Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 16

Tiziyamikira Mphatso ya Dipo

Tiziyamikira Mphatso ya Dipo

‘Mwana wa munthu anabwera . . . kudzapereka moyo wake dipo kuwombola anthu ambiri.’​—MALIKO 10:45.

NYIMBO NA. 18 Tikuthokoza Chifukwa cha Dipo

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1-2. Kodi dipo n’chiyani, nanga n’chifukwa chiyani lili lofunika?

ADAMU yemwe anali wangwiro, atachimwa anataya mwayi wokhala ndi moyo wosatha. Zimene anachitazi sizinakhudze iye yekha koma zinakhudzanso ana ake onse. Adamu analibe chifukwa chomveka chodzikhululukira chifukwa anachimwa mwadala. Koma nanga bwanji ana ake? Iwo sanalakwe chilichonse. (Aroma 5:12, 14) Ndiye kodi pali chilichonse chomwe chikanachitika kuti apulumutsidwe ku chilango cha imfa chimene kholo lawo linkayenera kulandira? Inde, tikutero chifukwa Adamu atangochimwa, Yehova anayamba kuulula pang’onopang’ono zimene adzachite kuti apulumutse ana a Adamu ku uchimo ndi imfa. (Gen. 3:15) Pa nthawi yake yoyenera, Yehova anatumiza Mwana wake padziko lapansi “kudzapereka moyo wake dipo kuwombola anthu ambiri.”​—Maliko 10:45; Yoh. 6:51.

2 Kodi dipo n’chiyani? M’Malemba a Chigiriki, mawu akuti dipo amanena za malipiro amene Yesu anapereka powombola zimene Adamu anataya. (1 Akor. 15:22) N’chifukwa chiyani timafunikira dipo? Chifukwa mogwirizana ndi Chilamulo, chilungamo cha Yehova chinkafuna kuti moyo uzilipira moyo. (Eks. 21:23, 24) Adamu anataya moyo wangwiro choncho pofuna kukwaniritsa chilungamo cha Mulungu, Yesu anaperekanso moyo wake wangwiro. (Aroma 5:17) Apatu Yesu anakhala “Atate Wosatha” kwa onse amene amakhulupirira dipo.​—Yes. 9:6; Aroma 3:23, 24.

3. Mogwirizana ndi Yohane 14:31 ndi 15:13, n’chifukwa chiyani Yesu anali wofunitsitsa kupereka moyo wake wangwiro?

3 Yesu anali wofunitsitsa kupereka moyo wake chifukwa choti amakonda kwambiri Atate wake wakumwamba komanso anthu. (Werengani Yohane 14:31; 15:13.) Chikondi chimenechi chinamuthandiza kukhalabe wokhulupirika kwa moyo wake wonse ndi kukwaniritsa chifuniro cha Atate wake. Zimene anachitazi zinathandiza kuti cholinga chimene Yehova anali nacho chokhudza anthu ndi dziko lapansili chidzakwaniritsidwe. Munkhaniyi tikambirana chifukwa chake Mulungu analola kuti Yesu avutike kwambiri asanafe. Tikambirananso mwachidule chitsanzo cha munthu wina amene analemba nawo Baibulo, yemwe ankayamikira kwambiri dipo. Pomaliza tikambirana mmene tingasonyezere kuti timayamikira dipo komanso zimene Yehova ndi Yesu anatichitira.

N’CHIFUKWA CHIYANI MULUNGU ANALOLA KUTI YESU AVUTIKE?

