MBILI YANGA
Tinaphunzila Kusakana Utumiki Umene Yehova Watipatsa
PAMBUYO pa cimphepo camphamvu, madzi mu mtsinje anacita matope kwambili ndipo anali kuthamanga kwambili cakuti anali kukankha miyala ikulu-ikulu. Tinali kufuna kuwolokela kutsidya lina, koma madzi amphamvu anali atakokolola ulalo. Ine na mwamuna wanga Harvey, pamodzi na wotimasulila citundu ca Ciamisi tinacita mantha ndipo tinasoŵa cocita. Abale kumtunda akuyang’ana, tinayamba kuwoloka. Tinayamba na kuika galimoto yathu yaing’ono pa galimoto yaikulu yalole. Ndiyeno popanda nthambo kapena macheni omangila galimoto kuti isamasunthe-sunthe, pang’ono-pang’ono loleyo inayamba kuwoloka mtsinje wa madzi othamangawo. Ulendowo unaoneka wautali kwambili, koma tinawoloka bwino-bwino mpaka kufika kumtunda, ndipo paulendo wonsewo tinali kungopemphela kwa Yehova. Umo munali mu 1971. Panthawiyo tinali kugombe la nyanja ku Taiwan, kutali kwambili na kwathu. Lekani nikusimbileni mbili yathu.
MMENE TINAPHUNZILILA KUKONDA YEHOVA
M’bale Harvey ndiye anali wamkulu m’banja la ana anayi. Banja lawo linaphunzilila coonadi m’tauni ya Midland Junction, ku Western Australia, pamene zacuma zinali zovuta kwambili m’zaka za m’ma 1930. M’bale Harvey anakula akukonda Yehova, ndipo anabatizika ali na zaka 14. Posapita nthawi, anaphunzila kusakana utumiki uliwonse umene angapatsidwe. Nthawi ina ali wamng’ono, anapemphedwa kuŵelenga Nsanja ya Mlonda pamsonkhano wa mpingo, koma anakana poganiza kuti ni wosayenelela. Koma m’bale wina anam’thandiza mwa kumuuza kuti: “Ngati wina m’gulu la Yehova wakupempha kucita zinazake, ndiye kuti waona kuti ndiwe woyenelela!”—2 Akor. 3:5.
Ine n’naphunzilila coonadi ku England, kumene amayi na mlongo wanga wamkulu anaphunzilila. Poyamba, atate anali wotsutsa, koma patapita nthawi nawonso anaphunzila coonadi. Atate sanali kufuna kuti nibatizike n’sanakwanitse zaka 10, koma n’nabatizikabe nili na zaka 9. N’nadziikila colinga cocita upainiya wanthawi zonse, komanso kukakhala mmishonale. Komabe, atate sanali kufuna kuti niyambe upainiya wanthawi zonse n’sanakwanitse zaka 21. Sin’nali kufuna kuyembekeza kwa nthawi yaitali conco. Koma n’tangokwanitsa zaka 16,
ananilola kukakhala na mlongo wanga wamkulu ku Australia, amene anasamukila ku dzikolo. Ndipo n’takwanitsa zaka 18 n’nayamba upainiya wanthawi zonse.Ku Australia, n’nakumana na m’bale Harvey. Tonse tinali na colinga cotumikila Yehova monga amishonale. Ndipo tinakwatilana mu 1951. Titacita upainiya pamodzi kwa zaka ziŵili, tinapemphedwa kuyamba nchito ya m’dela. Dela lathu ku Western Australia linali lalikulu kwambili, ndipo nthawi zambili tinali kuyenda na galimoto ku madela ouma akutali.
COLINGA CATHU CINAKWANILITSIDWA
Mu 1954, tinaitanidwa kukaloŵa sukulu ya Giliyadi ya kalasi nambala 25. Colinga cathu cokhala amishonale cinali citatsala pang’ono kukwanilitsidwa! Tinafika mu mzinda wa New York na sitima ya pamadzi, kenako tinayamba kuphunzila Baibo mozama. Monga mbali ya maphunzilo, tinafunika kuphunzila Cisipanishi, cimene cinali covuta kwa mwamuna wanga Harvey, cifukwa anali kuvutika kuchula ma r.
