Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 13

Yehova Adzakutetezani—Motani?

Yehova Adzakutetezani—Motani?

“Ambuye [Mulungu] ndi wokhulupilika ndipo adzakulimbitsani ndi kukutetezani kwa woipitsitsayo.”—2 ATES. 3:3.

NYIMBO 124 Tikhale Okhulupilika Nthawi Zonse

ZIMENE TIKAMBILANE *

1. N’cifukwa ciani Yesu anapempha Yehova kuti ayang’anile ophunzila ake?

PATSIKU lothela kukhala na moyo monga munthu, m’madzulo, Yesu anali kuganizila za mavuto amene ophunzila ake anali kudzakumana nawo. Cifukwa cokonda mabwenzi ake, Yesu anapempha atate wake kuti ‘awayang’anile kuopela woipayo.’ (Yoh. 17:14, 15) Yesu anadziŵa kuti iye akadzabwelela kumwamba, Satana adzapitiliza kucita nkhondo na aliyense wofuna kutumikila Yehova. N’zoonekelatu kuti anthu a Yehova anali kudzafunikila citetezo.

2. Tingakhale bwanji otsimikiza kuti Yehova adzayankha mapemphelo athu?

2 Yehova anayankha pemphelo la Yesu cifukwa com’konda pokhala Mwana wake. Ngati timayesetsa kukondweletsa Yehova, nayenso adzatikonda, ndipo adzamvetsela mapemphelo athu opempha thandizo na citetezo. Monga mutu wa banja wacikondi, Yehova adzapitiliza kusamalila ana ake mwacikondi. Cifukwa kusacita zimenezi kunganyozetse dzina lake na kuwononga mbili yake!

3. N’cifukwa ciani tifunikila citetezo ca Yehova masiku ano?

3 Tikufunikila citetezo ca Yehova kuposa kale lonse. Satana anam’pitikitsa kumwamba “ndipo ali ndi mkwiyo waukulu.” (Chiv. 12:12) Iye wapangitsa ena mwa anthu amene amatizunza kukhulupilila kuti akucita “utumiki wopatulika kwa Mulungu.” (Yoh. 16:2) Ena amene sakhulupilila Mulungu amatizunza cifukwa sitigwilizana nawo pa mfundo zimene dzikoli limayendela. Kaya anthu atizunze pa zifukwa zotani, siticita mantha. Cifukwa ciani? Cifukwa mawu a Mulungu amati: “Ambuye [Mulungu] ndi wokhulupilika ndipo adzakulimbitsani ndi kukutetezani kwa woipitsitsayo.” (2 Ates. 3:3) Kodi Yehova amatiteteza bwanji? Tiyeni tikambilane njila ziŵili.

YEHOVA AMATIPATSA ZIDA ZONSE ZANKHONDO

4. Malinga na Aefeso 6:13-17, kodi Yehova watipatsa ciani kuti atiteteze?

4 Yehova watipatsa zida zonse zankhondo zimene zingatiteteze ku misampha ya Satana. (Ŵelengani Aefeso 6:13-17.) Zida zauzimu zankhondo zimenezi n’zolimba ndiponso zothandiza! Koma tingakhale otetezeka kokha ngati tavala zida zonse zankhondo na kusazivula. Kodi cida ciliconse ciimila ciani? Tiyeni tikambilane.

5. Kodi lamba wacoonadi n’ciani? Nanga n’cifukwa ciani tiyenela kumuvala?

5 Lamba wacoonadi aimila coonadi copezeka m’Mawu a Mulungu, Baibo. N’cifukwa ciani tifunika kuvala lamba ameneyu? Cifukwa Satana ni “tate wake wa bodza.” (Yoh. 8:44) Iye wakhala akunama bodza kwa zaka masauzande, ndipo ‘wasoceletsa dziko lonse lapansi kumene kuli anthu’! (Chiv. 12:9) Koma coonadi copezeka m’Baibo cimatiteteza kuti tisanyengedwe. Kodi timavala bwanji lamba wophiphilitsa ameneyu? Timacita zimenezi mwa kuphunzila zoona zokhudza Yehova, mwa kum’lambila mu “mzimu ndi coonadi,” komanso mwa kucita zinthu zonse moona mtima.—Yoh. 4:24; Aef. 4:25; Aheb. 13:18.