Ganizirani mavuto onse amene Yesu anakumana nawo kuti apereke moyo wake monga dipo (Onani ndime 4)

4. Fotokozani mmene Yesu anafera.

4 Taganizirani zimene zinachitika patsiku lomaliza Yesu asanafe. Ngakhale kuti akanatha kuitanitsa angelo ambirimbiri kuti amuteteze, iye analola kuti asilikali a Chiroma amugwire komanso kumumenya mopanda chifundo. (Mat. 26:52-54; Yoh. 18:3; 19:1) Iwo anamukwapula ndi chikwapu chimene chinasiya mabala aakulu pathupi lake. Kenako anamunyamulitsa mtengo wolemera kumsana kwake komwe kunali mabala okhaokha. Yesu anayamba kukwakwaza mtengowo kupita nawo kumalo komwe ankakamuphera koma atangoyenda pang’ono, asilikaliwo analamula munthu wina kuti amunyamulire mtengowo. (Mat. 27:32) Atafika kumalowo, asilikaliwo anakhomerera manja ndi mapazi ake kumtengowo ndi misomali. Ataimika mtengowo, mabala a misomali aja anawonjezeka chifukwa cha kulemera kwa thupi lake. Anzake a Yesu anamva chisoni kwambiri ndipo mayi ake ankangolira koma atsogoleri a Chiyuda ankamunyogodola. (Luka 23:32-38; Yoh. 19:25) Yesu anavutika ndi ululu umenewu kwa maola angapo. Mtima ndi mapapo ake zinkalephera kugwira bwino ntchito ndipo ankapuma movutikira. Atangotsala pang’ono kufa komanso ataona kuti wayesetsa kuchita zonse mokhulupirika, anapereka pemphero lake lomaliza kwa Yehova. Kenako anaweramitsa mutu wake n’kupereka moyo wake. (Maliko 15:37; Luka 23:46; Yoh. 10:17, 18; 19:30) Imeneyitu inali imfa yopweteka kwambiri komanso yochititsa manyazi.

5. Kodi n’chiyani chimene Yesu ankadera nacho nkhawa kwambiri kuposa imfa yake?

5 Yesu sankada nkhawa kwambiri chifukwa cha njira imene anagwiritsa ntchito pofuna kumupha. Koma chinkamudetsa nkhawa kwambiri ndi chifukwa chimene anamuphera. Iye ankaimbidwa mlandu wakuti anali wonyoza Mulungu, munthu amene sankalemekeza Mulungu komanso dzina lake. (Mat. 26:64-66) Zimenezi zinkamupweteka kwambiri Yesu moti ankalakalaka Atate wake atamuchotsera chitonzo chimenechi. (Mat. 26:38, 39, 42) Ndiye n’chifukwa chiyani Yehova analola kuti Mwana wake wokondedwa avutike chonchi komanso kufa? Tiyeni tikambirane zifukwa zitatu.

6. N’chifukwa chiyani Yesu ankayenera kupachikidwa pamtengo wozunzikirapo?

6 Choyamba, Yesu ankayenera kupachikidwa pamtengo kuti amasule Ayuda ku temberero linalake. (Agal. 3:10, 13) Iwo anali atalonjeza kuti adzamvera Chilamulo cha Mulungu koma analephera kuchitsatira. Choncho iwo anali otembereredwa kuwonjezera pa mfundo yoti ankayenera kufa popeza anali ana a Adamu yemwe anali wochimwa. (Aroma 5:12) Chilamulo chimene Mulungu anapereka kwa Aisiraeli, chinkanena kuti munthu amene wapalamula mlandu womwe chilango chake ndi imfa, aziphedwa kenako thupi lake lizipachikidwa pamtengo. * (Deut. 21:22, 23; 27:26) Choncho pamene Yesu anapachikidwa pamtengo, anathandiza kuti Ayuda amasulidwe ku temberero lawo ndiponso kuti athe kupindula ndi nsembe ya dipo ngakhale kuti anali atamukana.

