Mafunso Ochokera Kwa Owerenga
N’chifukwa chiyani Akhristu ayenera kusamala kwambiri akamagwiritsa ntchito mapulogalamu otumizira ndi kulandirira mauthenga?
Akhristu ena amagwiritsa ntchito njira zamakono polankhulana ndi achibale awo komanso Akhristu anzawo. Komabe, Akhristu olimba mwauzimu amakumbukira malangizo akuti: “Wochenjera amene waona tsoka amabisala. Koma anthu osadziwa zinthu amene amangopitabe amalangidwa.”—Miy. 27:12.
Timadziwa kuti Yehova amafuna kutiteteza. Choncho siticheza ndi anthu ochotsedwa, amene amayambitsa magawano kapena amene amaphunzitsa zinthu zabodza. (Aroma 16:17; 1 Akor. 5:11; 2 Yoh. 10, 11) Komanso tikudziwa kuti pali ena omwe amabwera kumisonkhano koma satsatira malamulo a m’Baibulo. (2 Tim. 2:20, 21) Ndiye tikamasankha anthu ocheza nawo, timafunika kukumbukira zimenezi. Komatu izi si zophweka ngati anthuwo timacheza nawo pogwiritsa ntchito njira zotumizirana mauthenga.
Tiyenera kukhala osamala posankha anzathu abwino ocheza nawo, makamaka tikamatumizirana mauthenga m’magulu okhala ndi anthu ambiri. Akhristu ena zinthu sizinawayendere bwino chifukwa cholowa m’magulu ngati amenewa. Ndipotu zingakhale zovuta kuti m’bale kapena mlongo adziwe anthu abwino ocheza nawo ngati gululo lili ndi anthu mahandiredi kapena masauzande. Tikutero chifukwa zingakhale zovuta kudziwa bwino munthu aliyense pagululo komanso kudziwa ngati ali ndi chikhulupiriro cholimba. Lemba la Salimo 26:4, limati: “Sindinakhale pansi pamodzi ndi anthu achinyengo. Ndipo sindinayanjane ndi anthu obisa umunthu wawo.” Zimenezi zikusonyeza kuti ndi bwino kuti tizitumizirana mauthenga ndi anthu okhawo amene timawadziwa.
Ngakhale Mkhristu atakhala kuti amatumizirana mauthenga ndi ena pagulu la anthu ochepa, ayenera kusamala ndi nthawi imene amathera komanso nkhani zimene anthu pagululo amakamba. Sitiyenera kuganiza kuti timafunika kuyankha uthenga uliwonse umene anzathu alemba pagulu kaya nkhaniyo ndi yotani kapenanso atenga nthawi yaitali bwanji akukambirana. Paulo anachenjeza Timoteyo za anthu amene amakhala “amiseche ndi olowerera nkhani za eni.” (1 Tim. 5:13) Masiku ano, n’zotheka kuchita zofanana ndi zimenezi kudzera pazipangizo zamakono.
Mkhristu wolimba mwauzimu samvetsera kapena kulankhulapo pa nkhani zachinsinsi kapena zoimba mlandu Akhristu ena. (Sal. 15:3; Miy. 20:19) Iye samvetsera kapena kuuza ena nkhani zimene zimaoneka zokopa koma zomwe zilibe umboni. (Aef. 4:25) Timalandira nkhani zabwino zambiri zochokera m’Baibulo komanso malipoti omwe tingawadalire kudzera pa jw.org komanso m’mapulogalamu a mwezi ndi mwezi a JW Broadcasting®.
A Mboni ena amagwiritsa ntchito njira zotumizirana mauthenga pofuna kugulitsa, kugula, kutsatsa malonda komanso pofuna kupeza anthu antchito. Zinthu zimenezi ndi zamalonda ndipo sizikhudzana ndi kulambira kwathu. Akhristu amene amafuna kuti ‘moyo wawo ukhale wosakonda ndalama,’ amapewa kugwiritsa ntchito ubale wathu n’cholinga chofuna kupeza ndalama.—Aheb. 13:5.
Kodi tiyenera kugwiritsa ntchito mapulogalamu otumizira mauthenga pofuna kupempha ndalama zothandizira abale ndi alongo athu omwe akumana ndi mavuto ena kapena ngozi zam’chilengedwe? Timakonda kwambiri abale athu ndipo nthawi zonse timathandizana komanso kulimbikitsana. (Yak. 2:15, 16) Koma kuchita zimenezi potumizirana mauthenga kudzera m’magulu okhala ndi anthu ambiri kungasokoneze zimene mpingo kapena ofesi ya nthambi yakonza pofuna kuthandiza anthu amene akumana ndi mavuto enaake. (1 Tim. 5:3, 4, 9, 10, 16) Ndipotu palibe aliyense wa ife amene angafune kuchititsa anthu ena kuti aziona ngati tapatsidwa utumiki winawake wapadera wosamalira nkhosa za Mulungu.
Timafunitsitsa kuchita zinthu zimene zingapangitse kuti Mulungu alemekezedwe. (1 Akor. 10:31) Choncho mukamafuna kutumiza mauthenga pogwiritsa ntchito mapulogalamu kapena njira zina zamakono, muziganizira kuopsa kwake ndiponso muzikhala osamala.