Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 22

Muzithandiza Wophunzira Baibulo Kuti Abatizidwe

Muzithandiza Wophunzira Baibulo Kuti Abatizidwe

“Aliyense wa inu abatizidwe.”​—MAC. 2:38.

NYIMBO NA. 72 Tikulalikira Choonadi Chonena za Ufumu

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1. Kodi anthu omwe anasonkhana ku Yerusalemu anauzidwa kuti achite chiyani?

GULU lalikulu la amuna ndi akazi ochokera m’mayiko ambiri komanso olankhula zinenero zosiyanasiyana linasonkhana ku Yerusalemu. Pa tsiku limeneli panachitika chinthu china chapadera. Ayuda ena anayamba kulankhula zinenero za alendo ochokera m’mayiko enawo. Zimenezi zinali zodabwitsa, koma zimene Ayudawo komanso mtumwi Petulo analankhula ndi zomwe zinali zapadera kwambiri. Unali uthenga wonena kuti anthuwo angapulumutsidwe ngati atakhulupirira Yesu Khristu. Uthengawo unawafika pamtima anthuwo. Iwo anakhudzidwa kwambiri moti anafunsa kuti: “Tichite chiyani pamenepa?” Poyankha Petulo anawauza kuti: “Aliyense wa inu abatizidwe.”​—Mac. 2:37, 38.

M’bale ndi mkazi wake akuphunzira Baibulo ndi wachinyamata wina ndipo akugwiritsa ntchito buku lakuti Mungakhale ndi Moyo Mpaka Kalekale (Onani ndime 2)

2. Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi? (Onani chithunzi chapachikuto.)

2 Zimene zinachitika pambuyo pake zinali zodabwitsa. Anthu pafupifupi 3000 anabatizidwa tsiku limeneli n’kukhala ophunzira a Khristu. Ichi chinali chiyambi cha ntchito yaikulu yophunzitsa anthu imene Yesu analamula otsatira ake kuti azigwira. Ntchito imeneyi yakhala ikuchitika mpaka m’nthawi yathu ino. Koma masiku ano sitingaphunzitse munthu n’kubatizidwa tsiku lomwelo. Zikhoza kutenga miyezi, chaka kapenanso kuposa, kuti munthu afike pobatizidwa. Ngati mukuphunzira Baibulo ndi winawake mungavomereze kuti ntchito yophunzitsa munthu imafunika khama. Munkhaniyi tikambirana mmene tingathandizire wophunzira Baibulo kuti afike pobatizidwa.

MUZITHANDIZA WOPHUNZIRA BAIBULO KUTI AZIGWIRITSA NTCHITO ZIMENE AKUPHUNZIRA

3. Mogwirizana ndi Mateyu 28:19, 20, kodi wophunzira Baibulo ayenera kuchita chiyani kuti afike pobatizidwa?

3 Wophunzira Baibulo asanabatizidwe, ayenera kumagwiritsa ntchito zimene amaphunzira. (Werengani Mateyu 28:19, 20.) Akamachita zimenezi angafanane ndi “munthu wochenjera” wa m’fanizo la Yesu, yemwe anakumba kwambiri pansi kuti amange nyumba yake pathanthwe. (Mat. 7:24, 25; Luka 6:47, 48) Ndiye kodi tingathandize bwanji wophunzira Baibulo kuti azigwiritsa ntchito zimene akuphunzira. Tiyeni tikambirane zinthu zitatu zimene tingachite.

4. Kodi tingathandize bwanji wophunzira Baibulo kupita patsogolo mpaka kufika pobatizidwa? (Onaninso bokosi lakuti “Muzithandiza Wophunzira Wanu Kukhala ndi Zolinga Komanso Kuzikwaniritsa.”)

4 Muzithandiza wophunzira wanu kuti azikhala ndi zolinga. N’chifukwa chiyani muyenera kuchita zimenezi? Taganizirani izi: Ngati mukuyenda pa ulendo wautali, mumatha kuima pamalo ena osangalatsa kuti mupume. Zimenezo zingakuthandizeni kuti musaone kutalika ulendowo. Mofanana ndi zimenezi, wophunzira Baibulo akamakhala ndi zolinga zing’onozing’ono n’kumazikwaniritsa angazindikire kuti akhoza kukwaniritsa cholinga chake chofuna kubatizidwa. Mungagwiritse ntchito tizigawo takuti “Zolinga” m’buku lakuti, Mungakhale ndi Moyo Mpaka Kalekale pothandiza wophunzira wanu. Pa mapeto pa phunziro lililonse, muzikambirana ndi wophunzirayo kugwirizana kumene kulipo pakati pa zolinga zimene zatchulidwa ndi zimene waphunzira. Ngati mukuganizira zolinga zina zimene mukufuna wophunzira wanu azikwaniritse, mungalembe pa kagawo kakuti “Zina.” Nthawi zambiri muzigwiritsa ntchito kagawo kameneka pokambirana ndi wophunzira wanu zolinga zimene angazikwaniritse kwa nthawi yochepa kapena kwa nthawi yaitali.