7. Kodi chifukwa chachiwiri chomwe Mulungu analolera kuti Mwana wake avutike ndi chiti?

7 Taganizirani chifukwa chachiwiri chimene chinapangitsa Mulungu kulola kuti Mwana wake avutike. Iye ankakonzekeretsa Yesu kuti adzakwaniritse udindo wake wam’tsogolo monga mkulu wa ansembe. Yesu anaona mmene zimakhalira zovuta kumvera Mulungu ukakumana ndi mayesero aakulu. Iye anapanikizika kwambiri mpaka anafika popempha Yehova kuti amuthandize, ‘akufuula komanso akugwetsa misozi.’ Popeza kuti anavutikapo kwambiri chonchi, Yesu amamvetsa mmene timamvera ndipo “amatha kuthandiza anthu amene akuyesedwa.” Timayamikira kwambiri kuti Yehova anatipatsa mkulu wa ansembe wachifundo, yemwe ‘amatimvera chisoni pa zofooka zathu.’​—Aheb. 2:17, 18; 4:14-16; 5:7-10.

8. Kodi chifukwa chachitatu chomwe Mulungu analolera kuti Yesu ayesedwe kwambiri ndi chiti?

8 Chifukwa chachitatu chimene Yehova analolera kuti Yesu avutike kwambiri n’choti ankafuna kupereka yankho pa funso lofunika kwambiri, lakuti: Kodi anthu angakhalebe okhulupirika kwa Yehova ngakhale atakumana ndi mayesero aakulu? Satana amatsutsa zimenezi. Iye amanena kuti anthu amatumikira Mulungu ndi zolinga zadyera. Ndipo amakhulupirira kuti mofanana ndi kholo lawo Adamu, anthu sakonda Yehova. (Yobu 1:9-11; 2:4, 5) Popeza kuti Yehova sankakayikira kuti Mwana wake akhalabe wokhulupirika, iye analola kuti Yesu ayesedwe kwambiri. Yesu anakhalabe wokhulupirika ndipo anasonyeza kuti Satana ndi wabodza.

WOLEMBA BAIBULO AMENE ANKAYAMIKIRA KWAMBIRI DIPO

9. Kodi mtumwi Yohane anatipatsa chitsanzo chotani?

9 Kuphunzira za dipo kwathandiza Akhristu ambiri kukhala ndi chikhulupiriro cholimba. Iwo amapitirizabe kulalikira ngakhale kuti amatsutsidwa komanso akhala akupirira mayesero osiyanasiyana pa moyo wawo. Taganizirani chitsanzo cha mtumwi Yohane. Iye ankalalikira mokhulupirika choonadi chonena za Khristu komanso dipo mwina kwa zaka zoposa 60. Ali ndi zaka za m’ma 90, ulamuliro wa Roma unamuika m’ndende pachilumba cha Patimo chifukwa chomuganizira kuti anali munthu woopsa. Koma kodi iye analakwa chiyani? Iwo anamumanga chifukwa “cholankhula za Mulungu ndi kuchitira umboni za Yesu.” (Chiv. 1:9) Yohane anapereka chitsanzo chabwino pa nkhani yokhala ndi chikhulupiriro komanso kupirira.

10. Kodi mabuku a m’Baibulo omwe Yohane analemba, amasonyeza bwanji kuti ankayamikira dipo?

10 Mabuku a m’Baibulo omwe Yohane analemba, amasonyeza kuti ankakonda kwambiri Yesu ndipo ankayamikira dipo. Iye analemba zokhudza dipo kapena madalitso amene timapeza chifukwa cha dipolo, maulendo oposa 100. Mwachitsanzo, Yohane analemba kuti: “Wina akachita tchimo, tili ndi mthandizi wolungama, Yesu Khristu, amene ali ndi Atate.” (1 Yoh. 2:1, 2) Mabuku amene Yohane analemba, amatsindikanso kufunika kochitira “umboni za Yesu.” (Chiv. 19:10) N’zoonekeratu kuti Yohane ankayamikira kwambiri dipo. Ndiye kodi tingasonyeze bwanji kuti nafenso timayamikira dipo?

KODI TINGASONYEZE BWANJI KUTI TIMAYAMIKIRA DIPO?

