Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 15

Zimene Tingaphunzile pa Mawu Othela a Yesu

Zimene Tingaphunzile pa Mawu Othela a Yesu

“Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, amene ndikukondwela naye, muzimumvela.”—MAT. 17:5.

NYIMBO 17 ‘Nifuna’

ZIMENE TIKAMBILANE *

1-2. Kodi panacitika zotani pamene Yesu anakamba mawu ake otsiliza?

NI NTHAWI yamasana, pa Nisani 14, mu 33 C.E. Yesu atanamizilidwa na kuweluzidwa pa mlandu womusemela, akunyodoledwa, kuzunzidwa mwankhanza, na kukhomeleledwa pa mtengo wozunzikilapo. Pamene akumukhomelela, misomali ikuloŵa m’manja mwake na m’mapazi. Kupuma kulikonse n’kopweteka, kukamba mawu alionse n’koŵaŵa. Koma afunika alankhulebe, cifukwa ali na mawu ofunika kwambili.

2 Tiyeni tikambilane mawu amene Yesu anakamba pamene anali kufa pa mtengo wozunzikilapo, na zimene tingaphunzile pa mawuwo. M’mawu ena, tingakambe kuti tiyeni ‘timumvetsele.’—Mat. 17:5.

“ATATE, AKHULULUKILENI”

3. Kodi Yesu ayenela kuti anali kukamba ndani pamene ananena kuti “Atate, akhululukileni”?

3 Kodi Yesu anakamba ciani? Atakhomeledwa pa mtengo wozunzikilapo, Yesu anapemphela kuti: “Atate, akhululukileni.” Kukhululukila ndani? Mawu ake otsatila atipatsa cithunzi. Iye anati: “Sakudziŵa cimene akucita.” (Luka 23:33, 34) Zioneka kuti Yesu anali kukamba asilikali aciroma amene anamukhomelela misomali m’manja mwake na m’mapazi ake. Iwo sanali kudziŵa kuti Yesu anali ndani kweni-kweni. Iye mwina anaganizilanso za anthu ena m’gulu amene anali kufuna kuti iye aphedwe ndithu koma pambuyo pake anali kudzakhulupilila mwa iye. (Mac. 2:36-38) Yesu sanalole kuti zopanda cilungamo zimene anacitilidwa, zimupangitse kukalipa na kusunga mkwiyo. (1 Pet. 2:23) M’malomwake, anapempha Yehova kuti akhululukile anthu amene anali kumupha.

4. Kodi tingaphunzile ciani pa citsanzo ca Yesu ca kukhala wokonzeka kukhululukila anthu amene anali kumutsutsa?

4 Kodi tingaphunzile ciani pa mawu a Yesu? Mofanana na Yesu, tiyenela kukhala okonzeka kukhululukila ena. (Akol. 3:13) Anthu ena kuphatikizapo acibale athu, angatitsutse cifukwa samvetsetsa zimene timakhulupila komanso mmene timacitila zinthu mu umoyo wathu. Angatinenele mabodza, kuticitsa manyazi pamaso pa ena, kutiwonongela zofalitsa, kapena kutiopseza kuti adzativulaza. M’malo mosunga cakukhosi, tingapemphe Yehova kuti atsegule maso a anthu otitsutsawo, kuti tsiku lina akaphunzile coonadi. (Mat. 5:44, 45) Nthawi zina, kukhululuka kungakhale kovuta maka-maka ngati tinacitilidwa zinthu zoipa kwambili. Koma ngati tilola mkwiyo na kusunga cakukhosi kuzika mizu mu mtima mwathu, timadzivulaza tekha. Mlongo wina anafotokoza kuti: “N’nazindikila kuti kukhululuka sikutanthauza kulekelela zolakwa, kapena kulola anthu kunitenga mopepuka. Kumatanthauza kusankha kungocotsa cakukhosi.” (Sal. 37:8) Tikasankha kukhululuka, timapewa kukhalabe okwinyilila cifukwa ca zoipa zimene zinaticitikila.—Aef. 4:31, 32.