5. Pa Maliko 10:17-22, kodi Yesu anauza munthu wina wolemera kuti achite chiyani, nanga n’chifukwa chiyani?

5 Muzithandiza wophunzira wanu kusintha zinthu pa moyo wake. (Werengani Maliko 10:17-22.) Yesu ankadziwa kuti zikanakhala zovuta kuti munthu wina wolemera agulitse zinthu zake zonse. (Maliko 10:23) Komabe iye anamuuza kuti achite zimenezi ngakhale kuti kunali kusintha kwakukulu pa moyo wake. Yesu anamuuza izi chifukwa ankamukonda kwambiri. Nthawi zina tingalephere kulimbikitsa wophunzira wathu kuti asinthe zinthu zina pa moyo wake poganiza kuti sanakonzeke kuchita zimenezi. Zingatenge nthawi yaitali kuti anthu ena asiye zimene anazolowera n’kuvala umunthu watsopano. (Akol. 3:9, 10) Koma mukakambirana naye mofulumira zinthu zimene afunika kusintha, wophunzirayo amayambanso kusintha mofulumira. Mukamakambirana naye nkhani ngati zimenezi mumasonyeza kuti mumamuganizira.​—Sal. 141:5; Miy. 27:17.

6. N’chifukwa chiyani tiyenera kugwiritsa ntchito mafunso othandiza munthu kufotokoza maganizo ake?

6 N’zofunika kuti tizifunsa wophunzira wathu mafunso omuthandiza kufotokoza maganizo ake pa nkhani inayake. Muzifunsa mafunso oterewa kuti muzidziwa zimene wophunzira wanu amadziwa komanso kukhulupirira. Mukamachita zimenezi kawirikawiri zidzakhala zosavuta kuti m’tsogolo mudzathe kukambirana naye nkhani zimene n’zovuta kuti azivomereze. Mu buku la Mungakhale ndi Moyo Mpaka Kalekale, muli mafunso ambiri angati amenewa. Mwachitsanzo, m’phunziro 04 muli funso lakuti: “Ndiye mukuona kuti Yehova amamva bwanji mukamagwiritsa ntchito dzina lake?” M’phunziro 09 muli funso lakuti: “Tchulani zinthu zina zimene mungakonde kupempherera.” Poyamba wophunzira wanu angamatenge nthawi yaitali kuti ayankhe mafunso amenewa. Mungamuthandize kuti aziganiza pogwiritsa ntchito zithunzi komanso Malemba.

7. Kodi tingagwiritse ntchito bwanji nkhani zimene zinachitikira anthu ena kuti tiziphunzitsa mogwira mtima?

7 Wophunzira wanu akamvetsa zimene ayenera kuchita, muzigwiritsa ntchito nkhani zofotokoza zimene zinachitikira anthu ena pomulimbikitsa kuti azichita zimene waphunzira. Mwachitsanzo, ngati wophunzira wanu zimamuvuta kupezeka pamisonkhano mungamuonetse vidiyo yakuti Yehova Anandisamalira, yomwe ili pa kagawo kakuti “Onani Zinanso,” muphunziro 14. M’mitu yambiri m’buku lakuti Mungakhale ndi Moyo Mpaka Kalekale, mungapeze zitsanzo za zimene zinachitikira anthu ena pa kagawo kakuti “Fufuzani Mozama,” komanso kakuti “Onani Zinanso.” * Muzisamala kuti musamayerekezere wophunzira wanu ndi anthu ena pomuuza kuti, “Ngati uyu anakwanitsa ndiye kuti inunso mungakwanitse.” Muzilola wophunzira wanu kuti aziona yekha zimenezo. Inuyo muzingokambirana naye mfundo zimene zinathandiza munthu amene watchulidwa muvidiyoyo. Mwina mungatchule lemba kapena zinthu zina zimene zinamuthandiza. Ndipo ngati n’zotheka muzifotokoza mmene Yehova anathandizira munthuyo.

