NKHANI YOPHUNZIRA 14

“Muzitsatira Mapazi Ake Mosamala Kwambiri”

“Muzitsatira Mapazi Ake Mosamala Kwambiri”

“Khristu anavutika chifukwa cha inu, ndipo anakusiyirani chitsanzo kuti mutsatire mapazi ake mosamala kwambiri.”​1 PET. 2:21.

NYIMBO NA. 13 Khristu ndi Chitsanzo Chathu

ZIMENE TIPHUNZIRE *

Yesu anatisiyira chitsanzo kuti tizitsatira mapazi ake mosamala kwambiri (Onani ndime 1-2)

1-2. Kodi zingatheke bwanji kutsatira mapazi a Yesu? Perekani chitsanzo.

YEREKEZERANI kuti muli m’gulu la anthu amene akuyenda m’chipululu choopsa momwe muli mchenga wambiri. Muli ndi munthu amene akukutsogolerani yemwe akudziwa bwino deralo. Pamene akuyenda, mapazi ake akudinda mumchenga. Kenako mukuzindikira kuti munthu wokutsogolerani uja sakuonekanso. Komabe simukuda nkhawa. M’malomwake inu ndi anzanu amene muli nawo mukuyesetsa kutsatira mapazi a munthuyo mosamala kwambiri.

2 Mofanana ndi zimenezi, tingati Akhristufe tikuyenda m’chipululu choopsa chomwe ndi dziko loipali. Koma timayamikira kuti Yehova anatipatsa wotitsogolera wabwino kwambiri, yemwe ndi Mwana wake Yesu Khristu, amene tiyenera kutsatira mapazi ake mosamala kwambiri. (1 Pet. 2:21) Mogwirizana ndi Buku lina lofotokoza za Baibulo, palembali Petulo anayerekezera Yesu ndi munthu amene akutsogolera anthu ena kukaona malo. Mofanana ndi munthu amene akutsogolera anthu pokaona malo uja yemwe mapazi ake adinda mumchenga, tingati nayenso Yesu anasiya zidindo za mapazi ake kuti titsatire. Tsopano tiyeni tikambirane mafunso atatu pa nkhani yokhudza kutsatira mapazi a Yesu. Kodi kutsatira mapazi a Yesu kumatanthauza chiyani? N’chifukwa chiyani tiyenera kutsatira mapazi akewo? Nanga tingawatsatire bwanji?

KODI KUTSATIRA MAPAZI A YESU KUMATANTHAUZA CHIYANI?

3. Kodi kutsatira mapazi a winawake kumatanthauza chiyani?

3 Kodi kutsatira mapazi a winawake kumatanthauza chiyani? Nthawi zina m’Baibulo mawu akuti “kuyenda” komanso “mapazi” amatanthauza zimene munthu amachita pa moyo wake. (Gen. 6:9; Miy. 4:26) Ndiye zimenezi, tingaziyerekezere ndi zidindo za mapazi zimene amasiya akamayenda. Choncho kutsatira mapazi a winawake kumatanthauza kutengera chitsanzo chake.

4. Kodi kutsatira mapazi a Yesu kumatanthauza chiyani?

4 Ndiye kodi kutsatira mapazi a Yesu kumatanthauza chiyani? Mwachidule tingati kumatanthauza kutengera chitsanzo chake. Mulemba limene pachokera nkhaniyi, mtumwi Petulo kwenikweni ankafotokoza chitsanzo chabwino chimene Yesu anatipatsa pa nkhani yopirira. Komabe pali zinthu zambiri zimene Yesu anachita zomwe tiyenera kutsanzira. (1 Pet. 2:18-25) Ndipotu zonse zimene Yesu ankalankhula komanso kuchita pa moyo wake ndi chitsanzo chabwino chimene tiyenera kutengera.

