Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 6

“Mutu wa Mkazi Ndi Mwamuna”

“Mutu wa Mkazi Ndi Mwamuna”

“Mutu wa mkazi ndi mwamuna.”​—1 AKOR. 11:3.

NYIMBO 13 Khristu ni Citsanzo Cathu

ZIMENE TIKAMBILANE *

1. Posankha munthu womanga naye banja, kodi mlongo amene ni mbeta ayenela kudzifunsa mafunso ati?

AKHRISTU onse, ali pansi pa umutu wangwilo wa Yesu Khristu. Komabe, mkazi wacikhristu akaloŵa m’banja, amakhala pansi pa umutu wa mwamuna wopanda ungwilo. Zimenezi zingakhale zovuta. Conco, poganizila za munthu womanga naye banja, mkazi angacite bwino kudzifunsa kuti: ‘N’ciani cionetsa kuti m’baleyu adzakhala mutu wa banja wabwino? Kodi amaika zinthu zauzimu patsogolo mu umoyo wake? Ngati ayi, kodi angadzakhaledi mutu wa banja wabwino tikadzakwatilana?’ Mlongoyo angacitenso bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi ine nili na makhalidwe otani amene adzatithandiza m’cikwati? Kodi ndine woleza mtima, komanso woolowa manja? Kodi nili paubale wolimba na Yehova?’ (Mlal. 4:9, 12) Cimwemwe cimene mkazi adzapeza m’banja, cimadalilanso pa zosankha zimene akupanga asanaloŵe m’banja.

2. Tikambilane ciani m’nkhani ino?

2 Alongo oculuka amapeleka citsanzo cabwino kwambili pankhani yogonjela amuna awo. Ndipo timawayamikila ngako! Timakondwela kwambili kutumikila Yehova pamodzi na akazi okhulupilika amenewa! M’nkhani ino, tikambilane mayankho pa mafunso atatu awa: (1) Ni mavuto ena ati amene akazi amakumana nawo? (2) N’cifukwa ciani mkazi amasankha kugonjela mwamuna wake? (3) Kodi amuna na akazi acikhristu angaphunzile ciani pa citsanzo ca Yesu, Abigayeli, komanso Mariya mayi wa Yesu pankhani ya kugonjela?

KODI AKAZI ACIKHRISTU AMAKUMANA NA MAVUTO OTANI?

3. N’cifukwa ciani kulibe cikwati cangwilo?

3 Cikwati ni mphatso yabwino kwambili yocokela kwa Mulungu, koma anthu ni opanda ungwilo. (1 Yoh. 1:8) N’cifukwa cake Mawu a Mulungu amacenjeza okwatilana kuti adzakumana na mavuto amene amafotokozedwa kuti “nsautso m’thupi mwawo.” (1 Akor. 7:28) Tiyeni tione ena mwa mavuto amene mkazi angakumane nawo.

4. N’cifukwa ciani mkazi angamaone kuti kugonjela mwamuna wake n’kudzipeputsa?

4 Mwina cifukwa ca mmene anakulila, mkazi angamaone kuti kugonjela mwamuna wake n’kudzipeputsa. Mlongo Marisol wa ku America anati: “Kumene n’nakulila, akazi anali kuuzidwa kuti afunika kukhala olingana na amuna pa ciliconse. Nidziŵa kuti Yehova ndiye anakhazikitsa dongosolo la umutu, ndipo anapatsa akazi mbali yocepelapo poyelekezela na amuna, koma yolemekezeka. Ngakhale n’telo, zimakhalabe zovutilako kuona umutu moyenelela.”

