni-ceni? (b) Nanga tikambilane ciani m’nkhani ino?

2 Koma sitifuna kutengela mzimu wa dziko wopanda cikondi. (Aroma 12:2) M’malomwake, tiyenela kuonetsa cikondi ceni-ceni kwa a m’banja lathu, maka-maka kwa abale na alongo athu a m’cikhulupililo. (Ŵelengani Aroma 12:10.) Kodi cikondi ceni-ceni n’ciani? Mawuwa amakamba za ubale wolimba wapakati pa anthu a m’banja limodzi. Cikondi cotelo n’cimene tiyenela kukulitsa m’banja lathu lauzimu, inde pakati pa abale na alongo athu acikhristu. Ngati tionetsa cikondi ceni-ceni, tidzathandiza kusunga mgwilizano, umene ni wofunika kwambili pa kulambila koona.—Mika 2:12.

3 Potithandiza kukhala na cikondi cimeneci na mmene tingacionetsele kwa ena, tiyeni tione zimene tingaphunzile ku zitsanzo za m’Baibo.

“YEHOVA NDI WACIKONDI CACIKULU”

4. Kodi Yakobo 5:11 itithandiza bwanji kudziŵa ukulu wa cikondi ca Yehova?

4 Baibo imatiuza makhalidwe abwino a Yehova. Mwacitsanzo, imatiuza kuti “Mulungu ndiye cikondi.” (1 Yoh. 4:8) Mawu amenewa cabe ni okopa cakuti timafuna kumuyandikila. Koma Baibo imakambanso kuti “Yehova ndi wacikondi cacikulu.” (Ŵelengani Yakobo 5:11) Izi zionetsa kuti Yehova ali na cikondi cacikulu pa ife!

5. Kodi Yehova amaonetsa bwanji cifundo? Nanga tingatengele bwanji citsanzo cake?

5 Onani kuti Yakobo 5:11 ichula cikondi cacikulu ca Yehova pamodzi na khalidwe la cifundo, limene limatipangitsanso kufuna kumuyandikila. (Eks. 34:6) Imodzi mwa njila zimene Yehova amationetsela cifundo ni mwa kutikhululukila zolakwa zathu. (Sal. 51:1) M’Baibo, mawu akuti cifundo amaphatikizapo zambili osati cabe kukhululukila ena. Cifundo ni mmene munthu amakhudzikila mtima kwambili akaona wina akuvutika, ndipo amakakamizika kucitapo kanthu kuti am’thandize munthuyo. Yehova amanena kuti ni wofunitsitsa kwambili kutithandiza, kuposa ngakhale mmene mayi amamvelela pofuna kuthandiza mwana wake. (Yes. 49:15) Tikamavutika, mwa cifundo cake Yehova amakhudzika kuti atithandize. (Sal. 37:39; 1 Akor. 10:13) Tingaonetse cifundo abale na alongo athu mwa kuwakhululukila, komanso kupewa kuwasungila cakukhosi akatilakwila. (Aef. 4:32) Koma njila yaikulu imene tingaonetsele cifundo, ni mwa kuthandiza abale na alongo athu akakhala pa mavuto. Ngati timaonetsa cifundo kwa ena cifukwa cowakonda, ndiye kuti tikutengela Yehova amene ni citsanzo capamwamba kwambili pa kuonetsa cifundo.—Aef. 5:1.

YONATANI NA DAVIDE ANAKHALA MABWENZI ‘OGWILIZANA KWAMBILI’

6. Kodi Yonatani na Davide anaonetsana bwanji cikondi cacikulu?

6 M’Baibo muli zitsanzo za anthu opanda ungwilo amene anaonetsa ceni-ceni. Ganizilani citsanzo ca Yonatani na Davide. Baibo imati: “Yonatani anagwilizana kwambili ndi Davide, moti anayamba kukonda Davide ngati mmene anali kudzikondela yekha.” (1 Sam. 18:1) Davide anadzozedwa kuti aloŵe m’malo Sauli kukhala mfumu. Pambuyo pake, Sauli anacitila nsanje Davide cakuti anafuna kumupha. Koma Yonatani mwana wa Sauli sanakhale kumbali ya atate ake pa ciwembu cofuna-funa Davide kuti amuphe. Yonatani na Davide analonjezana kuti adzakhalabe mabwenzi na kucilikizana nthawi zonse.—1 Sam. 20:42.

