Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 20

Pitirizani Kuona Utumiki Wanu Moyenera

Pitirizani Kuona Utumiki Wanu Moyenera

“Bzala mbewu zako . . . ndipo dzanja lako lisapume.”​MLAL. 11:6.

NYIMBO NA. 70 Fufuzani Anthu Oyenerera

ZIMENE TIPHUNZIRE *

Yesu atakwera kumwamba, ophunzira ake anachita khama kulalikira mu Yerusalemu komanso madera ena (Onani ndime 1)

1. Kodi Yesu anasiyira otsatira ake chitsanzo chotani, nanga iwo anachita chiyani? (Onani chithunzi chapachikuto.)

ALI PADZIKO lapansili, Yesu ankaona moyenera utumiki wake ndipo amafunanso otsatira ake aziona moyenera utumiki wawo. (Yoh. 4:35, 36) Ophunzira ake ankachita khama kugwira ntchito yolalikira pamene iye anali nawo limodzi. (Luka 10:1, 5-11, 17) Koma Yesu atagwidwa komanso kuphedwa, ophunzirawo kwa kanthawi kochepa anasiya kulalikira. (Yoh. 16:32) Ndiyeno ataukitsidwa iye analimbikitsa ophunzirawo kuti ayambirenso kugwira ntchito yolalikira mwakhama. Ndipo Yesu atakwera kumwamba iwo analalikira mwakhama kwambiri moti adani awo anafika podandaula kuti: “Taonani tsopano! Mwadzadza Yerusalemu yense ndi chiphunzitso chanuchi.”​—Mac. 5:28.

2. Kodi Yehova wadalitsa bwanji ntchito yolalikira?

2 Yesu ankatsogolera ntchito ya Akhristu oyambirira ndipo Yehova anawadalitsa moti anthu ambiri anakhala okhulupirira. Mwachitsanzo, pa Pentekosite mu 33 C.E., anthu pafupifupi 3,000 anabatizidwa. (Mac. 2:41) Ndipo chiwerengero cha ophunzira chinapitiriza kukula kwambiri. (Mac. 6:7) Komabe Yesu ananeneratu kuti ntchito yolalikira idzawonjezeka kwambiri m’masiku otsiriza.​—Yoh. 14:12; Mac. 1:8.

3-4. N’chifukwa chiyani m’madera ena ntchito yolalikira ndi yovuta, nanga tikambirana chiyani munkhaniyi?

3 Tonsefe timayesetsa kuti tiziona moyenera ntchito yathu yolalikira ndipo m’mayiko ena kuchita zimenezi n’kosavuta. N’chifukwa chiyani tikutero? Tikutero chifukwa anthu ambiri amasangalala kuphunzira Baibulo ndipo ena amachita kudikirira mpaka patapezeka wa Mboni kuti aziwaphunzitsa. Koma m’madera ena ofalitsa amakumana ndi mavuto pogwira ntchito yolalikira chifukwa anthu ambiri sapezeka pakhomo. Ndipo amene amapezeka pakhomo sasonyeza chidwi chofuna kuphunzira Baibulo.

4 Ngati mukukhala m’dera limene ntchito yolalikira ndi yovuta, mfundo za munkhaniyi zingakuthandizeni. Tiona zimene ena amachita kuti azikwanitsa kulalikira anthu ambiri. Tionanso chifukwa chake tiyenera kupitirizabe kukhala osangalala kaya anthu akumvetsera uthenga wathu kapena ayi.

MUZISANGALALABE NGAKHALE PAMENE SIMUKUPEZA ANTHU

5. Kodi a Mboni ambiri amakumana ndi mavuto otani?

5 M’madera ena a Mboni ambiri amavutika kuti alalikire anthu m’makomo awo. Ofalitsa ena amalalikira m’madera amene kuli nyumba zokhala ndi chitetezo chokhwima kapenanso mageti. Nyumba zimenezi zimakhala ndi mlonda yemwe salola wina aliyense kulowa ngati sanaitanidwe ndi eniake a nyumbazo. Ofalitsa ena amatha kupita mosavuta khomo ndi khomo koma anthu ambiri sapezeka panyumba. Pomwe ofalitsa ena amalalikira madera a kumidzi kapena akutali kwambiri komwe kumakhala anthu ochepa. Iwo amatha kuyenda mtunda wautali kuti akapeze munthu mmodzi yemwe mwinanso sangapezeke pakhomo. Ngati inunso mumakumana ndi mavuto amenewa simuyenera kutaya mtima. Ndiye kodi tingatani kuti tithe kulimbana ndi mavuto amenewa n’cholinga choti utumiki wathu uziyenda bwino?