“IWE UDZAKHALA NDI INE M’PARADAISO”

5. Kodi Yesu analonjeza ciani kwa mpandu amene anapacikidwa naye limodzi? Nanga n’cifukwa ciani anapanga lonjezo limenelo?

5 Kodi Yesu anakamba ciani? Apandu aŵili anapacikidwa pamodzi na Yesu. Poyamba, onse aŵili anali kumunyoza Yesu. (Mat. 27:44) Koma pambuyo pake, mmodzi wa iwo anasintha mtima wake. Iye anafika pozindikila kuti Yesu “sanalakwe ciliconse.” (Luka 23:40, 41) Mpanduyo anakhulupilila kuti Yesu adzaukitsidwa kwa akufa, ndipo tsiku lina adzalamulila monga mfumu. Iye anapempha Yesu wopacikidwayo kuti: “Yesu, mukandikumbukile mukakaloŵa mu ufumu wanu.” (Luka 23:42) Kukamba zoona, munthuyo anaonetsa cikhulupililo cacikulu zedi! Poyankha Yesu anamuuza kuti: “Ndithu ndikukuuza lelo, iwe udzakhala ndi ine [osati mu ufumu, koma] m’Paradaiso.” (Luka 23:43) Onani kuti Yesu popanga lonjezo limenelo anaseŵenzetsa mawu akuti “ndikukuuza,” “iwe,” ndiponso mawu akuti “ine.” Podziŵa kuti Atate wake ni wacifundo, Yesu anakamba mawu opatsa ciyembekezo mpanduyo amene anali pafupi kufa.—Sal. 103:8.

6. Kodi tingaphunzile ciani pa mawu amene Yesu anauza mpandu uja?

6 Kodi tingaphunzile ciani pa mawu a Yesu? Yesu ndiye cithunzi candendende ca Atate wake. (Aheb. 1:3) Yehova ni wokonzeka kutikhululukila na kutionetsa cifundo ngati tilapadi pa zoipa zimene tinacita kumbuyoku, ndiponso ngati tikhulupilila kuti tingakhululukidwe macimo athu cifukwa ca magazi okhetsedwa a Yesu Khristu. (1 Yoh. 1:7) Kwa ena, cimakhala covuta kukhulupilila kuti Yehova anawakhululukiladi zolakwa zawo zakumbuyo. Ngati umu ni mmene mumamvelela nthawi zina, ganizilani izi: Yesu ali pafupi kufa, anakamba mawu oonetsa cifundo kwa mpandu uja amene anali atangoyamba kumene kuonetsa cikhulupililo mwa iye. Nanga kuli bwanji Yehova kwa olambila ake okhulupilika, amene akuyesetsa kumvela malamulo ake? Mosakayika konse, adzawacitiladi cifundo cacikulu!—Sal. 51:1; 1 Yoh. 2:1, 2.

“UYU AKHALA MWANA WANU . . . AWA AKHALA MAYI AKO”

7. Kodi Yesu anakamba ciani kwa Mariya na Yohane malinga na Yohane 19:26, 27? Nanga n’cifukwa ciani anakamba zimenezi?

7 Kodi Yesu anakamba ciani? (Ŵelengani Yohane 19:26, 27.) Yesu anali kudela nkhawa amayi ake amene ayenela kuti anali amasiye panthawiyi. Mwina azing’ono ake akanatha kuwasamalila pa zakuthupi. Koma kodi n’ndani akanawasamalila kuuzimu? Baibo sionetsa kuti abale ake anali atakhala ophunzila ake panthawiyo. Koma Yohane anali mtumwi wokhulupilika, komanso mmodzi wa mabwenzi a Yesu apamtima. Yesu anali kuona kuti anthu amene anali kulambila naye Yehova, anali banja lake lauzimu. (Mat. 12:46-50) Yesu anali kum’konda kwambili mayi wake Mariya, ndipo anaonetsetsa kuti adzasamalidwa bwino. Conco anamuikiza m’manja mwa Yohane, podziŵa kuti adzam’samalila bwino kuuzimu. Kwa amayi ake, iye anati: “Uyu akhala mwana wanu.” Ndipo kwa Yohane anati: “Awa akhala mayi ako.” Kuyambila tsiku limenelo, Yohane anakhala monga mwana wa Mariya, ndipo Yohane anasamalila Mariya monga mayi ake omubala. Ndithudi, Yesu anaonetsa cikondi cacikulu kwa mayi wabwino kwambili ameneyo, amene anamusamalila atangobadwa komanso amene anaimilila pafupi na iye pa nthawi ya imfa yake.