Lamba: Coonadi copezeka m’Mawu a Mulungu

6. Kodi codzitetezela pacifuwa cacilungamo n’ciani? Nanga n’cifukwa ciani tifunika kucivala?

6 Codzitetezela pacifuwa cacilungamo cimaimila miyezo ya Yehova yolungama. N’cifukwa ciani tiyenela kuvala codzitetezela pacifuwa? Monga mmene covala pacifuwa cimatetezela mtima wa msilikali kuti asalasidwe, naconso codzitetezela pacifuwa cacilungamo cimateteza mtima wathu wophiphilitsa, kapena kuti munthu wathu wamkati kuzisonkhezelo zoipa za m’dzikoli. (Miy. 4:23) Yehova amafuna kuti tizim’konda na kum’tumikila na mtima wathu wonse. (Mat. 22:36, 37) Satana amayesa kugaŵanitsa mtima wathu mwa kutipangitsa kukonda zinthu zimene dzikoli limapeleka—zinthu zimene Yehova amadana nazo. (Yak. 4:4; 1 Yoh. 2:15, 16) Ngati izo zalepheleka, iye amayesa kutipangitsa kucita zinthu zosemphana na miyezo ya Yehova.

Codzitetezela pacifuwa: Miyezo yolungama ya Yehova

7. Kodi timavala bwanji codzitetezela pacifuwa cacilungamo?

7 Timavala codzitetezela pacifuwa cacilungamo mwa kutsatila miyezo ya Yehova ya cabwino na coipa, ndiponso kukhala umoyo wogwilizana na miyezo imeneyo. (Sal. 97:10) Ena amaona kuti miyezo ya Yehova ni yopanikiza. Koma ngati tingaleke kuseŵenzetsa mfundo za m’Baibo mu umoyo wathu, tingakhale monga msilikali amene wavula codzitetezela pacifuwa nkhondo ili mkati, cifukwa coganiza kuti n’colema ngako. Kucita zimenezi kungakhale kupusa kwambili. Kwa amene amakonda Yehova, malamulo ake ni “osalemetsa” koma opulumutsa moyo.—1 Yoh. 5:3.

8. Kodi kuveka mapazi athu nsapato zokonzekela kulengeza uthenga wabwino kumatanthauza ciani?

8 Paulo akutilimbikitsanso kuveka mapazi athu nsapato zokonzekela kulengeza uthenga wabwino wamtendele. M’mawu ena tingati tiyenela kukhala okonzeka nthawi zonse kulengeza uthenga wabwino wa Ufumu. Tikamauzako ena uthenga wa m’Baibo, cikhulupililo cathu cimalimba. N’zolimbikitsa kwambili kuona mmene anthu a Yehova padziko lonse akupezela mipata yolengeza uthenga wabwino. Iwo amacita zimenezi kunchito, kusukulu, kumalo a malonda, polalikila nyumba na nyumba, pokagula zinthu, pokacezela acibale osakhulupilila, poceza na anzawo, komanso ngakhale pamene sakucoka panyumba kwa kanthawi. Ngati tingacite mantha na kuleka kulalikila, tingafanane na msilikali amene wavula nsapato zake nkhondo ili mkati. Mapazi ake akhoza kuvulazidwa mosavuta. Cotulukapo cake n’cakuti cingakhale covuta kuti adziteteze akaukilidwa, ndipo sangakwanitse kutsatila malangizo a mkulu wa asilikali.

Nsapato: Kukhala wokonzeka kulalikila uthenga wabwin

9. N’cifukwa ciani tiyenela kunyamula cishango cacikulu cacikhulupililo?

9 Cishango cacikulu cacikhulupililo cimaimila cikhulupililo cimene tili naco mwa Yehova. Timakhulupilila kuti Yehova adzakwanilitsa malonjezo ake onse. Cikhulupililo cimeneco cimatithandiza ‘kuzimitsa mivi yonse yoyaka moto ya woipayo.’ N’cifukwa ciani tiyenela kunyamula cishango cacikulu cimeneci? Cifukwa cimatiteteza kuti tisatengeke na ziphunzitso za anthu ampatuko, kapena kucita mantha na mawu onyodola ocokela kwa anthu otsutsa. Popanda cikhulupililo sitingakhale na mphamvu zokwanitsa kukana, ena akatinyengelela kunyalanyaza miyezo ya Yehova. Kumbali ina, nthawi zonse tikaikila kumbuyo cikhulupililo cathu kunchito, kapena kusukulu, timanyamula cishango cathu. (1 Pet. 3:15) Nthawi zonse tikakana nchito ya malipilo apamwamba imene ingasokoneze pulogilamu yathu yauzimu, ndiye kuti tanyamula cishango cathu. (Aheb. 13:5, 6) Ndipo tikamatumikilabe Yehova ngakhale pamene tikutsutsidwa, ndiye kuti tikutetezedwa na cishango cathu.—1 Ates. 2:2.

