Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 7

Udindo Umene Akulu Ali Nawo Mumpingo

Udindo Umene Akulu Ali Nawo Mumpingo

‘Khristu ndi mutu wa mpingo, pokhala mpulumutsi wa thupilo.’​—AEF. 5:23.

NYIMBO NA. 137 Akazi Achikhristu Okhulupirika

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1. Perekani chifukwa chimodzi chimene chimachititsa kuti anthu m’banja la Yehova azigwirizana?

TIMASANGALALA kukhala m’banja la Yehova. N’chifukwa chiyani m’banjali anthu ake timakhala mwa mtendere komanso mogwirizana? Chifukwa chimodzi n’chakuti tonse timalemekeza zimene Yehova anakonza zoti ena azitsogolera. Ndipotu tikamvetsa bwino zimene Yehova anakonzazi ndi pamenenso timakhala ogwirizana kwambiri.

2. Kodi munkhaniyi tikambirana mayankho a mafunso ati?

2 Munkhaniyi tikambirana za amene ali ndi udindo wotsogolera mumpingo. Tikambirananso mayankho a mafunso awa: Kodi Yehova anapatsa alongo ntchito yotani mumpingo? Kodi n’zoona kuti m’bale aliyense ndi mutu wa mlongo aliyense? Kodi udindo umene akulu ali nawo pa abale ndi alongo ndi wofanana ndi umene bambo ali nawo pa mkazi ndi ana ake? Choyamba tiyeni tikambirane mmene tiyenera kuwaonera alongo.

KODI TIZIWAONA BWANJI ALONGO?

3. Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tiziyamikira kwambiri ntchito imene alongo athu amagwira?

3 Timayamikira kwambiri alongo athu amene amagwira ntchito mwakhama kusamalira mabanja awo, kulalikira uthenga wabwino komanso kuthandiza ena mumpingo. Tingamawayamikirenso kwambiri tikaganizira mmene Yehova ndi Yesu amawaonera. Tiphunziranso zambiri poona mmene Paulo ankachitira zinthu ndi akazi.

4. Kodi Baibulo limasonyeza bwanji kuti Yehova amaona kuti akazi ndi amtengo wapatali mofanana ndi amuna?

4 Baibulo limasonyeza kuti Yehova amaona kuti akazi ndi amtengo wapatali mofanana ndi amuna. Mwachitsanzo, limafotokoza kuti mu nthawi ya atumwi Yehova anapereka mzimu woyera kwa amuna ndi akazi omwe, kuti onse azitha kuchita zodabwitsa monga ngati kulankhula zinenero zosiyanasiyana. (Mac. 2:1-4, 15-18) Ndipotu Yehova anadzoza onsewa ndi mzimu woyera kuti akalamulire limodzi ndi Khristu. (Agal. 3:26-29) Yehova adzaperekanso mphoto ya moyo wosatha kwa amuna ndi akazi padziko lapansi. (Chiv. 7:9, 10, 13-15) Komanso onse amuna ndi akazi, anapatsidwa ntchito yolalikira ndi kuphunzitsa anthu uthenga wabwino. (Mat. 28:19, 20) Ndipotu buku la Machitidwe limatifotokozera ntchito imene mlongo wina dzina lake Purisikila anagwira. Iye limodzi ndi mwamuna wake Akula anathandiza munthu wina wophunzira kwambiri dzina lake Apolo kumvetsa choonadi molondola.​—Mac. 18:24-26.

5. Kodi lemba la Luka 10:38, 39 ndi 42, limasonyeza bwanji kuti Yesu ankalemekeza akazi?

5 Yesu ankalemekeza kwambiri akazi. Yesu sankatengera maganizo a Afarisi omwe ankaona kuti akazi ndi otsika. Afarisi sankalankhula ndi akazi pagulu ngakhale kukambirana nawo mfundo za m’Malemba. Koma Yesu ankakambirana mfundo zofunika za m’Malemba ndi amuna kuphatikizaponso akazi omwe anali ophunzira ake. * (Werengani Luka 10:38, 39, 42.) Iye ankapitanso limodzi ndi akazi kokalalikira. (Luka 8:1-3) Komanso Yesu anapereka mwayi kwa akazi woti akauze atumwi ake kuti iye waukitsidwa.​—Yoh. 20:16-18.