5. Kodi ena ali na maganizo otani osemphana na Malemba ponena za akazi?

5 Nthawi zina mkazi angakwatiwe na mwamuna amene amaganiza kuti akazi ni otsika. Mlongo Ivon wa ku South America anati: “M’dela lathu amuna amayambilila kudya, akazi amadya pambuyo pake. Ana acitsikana amagwila nchito zophika na kuyeletsa, koma ana aamuna amatumikilidwa na amayi awo komanso azilongosi awo, ndipo amauzidwa kuti ni ‘mafumu panyumba.’” Mlongo Yingling wa ku Asia, anati: “M’cinenelo cathu muli mwambi wotanthauza kuti akazi safunika kukhala anzelu kwambili, kapena amaluso apamwamba. Udindo wawo ni kugwila nchito zonse za pakhomo, ndipo saloledwa kuuza amuna awo malingalilo awo.” Mwamuna amene amatengela maganizo osemphana na malemba komanso opanda cikondi amenewa, amapangitsa umoyo wa mkazi wake kukhala wovuta. Amalephelanso kutengela citsanzo ca Yesu, ndipo sakondweletsa Yehova.—Aef. 5:28, 29; 1 Pet. 3:7.

6. Kodi akazi ayenela kucita ciani kuti alimbitse ubale wawo na Yehova?

6 Monga tinaonela m’nkhani yapita, Yehova amayembekezela kuti amuna acikhristu azisamalila mabanja awo kuuzimu, kuwaonetsa cikondi, na kuwasamalila kuthupi. (1 Tim. 5:8) Komabe, ngakhale kuti akazi okwatiwa amakhala otangwanika, ayenela kupatula nthawi tsiku lililonse yoŵelenga Mawu a Mulungu na kuwasinkha-sinkha, komanso kufikila Yehova m’pemphelo mocokela pansi pamtima. Kucita izi kungakhale kovuta. Akazi okwatiwa amakhala otangwanika kwambili. Conco, angamaone kuti alibe nthawi kapena mphamvu zocitila zimenezo. Komabe, m’pofunika ndithu kuti azipatulabe nthawi yocita zimenezo. Cifukwa ciani? Cifukwa Yehova amafuna kuti aliyense wa ife akhalebe paubwenzi wolimba na iye.—Mac. 17:27.

7. N’ciani cidzathandiza mkazi kulemekeza na kumvela mwamuna wake?

7 M’pomveka kuti mkazi angafunike kulimbikila kuti agonjele mwamuna wake wopanda ungwilo. Komabe, zidzakhala zosavuta kukwanilitsa gawo limene Yehova anam’patsa, ngati amvetsa na kuvomeleza zifukwa zake za m’Malemba.

N’CIFUKWA CIANI MKAZI AMASANKHA KUGONJELA MWAMUNA WAKE?

8. Mogwilizana na Aefeso 5:22-24, n’cifukwa ciani mkazi wacikhristu amasankha kugonjela mwamuna wake?

8 Mkazi wacikhristu amasankha kugonjela mwamuna wake cifukwa ni Yehova anam’patsa gawo limeneli. (Ŵelengani Aefeso 5:22-24.) Iye amakhulupilila Atate wake wakumwamba, podziŵa kuti nthawi zonse zocita zake zimacokela m’cikondi, ndipo akam’pempha kucita cina cake ndiye kuti n’comupindulila iye monga mkazi.—Deut. 6:24; 1 Yoh. 5:3.

9. N’ciani cimacitika ngati mlongo wacikhristu amalemekeza ulamulilo wa mwamuna wake?

9 Dzikoli, limalimbikitsa akazi kunyalanyaza miyezo ya Yehova na kuona kuti kugonjela n’kudzipeputsa. Koma anthu amene amalimbikitsa maganizo amenewa, samudziŵa Mulungu wathu wacikondi. Yehova sangapatse ana ake aakazi okondeka lamulo limene lingawapeputse. Mlongo amene amayesetsa kukwanilitsa gawo limene Yehova anam’patsa, amalimbikitsa mtendele m’nyumba yake. (Sal. 119:165) Iye, mwamuna wake, ana ake, onse amapindula.

10. Kodi tingaphunzile ciani pa zimene mlongo Carol ananena?

10 Mkazi amene amagonjela mwamuna wake wopanda ungwilo, amaonetsa kuti amakonda Yehova na kum’lemekeza, podziŵa kuti iye ndiye anakhazikitsa dongosolo la umutu. Mlongo Carol wa ku South America anati: “Nidziŵa kuti mwamuna wanga angalakwitse zinthu, komanso nimadziŵa kuti zimene nimacita akalakwitsa zinthu, zimaonetsa ngati nimaona ubwenzi wanga na Yehova kukhala wofunika. Conco, nimayesetsa kukhala wogonjela cifukwa nifuna kukondweletsa Atate wanga wakumwamba.”