Kusiyana kwa zaka sikunalepheletse Yonatani na Davide kuonetsana cikondi cacikulu (Onani ndime 6-9)

7. Kodi cimodzi mwa zifukwa zimene zikanalepheletsa Yonatani na Davide kukhala mabwenzi n’citi?

7 Cikondi cacikulu cimene cinali pakati pa Yonatani na Davide n’cocititsa cidwi kwambili tikaganizila zifukwa zina zimene zikanawalepheletsa kukhala mabwenzi. Mwacitsanzo, Yonatani anali wamkulu ngati zaka 30 kuposa Davide. Yonatani akanaganiza kuti sangakhale paubwenzi wolimba na munthu wamng’ono amene sadziŵa zambili mu umoyo. Koma iye sanatelo. Ndiponso sanaone Davide kukhala wosafunika kapena kucita naye zinthu mom’delela ayi.

8. N’cifukwa ciani muona kuti Yonatani anali bwenzi labwino kwambili kwa Davide?

8 Yonatani akanatha kucitila nsanje Davide. Monga mwana wa Mfumu Sauli, iye akanaumilila kuti ndiye woyenelela kuloŵa ufumu wa atate ake. (1 Sam. 20:31) Koma Yonatani anali wodzicepetsa, ndipo anali wokhulupilika kwa Yehova. Conco, iye anacilikiza Davide na mtima wonse podziŵa kuti Yehova ndiye anam’sankhilatu kukhala mfumu yakutsogolo. Iye analinso wokhulupilika kwa Davide, ngakhale kuti kucita zimenezi kunaputa mkwiyo wa Sauli.—1 Sam. 20:32-34.

9. Kodi Yonatani anali kuona Davide monga wopikisana naye? Fotokozani.

9 Yonatani anali na cikondi cacikulu pa Davide. Conco sanamuone monga wopikisana naye. Yonatani anali waluso polasa mivi na uta, ndipo anali msilikali wolimba mtima. Iye na atate ake, Sauli, anali kudziŵika kuti anali “aliwilo kuposa ciwombankhanga,” komanso “amphamvu kuposa mikango.” (2 Sam. 1:22, 23) Conco, Yonatani akanadzitukumula cifukwa ca zipambano zake. Komabe, analibe mzimu wa mpikisano ndipo sanam’citile nsanje Davide. M’malomwake, anali kucita cidwi na kulimba mtima kwa Davide, komanso kudalila kwake Yehova. Ndipo n’zocititsa cidwi kuti pamene Davide anapha Goliyati, Yonatani anayamba kukonda kwambili Davide monga mmene anali kudzikondela iye mwini. Kodi tingaonetse bwanji cikondi cacikulu cotelo kwa abale na alongo athu?

KODI TINGAONETSANE BWANJI CIKONDI CENI-CENI MASIKU ANO?

10. Kodi ‘kukondana kwambili kucokela mu mtima’ kumatanthauza ciani?

10 Baibo imatiuza kuti ‘tizikondana kwambili kucokela mu mtima.’ (1 Pet. 1:22) Yehova amapeleka citsanzo cabwino kwa ife. Cikondi cake n’cacikulu kwambili, cakuti tikakhalabe okhulupilika kwa iye, adzapitiliza kutikonda mpaka kale-kale. (Aroma 8:38, 39) Liwu la Cigiliki limene linamasulidwa kuti “kwambili” lili na lingalilo la “kunyindilila” kapena kuti “kuyesetsa.” Nthawi zina tingafunike kuyesetsa kapena kuti kulimbikila kuti tionetse cikondi ceni-ceni kwa okhulupilila anzathu. Ena akatikhumudwitsa tiyenela kupitiliza ‘kulolelana m’cikondi na kuyesetsa ndi mtima wonse kusunga umodzi wathu mwa mzimuwo ndi mwamtendele monga comangila cotigwilizanitsa.’ (Aef. 4:1-3) Ngati tiyesetsa kusunga ‘mtendele monga comangila cotigwilizanitsa,’ sitidzasumika maganizo pa zifooko za abale athu. Tidzayesetsa kuona abale athu mmene Yehova amawaonela.—1 Sam. 16:7; Sal. 130:3.