8. Kodi tingathandize bwanji wophunzira wathu kuti ayambe kukonda Yehova?

8 Muzithandiza wophunzira wanu kuti ayambe kukonda Yehova. Kodi mungachite bwanji zimenezi? Mukamaphunzira naye muziyesetsa kupeza mipata yomuthandiza kudziwa makhalidwe a Yehova. Muzimuthandiza kuona kuti Yehova ndi Mulungu wachimwemwe amene amathandiza anthu omwe amamukonda. (1 Tim. 1:11; Aheb. 11:6) Muzimufotokozera kuti zinthu zingamuyendere bwino kwambiri akamagwiritsa ntchito zimene akuphunzirazo, ndipo muzimuuza kuti umenewo ndi umboni woti Yehova amamukonda. (Yes. 48:17, 18) Wophunzirayo akamakonda kwambiri Yehova m’pamene angathe kusintha zinthu pa moyo wake.​—1 Yoh. 5:3.

MUZITHANDIZA WOPHUNZIRA KUTI ADZIWANE NDI A MBONI ENA

9. Mogwirizana ndi Maliko 10:29, 30, kodi n’chiyani chingathandize wophunzira Baibulo kuti asiye zinthu zina n’cholinga choti abatizidwe?

9 Kuti afike pobatizidwa, wophunzira Baibulo ayenera kudzimana zinthu zambiri. Mofanana ndi munthu wachuma tamutchula kale uja, ophunzira ena amafunika kusiya zinthu zina zomwe ali nazo. Mwachitsanzo, ngati ntchito imene amagwira ikusemphana ndi mfundo za m’Baibulo, iwo angafunike kupeza ntchito ina. Ambiri amafunika kusiya kucheza ndi anzawo omwe sakonda Yehova. Enanso angakanidwe ndi achibale awo omwe sasangalala ndi a Mboni za Yehova. Yesu ananena kuti kwa ena zingakhale zovuta kudzimana pa zinthu ngati zimenezi. Koma iye analonjeza kuti anthu amene angamutsatire sadzanong’oneza bondo. M’malomwake Yehova adzawapatsa abale ndi alongo, omwe adzakhale ngati banja lawo. (Werengani Maliko 10:29, 30.) Ndiye kodi mungathandize bwanji wophunzira Baibulo wanu kuti apeze mphatso yamtengo wapataliyi?

10. Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene Manuel ananena?

10 Muzimupanga wophunzira Baibulo kuti akhale mnzanu. N’zofunika kuti muzimusonyeza wophunzira wanu kuti mumamuganizira. N’chifukwa chiyani tikutero? Taonani zimene Manuel yemwe amakhala ku Mexico ananena. Pokumbukira zimene zinkachitika pamene ankaphunzira Baibulo iye anati: “Nthawi zonse tisanayambe kuphunzira, mphunzitsi wanga ankandifunsa kuti adziwe mmene zinthu zili pa moyo wanga. Ankandithandiza kuti ndizimasuka kukambirana naye nkhani zosiyanasiyana. Ndinkachita kuoneratu kuti amandiganizira.”

11. Kodi ophunzira Baibulo angapindule bwanji tikamapeza nthawi yocheza nawo?

11 Muzipeza nthawi yocheza ndi ophunzira anu ngati mmene Yesu ankachitira. (Yoh. 3:22) Ngati n’zoyenera, muziitanira kunyumba kwanu wophunzira Baibulo amene akupita patsogolo kuti mudzamwe naye tiyi, kudya chakudya kapena kuonera pulogalamu ya mwezi ndi mwezi ya JW Broadcasting. Ndipotu ngati kukuchitika maholide kapena zikondwerero zomwe wophunzira wanu sangapange nawo, iye angayamikire ngati mutamuitanira kunyumba kwanu. Kazibwe, yemwe amakhala ku Uganda ananena kuti: “Ndimaona kuti ndinkaphunzira zambiri zokhudza Yehova ndikamacheza ndi mphunzitsi wanga mofanana ndi mmene zinkakhalira akamandiphunzitsa Baibulo. Ndinkaona mmene Yehova amasamalira anthu ake komanso mmene ankasangalalira. Zimenezi ndi zomwe inenso ndinkafuna.”