11. N’ciani cimathandiza mlongo Aneese kukhululuka? Nanga tingaphunzilepo ciani pa zimene anakamba?

11 Cingakhale covuta kwa mkazi kuonetsa ulemu na kugonjela, ngati aona kuti mwamuna wake sasamala za mmene akumvelela komanso nkhawa zake. Onani zimene mlongo Aneese amacita zikakhala conco. Iye anati: “Nimapewa kukhala wokhumudwa. Nimakumbukila kuti tonsefe timalakwitsa. Colinga canga nikukhululuka na mtima wonse, mmene Yehova amacitila. Nikakhululuka, nimapezanso mtendele wamaganizo.” (Sal. 86:5) Ngati mkazi amakonda kukhululuka cimakhala cosavuta kwa iye kugonjela.

KODI TINGAPHUNZILE CIANI KU ZITSANZO ZA M’BAIBO?

12. Kodi m’Baibo muli zitsanzo zotani?

12 Ena amaganiza kuti munthu wogonjela ni wofooka. Koma maganizo amenewo ni olakwika kothelatu. Baibo ili na zitsanzo zambili za anthu ogonjela amene anali olimba mtima. Tiyeni tione zimene tingaphunzile kwa Yesu, Abigayeli, komanso Mariya.

13. N’cifukwa ciani Yesu amagonjela Yehova? Fotokozani.

13 Yesu amagonjela kwa Yehova, koma osati cifukwa cakuti alibe nzelu kapena maluso. Palibe munthu aliyense wanzelu amene anaphunzitsa momveka bwino, komanso mosavuta monga Yesu. (Yoh. 7:45, 46) Yehova anadziŵa kuti Yesu ni waluso kwambili cakuti anamulola kuseŵenza naye polenga zinthu m’cilengedwe. (Miy. 8:30; Aheb. 1:2-4) Ndipo kungocokela pamene Yesu anaukitsidwa, Yehova anam’patsa ‘ulamulilo wonse . . . kumwamba ndi padziko lapansi.’ (Mat. 28:18) Ngakhale kuti Yesu ni waluso kwambili, amayang’anabe kwa Yehova kaamba ka citsogozo. Cifukwa ciani? Cifukwa amawakonda Atate wake.—Yoh. 14:31.

14. Kodi amuna angaphunzile ciani (a) na mmene Yehova amaonela akazi? (b) pa mawu a pa Miyambo 31?

14 Zimene amuna angaphunzilepo. Yehova analinganiza zakuti mkazi azigonjela mwamuna wake osati cifukwa coona kuti akazi ni otsika kwa amuna ayi. Yehova anaonetsa zimenezi mwa kusankha akazi komanso amuna kuti akalamulile pamodzi na Yesu. (Agal. 3:26-29) Yehova anaonetsa kuti amadalila Mwana wake mwa kum’patsa ulamulilo. Mofananamo, mwamuna wanzelu amapatsako mkazi wake ulamulilo pamlingo woyenela. Pofotokoza za mkazi wabwino, Mawu a Mulungu amanena kuti amayang’anila nyumba yake, amagula na kusamalila malo, ndiponso amacita malonda. (Ŵelengani Miyambo 31:15, 16, 18.) Iye si kapolo amene alibe ufulu wofotokoza maganizo ake. M’malomwake, mwamuna wake amam’dalila mwa kumvetsela malingalilo ake. (Ŵelengani Miyambo 31:11, 26, 27.) Ngati mwamuna alemekeza mkazi wake mwa njila imeneyi, mkaziyo adzamugonjela mokondwela.

Kodi akazi abwino angaphunzile ciani pa citsanzo ca Yesu ca kugonjela Yehova? (Onani ndime 15)

15. Kodi akazi angaphunzile ciani ku citsanzo ca Yesu?

15 Zimene akazi angaphunzilepo. Ngakhale kuti Yesu anacita zinthu zazikulu, saona kuti kugonjela Yehova n’kudzipeputsa. (1 Akor. 15:28; Afil. 2:5, 6) Mofananamo, mkazi wabwino amene amatengela citsanzo ca Yesu saona kuti kugonjela mwamuna wake n’kudzipeputsa. Iye amacilikiza mwamuna wake osati cabe cifukwa comukonda, koma kweni-kweni cifukwa cokonda Yehova na kum’lemekeza.