Mkati mwa maphunzilowo, alangizi analengeza kuti amene angafune kukatumikila ku Japan alembetse maina awo kuti aloŵe kalasi yophunzila Cijapanizi. Tinaona kuti zingakhale bwino kulola gulu la Yehova kutisankhila kokatumikila. Posapita nthawi, M’bale Albert Schroeder anadziŵa kuti sitinalembetse maina athu. Iye anatiuza kuti: “Muganizileponso.” Titapitiliza kuzengeleza, M’bale Schroeder anakamba kuti: “Ine na alangizi ena takulembani. Mukaonela komweko ngati mudzakwanitsa kuphunzila Cijapanizi.” Harvey anaphunzila mosavuta cineneloci.
Titafika ku Japan mu 1955, tinapeza kuti munali cabe ofalitsa 500 m’dzikolo. Panthawiyo, ine n’nali na zaka 24, pamene Harvey anali na zaka 26. Tinatumizidwa kumzinda wa Kobe wapafupi na doko, kumene tinatumikila kwa zaka zinayi. Pambuyo pake, tinakondwela kwambili titapemphedwa kukatumikilanso m’nchito ya m’dela, ndipo tinali kutumikila kufupi na mzinda wa Nagoya. Tinali kukonda zonse mu utumiki wathu—abale, zakudya, komanso maonekedwe a malo. Koma posapita nthawi, tinakhalanso na mwayi wosakana utumiki umene Yehova watipatsa.
UTUMIKI WATSOPANO UNALINSO NA ZOPINGA ZAKE
Titatumikila m’nchito ya m’dela kwa zaka zitatu, ofesi yanthambi ya ku Japan inatipempha kukatumikila ku Taiwan pamodzi na anthu a kumeneko a mtundu wa Amis. Abale ena a mtundu wa Amis anakhala ampatuko, ndipo ofesi yanthambi * Tinali kuukonda utumiki wathu ku Japan, conco zinali zovuta kupanga cosankha cimeneci. Koma Harvey anali ataphunzila kusakana utumiki uliwonse umene wapatsidwa. Conco tinagwilizana kuti tipite.
ya ku Taiwan inali kufuna m’bale wodziŵa bwino Cijapanizi kuti akathandize kuthetsa mpatukowo.Tinafika ku Taiwan mu November 1962. Panthawiyo, m’dziko la Taiwan munali ofalitsa 2,271, ndipo ambili a iwo anali a mtundu wa Amis. Koma tinafunika kuphunzila Cichainizi coyamba. Tinali cabe na buku lophunzilila Cichainizi na mphunzitsi amene sanali kudziŵa kukamba Cizungu. Ngakhale n’conco, tinaphunzila cineneloco.
Patapita nthawi yocepa titafika ku Taiwan, Harvey anapatsidwa udindo wotumikila monga mtumiki wa nthambi. Popeza kuti ofesi yanthambi inali yaing’ono panthawiyo, mwamuna wanga Harvey anali kugwila nchito zonse za mu ofesi yake, na kutumikilabe pamodzi na abale a mtundu wa Amis kwa milungu itatu mwezi uliwonse. Nthawi na nthawi, anali kutumikilanso monga woyang’anila cigawo, ndipo nchito yake inali kuphatikizapo kukamba nkhani pa misonkhano. Harvey akanakwanitsa kukamba nkhani mu Cijapanizi, ndipo abale a mtundu wa Amis akanamvela. Komabe, boma linalola zipembedzo kucita misonkhano yawo mu Cichainizi cabe. Ngakhale kuti Harvey anali kuvutikila kukamba Cichainizi, anali kukambabe nkhani m’cineneloco ndipo m’bale wina anali kumasulila mu Ciamisi.
Dziko la Taiwan panthawiyo linali pansi pa ulamulilo wopondeleza. Conco, coyamba abale anafunika kutenga cilolezo asanacite misonkhano yadela. Kutenga zilolezo kunali kovuta, ndipo nthawi zambili apolisi anali kucedwa kupeleka zilolezo zimenezo. Ngati apolisi sanapeleke cilolezo mpaka mlungu wa msonkhano, Harvey anali kukhalabe papolisi kufikila atapatsidwa cilolezo. Popeza kuti apolisi anali kucita manyazi kuti munthu wa kudziko lina azingoyembekeza papolisi, njilayo inali kuthandiza.