Ngati timayamikira kwambiri dipo, tidzapewa kuchita machimo (Onani ndime 11) *

11. Kodi chingatithandize n’chiyani kuti tizipewa mayesero?

11 Tizipewa kuchita tchimo. Ngati timayamikira kwambiri dipo, tidzapewa maganizo akuti: ‘Ndikamayesedwa palibe chifukwa chomavutika ndi kupewa mayeserowo. Ndikhoza kuchita tchimolo kenako n’kupempha Mulungu kuti andikhululukire.’ M’malomwake tikamayesedwa kuti tichite zinazake zoipa, tidzanena kuti: ‘Ndingachitirenji zimenezi poganizira zabwino zonse zomwe Yehova ndi Yesu andichitira.’ Ndiyeno mungapemphe Yehova kuti akupatseni mphamvu, pomuchonderera kuti: ‘Musalole kuti ndigonje pa mayeserowa.’​—Mat. 6:13.

12. Kodi tingagwiritse ntchito bwanji malangizo a pa 1 Yohane 3:16-18?

12 Tizikonda abale ndi alongo athu. Tikamakonda abale ndi alongo athu, timasonyezanso kuti timayamikira dipo. N’chifukwa chiyani tikutero? Tikutero chifukwa Yesu sanafere ife tokha koma anaferanso abale ndi alongo athuwo. Ndiye ngati Yesu anali wofunitsitsa kuwafera, n’zoonekeratu kuti amawakonda kwambiri. (Werengani 1 Yohane 3:16-18.) Timasonyeza kuti timakonda abale ndi alongo athu kudzera m’zochita zathu. (Aef. 4:29, 31–5:2) Mwachitsanzo, timawathandiza akadwala kapena akakumana ndi mavuto aakulu kuphatikizapo ngozi zam’chilengedwe. Koma kodi tiyenera kuchita chiyani Mkhristu mnzathu akalankhula kapena kuchita zinthu zimene zatikhumudwitsa?

13. N’chifukwa chiyani tiyenera kumakhululukira ena?

13 Kodi nthawi zina zimakuvutani kukhululukira Mkhristu mnzanu? (Lev. 19:18) Ngati ndi choncho, muzitsatira malangizo akuti: “Pitirizani kulolerana ndi kukhululukirana ndi mtima wonse, ngati wina ali ndi chifukwa chodandaulira za mnzake. Monga Yehova anakukhululukirani ndi mtima wonse, inunso teroni.” (Akol. 3:13) Nthawi iliyonse imene takhululukira m’bale kapena mlongo, timasonyeza Atate wathu wakumwamba kuti timayamikira kwambiri dipo. Ndiye kodi tingatani kuti tipitirize kuyamikira kwambiri mphatso imene Mulungu anatipatsayi?

KODI TINGACHITE CHIYANI KUTI TIZIYAMIKIRA KWAMBIRI DIPO?

14. Kodi ndi njira inanso iti imene ingatithandize kuti tiziyamikira kwambiri dipo?

14 Tizithokoza Yehova chifukwa cha dipo. Mlongo wina wazaka 83 dzina lake Joanna, yemwe amakhala ku India anati: “Ndimaona kuti n’zofunika kuti tsiku lililonse m’mapemphero anga ndizithokoza Yehova chifukwa cha dipo.” Inunso tsiku lililonse mukamapemphera panokha, muziganizira zimene munalakwitsa patsikulo n’kupempha Yehova kuti akukhululukireni. Koma ngati mwachita tchimo lalikulu mungafunike kuuzanso akulu. Iwo adzakuthandizani mwachikondi komanso kukupatsani malangizo ochokera m’Mawu a Mulungu. Akuluwo adzapemphera nanu kupempha Yehova kuti akukhululukireni pogwiritsa ntchito dipo la Yesu kuti “muchiritsidwe” kapena kuti mukhalenso naye pa ubwenzi.​—Yak. 5:14-16.