Eodiya na Suntuke analimbikitsidwa kukhala amaganizo amodzi. Nafenso nthawi zina cingativute kugwilizana na abale na alongo athu (Onani ndime 11)

11. N’cifukwa ciani cimakhala covuta nthawi zina kuonetsana cikondi ceni-ceni?

11 Nthawi zina zimakhala zovuta kuonetsa cikondi ceni-ceni kwa abale na alongo athu, maka-maka ngati timadziŵa zifooko zawo. Zioneka kuti Akhristu ena m’nthawi ya atumwi analinso na vuto limeneli. Mwacitsanzo, zioneka kuti cinali cosavuta Eodiya na Suntuke kugwila nchito “limodzi ndi [Paulo] pa nchito ya uthenga wabwino.” Koma pa zifukwa zina, cinakhala covuta kwa Eodiya na Suntuke kukhala ogwilizana. Mwa ici, Paulo anawalimbikitsa kuti “akhale amaganizo amodzi mwa Ambuye.”—Afil. 4:2, 3.

Akulu acinyamata komanso acikulile angakhale paubwenzi wolimba (Onani ndime 12)

12. Kodi tingaonetse bwanji cikondi cacikulu kwa abale na alongo athu?

12 Kodi tingaonetse bwanji cikondi cacikulu kwa abale na alongo athu masiku ano? Tikawadziŵa bwino Akhristu anzathu, cimakhala cosavuta kuwamvetsa, na kuwaonetsa cikondi ceni-ceni. Tingakhale nawo paubwenzi mosasamala kanthu za msinkhu kapena cikhalidwe cawo. Kumbukilani kuti Yonatani anali wamkulu na zaka pafupifupi 30 kuposa Davide. Ngakhale n’telo, iye anakhala naye paubwenzi wolimba. Kodi pali wina mu mpingo mwanu amene ni wamkulu kapena wamng’ono pa imwe, amene mungam’pange bwenzi lanu? Mukacita zimenezi, mudzaonetsa kuti ‘mumakonda gulu lonse la abale.’—1 Pet. 2:17.

Onani ndime 12 *

13. N’cifukwa ciani sitingakhale woyandikana cimodzimodzi na aliyense mu mpingo?

13 Kodi kuonetsa cikondi cacikulu kwa okhulupilila anzathu, kutanthauza kuti aliyense mumpingo tidzakhala oyandikana naye mofanana? Ayi, zimenezo n’zosatheka. Sikulakwa kukhala woyandikana kwambili na anthu ena kuposa ena, mwina cifukwa cokonda zinthu zofanana. Yesu anacha atumwi ake onse kuti “mabwenzi,” koma anali kukonda kwambili Yohane. (Yoh. 13:23; 15:15; 20:2) Ngakhale n’telo, Yesu sanali kucita zinthu mokondela Yohane ayi. Mwacitsanzo, Yohane na m’bale wake Yakobo atapempha malo apamwamba mu Ufumu wa Mulungu, Yesu anawauza kuti: “Kunena zokhala kudzanja langa lamanja kapena lamanzele, si ine wopeleka mwayi umenewo.” (Maliko 10:35-40) Potengela citsanzo ca Yesu, ifenso sitiyenela kucita zinthu mokondela mabwenzi athu apamtima. (Yak. 2:3, 4) Kucita zimenezi kungabweletse mzimu wa magaŵano, umene ulibe malo mu mpingo wacikhristu.—Yuda 17-19.

