Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MBIRI YA MOYO WANGA

Tinaphunzira Kuti Tisamakane Yehova Akatipatsa Zochita

Tinaphunzira Kuti Tisamakane Yehova Akatipatsa Zochita

KUNALI kutangogwa chimvula champhamvu ndipo madzi a mumtsinje anali matope okhaokha komanso ankathamanga kwambiri atatenga miyala ikuluikulu. Ine ndi mwamuna wanga Harvey limodzi ndi amene ankatimasulira chilankhulo cha Chiamisi tinachita mantha kwambiri ndipo tinkaona kuti ndife osatetezeka. Kenako tinayamba kuwoloka ndipo abale omwe anali tsidya lina la mtsinjewo ankatiyang’ana koma motidera nkhawa. Choyamba, tinakweza galimoto yathu m’galimoto ina yomwe inali yokulirapo. Koma panalibe zingwe kapena tcheni zimene zikanathandiza kuti galimoto yaing’onoyi isagwe. Kenako galimoto yaikuluyo inayamba kuwoloka pang’onopang’ono. Zinkangooneka ngati sizitheka kukafika tsidya linalo koma mwamwayi tinawoloka bwinobwino. Pa nthawi yonseyi tinkangopemphera kwa Yehova. Zimenezi zinachitika mu 1971. Pa nthawiyi tinali tili kum’mawa kwa dziko la Taiwan, komwe ndi mtunda wa makilomita masauzande ambiri kuchokera kudziko lakwathu. Dikirani ndikufotokozereni nkhani yonse.

TINAPHUNZIRA KUKONDA YEHOVA

Harvey anali woyamba kubadwa m’banja lakwawo lomwe linali ndi ana 4. Banja lawo linaphunzira choonadi ku Midland Junction ku Western Australia, pa nthawi imene kunali mavuto a zachuma cha m’ma 1930. Harvey ankakonda kwambiri Yehova ndipo anabatizidwa ali ndi zaka 14. Pasanapite nthawi, iye anaphunzira mfundo yofunika yoti asamakane akauzidwa kuti achite zinazake mumpingo. Nthawi inayake ali mnyamata, iye anakana atapemphedwa kuti awerenge Nsanja ya Olonda pamisonkhano chifukwa ankaona kuti sangakwanitse. Koma m’bale amene anamupempha kuti awerengeyo anamuuza kuti, “Winawake m’gulu la Yehovali akakupempha kuti uchite zinazake, ndiye kuti akuona kuti ungakwanitse.”​2 Akor. 3:5.

Ndinaphunzira choonadi ku England, limodzi ndi mayi anga komanso mkulu wanga. Poyamba bambo anga ankadana ndi a Mboni koma pambuyo pake nawonso anaphunzira choonadi. Chifukwa choti pa nthawiyo bambo ankatsutsa, ndinachita zosemphana ndi zofuna zawo ndipo ndinabatizidwa ndisanakwanitse zaka 10. Ndinali ndi cholinga choti ndichite upainiya kenako ndidzakhale mmishonale. Koma bambo sanandilole, anandiuza kuti ndidzachite upainiya ndikadzakwanitsa zaka 21. Sindinkafuna kuti ndidikire kwa nthawi yaitali choncho. Ndiye ndili ndi zaka 16, bambo anandilola kumakakhala ndi mchemwali wanga yemwe anasamukira m’dziko la Australia. Choncho nditakwanitsa zaka 18 ndinayamba upainiya.

Pa tsiku la ukwati wathu mu 1951

Ndili ku Australia m’pamene ndinakumana ndi Harvey. Tinali ndi zolinga zofanana zofuna kutumikira Yehova monga amishonale. Tinakwatirana mu 1951. Titachita upainiya limodzi kwa zaka ziwiri, tinapemphedwa kukachita utumiki woyang’anira dera. Dera limene tinkayendera linali chigawo chachikulu cha ku Western Australia. Choncho nthawi zambiri tinkayenda pagalimoto maulendo ataliatali kupita kumadera akutali kwambiri.