6. Kodi ntchito yolalikira imafanana bwanji ndi ntchito ya usodzi?

6 Yesu anayerekezera ntchito yolalikira ndi zimene asodzi amachita. (Maliko 1:17) Asodzi ena amatha kugwira ntchito kwa masiku angapo osapha nsomba. Koma iwo sataya mtima, m’malomwake amangosintha mmene akugwirira ntchito yawo. Iwo amatha kungosintha nthawi, malo komanso njira zimene amagwiritsa ntchito. Ifenso tingachite chimodzimodzi pamene tikugwira ntchito yolalikira. Tiyeni tikambirane zinthu zina zimene zingatithandize.

Tikamalalikira m’dera limene anthu ambiri sapezeka pakhomo tizisintha nthawi, malo komanso njira zolalikirira (Onani ndimes 7-10) *

7. Kodi chingachitike n’chiyani tikamasintha nthawi yolalikirira?

7 Muzisintha nthawi yolalikirira. Tingalalikire kwa anthu ambiri ngati titapita pa nthawi imene amapezeka panyumba. Ndipotu zoona n’zakuti munthu akapita kukayenda, nthawi ina amabwereranso panyumba pake. Abale ndi alongo ambiri amaona kuti zimawathandiza akamalalikira masana kapena madzulo chifukwa anthu ambiri amakhala ali panyumba. Kuwonjezera pamenepo, pa nthawi imeneyi eni nyumba amakhala ndi mpata komanso omasuka moti amakhala okonzeka kumvetsera. Mwinanso zimene David, yemwe ndi mkulu amachita zingakuthandizeni. Iye ananena kuti akalalikira kwa kanthawi m’gawo limene ali, amabwereranso ndi mnzake amene ali naye kunyumba zimene sanapezeko anthu. David anati: “Ndimadabwa kuti timapeza anthu ambiri panyumba zawo tikabwererakonso.” *

Tikamalalikira m’dera limene anthu ambiri sapezeka pakhomo, tizisintha nthawi (Onani ndimes 7-8)

8. Kodi tingagwiritse ntchito bwanji mfundo ya pa Mlaliki 11:6 tikamagwira ntchito yolalikira?

8 Ngati sitinapeze anthu panyumba zawo tisamafooke. Lemba limene likutsogolera nkhaniyi likutikumbutsa maganizo amene tiyenera kukhala nawo. (Werengani Mlaliki 11:6.) David, yemwe tamutchula kale uja sanafooke. Atayesa kulalikira maulendo angapo panyumba ina koma osapezapo anthu, ulendo wina anapeza mwininyumba. Mwininyumbayo anasangalala kukambirana mfundo za m’Baibulo ndi David ndipo anati: “Ndakhala ndili pano kwa zaka pafupifupi 8, koma sindinakumanepo ndi wa Mboni panyumba panga pano.” David anati: “Ndaona kuti tikayesetsa kuti tipeze anthu panyumba pawo, nthawi zambiri iwo amakhala okonzeka kumvetsera uthenga umene timalalikira.”

Tikamalalikira m’dera limene anthu ambiri sapezeka pakhomo, tizisintha malo (Onani ndime 9)

9. Kodi a Mboni ena amatani kuti alalikire anthu amene n’kovuta kuwapeza pakhomo?

9 Muzisintha malo olalikira. Pofuna kulalikira kwa anthu amene sapezeka pakhomo ofalitsa ena amasintha malo amene amalalikira. Mwachitsanzo iwo amaona kuti kulalikira mumsewu kapena kugwiritsa ntchito timashelefu kumathandiza kuti athe kupeza anthu amene amakhala m’nyumba zimene kulalikira khomo ndi khomo n’kosaloledwa. Akatero amatha kulankhula ndi anthu amene sakanatha n’komwe kuwalalikira. Komanso ofalitsa ambiri amaona kuti anthu amavomera kukambirana kapena kulandira mabuku athu akakumana nawo m’mapaki, m’misika kapenanso m’malo ena amalonda. Floiran, yemwe ndi woyang’anira dera ku Bolivia anati: “Timakalalikira m’misika ndi malo a malonda pakati pa 1 koloko ndi 3 koloko masana chifukwa nthawi imeneyi ogulitsa malonda sakhala otanganidwa kwambiri. Nthawi zambiri iwo amamvetsera ndipo timayambitsa maphunziro a Baibulo.”

