Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 7

Kumvetsa Tanthauzo la Umutu Mumpingo

Kumvetsa Tanthauzo la Umutu Mumpingo

Khristu ali mutu wa mpingo, pokhala mpulumutsi wa thupilo.’​AEF. 5:23.

NYIMBO 137 Azimayi Okhulupilika, Alongo Athu

ZIMENE TIKAMBILANE *

1. Mwa zina, n’ciani cimapangitsa banja la Yehova kukhala logwilizana?

TIMAKONDWELA kukhala m’banja la Yehova. N’cifukwa ciani banja lathu ni lamtendele komanso logwilizana? Cifukwa cimodzi n’cakuti tonsefe timacita zonse zotheka polemekeza dongosolo la umutu limene Yehova anakhazikitsa. Ndipo kumvetsa bwino dongosolo la umutu, kudzatithandiza kukhala ogwilizana kwambili.

2. Kodi tipeza mayankho pa mafunso ati m’nkhani ino?

2 M’nkhani ino, tidzakambilana za umutu mumpingo. Tidzapezanso mayankho pa mafunso aya: Kodi alongo ali na mbali yanji mumpingo? Kodi n’zoona kuti m’bale aliyense ni mutu wa mlongo aliyense? Kodi ulamulilo umene akulu ali nawo pa abale na alongo ni wolingana na umene mutu wa banja ali nawo pa mkazi wake na ŵana ŵake? Coyamba, tiyeni tikambilane mmene tiyenela kuwaonela alongo.

KODI ALONGO TIYENELA KUWAONA BWANJI?

3. Kodi tingakulitse bwanji ciyamikilo cathu pa nchito zimene alongo athu amacita?

3 Timawayamikila kwambili alongo athu amene amagwila nchito molimbika posamalila mabanja awo, kulalikila uthenga wabwino, na kucilikiza mpingo. Tingakulitse ciyamikilo cathu pa iwo mwa kudziŵa mmene Yehova na Yesu amawaonela. Tidzaphunzilanso mmene mtumwi Paulo anali kucitila zinthu na azimayi.

4. Kodi Baibo imaonetsa bwanji kuti Yehova amaona akazi komanso amuna kuti ni ofunika?

4 Baibo imaonetsa kuti kwa Yehova, amuna komanso akazi ni ofunika mofanana. Mwacitsanzo, imaonetsa kuti m’nthawi ya atumwi, Yehova anapeleka mzimu woyela kwa akazi komanso kwa amuna, ndipo anawapatsa mphamvu yocita zozizwitsa monga kulankhula zinenelo zosiyana-siyana. (Mac. 2:1-4, 15-18) Onse, amuna na akazi anadzozedwa na mzimu woyela, ndipo ali na ciyembekezo cokalamulila pamodzi na Khristu. (Agal. 3:26-29) Akazi komanso amuna, adzalandila mphoto ya moyo wosatha padziko lapansi. (Chiv. 7:9, 10, 13-15) Ndipo onse, amuna na akazi, anapatsidwa nchito yolalikila na kuphunzitsa anthu uthenga wabwino. (Mat. 28:19, 20) Buku la Macitidwe limafotokoza nchito ya mlongo wina dzina lake Purisikila, amene pamodzi na mwamuna wake Akula, anathandiza kufotokoza coonadi molondola kwa mwamuna wina wophunzila bwino, dzina lake Apolo.—Mac. 18:24-26.

5. Kodi Luka 10:38, 39, 42, ionetsa kuti Yesu anali kuwaona bwanji akazi?

5 Yesu anali kulemekeza akazi. Iye sanatsatile miyambo ya Afarisi. Iwo anali kuona kuti akazi ni otsika, ndipo sanali kukamba nawo n’komwe pagulu ngakhale kukambilana nawo Malemba. Koma Yesu anali kukambilana na akazi mfundo za coonadi pamodzi na amuna. * (Ŵelengani Luka 10:38, 39, 42.) Iye analolanso akazi kupita naye kokalalikila. (Luka 8:1-3) Ndipo Yesu anapatsa mwayi akazi kuti akauze atumwi kuti iye waukitsidwa kwa akufa.—Yoh. 20:16-18.