Pambuyo potumiza zakudya kwa Davide na asilikali ake, Abigayeli apita kwa Davide. Kenako, agwada pansi na kupempha Davide kuti asapalamule mlandu wa magazi mwa kubwezela (Onani ndime 16)

16. Malinga na 1 Samueli 25:3, 23-28, kodi Abigayeli anakumana na mavuto otani? (Onani cithunzi pacikuto.)

16 Abigayeli anali na mwamuna dzina lake Nabala. Mwamunayo anali wodzikonda, wonyada, komanso wosayamikila. Ngakhale n’conco, Abigayeli sanayese kupeza njila yamadulila yothetsela cikwati cake. Iye akanafuna akanangokhala cete na kulekelela Davide na asilikali ake kupha mwamuna wake. M’malomwake anacita zonse zotheka kuti ateteze mwamuna wake Nabala pamodzi na onse a m’banja lawo. Tangoganizilani kulimba mtima kumene Abigayeli anaonetsa! Iye anayandikila asilikali 400 na kuyamba kukamba na Davide mwaulemu. Anali wokonzeka kuonedwa wolakwa cifukwa ca zocita za mwamuna wake. (Ŵelengani 1 Samueli 25:3, 23-28.) Davide anazindikila kuti Yehova waseŵenzetsa mkazi wolimba mtima ameneyu pomupatsa malangizo ofunikila kuti asacite chimo lalikulu.

17. Kodi amuna angaphunzilepo ciani pankhani ya Davide na Abigayeli?

17 Zimene amuna angaphunzilepo. Abigayeli anali mkazi wanzelu. Davide mwanzelu anamvela malangizo ake. Ndipo cotulukapo cake n’cakuti anapewa kucita zinthu zimene zikanam’pangitsa kukhala na mlandu wa magazi. Mofananamo, mwamuna wanzelu amaganizila mosamala malingalilo a mkazi wake popanga zosankha zikulu-zikulu. Mwina malingalilo a mkazi angathandize mwamuna wake kupanga cosankha canzelu.

18. Kodi akazi angaphunzilepo ciani pa citsanzo ca Abigayeli?

18 Zimene akazi angaphunzilepo. Mkazi amene amakonda Yehova na kum’lemekeza amapindulitsa banja lake ngakhale kuti mwamuna wake satumikila Yehova kapena kutsatila mfundo zake. Iye sayesa kupeza njila yothetsela cikwati cake yosagwilizana na Malemba. M’malomwake, amayesetsa kulimbikitsa mwamuna wake kuphunzila za Yehova mwa kukhala waulemu, komanso wogonjela. (1 Pet. 3:1, 2) Koma ngakhale kuti mwamuna wake sangasankhe kutumikila Yehova, Yehova amakondwela ngati mkazi ni wokhulupilika kwa iye, komanso wogonjela mwamuna wake.

19. Ni pa zocitika ziti pamene mkazi sangamvele mwamuna wake?

19 Koma mkazi wacikhristu wogonjela, sangacilikize mwamuna wake ngati wam’pempha kucita zinthu zophwanya malamulo a m’Baibo kapena mfundo zake. Mwacitsanzo, mwina mwamuna wosakhulupilila wa mlongo angamuuze kuti aname, abe, kapena kuti acite zinthu zina zosagwilizana na Malemba. Akhristu onse, kuphatikizapo alongo okwatiwa, afunika kukhala okhulupilika kwa Yehova Mulungu coyamba. Ngati mlongo wapemphedwa kuphwanya mfundo za m’Baibo, ayenela kukana na kufotokoza mwaulemu, koma molimba mtima cifukwa cake wakana kucita zimene mwamuna wake wamupempha.—Mac. 5:29.