Tikamalalikira m’dera limene anthu ambiri sapezeka pakhomo, tizisintha njira zolalikirira (Onani ndime 10)

10. Kodi n’chiyaninso china chimene tingachite kuti tizitha kulalikira anthu ambiri?

10 Muzisintha njira zolalikirira. Tiyerekeze kuti mwakhala mukuyesetsa kuti mulalikire wina wake. Mwakhala mukupita kunyumba kwake pa nthawi zosiyanasiyana koma simum’peza. Kodi pali zinanso zimene mungachite kuti mumulalikire munthu ameneyu? Katarína ananena kuti, “Anthu amene sindiwapeza panyumba ndimawalembera makalata n’kuwafotokozera zimene ndikanawauza ndikanakumana nawo.” Kodi pamenepa tikuphunzirapo chiyani? Muzigwiritsa ntchito njira zosiyanasiyana zolalikirira kuti mukwanitse kulalikira anthu onse a m’gawo lanu.

TIZISANGALALABE NGAKHALE PAMENE ANTHU SAKUFUNA KUMVETSERA

11. N’chifukwa chiyani anthu ambiri safuna kumvetsera uthenga wathu?

11 Anthu ena sachita chidwi ndi uthenga wathu. Iwo saona kufunika kodziwa Mulungu kapena mfundo za m’Baibulo. Samakhulupirira Mulungu chifukwa amaona mavuto ambiri amene akuchitika m’dzikoli. Iwo safuna kumvetsera uthenga wa m’Baibulo chifukwa cha chinyengo cha atsogoleri a chipembedzo omwe amati amatsatira mfundo za m’Baibulo. Ena amatanganidwa ndi ntchito, kusamalira banja kapenanso kulimbana ndi mavuto awo ndipo amalephera kuzindikira mmene Baibulo lingawathandizire. Ndiye tingatani kuti tizisangalalabe ngati anthu amene timawalalikira saona kufunika kwa uthenga wathu?

12. Kodi mfundo ya pa Afilipi 2:4, ingatithandize bwanji mu utumiki?

12 Muzisonyeza kuti mumawaganizira. Anthu ambiri amene poyamba sankachita chidwi ndi uthenga wabwino anayamba kumvetsera chifukwa choti ofalitsa anasonyeza kuti amawaganizira. (Werengani Afilipi 2:4.) Mwachitsanzo, David yemwe tamutchula kale uja anati, “Ngati munthu wina wanena kuti sakufuna tikambirane naye timaika Baibulo ndi mabuku athu m’chikwama n’kumuuza kuti: ‘Tingakonde kudziwa chifukwa chake simukufuna kuti tikambirane.’” Anthu amatha kudziwa ngati tasonyeza kuti timawaganizira. Akhoza kuiwala zimene tanena, koma sangaiwale zimene tinachita posonyeza kuti timawaganizira. Ngakhale mwininyumba asatilole kuti tilankhule naye, zochita komanso nkhope yathu zingasonyeze kuti timamuganizira.

13. Kodi tingasinthe bwanji uthenga wathu kuti uzigwirizana ndi eni nyumba?

13 Timasonyeza kuti timaganizira ena tikamasintha uthenga wathu kuti ugwirizane ndi eni nyumba. Mwachitsanzo, kodi pali chinachake chimene chikusonyeza kuti pakhomopo pali ana? Ngati zili choncho mwina makolowo angasangalale kudziwa malangizo a m’Baibulo okhudza kulera ana kapena mfundo zothandiza kukhala ndi banja losangalala. Kodi pachitseko cha mwininyumbayo pali maloko angapo? Ngati ndi choncho mwina mungakambirane naye zokhudza uchigawenga komanso mantha amene anthu ambiri ali nawo m’dzikoli, ndipo mwininyumbayo angasangalale kudziwa kuti zimenezi zidzatha. Mulimonse mmene zingakhalire, tizithandiza anthu amene akufuna kumvetsera uthenga wathu kudziwa mmene malangizo a m’Baibulo angawathandizire. Katarína yemwe tamutchula kale uja ananena kuti, “Nthawi zonse ndimaganizira mmene mfundo za m’Baibulo zandithandizira pa moyo wanga.” Zimenezi zimamuthandiza Katarína kuti azilankhula mochokera pansi pamtima ndipo anthu amatha kuona kuti iye amakhulupirira kwambiri zimene akufotokozazo.