MALOTO ATHU ANAKWANIRITSIDWA

Pa Mwambo wa Omaliza Sukulu ya Giliyadi ku Yankee Stadium mu 1955

Mu 1954, tinaitanidwa kukalowa kalasi nambala 25 ya sukulu ya Giliyadi. Apa cholinga chathu chofuna kudzakhala amishonale chinayamba kununkhira. Tinafika ku New York pasitima ya pamadzi ndipo kumeneku tinali ndi mwayi wophunzira Baibulo mozama. Monga mbali ya maphunziro athu tinkayenera kuphunzira Chisipanishi, zomwe sizinali zophweka kwa Harvey chifukwa ankavutika kutchula bwinobwino chilembo cha ‘r’ mu Chisipanishi.

Pa nthawi ya sukuluyi alangizi athu anatiuza kuti onse amene akufuna kukatumikira ku Japan, alembe mayina awo n’cholinga choti alowe kalasi yophunzira Chijapanizi. Ife tinkaona kuti ndibwino kuti gulu la Yehova lichite kutisankhira koti tikatumikire. Pasanapite nthawi, M’bale Albert Schroeder, mmodzi wa alangizi athu anazindikira kuti sitinalembe mayina athu. Ndiye anatiuza kuti: “Muiganizirenso kwambiri nkhaniyi.” Pamene anaona kuti tikuzengelezabe, M’bale Schroeder anabweranso kudzatiuza kuti: “Ine limodzi ndi alangizi anzanga talemba mayina anu. Tikufuna tione ngati mungakwanitse kuphunzira Chijapanizi.” Apa Harvey sanavutike kuphunzira chilankhulo chimenechi.

Tinafika ku Japan mu 1955 ndipo pa nthawiyo m’dzikoli munali ofalitsa 500 okha. Harvey anali ali ndi zaka 26 ndipo ineyo ndinali ndi zaka 24. Tinapemphedwa kukatumikira kudoko la tauni yotchedwa Kobe, komwe tinatumikirako kwa zaka 4. Tinasangalala atatipempha kuti tizichitanso utumiki woyang’anira dera ndipo tinkayendera dera lapafupi ndi mzinda wa Nagoya. Tinkasangalala kwambiri ndi chilichonse chokhudza utumiki wathu kuphatikizapo abale, chakudya komanso malo ake omwe anali okongola. Koma pasanapite nthawi, tinali ndi mwayi winanso wochita zinthu zina zomwe Yehova ankafuna kuti tichite.

UTUMIKI WATSOPANO UNABWERETSA MAVUTO ATSOPANO

Ine ndi Harvey limodzi ndi amishonale ena ku Kobe ku Japan, mu 1957

Titachita utumiki woyang’anira dera kwa zaka zitatu, abale ku ofesi ya nthambi ya ku Japan anatipempha ngati tingakonde kupita ku Taiwan kuti tikathandize pa ntchito yolalikira kwa anthu a mtundu wa Chiamisi. Pa nthawiyi, abale ena a mtunduwu anali atayamba mpatuko. Choncho abale a ku ofesi ya nthambi ya ku Taiwan ankafuna m’bale amene amadziwa kulankhula Chijapanizi n’cholinga choti akathandize kuthetsa mpatukowo. * Tinkakonda kwambiri utumiki wathu ku Japan choncho kuvomera kupita ku Taiwan siinali nkhani yophweka. Koma paja Harvey anaphunzira mfundo yakuti sayenera kukana ngati atapatsidwa utumiki winawake, ndiye tinavomera kupita.

Tinafika ku Taiwan mu November 1962. Pa nthawiyi kunali ofalitsa 2,271 ndipo ambiri anali a mtundu wa Chiamisi. Koma choyamba tinkafunika kuphunzira Chitchainizi. Tinali ndi buku limodzi lophunzitsa Chitchainizi komanso mphunzitsi amene sankadziwanso Chingelezi, komabe tinakwanitsa kuphunzira.