ULENDO WOYAMBA UMENE N’NAKWELA PHILI
Pa milungu yonse imene tinagwila nchito na abale, tinali kuyenda mitunda yaitali yotenga ola limodzi kapena kuposapo. Tinali kukwela mapili na kuwoloka mitsinje. Nimakumbukila ulendo woyamba umene n’nakwela phili. Titadya cakudya cam’maŵa msanga-msanga, tinapita kukakwela basi yonyamuka na 05:30 m’maŵa, kupita kumudzi wina wakutali. Ndiyeno tinawoloka mtsinje na miyendo, kenako tinakwela phili lotsetseleka. Phililo linali lotsetseleka kwambili cakuti nimati nikaponya maso patsogolo, m’bale amene anali patsogolo panga pokwela phililo anali kungooneka miyendo yokha basi.
Tsikulo m’maŵa, mwamuna wanga analalikila limodzi na abale a kumeneko, pamene ine n’nalalikila nekha m’mudzi wina wa anthu okamba Cijapanizi. Podzafika m’ma 13:00 koloko, n’nali kumvela monga nidzakomoka cifukwa sin’nadye kwa maola ambili. N’takumana na Harvey, panalibe m’bale wina aliyense. Iye anali atasinthanitsa magazini angapo na mazila atatu a nkhuku. Harvey ananionetsa momwela dzila mwa kuiboola pang’ono. Ngakhale kuti sanali kumveka kukoma, n’namwa imodzi. Koma kodi ndani akanatenga dzila lacitatu? N’nalitenga ndine, cifukwa mwamuna wanga anaona kuti sangakwanitse kuninyamula ngati ningakomoke na njala m’phili.
KASAMBIDWE KACILENDO
Zimene zinacitika pamsonkhano wadela wina zinali zacilendo. Tinali kukhala m’nyumba ya m’bale wina pafupi kwambili na Nyumba ya Ufumu. Popeza kuti anthu a mtundu wa Amis amaona kuti kusamba n’kofunika kwambili, mkazi wa woyang’anila dela anatikonzela madzi osamba. Mwamuna wanga ananipempha kuti niyambe ndine kukasamba cifukwa iye anali wotangwanika. Panali ziŵiya zitatu zoseŵenzetsa: shomeka ya madzi ozizila, ya madzi otentha, komanso ina yopanda madzi. N’nadabwa kuti mkazi wa woyang’anila dela anaika zonsezi pabwalo pa nyumba mopenyana na Nyumba ya Ufumu, kumene abale anali kukonzekela za msonkhano wadela. N’napempha mkazi wa woyang’anila delayo kuti anibweletseleko cocinga monga katani. Iye ananibweletsela pulasitiki yoonetsa mkati. N’naganiza zopita kuseli kwa nyumba, koma kumeneko atsekwe anali ataloŵetsa mitu yawo mkati mwa mpanda, ndipo anali okonzeka kunzonzoola aliyense amene angafike pafupi. N’nati mu mtima: ‘Abale ni otangwanika kwambili ndipo sangaone kuti nisamba. Ndipo ngati sinisamba, nidzaŵakhumudwitsa. Tiyeni nazo!’ Conco n’nasamba.
MABUKU A ANTHU A MTUNDU WA AMIS
Harvey anazindikila kuti abale a mtundu wa Amis anali kuvutika kupita patsogolo mwauzimu, cifukwa ambili sanali kudziŵa kuŵelenga ndipo analibe mabuku m’cinenelo cawo. Popeza kuti cinenelo ca Ciamisi cinali citangoyamba kulembedwa mwa kuseŵenzetsa zilembo zaciroma, tinaona kuti n’zothandiza kuphunzitsa abale kuŵelenga citundu cawo. Imeneyo inali nchito yaikulu, koma m’kupita kwa nthawi abale anayamba kuphunzila okha za Yehova. Mabuku a m’Ciamisi anayamba kupezeka ca mu 1966, ndipo mu 1968, Nsanja ya Mlonda inayamba kufalitsidwa m’cineneloci.
Komabe, boma linali kuletsa zofalitsa zimene sizinali m’Cichainizi. Conco pofuna kupewa mavuto, Nsanja ya Mlonda ya Ciamisi inali kufalitsidwa m’njila zosiyana-siyana. Mwacitsanzo, Nsanja ya Mlonda imene tinali kuseŵenzetsa kwa kanthawi, inali na mawu a Cichainizi Mandarin komanso a Ciamisi. Ngati tapeza anthu acidwi, tinali kuseŵenzetsa magaziniwo powaphunzitsa Cichainizi. Kucokela nthawiyo, gulu la Yehova lakhala likufalitsa mabuku ambili m’cinenelo ca Ciamisi, pofuna kuthandiza anthu amenewa kuphunzila coonadi.—Mac. 10:34, 35.