Onani ndime 20 *

20. Tidziŵa bwanji kuti Mariya anali paubale wolimba na Yehova?

20 Mariya anali paubale wolimba na Yehova. Mosakaikila, iye anali kuwadziŵa bwino Malemba. Pokambilana na Elizabeti mayi wa Yohane M’batizi, Mariya anagwila mawu Malemba Aciheberi nthawi zoposa 20. (Luka 1:46-55) Ndipo ganizilani izi, ngakhale kuti Mariya anali pa citomelo na Yosefe, mngelo wa Yehova sanayambile kuonekela kwa Yosefe. Koma mngeloyo coyamba, anakamba na Mariya mwacindunji na kumuuza kuti adzabeleka Mwana wa Mulungu. (Luka 1:26-33) Yehova anali kum’dziŵa bwino Mariya ndipo anali na cidalilo cakuti adzasamalila Mwana wake na kum’konda. Mosakaika konse, Mariya anakhalabe paubale wolimba na Yehova ngakhale pambuyo pa imfa ya Yesu na kuukitsidwa kwake kupita kumwamba.—Mac. 1:14.

21. Kodi amuna angaphunzilepo ciani pa zimene Baibo imakamba za Mariya?

21 Zimene amuna angaphunzilepo. Mwamuna wanzelu amakondwela ngati mkazi wake amawadziŵa bwino Malemba. Iye sakhumudwa kapena kuganiza kuti mkazi wake afuna kum’landa umutu. Mwamunayo amadziŵa kuti ngati mkazi wake ali na cidziŵitso cokwanila pa Baibo na mfundo zake, angakhale wothandiza kwambili m’banja mwawo. Ngakhale kuti mkazi angakhale wophunzila kwambili kuposa mwamuna wake, ni udindo wa mwamuna wake kutsogolela pa kulambila kwa pabanja komanso pa zocitika zina zauzimu.—Aef. 6:4.

Kodi akazi angaphunzile ciani kwa Mariya mayi wa Yesu, pankhani ya kuphunzila Baibo na kusinkha-sinkha? (Onani ndime 22) *

22. Kodi akazi angaphunzile ciani kwa Mariya?

22 Zimene akazi angaphunzilepo. Mkazi amafunika kugonjela mwamuna wake, koma amafunikanso kulimbitsa cikhulupililo cake payekha. (Agal. 6:5) Conco, afunika kupatula nthawi yocita phunzilo laumwini na kusinkha-sinkha. Kucita zimenezi kudzam’thandiza kukonda Yehova na kumulemekeza, komanso kupeza cimwemwe pamene agonjela mwamuna wake.

23. Kodi akazi ogonjela amapindula bwanji? Nanga kodi kugonjela kwawo kumapindulitsa bwanji mabanja awo na mpingo?

23 Akazi amene amagonjela amuna awo cifukwa cokonda Yehova, amapeza cimwemwe coculuka komanso amakhala okhutila kuposa aja amene amakana dongosolo la Yehova la umutu. Iwo amapeleka citsanzo cabwino kwa anyamata na atsikana. Amathandizanso kuti m’banja na mu mpingo, mukhale cikondi na mtendele. (Tito 2:3-5) Masiku ano, atumiki a Yehova okhulupilika ambili ni akazi. (Sal. 68:11) Aliyense wa ife, mwamuna kapena mkazi, ali na mbali imene angacite mu mpingo. Nkhani yotsatila idzafotokoza mmene aliyense wa ife angacitile mbali yake.

NYIMBO 131 “Cimene Mulungu Wacimanga Pamodzi”

^ ndime 5 Yehova anakonza zakuti mkazi wokwatiwa azigonjela mwamuna wake. Kodi izi zitanthauza ciani? Amuna na akazi acikhristu angaphunzile zambili pankhani ya kugonjela kucokela kwa Yesu, komanso kwa akazi ena amene nkhani zawo zinalembedwa m’Baibo.

^ ndime 68 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Pokambilana na Elizabeti, mayi wa Yohane M’batizi, Mariya anatha kuchula kucokela pamtima mawu a m’Malemba Aciheberi.

^ ndime 70 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Mkazi wacikhristu ayenela kupatula nthawi yophunzila Baibo kuti akhalebe na cikhulupililo colimba.