8. Kodi tingaphunzilepo ciani pa mawu amene Yesu anauza Mariya na Yohane?

8 Kodi tingaphunzile ciani pa mawu a Yesu? Ubale wathu na abale na alongo athu acikhristu ungakhale wolimba kwambili kuposa ubale wathu na acibale akuthupi. Acibale athu angatitsutse kapena kutisiya. Koma Yesu analonjeza kuti tikamamatilabe Yehova na gulu lake, ‘tidzapeza zoculuka kuwilikiza maulendo 100’ kuposa zimene tingataye. Ambili adzakhala ana athu okondedwa, amayi kapena atate. (Maliko 10:29, 30) Kodi mumamvela bwanji kukhala m’banja lauzimu limene ni logwilizana mwa cikhulupililo na cikondi​—inde cikondi pa Yehova komanso pa wina na mnzake?—Akol. 3:14; 1 Pet. 2:17.

“MULUNGU WANGA, MWANDISIYILANJI INE?”

9. Kodi mawu a Yesu a pa Mateyu 27:46 atiuza mfundo zotani?

9 Kodi Yesu anakamba ciani? Yesu atatsala pang’ono kumwalila anafuula kuti: “Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyilanji ine?” (Mat. 27:46) Baibo siifotokoza cifukwa cake Yesu anakamba mawu amenewa. Koma tiyeni tione mfundo zimene tikupeza pa mawu amenewa. Mfundo yoyamba ni yakuti mwa kukamba mawu amenewa, Yesu anakwanilitsa ulosi wa pa Salimo 22:1. * Cina, mawu amenewo anaonetselatu kuti Yehova ‘sanali kumuchinga’ Mwana wake. (Yobu 1:10) Yesu anali kudziŵa kuti Atate wake anali atam’peleka kothelatu m’manja mwa adani ake n’colinga cakuti ayesedwe mofikapo kuposa mmene munthu wina aliyense anayesedwela. Kuwonjezela apo mawu amenewa anatsimikizila kuti iye analibe mlandu uliwonse woyenela imfa.

10. Kodi tingaphunzilepo ciani pa mawu a Yesu opita kwa Atate wake?

10 Kodi tingaphunzile ciani pa mawu a Yesu? Phunzilo limodzi limene tingatengepo n’lakuti tisamayembekezele kuti Yehova azitichinga ku mavuto oyesa cikhulupililo cathu. Monga mmene Yesu anayesedwela mpaka imfa, nafenso tifunika kukhala okonzeka kufela cikhulupililo cathu, ngati pangafunike kutelo. (Mat. 16:24, 25) Komabe, tili na cidalilo cakuti Mulungu sangalole kuti tiyesedwe mpaka kufika pamene sitingathe kupilila. (1 Akor. 10:13) Phunzilo lina n’lakuti, mofanana na Yesu, nafenso tingavutike ngakhale kuti sitinalakwe ciliconse. (1 Pet. 2:19, 20) Anthu amene amatitsutsa amacita zimenezo osati cifukwa cakuti talakwitsa zina zake, koma cifukwa cakuti sitili mbali ya dziko ndipo timacitila umboni za coonadi. (Yoh. 17:14; 1 Pet. 4:15, 16) Yesu anali kudziŵa cifukwa cake Yehova analola kuti iye avutike. Atumiki a Yehova nthawi zina samvetsa cifukwa cake Yehova walola kuti iwo akumane na mayeso ena ake. (Hab. 1:3) Mulungu wathu woleza mtima ndiponso wacifundo, amadziŵa kuti anthu otelo sikuti alibe cikhulupililo. Iwo amafunika citonthozo cimene iye angapeleke.—2 Akor. 1:3, 4.