14. Mogwirizana ndi Miyambo 27:17, kodi ofalitsa angathandizane bwanji akamalalikira?

14 Muzilola kuti ena akuthandizeni. Mu nthawi ya Atumwi, Paulo anaphunzitsa Timoteyo mmene angalalikirire komanso kuphunzitsa ndipo anamulimbikitsa kuti aziphunzitsanso ena zimenezo. (1 Akor. 4:17) Mofanana ndi Timoteyo, ifenso tingaphunzire zambiri kwa ena amene ali ndi luso mumpingo. (Werengani Miyambo 27:17.) Taganizirani chitsanzo cha m’bale wina dzina lake Shawn. Kwa kanthawi iye anachita upainiya m’dera lina lakumudzi kumene anthu ambiri ankakonda kwambiri chipembedzo chawo. Ndiye kodi n’chiyani chinamuthandiza kuti azisangalala ndi utumiki wake? Iye anati, “Ndinkayesetsa kuti ndikamalalikira ndikhale ndi munthu wina ndipo tikamachoka nyumba ina kupita nyumba ina tinkakambirana zimene tingachite kuti tiwonjezere luso lathu lophunzitsa. Mwachitsanzo, tinkakambirana zimene tachita pakhomo limene tangomaliza kulalikira n’kuona zomwe tingachite ngati titakumananso ndi zomwe takumana nazo pakhomo limenelo.”

15. N’chifukwa chiyani pemphero lili lofunika kwambiri?

15 Muzipempha Yehova kuti akuthandizeni. Muzipempha Yehova kuti akuthandizeni pa nthawi iliyonse imene mukugwira ntchito yolalikira. Tikutero chifukwa popanda kuthandizidwa ndi mzimu wake womwe ndi wamphamvu, sitingakwanitse kugwira ntchitoyi. (Sal. 127:1; Luka 11:13) Mukamapemphera kwa Yehova, muzitchula zenizeni zimene mukufuna kuti akuthandizeni. Mwachitsanzo, mungamupemphe kuti akutsogolereni kwa anthu oyenerera omwe akufuna kumvetsera. Kenako muzichita zinthu mogwirizana ndi pemphero lanu polalikira kwa aliyense amene mwakumana naye.

16. Kodi kuphunzira Baibulo patokha kungatithandize bwanji pa ntchito yathu yolalikira?

16 Muzikhala ndi nthawi yophunzira Baibulo panokha. Mawu a Mulungu amati: “Muzindikire chimene chili chifuniro cha Mulungu, chabwino, chovomerezeka ndi changwiro.” (Aroma 12:2) Tikamaphunzira m’pamene timamudziwa bwino Mulungu, ndipo tikamauza ena zokhudza Mulunguyo, iwo amatha kuoneratu kuti tikukhulupirira kwambiri zimene tikuwauza. Katarína yemwe tamutchula uja ananena kuti: “Nthawi ina mbuyomu ndinazindikira kuti ndifunika kuwonjezera chikhulupiriro changa pamfundo zina za m’Baibulo. Choncho ndinayamba kuphunzira mwakhama kuti ndipeze umboni woti kuli Mlengi, Baibulo ndi Mawu a Mulungu komanso kuti Mulungu ali ndi gulu padzikoli.” Katarína ananena kuti kuphunzira Baibulo payekha kwalimbitsa chikhulupiriro chake ndipo kwamuthandiza kuti azisangalala akakhala mu utumiki.

CHIFUKWA CHAKE TIYENERA KUPITIRIZA KUONA MOYENERA UTUMIKI WATHU

17. N’chiyani chinathandiza Yesu kuti apitirizebe kukhala ndi maganizo oyenera pa ntchito yolalikira?

17 Yesu anapitirizabe kugwira ntchito yolalikira ngakhale kuti anthu ena sankafuna kumvetsera uthenga wake. Iye anachita zimenezi chifukwa ankadziwa kuti anthu afunika kudziwa choonadi ndipo anali wofunitsitsa kuthandiza anthu ambiri kuti amve uthenga wa Ufumu. Ankadziwanso kuti anthu ena omwe poyamba sankafuna kumvetsera adzasintha. Chitsanzo ndi zimene zinachitika ndi anthu a m’banja lake. Pa zaka zitatu zimene Yesu anachita utumiki wake, palibe m’bale wake aliyense amene anakhala wophunzira wake. (Yoh. 7:5) Koma iye ataukitsidwa abale akewo anakhala Akhristu.​—Mac. 1:14.