6. Kodi mtumwi Paulo anasonyeza bwanji kuti ankalemekeza akazi?

6 Mtumwi Paulo anakumbutsa Timoteyo kuti azilemekeza akazi. Paulo anamuuza kuti aziona ‘akazi achikulire ngati amayi ake’ komanso ‘akazi achitsikana ngati alongo ake.’ (1 Tim. 5:1, 2) Ngakhale kuti Paulo anachita zambiri pothandiza Timoteyo kuti akhale ndi chikhulupiriro cholimba, iye ankadziwa kuti amayi ake ndi agogo ake ndi amene anayambirira kumuphunzitsa “malemba oyera.” (2 Tim. 1:5; 3:14, 15) M’kalata imene analembera Akhristu a ku Roma, Paulo anaperekanso moni kwa alongo pochita kuwatchula mayina. Si kuti Paulo ankangoona utumiki umene alongo ankachita, koma ankawayamikiranso chifukwa cha zimenezi.​—Aroma 16:1-4, 6, 12; Afil. 4:3.

7. Kodi tsopano tikambirana mafunso ati?

7 Monga mmene taonera mundime zapitazi, palibe Malemba amene amasonyeza kuti alongo ndi otsika poyerekezera ndi abale. Alongo athu okondedwawa ndi ofunika kwambiri ndipo akulu amawadalira kuti angathandize kuti mumpingo anthu azikhala mwamtendere komanso mogwirizana. Komabe tiyenera kupeza mayankho a mafunso ngati awa: N’chifukwa chiyani Yehova amafuna kuti alongo azivala chinachake kumutu pa zochitika zina? Popeza kuti abale ndi amene amaikidwa kukhala akulu kapena atumiki othandiza, kodi zimenezi zikutanthauza kuti m’bale aliyense ndi mutu wa mlongo aliyense mumpingo?

KODI M’BALE ALIYENSE NDI MUTU WA MLONGO ALIYENSE?

8. Mogwirizana ndi Aefeso 5:23, kodi m’bale aliyense ndi mutu wa mlongo aliyense? Fotokozani.

8 Yankho lachidule ndi lakuti ayi. M’bale samakhala mutu wa alongo onse mumpingo, koma Khristu. (Werengani Aefeso 5:23.) M’banja mwamuna ndi amene amakhala mutu wa mkazi wake. Mwana wamwamuna wobatizidwa si mutu wa mayi ake. (Aef. 6:1, 2) Ndipo mumpingo, udindo wa akulu pa abale ndi alongo uli ndi malire. (1 Ates. 5:12; Aheb. 13:17) Akazi osakwatiwa omwe sakukhala ndi bambo awo ndi mayi awo, amapitirizabe kulemekeza makolo awo komanso akulu. Komabe mofanana ndi abale mumpingo, nawonso mutu wawo ndi Yesu.

Omwe sali pabanja ndipo sakukhala ndi makolo awo mutu wawo ndi Yesu (Onani ndime 8)

9. N’chifukwa chiyani nthawi zina alongo ayenera kuvala chinachake kumutu?

9 N’zoona kuti Yehova anasankha kuti amuna azitsogolera pa nkhani yophunzitsa komanso pa zinthu zina zokhudza kulambira mumpingo, koma sanapereke udindo umenewu kwa akazi. (1 Tim. 2:12) N’chifukwa chiyani anachita zimenezi? Chifukwa chake ndi chofanana ndi chimene anasankhira kuti Yesu akhale mutu wa mwamuna, chomwe ndi kuonetsetsa kuti zinthu m’banja lake zikuchitika mwadongosolo. Ndiye ngati pa zifukwa zina mlongo akufunika kuchita zinazake zomwe zimafunika kuchitidwa ndi m’bale, Yehova amafuna kuti mlongoyo avale chinachake kumutu. * (1 Akor. 11:4-7) Yehova amafuna kuti akazi azichita zimenezi osati chifukwa choti amawaona kuti ndi otsika, koma amafuna kuwapatsa mwayi wosonyeza kuti amalemekeza zimene iye anakonza zoti amuna azitsogolera. Ndiye poganizira zimenezi, tiyeni tikambirane yankho la funso lakuti: Kodi amuna omwe ndi mitu ya mabanja komanso akulu ali ndi udindo wotani?