“NDIKUMVA LUDZU”

11. N’cifukwa ciani Yesu anakamba mawu a pa Yohane 19:28?

11 Kodi Yesu anakamba ciani? (Ŵelengani Yohane 19:28.) N’cifukwa ciani Yesu anakamba kuti: “Ndikumva ludzu”? Anakamba izi ‘kuti lemba likwanilitsidwe’—kutanthauza ulosi wa pa Salimo 22:15, umene umati: “Mphamvu yanga yauma gwaa, ngati phale. Lilime langa lamamatila kunkhama zanga.” Komanso, Yesu ayenela kuti anali na ludzu kwambili cifukwa ca mavuto onse amene anapitamo kuphatikizapo kuvutika na ululu pa mtengo wozunzikilapo. Anafunika thandizo kuti athetse ludzu lake.

12. Tingaphunzilepo ciani pa mawu a Yesu akuti “Ndikumva ludzu”?

12 Kodi tingaphunzile ciani pa mawu a Yesu? Yesu sanaganize kuti akafotokoza mmene anali kumvelela adzaoneka kuti ni wofooka. Nafenso sitiyenela kuganiza conco. Nthawi zambili, sitikonda kuuza ena zosoŵa zathu. Koma ngati taona kuti tikufunikila thandizo la wina, tisazengeleze kupempha ena kuti atithandize. Mwacitsanzo, ngati ndimwe wokalamba kapena wolemala, mungapemphe mnzanu kukupelekankoni ku sitolo kapena ku cipatala. Ngati tapsinjika maganizo kapena kulefuka, tingafunike kupempha mkulu kapena mnzathu wokhwima kuuzimu kuti atimvetsele kapena kutiuzako “mawu abwino” amene angatisangalatse. (Miy. 12:25) Tisaiŵale kuti abale na alongo athu amatikonda, ndipo amafuna kutithandiza “pakagwa mavuto.” (Miy. 17:17) Koma iwo sangadziŵe zimene tiganiza. Conco sangadziŵe kuti tifunikila thandizo ngati sitinawauze.

“NDAKWANILITSA CIFUNILO CANU!”

13. Kodi Yesu anakwanilitsa ciani mwa kusungabe umphumphu wake mpaka imfa?

13 Kodi Yesu anakamba ciani? Pofika m’ma 15:00 awazi pa Nisani 14, Yesu anafuula kuti: “Ndakwanilitsa cifunilo canu!” (Yoh. 19:30) Yesu atatsala pang’ono kutsilizika, anali atacita zonse zimene Yehova anali kufuna kuti acite. Mwa kusungabe umphumphu wake mpaka imfa, Yesu anakwanilitsa zinthu zambili. Coyamba, anaonetsa kuti Satana ni wabodza. Yesu anaonetsa kuti munthu wangwilo angakwanitse kusunga umphumphu wake mwangwilo mosasamala kanthu zonse zimene Satana angacite. Caciŵili, Yesu anapeleka moyo wake monga dipo. Cifukwa cakuti anapeleka moyo wake monga nsembe, zinatheka anthu opanda ungwilo kukhala pa ubale na Mulungu, na kuwapatsa ciyembekezo cokakhala na moyo kwamuyaya. Cacitatu, Yesu anaonetsa kuti Yehova ni wolamulila wolungama, ndipo anacotsa citonzo pa dzina la Atate wake.

14. Kodi tsiku lililonse tiyenela kuliona motani? Fotokozani.

14 Kodi tingaphunzile ciani pa mawu a Yesu? Tifunika kutsimikiza mtima kusunga umphumphu wathu tsiku lililonse. Onani zimene anakamba M’bale Maxwell Friend, amene anali mlangizi wa Sukulu ya Giliyadi. Pa msonkhano wa maiko, M’bale Friend pokamba nkhani yonena za kukhulupilika anati: “Musanene kuti mukacita maŵa zimene mungathe kucita lelo, kapena kuti mudzakamba maŵa zimene mungathe kukamba lelo. Kodi mudzakhalakodi maŵalo? Muziona tsiku lililonse kukhala monga lothela loonetsela kuti ndinu oyenelela kukakhala na moyo wosatha.” Tiziona tsiku lililonse kukhala monga lothela pa kusunga umphumphu wathu. Tikatelo, olo tiyang’anizane na imfa, tidzatha kukamba kuti, “Yehova, nacita zonse zimene nikanatha posunga umphumphu wanga, kuonetsa kuti Satana ni wabodza komanso nacotsa citonzo pa dzina lanu na kuonetsa kuti inu ndinu woyenela kulamulila!”