5. Kodi anthu omwe si angwiro, angathedi kutengera chitsanzo cha Yesu? Fotokozani.

5 Popeza kuti si ife angwiro, kodi tingathedi kutengera chitsanzo cha Yesu? Inde n’zotheka. Kumbukirani kuti Petulo sananene kuti tizitsatira mapazi a Yesu ndendende, m’malomwake iye anati ‘tizitsatira mapazi a [Yesu] mosamala kwambiri.’ Tikamayesetsa kuchita zonse zomwe tingathe potsatira mapazi ake mosamala kwambiri, tidzakhala tikumvera mawu a mtumwi Yohane akuti: ‘Pitirizani kuyenda mmene iyeyo [Yesu] anayendera.’​—1 Yoh. 2:6.

N’CHIFUKWA CHIYANI TIYENERA KUTSATIRA MAPAZI A YESU?

6-7. N’chifukwa chiyani tinganene kuti kutsatira mapazi a Yesu kumatithandiza kuti tikhale pa ubwenzi wolimba ndi Yehova?

6 Tikamatsatira mapazi a Yesu tidzakhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa choyamba n’chakuti Yesu anatisiyira chitsanzo chabwino cha zimene tiyenera kuchita kuti tizisangalatsa Mulungu. (Yoh. 8:29) Choncho tikamatsatira mapazi a Yesu, timasangalatsa Yehova. Ndipo tingakhale otsimikiza kuti Atate wathu wakumwamba adzakhala pa ubwenzi ndi onse amene amayesetsa kuti akhale anzake.​—Yak. 4:8.

7 Chifukwa chachiwiri n’chakuti nthawi zonse Yesu amatsanzira Atate wake. N’chifukwa chake iye ananena kuti: “Amene waona ine waonanso Atate.” (Yoh. 14:9) Tiyenera kutsanzira makhalidwe a Yesu komanso mmene ankachitira zinthu ndi anthu ena. Mwachitsanzo, iye anachitira chifundo munthu wakhate, mayi amene ankadwala matenda aakulu komanso ankamvera chisoni anthu amene aferedwa. Choncho tikamatsanzira Yesu, timakhalanso tikutsanzira Yehova. (Maliko 1:40, 41; 5:25-34; Yoh. 11:33-35) Tikamatsanzira kwambiri makhalidwe a Yehova, m’pamenenso ubwenzi wathu ndi iye umalimba kwambiri.

8. N’chifukwa chiyani tinganene kuti kutsatira mapazi a Yesu kungatithandize ‘kugonjetsa’ dziko?

8 Tikamatsatira mapazi a Yesu sitidzasokonezedwa ndi dziko loipali. Usiku woti aphedwa mawa lake, Yesu ananena kuti: “Ine ndaligonjetsa dziko.” (Yoh. 16:33) Iye ankatanthauza kuti sanalole kutengera maganizo, zolinga komanso zochita za anthu a m’dzikoli. Yesu sanaiwale cholinga chimene anamutumizira padzikoli, chomwe chinali kudzasonyeza kuti Yehova ndiye woyenera kulamulira. Nanga bwanji ifeyo? M’dzikoli muli zinthu zambiri zimene zingatisokoneze. Koma mofanana ndi Yesu, ngati tingaike maganizo athu onse pakuchita chifuniro cha Yehova, ifenso tingathe ‘kugonjetsa’ dziko.​—1 Yoh. 5:5.

9. Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tipitirize kuyenda panjira yopita ku moyo wosatha?

9 Tikamatsatira mapazi a Yesu tidzapeza moyo wosatha. Wachinyamata wina wolemera atafunsa Yesu zimene angachite kuti adzapeze moyo wosatha, iye anamuuza kuti: “Ubwere udzakhale wotsatira wanga.” (Mat. 19:16-21) Kwa Ayuda ena omwe sankakhulupirira kuti iye anali Khristu, Yesu anawauza kuti: “Nkhosa zanga . . . zimanditsatira. Ndidzazipatsa moyo wosatha.” (Yoh. 10:24-29) Nikodemo, yemwe anali mmodzi wa oweruza a khoti lalikulu la Ayuda, ankafuna kudziwa zambiri zokhudza zimene Yesu ankaphunzitsa. Yesu anamuuza kuti ‘aliyense wokhulupirira iye . . . adzakhala ndi moyo wosatha.’ (Yoh. 3:16) Timasonyeza kuti timakhulupirira Yesu tikamatsatira zimene anaphunzitsa komanso kutengera chitsanzo chake. Tikamachita zimenezi tidzapitiriza kuyenda panjira yopita ku moyo wosatha.​—Mat. 7:14.