UDINDO WA MITU YA MABANJA KOMANSO AKULU

10. N’chifukwa chiyani nthawi zina mkulu angafune kumapanga malamulo mumpingo?

10 Akulu amakonda Khristu komanso “nkhosa” zimene iye ndi Yehova anawapatsa kuti azizisamalira. (Yoh. 21:15-17) Chifukwa choti mkulu amasamalira mpingo, mwina akhoza kumaona kuti abale ndi alongo ali ngati ana ake. Iye akhoza kumaganiza kuti popeza mwamuna amakonza malamulo n’cholinga chofuna kuteteza banja lake, nayenso mkulu angathe kupanga malamulo amene akuona kuti angateteze nkhosa za Mulungu. Ndipotu abale ndi alongo ena akhoza kumalimbikitsa akulu kuti azichita zimenezi powapempha kuti aziwasankhira zochita. Koma kodi udindo umene akulu ali nawo mumpingo ndi wofanana ndi wa mitu ya mabanja?

Akulu amathandiza onse mumpingo kuti apitirize kukhala pa ubwenzi ndi Yehova komanso aziona kuti amawakonda. Yehova anapatsa akulu udindo woonetsetsa kuti mpingo uzikhala woyera (Onani ndime 11-12)

11. Kodi udindo wa mitu ya mabanja ndi wofanana bwanji ndi wa akulu mumpingo?

11 Mtumwi Paulo anasonyeza kuti pali kufanana kwina pakati pa udindo umene mitu ya mabanja imakhala nawo ndi udindo wa akulu. (1 Tim. 3:4, 5) Mwachitsanzo, Yehova amafuna kuti aliyense m’banja azimvera mutu wa banjalo. (Akol. 3:20) Mofanana ndi zimenezi, amafunanso kuti onse mumpingo azimvera akulu. Yehova amayembekezera kuti mitu ya mabanja komanso akulu azithandiza anthu amene amawatsogolera kuti azimukonda. Komanso onsewa amayesetsa kuthandiza anthu amene akuwatsogolera kuti aziona kuti amakondedwa. Ndipo mofanana ndi mitu ya mabanja yabwino, akulu amayesetsa kuthandiza abale ndi alongo amene akumana ndi mavuto. (Yak. 2:15-17) Kuwonjezera pamenepo, Yehova amafuna kuti akulu komanso mitu ya mabanja azithandiza anthu amene akuwatsogolera kutsatira mfundo zake ndipo amafunanso kuti iwo ‘asamapitirire zinthu zolembedwa’ m’Baibulo.​—1 Akor. 4:6.

Mitu ya mabanja inapatsidwa ndi Yehova udindo wotsogolera mabanja awo. Mwamuna wabwino amakambirana kaye ndi mkazi wake asanasankhe zochita (Onani ndime 13)

12-13. Mogwirizana ndi Aroma 7:2, kodi udindo wa mitu ya mabanja ndi wosiyana bwanji ndi wa akulu?

12 Komabe palinso kusiyana pakati pa udindo umene akulu ali nawo ndi udindo umene amuna omwe ndi mitu ya mabanja ali nawo. Mwachitsanzo, Yehova anapereka kwa akulu udindo woweruza komanso wochotsa munthu aliyense amene wachita tchimo koma osalapa.​—1 Akor. 5:11-13.

13 Yehova anapereka kwa mitu ya mabanja udindo wina umene sanaupereke kwa akulu. Iye anapatsa mwamuna udindo wopanga malamulo komanso kuwonetsetsa kuti aliyense m’banja lake akuwatsatira. (Werengani Aroma 7:2.) Mwachitsanzo, iye ali ndi ufulu wokhazikitsa nthawi imene ana ake ayenera kufika pakhomo madzulo. Alinso ndi mphamvu yopereka chilango kwa anawo ngati atalephera kumvera lamuloli. (Aef. 6:1) Komatu mwamuna wabwino amayamba wakambirana kaye ndi mkazi wake asanakhazikitse malamulo m’banja mwawo, pajatu awiriwa ndi “thupi limodzi.” *​—Mat. 19:6.

MUZILEMEKEZA KHRISTU MONGA MUTU WAMPINGO

Yesu, motsogoleredwa ndi Yehova, amapereka malangizo mumpingo wa Chikhristu (Onani ndime 14)

14. (a) Mogwirizana ndi Maliko 10:45, n’chifukwa chiyani n’zomveka kuti Yehova anasankha Yesu kuti akhale mutu wampingo? (b) Kodi udindo wa Bungwe Lolamulira ndi wotani? (Onani bokosi lakuti “Udindo wa Bungwe Lolamulira.”)