“NDIKUIKIZA MZIMU WANGA M’MANJA MWANU”

15. Malinga na Luka 23:46, kodi Yesu anali wotsimikiza za ciani?

15 Kodi Yesu anakamba ciani? (Ŵelengani Luka 23:46.) Na cidalilo conse, Yesu anakamba kuti: “Atate, ndikuikiza mzimu wanga m’manja mwanu.” Yesu anadziŵa kuti tsogolo lake linadalila pa Yehova, ndipo anali wotsimikiza kuti Atate wake adzamukumbukila.

16. Kodi tiphunzilapo ciani pa cocitika ca mnyamata wina wa Mboni wa zaka 15?

16 Kodi tingaphunzile ciani pa mawu a Yesu? Khalani wokonzeka kuika moyo wanu m’manja mwa Yehova. Kuti mucite zimenezo muyenela “kukhulupilila Yehova ndi mtima wanu wonse.” (Miy. 3:5) Ganizilani citsanzo ca mnyamata wina wa Mboni wa zaka 15, dzina lake Joshua, amene anali kudwala matenda akupha. Iye anakana njila zocizila matenda zophwanya lamulo la Mulungu. Atatsala pang’ono kufa, anauza amayi ake kuti: “Amama, nili m’manja mwa Yehova. . . . Cimene ningakuuzeni motsimikiza amama ni ici: Mosakayika konse, Yehova adzaniukitsa ndithu kwa akufa. Iye adziŵa zili mumtima mwanga ndipo nimam’konda kwambili.” Aliyense wa ife angacite bwino kudzifunsa kuti, ‘Ngati cikhulupililo canga cingayesedwe cifukwa cakuti moyo wanga uli paciopsezo, kodi nidzaika moyo wanga m’manja mwa Yehova na kukhulupilila kuti iye adzanikumbukila?’

17-18. Kodi taphunzila ciani m’nkhani ino? (Onaninso bokosi lakuti “ Zimene Tiphunzilapo pa Mawu Othela a Yesu.”)

17 Kukamba zoona, tingatengepo maphunzilo ofunika kwambili pa mawu othela a Yesu. Tiphunzilapo kuti tiyenela kukhululukila ena na kukhulupilila kuti Yehova adzatikhululukila. Tili na mwayi kukhala na banja labwino lauzimu la abale na alongo amene ni okonzeka kutithandiza. Koma tikafunikila thandizo, tiyenela kuwapempha kuti atithandize. Tidziŵa kuti Yehova adzatithandiza kupilila ciyeso ciliconse cimene tingakumane naco. Ndipo taona kufunika koona tsiku lililonse monga tsiku lothela loonetsela kuti tasunga umphumphu wathu tili na cidalilo conse kuti moyo wathu ni wotetezeka m’manja mwa Yehova.

18 Ndithudi, mawu amene Yesu anakamba atatsala pang’ono kufa pa mtengo wozunzikilapo, angatiphunzitse zambili! Mwa kuseŵenzetsa zimene taphunzila, tidzamvela mawu a Yehova onena za Mwana wake akuti: “muzimumvela.”—Mat. 17:5.

NYIMBO 126 Khalani Maso, Cilimikani, Khalani Amphamvu

^ ndime 5 Monga mmene ikambila Mateyu 17:5, Yehova amafuna kuti tizimvela Mwana wake. M’nkhani ino, tikambilana zina mwa zimene tingaphunzile pa zimene Yesu anakamba atatsala pang’ono kufa pa mtengo wozunzikilapo.

^ ndime 9 Kuti mudziŵe zifukwa zothekela zimene Yesu anagwilila mawu Salimo 22:1, onani “Mafunso Ocokela kwa Oŵelenga” m’magazini ino.