Mukamapita ndi ofalitsa osiyanasiyana kuphunziro la Baibulo, wophunzirayo sizimuvuta kuti ayambe kufika pamisonkhano (Onani ndime 12) *

12. N’chifukwa chiyani tiyenera kumapita ndi ofalitsa osiyanasiyana kuphunziro la Baibulo?

12 Muzitenga ofalitsa osiyanasiyana mukamapita kuphunziro lanu la Baibulo. Mwina nthawi zina tikhoza kuganiza zomangopita tokha kuphunziro lathu la Baibulo kapena kumangopita ndi wofalitsa yemwe yemweyo. Ngakhale kuti kuchita zimenezi si kolakwika, wophunzira wathu angapindule kwambiri ngati titamapitako ndi ofalitsa osiyanasiyana. Dmitrii, yemwe amakhala ku Moldova ananena kuti: “Wofalitsa aliyense amene ankabwera ndi mphunzitsi wanga ankafotokoza zinthu m’njira yosiyana. Izi zinandithandiza kuona njira zosiyanasiyana za mmene ndingagwiritsire ntchito zomwe ndikuphunzira. Komanso popeza ndinali nditadziwana kale ndi abale ndi alongo ambiri, nditafika koyamba pamisonkhano sindinkachita manyazi.”

13. N’chifukwa chiyani tiyenera kuthandiza wophunzira wathu kuti ayambe kusonkhana?

13 Muzithandiza wophunzira Baibulo kuti azipezeka pamisonkhano. N’chifukwa chiyani muyenera kuchita zimenezi? Chifukwa Yehova amafuna kuti olambira ake azisonkhana pamodzi, ndipo imeneyi ndi mbali ya kulambira kwathu. (Aheb. 10:24, 25) Kuwonjezera pamenepo, abale ndi alongo ali ngati anthu a m’banja lathu. Choncho tikakhala nawo pamisonkhano zimakhala ngati tili kunyumba ndipo tikudyera limodzi chakudya chokoma. Mukamalimbikitsa wophunzira wanu kuti azipezeka pamisonkhano, mumakhala mukumuthandiza kuchita chinthu chofunika kwambiri kuti abatizidwe. Koma mwina zingakhale zovuta kuti wophunzirayo ayambe kusonkhana. Ndiye kodi buku la Mungakhale ndi Moyo Mpaka Kalekale, lingamuthandize bwanji kulimbana ndi mavuto amene angamulepheretse kusonkhana?

14. Kodi tingalimbikitse bwanji wophunzira Baibulo kuti azipezeka pamisonkhano?

14 Muzigwiritsa ntchito phunziro 10 mu buku la Mungakhale ndi Moyo Mpaka Kalekale polimbikitsa wophunzira wanu kuti azipezeka pamisonkhano. Bukuli lisanatulutsidwe, ofalitsa ena aluso anapemphedwa kugwiritsa ntchito phunziroli polimbikitsa ophunzira awo kuti azipezeka pamisonkhano ndipo anaona kuti ndi lothandizadi. Komabe simuyenera kudikira mpaka mutafika phunziro 10 kuti muitanire wophunzira Baibulo kumisonkhano. Ngati n’zotheka, muzimuitanira kumisonkhano mukangoyamba kuphunzira naye ndipo muzichita zimenezi nthawi zonse. Dziwani kuti anthu amene akuphunzira Baibulo sakumana ndi mavuto ofanana. Choncho muzikhala tcheru kuti muziona zimene wophunzira wanu akukumana nazo ndipo muziganizira mmene mungamuthandizire. Musamataye mtima ngati pakutenga nthawi kuti wophunzira wanu ayambe kufika kumisonkhano. M’malomwake muzileza mtima ndipo musamasiye kumuitanira kumisonkhanoko.

MUZITHANDIZA WOPHUNZIRA BAIBULO WANU KUTI ASAMACHITE MANTHA

15. Kodi wophunzira Baibulo wathu akhoza kumachita mantha ndi zinthu ziti?

15 Kodi mumakumbukira nthawi imene munkachita mantha kuti mukhale wa Mboni za Yehova? Mwina munkaona kuti simungakwanitse kumagwira ntchito yolalikira. Mwinanso munkaopa kuti achibale komanso anzanu azikutsutsani. Ngati ndi choncho, ndiye kuti mungamvetse mmene wophunzira wanu angamvere. Yesu anavomereza kuti n’zotheka kuti munthu aziopa zimenezi. Komabe iye analimbikitsa otsatira ake kuti asamalole kuti mantha awalepheretse kutumikira Yehova. (Mat. 10:16, 17, 27, 28) Ndiye kodi Yesu anawathandiza bwanji, nanga tingatani kuti timutsanzire?

