Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 16

Pitilizani Kuyamikila Dipo

Pitilizani Kuyamikila Dipo

‘Mwana wa munthu anabwela kudzapeleka moyo wake dipo.’ —MALIKO 10:45.

NYIMBO 18 Tikuyamikani Cifukwa ca Dipo

ZIMENE TIKAMBILANE *

1-2. Kodi dipo n’ciani? Ndipo n’cifukwa ciani tifunikila dipo?

PAMENE munthu wangwilo Adamu anacimwa, iye anataya mwayi wokhala na moyo wosatha, osati moyo wake wokha, komanso ngakhale wa ana ake akutsogolo. Panalibiletu cifukwa ciliconse colungamitsa zimene Adamu anacita. Iye anacimwila dala. Koma bwanji za ana ake? Iwo sanatengeko mbali pa kucimwa kwa Adamu. (Aroma 5:12, 14) Koma kodi panali njila iliyonse yopulumutsila anawo ku cilango ca imfa cimene atate awo anayeneladi kulandila? Inde inalipo! Posapita nthawi Adamu atacimwa, Yehova anayamba kuvumbula pang’ono-pang’ono mmene adzapulumutsila mbadwa mamiliyoni za Adamu ku tembelelo la ucimo na imfa. (Gen. 3:15) Panthawi yake yoyenelela, Yehova anatumiza mwana wake kucokela kumwamba “kudzapeleka moyo wake dipo kuwombola anthu ambili.”—Maliko 10:45; Yoh. 6:51.

2 Kodi dipo n’ciani? M’Malemba Acikhristu Acigiriki, dipo ni malipilo amene Yesu anapeleka ogulilanso zimene Adamu anataya. (1 Akor. 15:22) N’cifukwa ciani tifunikila dipo? Cifukwa malinga na cilamulo, cilungamo ca Yehova cinali kufuna kuti moyo uzilipila moyo. (Eks. 21:23, 24) Adamu anataya moyo wake wangwilo. Conco pokwanilitsa cilungamo ca Mulungu, Yesu anapeleka moyo wake wangwilo. (Aroma 5:17) Ndiye cifukwa cake anakhala “Atate Wosatha” wa onse amene amakhulupilila dipo.—Yes. 9:6; Aroma 3:23, 24.

3. Malinga na Yohane 14:31; komanso 15:13, n’cifukwa ciani Yesu anali wokonzeka kupeleka moyo wake wangwilo?

3 Yesu anali wokonzeka kupeleka moyo wake cifukwa cokonda kwambili Atate wake wa kumwamba na ife. (Ŵelengani Yohane 14:31; 15:13.) Mosonkhezeledwa na cikondi cimeneco, iye anatsimikiza mtima kusunga umphumphu wake mpaka imfa, na kukwanilitsa cifunilo ca Atate wake. Yesu anacita zimenezi mwa kukhalabe wokhulupilika mpaka imfa. Mwa ici, colinga ca Yehova ca poyamba kwa anthu na dziko lapansi cidzakwanilitsidwa. M’nkhani ino, tidzakambilana cifukwa cake Mulungu analola Yesu kuvutika kwambili asanamwalile. Tidzakambilananso mwacidule, citsanzo ca wolemba Baibo amene anayamikila dipo kwambili. Ndipo pamapeto pake, tikambilane mmene tingaonetsele kuti timayamikila dipo, na mmene tingakulitsile ciyamikilo cathu pa nsembe imene Yehova na Yesu anatipatsa.

N’CIFUKWA CIANI YEHOVA ANALOLA YESU KUVUTIKA?

Ganizilani mavuto onse amene Yesu anapilila popeleka dipo kaamba ka ife!(Onani ndime 4)

4. Fotokozani mmene Yesu anafela.

4 Ganizilani zimene zinacitikila Yesu patsiku lothela la moyo wake padziko lapansi. Ngakhale kuti akanatha kuitanitsa magulu ankhondo a angelo kudzam’teteza, iye analola kuti asilikali aciroma am’gwile na kumumenya mopanda cifundo. (Mat. 26:52-54; Yoh. 18:3; 19:1) Pom’kwapula, anaseŵenzetsa shamboko imene inali kunyotsola minofu pathupi pake. Kenako, anam’nyamulitsa cimtengo colema pamsana pake, apo magazi ali cu cu cu! Ndiyeno Yesu akuyamba kuguza cimtengoco kupita kumene anali kukamuphela. Posapita nthawi, asilikali aciroma analamula munthu wina kum’nyamulila mtengowo. (Mat. 27:32) Pamene Yesu anafika pamalo om’phelapo, asilikaliwo anam’khomelela misomali kumanja na kumapazi. Ndipo kulemela kwa thupi lake kunang’ambilako zilonda za misomali zija. Mabwenzi ake anagwidwa na cisoni cacikulu, ndipo amayi ake anali kungolila, pamene atsogoleli aciyuda anali kum’nyodola. (Luka 23:32-38; Yoh. 19:25) Ola lililonse linali losautsa kosaneneka. Mtima wake unapsinjika, m’cifuwa munathina, cakuti kupuma kunayamba kuvuta. Pamene anali kutsilizika, anapeleka pemphelo lothela lacipambano. Kenako anagwetsa mutu, na kupeleka moyo wake. (Maliko 15:37; Luka 23:46; Yoh. 10:17, 18; 19:30) Kunena zoona, Yesu anafa imfa yoŵaŵa yapang’ono-pang’ono, ndiponso yonyazitsa!