KODI TINGATSATIRE BWANJI MAPAZI A YESU MOSAMALA KWAMBIRI?

10. Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti ‘timudziwe’ bwino Yesu? (Yoh. 17:3)

10 Kuti tizitsatira mapazi a Yesu mosamala kwambiri, choyamba tiyenera kumudziwa bwino. (Werengani Yohane 17:3.) “Kudziwa” Yesu kulibe polekezera. Tiyenera kupitirizabe kuphunzira zambiri zokhudza iye kuti tidziwe makhalidwe ake, kaganizidwe kake komanso mfundo zake. Kaya takhala m’choonadi kwa nthawi yaitali bwanji, tiyenera kupitiriza kuchita khama kuti “tidziwe bwino” Yehova limodzi ndi Mwana wake.

11. Kodi m’mabuku 4 a Uthenga Wabwino muli nkhani zotani?

11 Pofuna kutithandiza kuti timudziwe bwino Mwana wake, mwachikondi Yehova anaika mabuku 4 a Uthenga Wabwino m’Mawu ake. M’mabuku amenewa muli nkhani zokhudza moyo wa Yesu komanso utumiki wake. Mabuku a Uthenga Wabwino amafotokoza zimene Yesu analankhula, anachita komanso mmene ankamvera. Mabuku 4 amenewa amatithandiza kuti ‘tiziganizira mozama’ chitsanzo cha Yesu. (Aheb. 12:3) M’mawu ena tingati m’mabuku amenewa muli zidindo za mapazi a Yesu zimene anatisiyira. Choncho tikamaphunzira mabuku a Uthenga Wabwino, tingafike pomudziwa bwino kwambiri Yesu. Ndipo zimenezi zingathandize kuti tizitsatira mapazi ake mosamala kwambiri.

12. Kodi tingatani kuti tizipindula kwambiri ndi mabuku a Uthenga Wabwino?

12 Kuti tizipindula ndi mabuku a Uthenga Wabwino pali zambiri zimene tiyenera kuchita osati kungowerenga. Tiyenera kupeza nthawi yowaphunzira mosamala komanso kuganizira mozama zimene tikuphunzirazo. (Yerekezerani ndi Yoswa 1:8.) Tiyeni tikambirane mfundo ziwiri zomwe zingatithandize kuganizira mozama komanso kugwiritsa ntchito zimene tingaphunzire m’mabuku a Uthenga Wabwino.

13. Kodi mungatani kuti muziona kuti nkhani za m’mabuku a Uthenga Wabwino ndi zenizeni?

13 Choyamba, muziona kuti nkhani imene mukuwerengayo ndi yeniyeni. Muziyerekezera kuti mukuona komanso kumva zimene zinkachitika. Kuti muthe kuchita zimenezi, muzifufuza m’mabuku amene gulu la Yehova limatipatsa. Muziona mavesi a patsogolo ndi a pambuyo pa nkhani imene mukuwerengayo kuti mudziwe nkhani yonse. Muzifufuza zambiri zokhudza anthu komanso malo omwe atchulidwa. Muziyerekezera nkhani imene mukuwerengayo ndi nkhani yofanana nayo imene ili mu buku lina la Uthenga Wabwino. Nthawi zina olemba Uthenga Wabwino ankalemba mfundo zina zochititsa chidwi zimene ena sanalembe.

14-15. Kodi tingatani kuti tizigwiritsa ntchito mfundo za m’mabuku a Uthenga Wabwino pa moyo wathu?

14 Chachiwiri, muzigwiritsa ntchito mfundo za m’mabuku a Uthenga Wabwino pa moyo wanu. (Yohane 13:17) Mukaphunzira nkhani inayake m’mabuku a Uthenga Wabwino muzidzifunsa kuti: ‘Kodi pali phunziro limene ndapeza munkhaniyi lomwe ndingagwiritse ntchito pa moyo wanga? Kodi ndingagwiritse ntchito bwanji mfundo za munkhaniyi pothandiza anthu ena?’ Yesani kuganizira munthu winawake amene mumamudziwa, ndiye mwachikondi komanso mwaluso m’fotokozereni zimene mwaphunzira.

