Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Zonsezi Zinatheka Cifukwa ca Kumwetulila!

Zonsezi Zinatheka Cifukwa ca Kumwetulila!

ATSIKANA aŵili anali kuyenda mu mzinda wa Baguio ku Philippines. Iwo anaona kasitandi ka ulaliki wapoyela, koma sanapatukilepo. Mlongo Helen amene anali pa kasitandipo, anamwetulila mwaubwenzi atawayang’ana. Atsikanawo anapitiliza ulendo wawo, koma anakondwela kwambili cifukwa ca kumwetulila mwaubwenzi kwa mlongo Helen.

Atsikanawo pobwelela kunyumba pa basi, anaona cizindikilo cacikulu ca jw.org pa Nyumba ya Ufumu. Iwo anakumbukila kuti n’cimene anaonanso pa kasitandi ka ulaliki kaja. Iwo anatsika m’basiyo, na kupita kukayang’ana nthawi zosonkhana za mipingo yosiyana-siyana zimene zinandandalikidwa pa cikwangwani ca pageti ya Nyumba ya Ufumu.

Atsikana aŵiliwo anapezeka pa msonkhano wotsatila. Pamene anali kuloŵa m’Nyumba ya Ufumu, iwo anadabwa kuona mlongo Helen! Mwamsanga anam’kumbukila mlongoyo kuti ni munthu uja amene anawamwetulila mwansangala. Mlongo Helen anati: “Iwo atabwela kwa ine n’nada nkhawa. N’naganiza kuti mwina n’nalakwitsa cina cake.” Koma atsikanawo anafotokozela mlongo Helen kuti anali atamuona pa kasitandi ka ulaliki.

Atsikanawo anasangalala na msonkhanowo komanso mayanjano, ndipo anamva kukhala omasuka. Ataona ena akuyeletsa mu Nyumba ya Ufumu pambuyo pa msonkhanowo, anapempha kuti athandizeko. Mmodzi wa atsikanawo anapita ku dziko lina, koma mtsikana winayo anayamba kupezeka kumisonkhano, ndipo anayamba kuphunzila Baibo—Inde, zonsezi zinatheka cifukwa ca kumwetulila!