NTHAWI YA KUYELETSA
Ca m’ma 1960 komanso m’ma 1970, abale ambili anali ataleka kutsatila miyezo ya Mulungu. Cifukwa cakuti sanamvetse bwino mfundo za m’Baibo, ena anali kucita zaciwelewele, kuledzela, kukoka fodya, komanso kuseŵenzetsa amkolabongo ena monga betel nut. Harvey anayendela mipingo yambili pofuna kuthandiza abale kumvetsa mmene Yehova amaonela nkhani zimenezi. Pa ulendo wina wotele, m’pamene tinali na cocitika cimene nafotokoza kuciyambi.
Abale odzicepetsa anali okonzeka kusintha. Koma comvetsa cisoni n’cakuti ena ambili sanasinthe, ndipo ciŵelengelo ca ofalitsa ku Taiwan cinatsika kwambili kucoka pa 2,450 kufika pa ofalitsa 900 pa zaka 20. Izi zinali zolefula kwambili. Komabe, tinadziŵa kuti Yehova sangadalitse gulu lodetsedwa. (2 Akor. 7:1) Patapita nthawi, anthu m’mipingo analeka makhalidwe oipa, ndipo na thandizo la Yehova, tsopano m’dziko la Taiwan muli ofalitsa opitilila 11,000.
Kucokela mu 1980 kupita kutsogolo, tinaona kuti abale na alongo m’mipingo ya Ciamisi anali kupita patsogolo mwauzimu. Ndipo Harvey tsopano anayamba kuthela nthawi yoculuka kuthandiza anthu okamba Cichainizi. Iye anakondwela kwambili kuthandiza amuna a alongo ambili kuphunzila coonadi. Nikumbukila kuti nthawi ina iye ananiuza kuti anakondwela kwambili ataona mmodzi wa amuna amenewo akupemphela kwa Yehova kwa nthawi yoyamba. Nanenso nimakondwela kuti nathandiza anthu ambili oona mtima kuyandikila Yehova. N’nalinso na mwayi wotumikila pa ofesi yanthambi ya ku Taiwan, pamodzi na ana aŵili a munthu amene n’nali kuphunzila naye Baibo.
IMFA YA MWAMUNA WANGA
Tsopano nili nekha. Mwamuna wanga wokondeka, amene n’nakhala naye m’cikwati kwa zaka pafupi-fupi 59, anamwalila na khansa pa January 1, 2010. Iye anakhala mu utumiki wanthawi zonse pafupi-fupi zaka 60! Nimamuyewa kwambili. Koma ndine wokondwela kuti n’namucilikiza panthawi yonse imene tinatumikila m’maiko ocititsa cidwi aŵili. Tinaphunzila kukamba zinenelo ziŵili zovuta za ku Asia, ndipo Harvey anaphunzilanso ngakhale kuzilemba.
Patapita zaka zingapo, Bungwe Lolamulila linaniuza kuti zingakhale bwino nibwelele ku Australia cifukwa ca ukalamba. Poyamba n’nati: ‘Sinifuna kucokako ku Taiwan.’ Koma Harvey ananiphunzitsa kuti siniyenela kukana zilizonse zimene gulu la Yehova linganiuze, conco sin’nakane. Pambuyo pake, n’naona kuti malangizo akuti nisamuke anali anzelu.
Masiku ano, nimatumikila pa ofesi yanthambi ya ku Australasia, ndipo kumapeto kwa mlungu nimatumikila pamodzi na mpingo wathu. Ndine wokondwela kuti nimaseŵenzetsa Cijapanizi na Cichainizi poonetsa anthu malo pa Beteli. Niyembekezela mwacidwi kukwanilitsidwa kwa lonjezo la kuuka kwa akufa. Nidziŵa kuti Yehova adzam’kumbukila mwamuna wanga Harvey, amene anaphunzila kusakana zilizonse zimene iye angamuuze.—Yoh. 5:28, 29.
^ ndime 14 Ngakhale kuti tsopano cinenelo ca boma ku Taiwan ni Cichainizi, kwa zaka zambili kumbuyoko, Cijapanizi ndiye cinali cinenelo ca boma. Conco, mitundu yambili ya anthu ku Taiwan inali kukamba Cijapanizi.