15 Tiyeni tikambirane chitsanzo chosonyeza mmene tingagwiritsire ntchito mfundo ziwirizi. Tikambirana nkhani ya mkazi wamasiye wosauka yemwe Yesu anamuona m’kachisi.

MKAZI WAMASIYE WOSAUKA

16. Kodi mungafotokoze bwanji nkhani imene ili pa Maliko 12:41?

16 Muziona kuti nkhaniyo ndi yeniyeni. (Werengani Maliko 12:41.) Yerekezerani kuti mukuona zimene zikuchitika. Tsiku lake ndi pa Nisani 11, mu 33 C.E. ndipo kwangotsala masiku ochepa kuti Yesu aphedwe. Pa tsikuli Yesu wakhala akuphunzitsa kwa maola ambiri m’kachisi. Koma atsogoleri achipembedzo akhala akumutsutsa kwambiri. Ena anali atamufunsa zokhudza ulamuliro umene amachitira zinthu. Enanso anamufunsa mafunso ovuta n’kumaganiza kuti alephera kuyankha. (Maliko 11:27-33; 12:13-34) Tsopano Yesu wapita kumbali ina ya kachisiyo. Kumeneku, komwe mwina kunkatchedwa Bwalo la Akazi, Yesu akutha kuona zoponyamo zopereka zomwe zili m’mbali mwa khoma. Iye wakhala pansi ndipo akuyang’anitsitsa pamene anthu akuponya zopereka zawo. Iye akuona anthu olemera akuponya ndalama zasiliva zambiri. Mwinanso wakhala pafupi kwambiri moti akutha kumva phokoso la ndalamazo zikamagwera moponya zoperekamo.

17. Kodi mkazi wamasiye wosauka wotchulidwa pa Maliko 12:42, anachita chiyani?

17 Werengani Maliko 12:42. Patapita kanthawi Yesu akuona mayi wina “wamasiye wosauka.” (Luka 21:2) Mayiyu ndi wosauka kwambiri moti amavutika kupeza zinthu zofunika pa moyo. Komabe mayiyu akupita pomwe pali choponyamo zopereka ndipo akuponya timakobidi tiwiri, tomwe mwina sitinamveke phokoso n’komwe. Yesu wadziwa kuti mayiyu waponya timalepitoni tiwiri, tomwe tinali timakobidi tochepa mphamvu kwambiri pa nthawiyo. Ndalamayi inali yosakwana kugula ngakhale mpheta imodzi, yomwe inali m’gulu la mbalame zotchipa kwambiri zimene anthu ankadya.

18. Mogwirizana ndi Maliko 12:43, 44, kodi Yesu anafotokoza zotani zokhudza chopereka cha mayi wamasiye?

18 Werengani Maliko 12:43, 44. Yesu wachita chidwi kwambiri ndi mayi wamasiyeyu. Choncho akuitana ophunzira ake n’kuwauza kuti: “Mkazi wamasiye wosaukayu waponya zochuluka kuposa onse.” Kenako akunena kuti: “Onsewo [makamaka anthu olemera] aponya zimene atapa pa zochuluka zimene ali nazo, koma mayiyu, mu umphawi wake, waponya zonse zimene anali nazo, inde zonse zochirikizira moyo wake.” Popereka ndalama zonse zomwe anali nazo patsikulo, mayi wamasiyeyo ankakhulupirira kwambiri kuti Yehova amusamalira.​—Sal. 26:3.