15. N’chifukwa chiyani tiyenera kupeza nthawi yowerenga komanso kuganizira mozama za dipo?

15 Tiziganizira mozama zokhudza dipo. Mlongo wina wazaka 73, dzina lake Rajamani ananena kuti: “Nthawi zonse ndikamawerenga zokhudza mavuto amene Yesu anakumana nawo, ndimagwetsa misozi.” N’kutheka kuti nanunso mumamva chisoni mukaganizira mmene Mwana wa Mulungu anavutikira. Koma mukamaganizira kwambiri nsembe ya Yesu m’pamene mumayamba kumukonda kwambiri iyeyo komanso Atate wake. Kuti muziganizira mozama zokhudza dipo, bwanji osakonza zoti muphunzire za nkhaniyi pa kulambira kwanu kwa pabanja kapena mukamaphunzira panokha?

Pogwiritsa ntchito zinthu zosavuta kupeza, Yesu anasonyeza ophunzira ake mmene angachitire mwambo wokumbukira imfa yake (Onani ndime 16)

16. Kodi kuphunzitsa ena zokhudza dipo kumatithandiza bwanji? (Onani chithunzi chapachikuto.)

16 Tiziphunzitsa ena zokhudza dipo. Tikamauza ena zokhudza dipo m’pamene nafenso timaliyamikira kwambiri. Tili ndi mabuku ndi mavidiyo ambiri amene amatithandiza kufotokozera ena chifukwa chake Yesu anatifera. Mwachitsanzo, tikhoza kugwiritsa ntchito phunziro 4, m’kabuku kakuti Uthenga Wabwino Wochokera kwa Mulungu. Phunziro limeneli lili ndi mutu wakuti, “Kodi Yesu Khristu Ndani?” Tingathenso kugwiritsa ntchito mutu 5, m’buku lakuti Zimene Baibulo Limaphunzitsa, womwe umati, “Dipo la Yesu Ndi Mphatso Yamtengo Wapatali Imene Mulungu Anatipatsa.” Ndipotu chaka chilichonse timasonyeza kuti timayamikira kwambiri dipo tikapezeka pamwambo wokumbukira imfa ya Yesu komanso tikamachita khama kuitanira ena kumwambowu. Apatu Yehova anatipatsa mwayi wamtengo wapatali wophunzitsa ena zokhudza Mwana wake.

17. N’chifukwa chiyani dipo ndi mphatso yamtengo wapatali imene Mulungu anatipatsa?

17 Mosakayikira, tili ndi zifukwa zabwino zotichititsa kupitirizabe kuyamikira kwambiri dipo. Chifukwa cha dipo, timatha kukhala pa ubwenzi ndi Yehova ngakhale kuti si ife angwiro. Dipo lidzatheketsanso kuti ntchito za Mdyerekezi ziwonongedwe kotheratu. (1 Yoh. 3:8) Komanso dipo lidzathandiza kuti cholinga chimene Mulungu anali nacho chokhudza dziko lapansi chikwaniritsidwe ndipo dziko lonseli lidzakhala paradaiso. Pa nthawiyo aliyense azidzakonda Yehova komanso kumutumikira. Choncho, tiyeni tsiku lililonse tizifufuza njira zimene tingasonyezere kuti timayamikira kwambiri dipo, limene ndi mphatso yamtengo wapatali imene Mulungu anatipatsa.

NYIMBO NA. 20 Munapereka Mwana Wanu Wobadwa Yekha

^ ndime 5 Kodi n’chifukwa chiyani Yesu anaphedwa mwankhanza? Nkhaniyi iyankha funso limeneli. Itithandizanso kuti tiziyamikira kwambiri mphatso ya dipo.

^ ndime 6 Chinali chikhalidwe cha Aroma kukhomerera kapena kumangirira pamtengo munthu amene wapalamula mlandu ali wamoyo. Ndipo Yehova analola kuti Mwana wake aphedwe mwanjira imeneyi.

^ ndime 55 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Abale akupewa mayesero, wina akupewa kuona zithunzi zosayenera, wina akukana kusuta fodya ndipo wina akukana kulandira ziphuphu.