Titangofika kumene ku Taiwan, Harvey anapatsidwanso utumiki wina ku ofesi ya nthambi monga mtumiki wa nthambi. Ofesi ya nthambiyo inali yaing’ono choncho mwezi uliwonse Harvey ankatha kugwira ntchito ku ofesi ya nthambi komanso kukagwira ntchito ndi abale a Chiamisi aja kwa milungu pafupifupi itatu. Komanso nthawi ndi nthawi, iye ankatumikira monga woyang’anira chigawo zomwe zinkaphatikizapo kukamba nkhani pamisonkhano ikuluikulu. Pa nthawiyo, iye akanatha kumakamba nkhani m’Chijapanizi abale a mtundu wa Chiamisi n’kumamva bwinobwino. Koma boma linkalola kuti misonkhano ili yonse yachipembedzo izichitika m’Chitchainizi basi. Choncho Harvey anakakamizika kumakamba nkhani m’Chitchainizi ngakhale kuti anali asanachidziwe bwinobwino. Ndipo pankakhala m’bale wina yemwe ankatanthauzira m’chilankhulo cha Chiamisi.

Pofuna kumvera malamulo tinkafunika kupempha akuluakulu a boma kuti atipatse chilolezo ngati tikufuna kuchita msonkhano waukulu. Kuti tipatsidwe chilolezochi sizinkakhala zophweka. Nthawi zambiri zinkapezeka kuti akuluakulu a boma avomereza mochedwa pempho lathu. Ngati mlungu umene timayenera kuchita msonkhano wafika koma sanatipatsebe chilolezo, Harvey ankanyamuka n’kukakhala ku maofesi a akuluakuluwo kufikira atatipatsa chilolezocho. Njirayi inkathandiza chifukwa akuluakulu a bomawo ankachita manyazi kuti mlendo wochokera kudziko lina azingokhala m’maofesi mwawo kudikirira kuti athandizidwe.

NTHAWI YANGA YOYAMBA KUKWERA PHIRI

Ku Taiwan tikuwoloka mtsinje wina womwe ndi wosazama popita kukalalikira

Pa milungu imene tinkapita kukathandiza abale a Chiamisi ija, tinkafunika kuyenda maulendo ataliatali mwina kwa ola limodzi kapena kuposa. Tinkafunikanso kukwera mapiri komanso kuwoloka mitsinje. Ndimakumbukira nthawi yoyamba imene ndinakwera phiri. Titadya chakudya cham’mawa, tinapita kukakwera basi cha m’ma hafu 5 m’mawa, kupita kumudzi wina womwe unali kutali kwambiri. Tinawoloka mtsinje wina waukulu kenako tinakakwera phiri. Chitunda chake chinali chokwera kwambiri moti ukatukula mutu n’kuyang’ana kumene ukupita unkatha kuona kuphazi kwa munthu amene anali kutsogolo kwako.

Titafika, Harvey analowa mu utumiki limodzi ndi abale a kuderalo ndipo ine ndinapita kumakalalikira pa kamudzi kena kapafupi komwe kanali ndi anthu olankhula Chijapanizi. Pofika cha m’ma 1 koloko ndinali nditafookeratu chifukwa panali patapita maola ambiri kuchokera pamene ndinadya chakudya cham’mawa chija. Pamene ndimadzakumana ndi Harvey sitinadziwe kumene abale ena aja anali. Harvey anali atasinthanitsa magazini ndi mazira atatu pamene amalalikira. Iye anandisonyeza mmene ndingadyere mazirawo poboola pamwamba pake n’kundipatsa kuti ndimwe. Ngakhale kuti sizinkakoma, koma ndinamwa ndipo nayenso anamwa dzira lina. Koma funso linali lakuti, ‘ndani amwe dzira lachitatulo?’ Ndiye Harvey anaona kuti ndi bwino ndimwe ineyo n’cholinga choti ndisakomoke poopa kuti angalephere kundinyamula potsika phiri lija chifukwa nayenso anali ndi njala.