6. Kodi mtumwi Paulo anaonetsa bwanji kuti anali kulemekeza akazi?

6 Mtumwi Paulo anakumbutsa Timoteyo kuti azilemekeza akazi. Paulo anamuuza kuti aziona ‘akazi acikulile ngati amayi ake’ komanso ‘akazi acitsikana ngati alongo ake.’ (1 Tim. 5:1, 2) Paulo anacita zambili pothandiza Timoteyo kukhala Mkhristu wokhwima. Ngakhale n’telo, iye anali kudziŵa kuti amayi ake a Timoteyo, komanso ambuye ŵake, ndiwo anayamba kum’phunzitsa “malemba oyela.” (2 Tim. 1:5; 3:14, 15) M’kalata imene Paulo analembela Aroma, anapeleka moni kwa alongo mwa kuwachula maina. Iye anali kudziŵa nchito zimene alongowo anali kucita, ndipo anawayamikila pa nchito zawo monga Akhristu.—Aroma 16:1-4, 6, 12; Afil. 4:3.

7. Kodi tikambilane mafunso ati lomba?

7 Monga taonela m’ndime zapitazi, palibe maziko a m’Malemba oonetsa kuti alongo ni otsika kwa abale. Alongo athu acikondi komanso owolowa manja amathandiza kwambili mumpingo, ndipo akulu amadalila thandizo lawo polimbikitsa mtendele na mgwilizano mumpingo. Koma pali mafunso ena amene afunika mayankho. Mwacitsanzo: N’cifukwa ciani Mulungu amafuna kuti mlongo azivala cakumutu pa zocitika zina? Popeza kuti ni abale cabe amene amaikidwa kukhala akulu kapena atumiki othandiza, kodi izi zitanthauza kuti m’bale aliyense ni mutu wa mlongo aliyense mumpingo?

KODI M’BALE ALIYENSE NI MUTU WA MLONGO ALIYENSE?

8. Malinga na Aefeso 5:23, kodi m’bale aliyense ni mutu wa mlongo aliyense? Fotokozani.

8 Yankho lacidule ni ayi! M’bale si mutu wa alongo onse mumpingo. Koma Khristu ndiye mutu wawo. (Ŵelengani Aefeso 5:23.) M’banja, mwamuna ali na ulamulilo pa mkazi wake. Mwana wobatizika wamwamuna si mutu wa amayi ake ayi. (Aef. 6:1, 2) Ndipo mumpingo, ulamulilo wa akulu pa abale na alongo uli na malile. (1 Ates. 5:12; Aheb. 13:17) Akazi osakwatiwa amene sakhala na makolo awo amapitiliza kulemekeza makolowo komanso akulu. Komabe, mofanana na amuna onse mumpingo, Yesu cabe ndiye mutu wawo.

Amene sali pabanja ndipo sakhala na makolo awo, ali pansi pa umutu wa Yesu (Onani ndime 8)

9. N’cifukwa ciani alongo nthawi zina amafunika kuvala cakumutu?

9 Ngakhale n’telo, Yehova anaika amuna kuti azitsogolela pa kuphunzitsa na kulambila mumpingo, ndipo sanapatse akazi udindowo. (1 Tim. 2:12) Cifukwa ciani? Kuti mumpingo mukhale dongosolo, monga mmene Yehova anaikila Yesu kukhala mutu wa mwamuna kuti m’banja mukhale dongosolo. Ngati pa zifukwa zina mlongo afunika kucita mbali imene kambili imasamalidwa na m’bale, Yehova amafuna kuti iye avale cakumutu. * (1 Akor. 11:4-7) Yehova amafuna alongo kucita zimenezi osati kuti awapeputse, koma kuwapatsa mwayi woonetsa kuti amalemekeza dongosolo la umutu limene iye anakhazikitsa. Tili na mfundo zimenezi m’maganizo, tiyeni lomba tipeze yankho la funso ili: Kodi mitu ya mabanja komanso akulu, ali na ulamulilo wotani?