16. Kodi tingathandize bwanji wophunzira Baibulo wathu kuti aziuza ena zimene amakhulupirira?

16 Nthawi zonse muziphunzitsa wophunzira wanu mmene angafotokozere kwa ena zimene amakhulupirira. Ophunzira a Yesu ayenera kuti ankachita mantha iye atawatumiza kuti akalalikire. Koma Yesu anawathandiza powauza uthenga komanso malo oti akalalikire. (Mat. 10:5-7) Ndiye kodi tingamutsanzire bwanji Yesu? Tizithandiza wophunzira wathu kudziwa anthu amene angawalalikire. Mwachitsanzo, mungamufunse ngati akudziwa munthu wina amene mfundo inayake ya m’Baibulo ingamuthandize. Kenako mungamuthandize kukonzekera komanso kumusonyeza mmene angafotokozere zimenezo mosavuta. Mungamuthandize pogwiritsa ntchito tizigawo takuti “Zimene Ena Amanena,” komanso “Munthu Wina Angafunse Kuti,” tomwe tili m’buku lakuti Mungakhale ndi Moyo Mpaka Kalekale. Mukamachita zimenezi, muzimuphunzitsa mmene angagwiritsire ntchito Baibulo popereka mayankho mwaluso komanso mosavuta.

17. Pothandiza wophunzira wathu kuti azidalira Yehova, kodi tingagwiritse ntchito bwanji lemba la Mateyu 10:19, 20, 29-31?

17 Muzithandiza wophunzira Baibulo wanu kuti azidalira Yehova. Yesu anatsimikizira ophunzira ake kuti Yehova adzawathandiza chifukwa amawakonda. (Werengani Mateyu 10:19, 20, 29-31.) Muzikumbutsa wophunzira wanu kuti nayenso Yehova azimuthandiza. Mungamuthandize kuti azidalira Yehova mukamatchula zolinga zake pamene mukupemphera naye. Franciszek, yemwe amakhala ku Poland ananena kuti: “Mphunzitsi wanga ankatchula zolinga zanga akamapemphera nane. Nditaona mmene Yehova ankayankhira mapemphero a mphunzitsi wangayo, mwamsanga inenso ndinayamba kumapemphera. Ndinaona kuti Yehova anandithandiza pamene ndinkapempha nthawi kuntchito imene ndinali nditangoyamba kumene, kuti ndikachite nawo msonkhano wachigawo komanso ndizipezeka pamisonkhano ya mpingo.”

18. Kodi Yehova amamva bwanji akaona Akhristu akuchita khama kuphunzitsa ena?

18 Yehova amakonda kwambiri anthu amene timaphunzira nawo Baibulo. Amakondanso kwambiri Akhristu amene amachita khama kuphunzitsa ena kuti akhale naye pa ubwenzi ndipo amawayamikira chifukwa cha zimenezi. (Yes. 52:7) Ngati panopa simukuchititsa phunziro la Baibulo, mungathandizebe ophunzira Baibulo kupita patsogolo mpaka kufika pobatizidwa popita ndi ofalitsa ena kumaphunziro awo.

NYIMBO NA. 60 Akamvera Adzapeza Moyo

^ ndime 5 Munkhaniyi tikambirana mmene Yesu anathandizira anthu kuti akhale ophunzira ake komanso zimene tingachite kuti timutsanzire. Tikambirananso zinthu zina zimene zili m’buku latsopano lakuti, Mungakhale ndi Moyo Mpaka Kalekale. Bukuli lakonzedwa kuti lizithandiza ophunzira Baibulo kupita patsogolo mpaka kufika pobatizidwa.

^ ndime 7 Mungapezenso nkhani zokhudza zochitika pa moyo wa anthu ena (1) mu Buku la Mboni za Yehova Lofufuzira Nkhani pa mutu wakuti “Baibulo,” “Lothandiza,” kenako “‘Baibulo Limasintha Anthu” (Nkhani za mu Nsanja ya Olonda)” komanso (2) pa JW Library® pa gawo la “Media,” pachigawo chakuti “Zochitika pa Moyo wa Anthu Ena.”

^ ndime 62 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: M’bale ndi mkazi wake akuphunzira Baibulo ndi wachinyamata wina. Pamaulendo ena wapita kuphunzirolo ndi abale ena.