18. N’chifukwa chiyani timapitirizabe kulalikira?

18 Sitingadziwiretu amene angadzakhale atumiki a Yehova. Anthu ena angatenge nthawi yaitali kuti aphunzire choonadi kusiyana ndi ena. Ngakhale anthu amene sakufuna kumvetsera uthenga wathu amaona zimene timachita komanso makhalidwe athu abwino, ndipo kenako angayambe “kutamanda Mulungu.”​—1 Pet. 2:12.

19. Mogwirizana ndi 1 Akorinto 3:6, 7, kodi tiyenera kukumbukira chiyani?

19 Tikamadzala komanso kuthirira mbewu za choonadi, tisamaiwale kuti Mulungu ndi amene amakulitsa. (Werengani 1 Akorinto 3:6, 7.) M’bale wina yemwe amatumikira ku Ethiopia, dzina lake Getahun, ananena kuti: “Kwa zaka zoposa 20 wa Mboni ndinalipo ndekha m’dera lina lomwe silinkalalikidwa kawirikawiri. Koma panopa kuli ofalitsa 14 ndipo 13 ndi obatizidwa kuphatikizapo mkazi ndi ana anga. Ndipo pamsonkhano uliwonse pamapezeka anthu pafupifupi 32.” Getahun amasangalala kuti anapitirizabe kulalikira komanso kudikira moleza mtima kuti Yehova akokere m’gulu lake anthu a mtima wabwino.​—Yoh. 6:44.

20. Kodi timafanana bwanji ndi ogwira ntchito yopulumutsa anthu?

20 Yehova amaona kuti moyo wa munthu aliyense ndi wamtengo wapatali. Iye watipatsa mwayi wogwira ntchito ndi Mwana wake posonkhanitsa anthu kuchokera m’mitundu yonse mapeto asanafike. (Hag. 2:7) Ntchito yathu yolalikira tingaiyerekezere ndi ntchito yopulumutsa anthu. Timakhala ngati tikugwira ntchito yopulumutsa anthu omwe akwiririka mumgodi. Ngakhale kuti pangapezeke opulumuka ochepa kwambiri, onse m’gulu la opulumutsa anthulo amakhala kuti agwira ntchito yofunika kwambiri. Zimenezi ndi zofanana ndi zimene timachita pa ntchito yathu yolalikira. Sitingadziwe kuti ndi anthu angati amene tingawapulumutse m’dziko loipa la Satanali, koma Yehova akhoza kugwiritsa ntchito aliyense wa ife powathandiza. Andreas yemwe amakhala ku Bolivia ananena kuti, “Ndimaona kuti munthu akaphunzira Baibulo mpaka kubatizidwa, zimakhala kuti ndi khama la anthu ambiri osati munthu mmodzi.” Choncho tiyeni ifenso tizikhala ndi maganizo ngati amenewa pa ntchito yathu yolalikira. Tikamachita zimenezi, Yehova adzatidalitsa ndipo tizisangalala kwambiri ndi ntchito yathu yolalikira.

NYIMBO NA. 66 Lengezani Uthenga Wabwino

^ ndime 5 Kodi tingatani kuti tizionabe utumiki wathu moyenera ngakhale pamene anthu ambiri sapezeka pakhomo kapenanso sasangalala ndi uthenga wathu? Nkhaniyi itithandiza kudziwa zimene tingachite kuti tizisangalalabe pamene tikugwira ntchito yolalikira.

^ ndime 7 Ofalitsa ayenera kugwiritsa ntchito njira zosiyanasiyana zolalikirira zomwe zafotokozedwa munkhaniyi mogwirizana ndi malamulo a m’dziko lawo okhudza kusunga chinsinsi cha anthu ena.

^ ndime 60 MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI: (Kuchokera pamwamba mpaka pansi): M’bale ndi mkazi wake akulalikira m’dera limene ndi zovuta kupeza anthu panyumba. Khomo loyamba mwiniwake wapita ku ntchito, wa khomo lachiwiri wapita kuchipatala ndipo wa khomo lachitatu wapita kukagula zinthu. Kenako akwanitsa kulalikira kwa munthu wa khomo loyamba uja atapitako pa nthawi ina pa tsikulo. Munthu wa khomo lachiwiri uja akumana naye pamene akulalikira m’malo opezeka anthu ambiri pafupi ndi chipatala. Ndipo akulalikira munthu wa khomo lachitatu lija pomuimbira foni.