CHINTHU CHINA CHACHILENDO KWA INE

Pamsonkhano wina wadera ndinaona zinthu zachilendo kwambiri. Tinkakhala m’nyumba ya m’bale wina, yemwe ankakhala pafupi ndi Nyumba ya Ufumu. Mkazi wa woyang’anira dera anatipatsa madzi osamba chifukwa anthu a mtundu wa Chiamisi amaona kuti akatero ndiye kuti amulandira bwino mlendo. Harvey anali atatanganidwa ndi zinthu zina ndiye anandiuza kuti ndikayambe kusamba. Mlongoyo anatiikira madzi otentha, ozizira komanso beseni lina lopanda kanthu. Koma chimene chinandidabwitsa n’chakuti anaika zinthuzi panja moyang’anana ndi ku Nyumba ya Ufumu kumene abale ankagwira ntchito yokonzekera msonkhano. Ndiye ndinamufunsa mkazi wa woyang’anira derayo ngati pangapezeke nsalu yoti ndidzitchingire. Iye anandibweretsera pepala la pulasitiki, loonekera mkati. Ndinaganiza zokasambira kuseri kwa nyumbayo koma vuto linali loti kunali atsekwe choncho ndinkaopa kuti andijompha. Kenako ndinadziuza kuti: ‘Komatu abalewo atanganidwa ndi ntchito ndipo sandiona kuti ndikusamba. Ndipo ngati sindisamba, eniake a nyumbawa akhumudwa.’ Moti kenako basi ndinasamba.

Titavala zovala zachikhalidwe cha anthu a Chiamisi

MABUKU A M’CHINENERO CHA CHIAMISI

Harvey anazindikira kuti zinali zovuta kwa abale a Chiamisi kuti akhale ndi chikhulupiriro cholimba chifukwa ambiri sankadziwa kulemba ndi kuwerenga komanso analibe mabuku m’chilankhulo chawo. Popeza kuti Chiamisi chinali chitayamba kulembedwa, tinaona kuti ndi nzeru kuwaphunzitsa abalewo kuwerenga. Imeneyi siinali ntchito yophweka koma n’kupita kwa nthawi, abalewa anayamba kukwanitsa kuphunzira za Yehova paokha. Mabuku a Chiamisi anayamba kupezeka cha m’ma 1960 ndipo Nsanja ya Olonda ya Chiamisi inayamba kufalitsidwa mu 1968.

Komabe vuto linali loti boma silinkalola kuti tizigawa mabuku omwe sanali a Chitchainizi. Choncho pofuna kupewa mavuto tinaona kuti ndi bwino kuti tisinthe mmene tinkakonzera Nsanja ya Olonda ya Chiamisi. Mwachitsanzo, kwa kanthawi ndithu mu Nsanja ya Olonda imeneyi munkalembedwa zilankhulo zonse ziwiri, Chiamisi ndi Chitchainizi. Choncho munthu akasonyeza chidwi n’kuyamba kuwerenga magazini athuwa ankapezeka kuti wayambanso kuphunzira Chitchainizi. Kuchokera nthawi imeneyo, gulu lakhala likutulutsa mabuku athu m’chinenero cha Chiamisi n’cholinga chofuna kuthandiza anthu kudziwa choonadi cha m’Baibulo.​—Mac. 10:34, 35.

NTHAWI YOYERETSA

Cha m’ma 1960 komanso m’ma 1970, abale ambiri a Chiamisi sankatsatira mfundo za Mulungu. Chifukwa choti sankamvetsa bwino mfundo za m’Baibulo, ena ankachita makhalidwe oipa monga chiwerewere, kuledzera, kusuta komanso kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo. Ndiye Harvey ankapita m’mipingo yosiyanasiyana kukathandiza abale kudziwa mmene Yehova amaonera nkhani zimenezi. Moti paulendo wina ndi pamene tinakumana ndi zija ndafotokoza kumayambiriro kwa nkhaniyi.