5. N’ciani cinali coŵaŵa kwambili kwa Yesu kuposa mmene anam’phela?

5 Ngakhale n’telo, cinamuŵaŵa kwambili Yesu si cakuti adzafa monyozeka ayi. Cimene cinamuvutitsa maganizo kwambili ni mlandu umene anam’patsa monga cifukwa comuphela. Anamusemela mlandu wabodza wakuti anali wonyoza Mulungu—munthu wosalemekeza Mulungu kapena dzina la Mulungu. (Mat. 26:64-66) Kuganizila mlandu umene anapatsidwa umenewu kunam’vutitsa maganizo kwambili Yesu, cakuti anapempha Atate wake kuti zocititsa manyazi zimenezi zisam’citikile. (Mat. 26:38, 39, 42) Koma n’cifukwa ciani Yehova analola kuti mwana wake wokondekayo avutike motelo mpaka kufa? Tiyeni tikambilane zifukwa zitatu.

6. N’cifukwa ciani Yesu anayenela kupacikidwa pamtengo wonzunzikilapo?

6 Coyamba, Yesu anayenela kupacikidwa pamtengo kuti amasule Ayuda ku tembelelo. (Agal. 3:10, 13) Iwo analonjeza kuti adzasunga Cilamulo ca Mulungu koma analephela kutalitali! Mwa ici, tembelelo limeneli linangowonjezela pa limene anali nalo kale monga ana ocimwa a Adamu. (Aroma 5:12) Malinga na Cilamulo ca Mulungu kwa Aisiraeli, cinakamba kuti munthu akacita chimo loyenela imfa ayenela kuphedwa. Pambuyo pake, mtembo wake ungapacikidwe pamtengo. * (Deut. 21:22, 23; 27:26) Conco Yesu popacikidwa pa mtengo, anapangitsa kuti mtundu umene unam’kanawo upindule na nsembe yake.

7. N’cifukwa caciŵili citi cimene Mulungu analolela Mwana wake kuvutika?

7 Ganizilani cifukwa caciŵili cimene Mulungu analolela Mwana wake kuvutika. Anali kuphunzitsa Yesu kuti akacite bwino udindo wake kutsogolo monga Mkulu wa Ansembe wathu. Yesu anadzionela yekha mmene kumakhalila kovuta kumvela Mulungu pokumana na mayeselo aakulu. Iye anapanikizika kwambili cakuti anapempha thandizo “mofuula komanso akugwetsa misozi.” Popeza kuti Yesu anapitamo m’mavuto opsinja maganizo koopsa, amadziŵa zimene timafunikila, ndipo ‘amatha kutithandiza tikamayesedwa.’ Ndife oyamikila cotani nanga kwa Yehova posankha Mkulu wa Ansembe wacifundo amene ‘angatimvele cisoni pa zofooka zathu’!—Aheb. 2:17, 18; 4:14-16; 5:7-10.

8. Nanga cifukwa cacitatu cimene Mulungu analolela Yesu kuvutika kwambili n’citi?

8 Cacitatu, Yehova analola Yesu kuvutika kwambili conco, kotelo kuti ayankhe funso lofunika kwambili lakuti: Kodi anthu angakhaledi okhulupilika kwa Yehova pamene ali pamayeso aakulu? Satana amakamba kuti ayi! Iye amati anthu amangotumikila Mulungu cifukwa cofunapo phindu linalake cabe. Ndipo amakhulupilila kuti monga atate wawo Adamu, iwo si odzipeleka na mtima wonse kwa Yehova. (Yobu 1:9-11; 2:4, 5) Podalila kukhulupilika kwa Mwana wake, Yehova analola kuti Yesu ayesedwe mpaka mapeto a kupilila kwa munthu. Ndipo Yesu anasungadi umphumphu wake, na kuonetsa kuti Satana ni wabodza.