Mofanana ndi Yesu muziyamikira onse amene akuyesetsa kuchita zonse zomwe angathe potumikira Yehova (Onani ndime 19-20) *

19. Kodi tingaphunzire chiyani pa zimene Yesu ananena zokhudza mayi wamasiye?

19 Muzigwiritsa ntchito mfundo za munkhaniyo pa moyo wanu. Dzifunseni kuti, ‘Kodi ndikuphunzira chiyani pa zimene Yesu ananena zokhudza mayi wamasiyeyu?’ Mosakayikira mayiyu ankafunitsitsa atapereka zambiri kwa Yehova. Komabe, iye anachita zonse zomwe angathe popereka kwa Yehova zinthu zabwino kwambiri. Ndipo Yesu ankadziwa kuti zimene mayiyu anapereka zinali zamtengo wapatali kwambiri kwa Yehova. Pamenepatu pali phunziro labwino kwambiri kwa ife. Yehova amayamikira tikamamupatsa zinthu zabwino kwambiri kapena kuti tikamamutumikira ndi mtima wonse. (Mat. 22:37; Akol. 3:23) Iye amasangalala akaona kuti tikuchita zonse zomwe tingathe. Zimenezi zikusonyeza kuti Yehova amayamikira kwambiri tikamagwiritsa ntchito nthawi ndi mphamvu zathu pomulambira, kaya mu utumiki kapena pamisonkhano.

20. Kodi tingagwiritse ntchito bwanji zimene taphunzira pa nkhani ya mayi wamasiye? Perekani chitsanzo.

20 Kodi tingagwiritse ntchito bwanji mfundo zimene taphunzira pa nkhani ya mayi wamasiye? Tayesani kuganizira za winawake amene angafunike kumutsimikizira kuti Yehova amasangalala ndi zimene akuchita pomutumikira. Mwachitsanzo, kodi pali mlongo wachikulire amene mumamudziwa, yemwe amadziimba mlandu kapena kudziona kuti ndi wosafunika chifukwa choti alibenso thanzi labwino komanso mphamvu zotha kuchitira zambiri mu utumiki ngati mmene ankachitira poyamba? Kapena kodi pali m’bale wina amene akudwala matenda aakulu ndipo amakhumudwa kuti sangathe kupezeka pamisonkhano yonse ku Nyumba ya Ufumu? Muzithandiza anthu ngati amenewa powalankhula “mawu alionse olimbikitsa.” (Aef. 4:29) Muzikambirana nawo mfundo zolimbikitsa zimene taphunzira munkhani ya mayi wamasiye wosauka. Mawu anu olimbikitsa angawatsimikizire kuti Yehova amasangalala tikamamupatsa zinthu zabwino kwambiri. (Miy. 15:23; 1 Ates. 5:11) Tikamayamikira ena chifukwa chochita zonse zomwe angathe potumikira Yehova ngakhale zitakhala zochepa, timakhala tikutsatira mapazi a Yesu mosamala kwambiri.

21. Kodi mwatsimikiza mtima kuchita chiyani?

21 Timayamikira kwambiri kuti m’mabuku a Uthenga Wabwino muli nkhani zambiri zofotokoza moyo wa Yesu, zimene zimatithandiza kuti tizitengera chitsanzo chake komanso kutsatira mapazi ake mosamala kwambiri. Bwanji osayesa kuphunzira mabuku a Uthenga Wabwino pa kulambira kwa pabanja kapena pophunzira Baibulo panokha? Kumbukirani kuti mungathe kupindula kwambiri mukamaona nkhani imene mukuwerengayo kuti ndi yeniyeni komanso kugwiritsa ntchito zimene mwaphunzirazo pa moyo wanu. Kuwonjezera pa kutsanzira zimene Yesu anachita, tiyeneranso kumvetsera zimene ananena. Munkhani yotsatira tidzakambirana zimene tingaphunzire pa mawu omaliza amene Yesu ananena atatsala pang’ono kuphedwa.

NYIMBO NA. 15 Tamandani Mwana Woyamba Kubadwa wa Yehova

^ ndime 5 Akhristu oona ayenera ‘kutsatira mapazi a [Yesu] mosamala kwambiri.’ Kodi iye anatisiyira “chitsanzo” chotani chimene tiyenera kutsatira? Munkhaniyi tipeza yankho la funso limeneli. Tikambirananso chifukwa chake tiyenera kutsatira mapazi ake mosamala kwambiri komanso mmene tingachitire zimenezi.

^ ndime 60 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Pambuyo poganizira mozama zimene Yesu ananena zokhudza mayi wosauka wamasiye, mlongo akuyamikira mlongo wina wachikulire chifukwa choyesetsa kuchita zonse zomwe angathe potumikira Yehova.