Abale odzichepetsa anali okonzeka kusintha koma chomvetsa chisoni n’choti ambiri sanasinthe. Moti chiwerengero cha ofalitsa ku Taiwan chinatsika kuchoka pa 2,450 mpaka kufika pafupifupi 900 m’zaka 20. Zimenezi zinali zofooketsa komabe tinkadziwa kuti Yehova sangadalitse gulu limene ndi lodetsedwa. (2 Akor. 7:1) Patapita nthawi, abale ku Taiwan anayamba kutumikira Yehova m’njira yovomerezeka. Yehova anawadalitsa kwambiri chifukwa cha zimenezi moti pano kuli ofalitsa oposa 11,000.

Kuyambira m’ma 1980 tinaona kuti abale ndi alongo a mipingo ya Chiamisi anayamba kukhala ndi chikhulupiriro cholimba. Zimenezi zinamupatsa mpata Harvey kuti ayambe kuthandiza anthu a Chitchainizi. Iye anasangalala kuthandiza amuna a alongo ena kuphunzira n’kukhala a Mboni za Yehova. Ndimakumbukira akundifotokozera mmene anasangalalira ataona mmodzi wa amuna amenewa akupemphera koyamba kwa Yehova. Inenso ndimasangalala kuti ndinali ndi mwayi wothandiza anthu a mitima yabwino kuti akhale pa ubwenzi ndi Yehova. Ndinasangalalanso kutumikira ku ofesi ya nthambi ya ku Taiwan limodzi ndi ana awiri a mmodzi mwa anthu omwe ndinkaphunzira nawo Baibulo.

NKHANI YOMVETSA CHISONI

Panopa ndinatsala ndekha. Pambuyo pokhala limodzi m’banja kwa zaka pafupifupi 59, mwamuna wanga wokondedwa Harvey, anamwalira ndi matenda a khansa pa 1 January 2010. Iye anachita utumiki wa nthawi zonse kwa zaka pafupifupi 60. Ndimamusowa kwambiri koma ndimasangalala kuti ndinatumikira naye limodzi pamene ntchito yolalikira inkayamba kumene m’mayiko awiri osangalatsa kwambiri. Ndipo pa nthawi imeneyi tinali ndi mwayi wophunzira zinenero ziwiri zovuta za ku Asia komanso Harvey anali ndi mwayi wophunzira ngakhale kulemba zilankhulo zimenezi.

Patapita zaka zochepa Harvey atamwalira, Bungwe Lolamulira linaona kuti ndibwererenso ku Australia. Poyamba ndinaganiza kuti, ‘Sindikufuna kuchoka ku Taiwan.’ Koma Harvey anandiphunzitsa kuti ndisamakane gulu la Yehova likandipempha kuti ndichite zinazake. Choncho ndinabwerera ku Australia. Pambuyo pake, ndinamvetsa chifukwa chake ndinkayenera kubwerera chifukwa tsopano ndinali nditakula ndipo ndinkafunika chisamaliro chapadera.

Ndimasangalala kugwiritsa ntchito Chijapanizi komanso Chitchainizi ndikamaonetsa anthu malo pa Beteli

Panopa ndikutumikira ku ofesi ya nthambi ya ku Australia ndipo kumapeto kwa mlungu ndimalalikira komanso kusonkhana ndi mpingo wina. Ku Beteli ndimasangalala kuonetsa malo alendo amene achokera ku Japan kapena ku China n’kumawafotokozera m’chinenero chawo. Panopa ndikuyembekezera mwachidwi nthawi imene Yehova adzakwaniritse lonjezo lake loukitsa anthu amene anamwalira. Ndikudziwa kuti iye akumukumbukira Harvey, yemwe anaphunzira kuti sayenera kukana, Yehovayo akamuuza kuti achite zinazake.​—Yoh. 5:28, 29.

^ ndime 14 Ngakhale kuti Chitchainizi ndi chilankhulo chachikulu m’dziko la Taiwan, Chijapanizi ndi chomwe chinali chilankhulo chachikulu kwa zaka zambiri. Choncho anthu a zikhalidwe zambiri ku Taiwan ankalankhulanso Chijapanizi.