Cishango: Cikhulupililo cimene tili naco mwa Yehova komanso m’malonjezo ake

10. Kodi cisoti colimba cacipulumutso n’ciani? Nanga n’cifukwa ciani tifunika kucivala?

10 Cisoti colimba cacipulumutso ni ciyembekezo cimene Yehova amatipatsa. Ciyembekezo cimeneci cidzatipulumutsa ku imfa, cifukwa iye adzaukitsa onse ocita cifunilo cake. (1 Ates. 5:8; 1 Tim. 4:10; Tito 1:1, 2) Monga mmene cisoti ceni-ceni cimatetezela mutu wa msilikali, ciyembekezo cacipulumutso cimateteza kaganizidwe kathu. Ciyembekezo cimeneci cimatithandiza kusumika maganizo athu pa malonjezo a Mulungu, ndiponso cimatithandiza kuona mavuto moyenela. Kodi timacivala bwanji cisoti cimeneci? Timacita zimenezi mwa kuona zinthu mmene Mulungu amazionela. Mwacitsanzo, timadalila Mulungu osati cuma cosadalilika.—Sal. 26:2; 104:34; 1 Tim. 6:17.

Cisoti colimba: Ciyembekezo ca moyo wosatha

11. Kodi lupanga la mzimu n’ciani? Nanga n’cifukwa ciani tiyenela kuliseŵenzetsa?

11 Lupanga la mzimu ni Mawu a Mulungu, Baibo. Lupanga limeneli lili na mphamvu zotha kuvumbula cinyengo camtundu uliwonse na kumasula anthu kuukapolo wa ziphunzitso zabodza, komanso ku zizoloŵezi zoipa. (2 Akor. 10:4, 5; 2 Tim. 3:16, 17; Aheb. 4:12) Timaphunzila moseŵenzetsela bwino lupanga limeneli mwa kucita phunzilo laumwini komanso kupitila m’maphunzilo amene timalandila m’gulu la Mulungu. (2 Tim. 2:15) Kuwonjezela pa zida zonse zankhondo, Yehova watipatsanso mtundu wina wamphamvu wacitetezo. Kodi citetezo cimeneco n’ciani?

Lupanga: Mawu a Mulungu, Baibo

SITIMENYA TEKHA NKHONDOYI

12. N’ciani cina cimene tifunikila, ndipo cifukwa ciani?

12 Msilikali wodziŵa nkhondo amadziŵa kuti pa iye yekha sangagonjetse gulu lalikulu la asilikali. Amafunikila thandizo la asilikali anzake. Mofananamo, nafenso sitingakwanitse kugonjetsa Satana na otsatila ake pa ife tekha. Timafunikila thandizo la abale na alongo athu. Yehova watipatsa gulu la padziko lonse la “abale” amene alipo kuti azitithandiza.—1 Pet. 2:17.

13. Malinga na Aheberi 10:24, 25, kodi timapindula bwanji tikamapezeka kumisonkhano yathu?

13 Njila imodzi imene timalandilila thandizo ni mwa kupezeka kumisonkhano yathu. (Ŵelengani Aheberi 10:24, 25.) Tonsefe timalefuka nthawi zina. Koma kupezeka kumisonkhano kumatitsitsimula. Timalimbikitsidwa na ndemanga zogwila mtima za abale na alongo athu. Nkhani za m’Baibo na zitsanzo zimatilimbikitsa kupitiliza kutumikila Yehova. Ndipo maceza olimbikitsa amene timakhala nawo misonkhano isanayambe ndiponso pambuyo pake amatilimbikitsa. (1 Ates. 5:14) Kuwonjezela apo, misonkhano yathu imatipatsa mwayi wokhala na cimwemwe cobwela cifukwa cothandiza ena. (Mac. 20:35; Aroma 1:11, 12) Misonkhano yathu imatithandizanso m’njila zambili. Imatithandiza kukulitsa maluso athu pa kamenyedwe ka nkhondo, titelo kunena kwake, mwa kutiphunzitsa kagwilidwe ka nchito yolalikila. Mwacitsanzo, timaphunzila mmene tingaseŵenzetsele zida zophunzitsila za mu Thuboksi Yathu. Conco muzikonzekela bwino misonkhano ya mpingo. Misonkhano ili mkati muzimvetsela mwachelu. Pambuyo pa misonkhano, seŵenzetsani zimene mwaphunzila. Mwa kucita zimenezi, mudzakhala “msilikali wabwino wa Khristu Yesu.”—2 Tim. 2:3.