14. Malinga na Afilipi 2:3, n’ciani cingatithandize kupewa mzimu wa mpikisano?

14 Tikamaonetsana cikondi ceni-ceni, tidzateteza mpingo ku mzimu wa mpikisano. Kumbukilani kuti Yonatani sanayese kupikisana na Davide. Sanamuone monga wopikisana naye pa mpando wacifumu. Tonsefe tingatengele citsanzo ca Yonatani. Musaone anchito anzanu kukhala opikisana nawo cifukwa ca maluso awo, ‘koma modzicepetsa onani ena kukhala okuposani.’ (Ŵelengani Afilipi 2:3.) Kumbukilani kuti aliyense pali zimene angacite pothandiza mpingo. Tikakhalabe odzicepetsa, tidzaona zabwino mwa abale na alongo athu, na kupindula na citsanzo ca kukhulupilika kwawo.—1 Akor. 12:21-25.

15. Kodi mwaphunzilapo ciani pa cocitika ca mlongo Tanya na banja lake?

15 Mavuto osayembekezeleka akatigwela, Yehova amatitonthoza kupitila mwa abale na alongo athu. Iwo amationetsa cikondi ceni-ceni, na kutipatsa thandizo lofunikila. Ganizilani zimene zinacitikila banja lina pa Ciŵelu pambuyo pa Msonkhano wa Maiko wa mu 2019, umene unacitikila ku America, wa mutu wakuti “Cikondi Sicitha!” Mlongo Tanya, mayi wa ana atatu anati: “Pamene tinali kubwelela ku hotela pa galimoto, galimoto ina inataya msewu n’kubwela kumbali yathu, na kugunda galimoto yathu. Palibe amene anavulala, ndipo tinacoka m’galimoto na kuimilila pa msewu tili odabwa. Ndiyeno munthu wina m’mbali mwa msewu anali kutikodola kuti tikaloŵe m’galimoto yake. Anapezeka kuti ni m’bale amene tinali naye ku msonkhano umenewo. Ndipo si iye yekha amene anaima. Abale athu asanu ocokela ku Sweden nawonso anaima. Alongo anakumbatila ine na mwana wanga mokhudzika mtima. Ndipo n’zimene tinali kufunikila panthawiyo! N’nawatsimikizila kuti tidzakhala bwino, koma iwo sanatisiye. Anakhalabe nafe mpaka pamene opeleka cithandizo ca kucipatala anafika. Abalewo anaonetsetsa kuti tili na zonse zofunikila. Panthawi yonse imene tinali pa vutoli, tinaona cikondi ca Yehova. Cocitikaco cinazamitsa cikondi cathu pa abale na alongo athu, komanso kukulitsa cikondi na ciyamikilo cathu pa Yehova.” Kodi mungakumbukile nthawi pamene munafunikila thandizo, ndipo wokhulupilila mnzanu anakuonetsani cikondi ceni-ceni?

16. Kodi tili na zifukwa zotani zoonetselana cikondi ceni-ceni?

16 Ganizilani zotulukapo zabwino zimene zimakhalapo tikamaonetsana cikondi ceni-ceni. Timatonthoza abale na alongo athu pokumana na mavuto. Timalimbitsa mgwilizano pakati pa anthu a Mulungu. Timaonetsanso kuti ndifedi ophunzila a Yesu, ndipo zimakopa anthu a maganizo abwino kuti ayambe kutumikila Yehova. Koposa zonse, timapeleka ulemelelo kwa “Tate wacifundo cacikulu ndi Mulungu amene amatitonthoza m’njila iliyonse,” Yehova. (2 Akor. 1:3) Inde, tiyeni tonse tipitilize kuonetsana cikondi ceni-ceni!

NYIMBO 130 Khalani Wokhululuka

^ ndime 5 Yesu ananena kuti ophunzila ake adzadziŵika na cikondi cimene amaonetsana pakati pawo. Tonsefe timayesetsa kuonetsa cikondi cimeneci. Tiyenela kukulitsa cikondi cathu pa abale athu mwa kuwakonda mmene timakondela anthu a m’banja lathu lakuthupi. Nkhani ino, idzatithandiza kukhala na cikondi ceni-ceni, na kuyesetsa kucionetsa kwa abale na alongo athu a m’cikhulupililo.

^ ndime 55 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Mkulu wacinyamata akulankhula malinga na zimene anaphunzila kwa mkulu wacikulile wacidziŵitso. Ndipo pa cithunzi cina, mkulu wacikulileyo akulandila mkulu wacinyamatayo na mkazi wake amene abwela ku nyumba kwake