WOLEMBA BAIBO AMENE ANAYAMIKILA DIPO KWAMBILI

9. Kodi mtumwi Yohane anatipatsa citsanzo cotani?

9 Akhristu ambili cikhulupililo cawo calimba cifukwa cophunzila za dipo. Iwo apitilizabe kulalikila ngakhale pamene akutsutsidwa ndipo apilila mayeso osiyana-siyana mpaka ukalamba wawo. Ganizilani citsanzo ca mtumwi Yohane. Iye mokhulupilika analalikila za coonadi ca Khristu na dipo mwina kwa zaka zoposa 60. Ali na zaka pafupi-fupi 100, anam’ganizila kuti akupeleka ciopsezo ku Ufumu wa Roma, cakuti anaponyedwa m’ndende pacisumbu ca Patimo. Pa mlandu wanji? ‘Kulankhula za Mulungu ndi kucitila umboni za Yesu.’ (Chiv. 1:9) Ndithudi, iye ni citsanzo cabwino ngako pa cikhulupililo na kupilila!

10. Kodi zolemba za Yohane zionetsa bwanji kuti anali kuyamikila dipo?

10 Yohane anaonetsa kuti amakonda kwambili Yesu na kuyamikila dipo lake mwa zimene analemba m’mabuku ake ouzilidwa. Koposa maulendo 100, iye anachula za dipo kapena mapindu amene tidzapeza kaamba ka dipo. Mwacitsanzo, Yohane analemba kuti: “Wina akacita chimo, tili ndi mthandizi wolungama, Yesu Khristu, amene ali ndi Atate.” (1 Yoh. 2:1, 2) Zolemba za Yohane zinagogomezanso kufunika ‘kocitila umboni za Yesu.’ (Chiv. 19:10) N’zoonekelatu kuti Yohane analiyamikila kwambili dipo. Kodi nafenso tingaonetse bwanji kuti timaliyamikila?

KODI MUNGAONETSE BWANJI KUTI MUMALIYAMIKILA DIPO?

Ngati dipo timaliyamikiladi, tidzakaniza mayeselo alionse ofuna kucita chimo (Onani ndime 11) *

11. N’ciani cingatithandize kukaniza mayeselo?

11 Tisagonje tikayesedwa kuti ticite chimo. Ngati timayamikiladi dipo, sitidzakhala na maganizo akuti: ‘Mayeselo akanikulila, m’pomveka kugonja. Ndipo nikacita chimo, nidzapempha cikhululukilo.’ M’malomwake tikayesedwa kuti ticite coipa tizinena kuti: ‘Iyayi! Ningacitilenji coipa ici nikaganizila zonse zimene Yehova na Yesu anicitila?’ Na maganizo amenewa, tingapemphe Yehova kuti atipatse mphamvu, na kum’condelela kuti: ‘Musalole kuti nigonje ku mayeselo.’—Mat. 6:13.

12. Tingaseŵenzetse bwanji uphungu wa pa 1 Yohane 3:16-18?

12 Kondani abale na alongo anu. Ngati tikonda abale na alongo athu, timaonetsanso kuti timayamikila dipo. Cifukwa ciani? Cifukwa Yesu anapeleka moyo wake kaamba ka ife, komanso kaamba ka abale na alongo athu. Conco ngati iye anali wokonzeka kuwafela, ndiye kuti amawaona kukhala ofunika kwambili. (Ŵelengani 1 Yohane 3:16-18.) Timaonetsa cikondi pa abale na alongo athu malinga na mmene timacitila nawo zinthu. (Aef. 4:29, 31; 5:2) Mwacitsanzo, timawathandiza akadwala kapena pamene akupilila mavuto aakulu, kuphatikizapo matsoka a zacilengedwe. Koma kodi tiyenela kucita ciani ngati wokhulupilila mnzathu wakamba kapena kucita zinthu zimene zatikhumudwitsa?

13. N’cifukwa ciani tiyenela kukhululukila ena?

13 Kodi mumakonda kusunga cakukhosi wokhulupilila mnzanu akakulakwilani? (Lev. 19:18) Ngati mumatelo, conde tsatilani malangizo aya: “Pitilizani kulolelana ndi kukhululukilana ndi mtima wonse, ngati wina ali ndi cifukwa codandaulila za mnzake. Monga Yehova anakukhululukilani ndi mtima wonse, inunso teloni.” (Akol. 3:13) Nthawi zonse tikakhululukila m’bale kapena mlongo wathu, timaonetsa Atate wathu wakumwamba kuti dipo timaliyamikila kwambili. Koma kodi tiyenela kucita ciani kuti tipitilize kuyamikila mphatso yocokela kwa Mulungu imeneyi?

TINGAKULITSE BWANJI CIYAMIKILO CATHU PA DIPO?