14. Kodi ni thandizo linanso liti limene tili nalo?

14 Tilinso na thandizo la angelo amphamvu miyanda-miyanda. Ganizilani zimene mngelo mmodzi cabe angacite! (Yes. 37:36) Ndiyeno ganizilani zimene gulu lankhondo lamphamvu la angelo lingakwanitse kucita. Palibe munthu kapena ciŵanda cimene cili na mphamvu kuposa gulu lamphamvu lankhondo la Yehova. Yehova ni wamphamvu zacikwane-kwane. Conco akakhala nafe, nthawi zonse tidzakhala amphamvu kuposa adani athu kaya akhale oculuka motani. (Ower. 6:16) Mawu amenewa ni oona. Muzikumbukila mfundo imeneyi nthawi zonse mukalefulidwa na zokamba kapena zocita za mnzanu wa kunchito, wa kusukulu, kapena wacibale wosakhulupilila. Kumbukilani kuti simuli mwekha pa nkhondoyi. Inu mukutsatila malangizo amene Yehova akupeleka.

YEHOVA ADZAPITILIZABE KUTITETEZA

15. Mogwilizana na Yesaya 54:15, 17, n’cifukwa ciani palibe amene angalepheletse anthu a Mulungu kugwila nchito yolalikila?

15 Dziko lolamulidwa na Satanali limadana nafe pa zifukwa zambili. Sititengako mbali ngakhale pang’ono m’zandale, ndipo siticitako nawo nkhondo. M’malomwake timalengeza dzina la Mulungu, kucilikiza Ufumu wake kuti ndiwo wokha umene udzabweletsa mtendele padzikoli, na kusunga miyezo yake yolungama. Timavumbula wolamulila wa dzikoli kuti ni wabodza la mkunkhuniza ndiponso wakupha. (Yoh. 8:44) Cina, timalengeza kuti posacedwapa dziko la Satanali lidzawonongedwa. Ngakhale n’telo, Satana na otsatila ake sadzakwanitsa kulepheletsa nchito yathu yolalikila. Ife tidzapitilizabe kutamanda Yehova mulimonse mmene tingathele! Ngakhale kuti Satana ni wamphamvu, iye sanakwanitse kulepheletsa uthenga wa Ufumu kufikila anthu padziko lonse. Zimenezi zatheka kokha cifukwa ca citetezo ca Yehova.—Ŵelengani Yesaya 54:15, 17.

16. Kodi Yehova adzawapulumutsa bwanji anthu ake pa cisautso cacikulu?

16 Kodi kutsogolo kudzacitika ciani? Panthawi ya cisautso cacikulu, Yehova adzatipulumutsa m’njila ziŵili zocititsa cidwi. Yoyamba, iye adzapulumutsa atumiki ake okhulupilika panthawi imene adzacititsa mafumu a dzikoli kuwononga Babulo wamkulu, Ufumu wa cipembedzo conama. (Chiv. 17:16-18; 18:2, 4) Yaciŵili, iye adzapulumutsa anthu ake pamene adzawononga mbali zotsala za dziko la Satana pa Aramagedo.—Chiv. 7:9, 10; 16:14, 16.

17. Kodi timapindula bwanji tikam’mamatilabe Yehova?

17 Ngati timamatilabe kwa Yehova, Satana sadzativulaza kothelatu. Ndipo iye ni amene adzawonongedwa kothelatu. (Aroma 16:2) Conco, valani zida zonse zankhondo ndipo musazivule! Musayese kumenya mwekha nkhondo. Cilikizani abale na alongo anu. Ndipo tsatilani malangizo a Yehova. Mukacita zimenezi mudzakhala na cidalilo cakuti atate wanu wakumwamba wacikondi, adzakulimbitsani na kukutetezani.—Yes. 41:⁠10.

NYIMBO 149 Nyimbo ya Cipambano

^ ndime 5 Baibo inalonjeza kuti Yehova adzatilimbitsa na kutiteteza ku zinthu zimene zingatiwononge mwauzimu komanso ku zina zimene zingatiwononge kothelatu. Nkhani ino iyankha mafunso aya: N’cifukwa ciani tiyenela kutetezedwa? Kodi Yehova amatiteteza bwanji? Nanga tifunika kucita ciani kuti tipindule na thandizo limene Yehova amapeleka?