14 Yehova anagwiritsa ntchito dipo pogula moyo wa onse mumpingo komanso aliyense amene angakhulupirire Yesu. (Werengani Maliko 10:45; Mac. 20:28; 1 Akor. 15:21, 22) Choncho m’pomveka kuti Yehova anasankha Yesu yemwe anapereka moyo wake monga dipo kuti akhale mutu wampingo. N’chifukwa chake Yesu ali woyenera kupanga malamulo oti anthu, mabanja komanso aliyense mumpingo azitsatira, ndipo ali ndi udindo woonetsetsa kuti aliyense akutsatira malamulowo. (Agal. 6:2) Kuwonjezera pa kupanga malamulo palinso zambiri zimene Yesu amachita. Iye amatisamalira ndipo amakonda wina aliyense wa ife.​—Aef. 5:29.

15-16. Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene mlongo wina dzina lake Marley komanso m’bale wina dzina lake Benjamin ananena?

15 Alongo amasonyeza kuti amalemekeza Khristu akamatsatira malangizo a amuna amene iye wawasankha kuti aziwatsogolera. Alongo ambiri angavomereze zimene mlongo wina dzina lake Marley, yemwe amakhala ku United States, ananena. Iye anati: “Ndimayamikira kwambiri udindo umene ndili nawo monga mkazi wokwatiwa komanso mlongo mumpingo. Nthawi zonse ndimayesetsa kuti ndizilemekeza udindo umene Yehova anapereka kwa mwamuna wanga komanso kwa akulu. Koma mwamuna wanga ndi abale mumpingo amandithandiza kuti zimenezi zisakhale zovuta, chifukwa amandilemekeza komanso kundiyamikira chifukwa cha ntchito imene ndimagwira.”

16 Abale akamalemekeza alongo, amasonyeza kuti amamvetsa zimene Yehova anakonza zoti amuna azitsogolera. M’bale wina dzina lake Benjamin, yemwe amakhala ku England, ananena kuti: “Ndimaphunzira zambiri mu ndemanga zimene alongo amapereka pamisonkhano. Ndimaphunziranso mfundo zimene zingandithandize ndikamaphunzira pandekha komanso zimene ndingachite kuti ndizilalikira ndiponso kuphunzitsa mwaluso mu utumiki. Ndimaona kuti alongo amagwira ntchito yofunika kwambiri.”

17. N’chifukwa chiyani tiyenera kumalemekeza zimene Yehova anakonza zoti ena azitsogolera?

17 Ngati onse mumpingo kaya ndi amuna, akazi, mitu ya mabanja komanso akulu amamvetsa komanso kulemekeza zimene Yehova anakonza zoti ena azitsogolera, mumpingo mumakhala mtendere. Ndipo chofunika kwambiri n’chakuti zimenezi zimathandiza kuti Atate wathu wakumwamba Yehova, azilemekezedwa.​—Sal. 150:6.

NYIMBO NA. 123 Tizigonjera Mulungu Mokhulupirika

^ ndime 5 Kodi Yehova anapatsa alongo ntchito yotani mumpingo? Kodi m’bale aliyense amakhala mutu wa mlongo aliyense mumpingo? Kodi udindo wa akulu mumpingo ndi wofanana ndi wa mitu ya mabanja? Munkhaniyi, tiona mmene Baibulo litithandizire kupeza mayankho a mafunsowa.

^ ndime 5 Onani ndime 6 munkhani yakuti “Muzilimbikitsa Alongo Mumpingo,” yomwe ili mu Nsanja ya Olonda ya September 2020.

^ ndime 13 Kuti mudziwe amene ayenera kusankhira banja, mpingo woti azikasonkhana, werengani ndime 17-19 munkhani yakuti, “Muziona Kuti Anthu Ena Ndi Ofunika Mumpingo” yomwe ili mu Nsanja ya Olonda ya August 2020.

^ ndime 59 Kuti mudziwe zambiri pa nkhaniyi onani buku lakuti, Kodi Mungatani Kuti ‘Mulungu Apitirize Kukukondani’? tsamba 209-212.

^ ndime 64 Kuti mudziwe zambiri zokhudza udindo wa Bungwe Lolamulira, onani Nsanja ya Olonda ya July 15, 2013, tsamba 20-25.