14. Ni njila imodzi iti imene tingakulitsile ciyamikilo cathu pa dipo?

14 Yamikilani Yehova kaamba ka dipo. Mlongo Joanna wa zaka 83 wa ku India anakamba kuti: “Niona kuti tsiku lililonse m’pofunika kwambili kuyamikila Yehova kaamba ka dipo m’mapemphelo anga.” M’mapemphelo anu aumwini, ganizilani zimene mwalakwitsa patsikulo, ndipo pemphani Yehova kuti akukhululukileni. Koma ngati mwacita chimo lalikulu, mudzafunikilanso thandizo la akulu. Iwo adzakumvetselani na kukupatsani uphungu wacikondi wopezeka m’Mawu a Mulungu. Adzapemphela nanu pamodzi, kupempha Yehova kuti alole nsembe ya Yesu kupitiliza kugwila nchito kuti “mucilitsidwe [mwauzimu].”—Yak. 5:14-16.

15. N’cifukwa ciani tiyenela kupeza nthawi yoŵelenga na kusinkha-sinkha pa dipo?

15 Sinkha-sinkhani pa dipo. Mlongo Rajamani wa zaka 73 ananena kuti: “Nikaŵelenga za mavuto amene Yesu anapitamo, maso anga amadzala na misozi.” Mwina na imwe mumakhudzika mtima ngako mukaganizila za mmene Mwana wa Mulungu anavutikila. Koma mukamasinkha-sinkha kwambili pa nsembe imene Yesu anapeleka, mudzakulitsa kwambili cikondi canu pa iye komanso pa Atate wake. Kuti mukathe kusinkha-sinkha bwino za dipo, bwanji osakafufuza na kuŵelenga za dipo pa phunzilo lanu laumwini?

Mwa kukonza cakudya cosalila zambili, Yesu anaonetsa ophunzila ake zimene angacite pokumbukila nsembe yake (Onani ndime 16)

16. Kodi kuphunzitsa ena za dipo kungatipindulitse bwanji? (Onani cithunzi pacikuto)

16 Phunzitsani ena za dipo. Nthawi zonse tikamauza ena za dipo, ciyamikilo cathu cimakula pa dipolo. Tili na zida zabwino kwambili zimene tingaseŵenzetse pophunzitsa ena za cifukwa cake Yesu anafunika kutifela. Mwacitsanzo, mungaseŵenzetse phunzilo 4 m’bulosha yakuti Uthenga Wabwino Wocokela Kwa Mulungu! Phunzilo limenelo lili na mutu wakuti “Kodi Yesu Khristu ndani?” Kapena tingaseŵenzetse mutu 5 m’buku lakuti Zimene Baibo Imaphunzitsa. Mutu umenewo uli na nkhani yakuti “Dipo ni Mphatso ya Mulungu Yopambana Zonse.” Ndipo caka ciliconse timazamitsa ciyamikilo cathu pa dipo mwa kupezeka pa Cikumbutso ca imfa ya Yesu, komanso mwa kuitanila ena mwakhama kuti akapezekepo. Ha! Ni mwayi waukulu cotani nanga umene Yehova watipatsa wophunzitsa ena za Mwana wake!

17. N’cifukwa ciani dipo ndiyo mphatso yopambana zonse, imene Mulungu anapatsa anthu?

17 Mosakayikila, tili na zifukwa zomveka zopitilizila kukhala oyamikila kaamba ka dipo. Cifukwa ca dipo tingakhale paubwenzi wolimba na Yehova ngakhale kuti ndife opanda ungwilo. Cifukwa ca dipo, nchito za Mdyelekezi zidzawonongedwa. (1 Yoh. 3:8) Cifukwa ca dipo, colinga ca Yehova ca poyamba cokhudza dziko lapansi cidzakwanilitsidwa. Dziko lonse lapansi lidzakhala paradaiso. Munthu aliyense amene mudzakumane naye m’dzikolo adzakhala wokonda Yehova na kum’tumikila. Conco, tiyeni tiyesetse tsiku lililonse kupeza mipata yoonetsela kuti timayamikila dipo. Inde, ndiyo mphatso yaikulu yopambana zonse, imene Mulungu anapatsa anthu!

NYIMBO 20 Munapeleka Mwana Wanu Wokondeka

^ ndime 5 N’cifukwa ciani Yesu anafa imfa yoŵaŵa conco? Nkhani ino iyankha funso limeneli. Idzatithandizanso kukulitsa ciyamikilo cathu pa dipo.

^ ndime 6 Mmene Aroma anali kuphela munthu wogamulidwa kuti aphedwe, anali kum’khomelela kapena kum’mangilila wamoyo pamtengo wozunzikilapo. Ndipo Yehova analola kuti Mwana wake aphedwe mwa njila imeneyo.

^ ndime 55 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: M’bale aliyense akukaniza ciyeso—coyang’ana zithunzi zolaula, cokoka fodya, kapena colandila ciphuphu.