ULAMULILO UMENE MITU YA MABANJA NA AKULU ALI NAWO

10. N’ciani cingapangitse mkulu kufuna kumapanga malamulo mumpingo?

10 Akulu amamukonda Khristu, komanso amakonda “nkhosa” zimene Yehova na Yesu anaziikiza m’manja mwawo kuti azisamalile. (Yoh. 21:15-17) Na zolinga zabwino, mkulu angamaganize kuti ali monga tate mumpingo. Iye angamaganize kuti ngati mutu wa banja ali na ufulu wopanga malamulo oteteza banja lake, ndiye kuti mkulu nayenso angapange malamulo amene aona kuti adzateteza nkhosa za Mulungu. Ndipo abale na alongo ena angamalimbikitse akulu kucita zinthu monga mitu yawo yauzimu, mwa kuwapempha kuwapangila zosankha. Koma kodi akulu mumpingo na mitu ya mabanja ali na ulamulilo wofanana?

Akulu amathandiza ofalitsa mumpingo kukhalabe olimba mwauzimu, na kuwathandiza kumva kuti amakondedwa. Yehova anawapatsa udindo wocotsa anthu osalapa mumpingo (Onani ndime 11-12)

11. Kodi udindo wa mitu ya mabanja na uja wa akulu ni wofananako pambali ziti?

11 Mtumwi Paulo anaonetsa kuti pali mbali zofanana pakati pa udindo wa mutu wa banja na udindo wa mkulu. (1 Tim. 3:4, 5) Mwacitsanzo, Yehova amafuna kuti a m’banja lake azimumvela monga mutu wawo. (Akol. 3:20) Amafunanso kuti ofalitsa mumpingo azimvela akulu. Yehova amafuna kuti mitu ya mabanja komanso akulu azionetsetsa kuti anthu amene ali pansi pa cisamalilo cawo ni olimba mwauzimu. Mitu ya mabanja na akulu, amafunikanso kulimbikitsa anthu amene ali pansi pa uyang’anilo wawo kumva kuti amakondedwa. Ndipo mofanana na mitu ya mabanja yabwino, akulu nawonso amaonetsetsa kuti anthu amene ali pansi pa cisamalilo cawo, akulandila thandizo pa nthawi zovuta. (Yak. 2:15-17) Pamwamba pa izi, Yehova amafunanso kuti akulu na mitu ya mabanja azilimbikitsa ena kutsatila miyezo yake, komanso ‘kusapitilila zinthu zolembedwa’ m’Baibo.—1 Akor. 4:6.

Mitu ya mabanja inapatsidwa udindo na Yehova, wotsogolela m’mabanja awo. Mwamuna amene ni mutu wa banja wacikondi, amafunsila kwa mkazi wake asanapange zosankha (Onani ndime 13)

12-13. Mogwilizana na Aroma 7:2, kodi udindo wa mitu ya mabanja komanso wa akulu umasiyana bwanji?

12 Komabe, palinso mbali zosiyana kwambili pakati pa udindo wa mkulu, na uja wa mutu wa banja. Mwacitsanzo, Yehova anapatsa akulu udindo wokhala oweluza na kucotsa anthu osalapa mumpingo.—1 Akor. 5:11-13.

13 Kumbali ina, Yehova anapatsa mitu ya mabanja ulamulilo umene akulu alibe. Mwacitsanzo, anapatsa mutu wa banja mphamvu zopanga malamulo m’banja mwake na kuonetsetsa kuti akutsatilidwa. (Ŵelengani Aroma 7:2.) Mutu wa banja alinso na ufulu woika nthawi imene ana ake ayenela kufika panyumba m’madzulo. Komanso, ali na mphamvu zopeleka cilango kwa ana ake ngati alephela kutsatila lamulo limenelo. (Aef. 6:1) Ndipo saiŵala kuti mwamuna amene ni mutu wa banja wacikondi, amafunsila kwa mkazi wake asanapange malamulo pa nyumba, cifukwa iwo ni “thupi limodzi.” *Mat. 19:6.

LEMEKEZANI KHRISTU MONGA MUTU WA MPINGO

Yesu, amene ali pansi pa umutu wa Yehova, amatsogolela mpingo wacikhristu (Onani ndime 14)

14. (a) Mogwilizana na zimene Maliko 10:45 imakamba, n’cifukwa ciani m’pake kuti Yehova anasankha Yesu kukhala mutu wa mpingo? (b) Kodi udindo wa Bungwe Lolamulila ni wotani? (Onani bokosi lakuti “ Udindo wa Bungwe Lolamulila.”)

14 Kupitila mu nsembe ya dipo, Yehova anagula moyo wa aliyense mumpingo. (Ŵelengani Maliko 10:45; Mac. 20:28; 1 Akor. 15:21, 22) Conco m’pake kuti anasankha Yesu, amene anapeleka moyo wake monga dipo kuti akhale mutu wa mpingo. Pokhala mutu wathu, Yesu ali na mphamvu zopanga malamulo amene munthu aliyense payekha, mabanja, komanso mpingo uyenela kutsatila. Iye alinso na mphamvu zoonetsetsa kuti malamulowo akutsatilidwa. (Agal. 6:2) Koma Yesu sapanga cabe malamulo. Amatidyetsa komanso amakonda aliyense wa ife.—Aef. 5:29.

15-16. Kodi mwaphunzila ciani pa zimene mlongo Marley na m’bale Benjamin anakamba?

15 Alongo amaonetsa kuti amalemekeza Khristu mwa kutsatila citsogozo ca amuna amene iye anawaika monga otsogolela. Alongo ambili, angagwilizane na zimene mlongo Marley wa ku America anakamba. Iye anati: “Nimayamikila malo anga monga mkazi wokwatiwa komanso mlongo mumpingo. Nthawi zina zimanivuta kuona moyenela dongosolo la Yehova la umutu. Koma cifukwa cakuti mwamuna wanga na abale mumpingo amanilemekeza na kuniyamikila, zimenezi zakhala zosavuta kwa ine.”

16 Abale amaonetsa kuti amamvetsa dongosolo la umutu mwa kulemekeza alongo. M’bale Benjamin wa ku England anati: “Naphunzila zambili kucokela pa ndemanga za alongo pamisonkhano, komanso pa malingalilo awo a mocitila phunzilo laumwini, na mmene ningakhalile waluso mu ulaliki. Niona kuti zimene amacita, n’zofunika kwambili.”

17. N’cifukwa ciani tiyenela kulemekeza dongosolo la umutu?

17 Ngati onse mumpingo—amuna, akazi, mitu ya mabanja, na akulu—amvetsa na kulemekeza dongosolo la umutu, mumpingo mumakhala mtendele. Ndipo koposa zonse, timatamanda Atate wathu wakumwamba wacikondi, Yehova.—Sal. 150:6.

NYIMBO 123 Gonjelani Dongosolo la Mulungu

^ ndime 5 Kodi alongo ali na mbali yanji mumpingo? Kodi m’bale aliyense ni mutu wa mlongo aliyense? Kodi akulu na mitu ya mabanja ali na ulamulilo wolingana? M’nkhani ino, tikambilana mafunso amenewa mogwilizana na zitsanzo zopezeka m’Mawu a Mulungu.

^ ndime 5 Onani ndime 6 m’nkhani yakuti “Muziwathandiza Alongo Mumpingo,” yopezeka mu Nsanja ya Mlonda ya September 2020.

^ ndime 13 Kuti mudziŵe zambili za amene ayenela kusankhila banja kosonkhana, onani ndime 17-19 m’nkhani yakuti “Lemekezani Wina Aliyense Mumpingo,” yopezeka mu Nsanja ya Mlonda ya August 2020.

^ ndime 59 Kuti mudziŵe zambili pa nkhaniyi, onani buku lakuti “Khalanibe M’cikondi ca Mulungu,” tsamba 209-212.

^ ndime 64 Kuti mudziŵe zambili za udindo wa Bungwe Lolamulila, onani Nsanja ya Mlonda ya July 1, 2013, tsa. 26-31.