Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 22

Thandizani Maphunzilo Anu a Baibo Kuti Akakhale Ophunzila Obatizika

Thandizani Maphunzilo Anu a Baibo Kuti Akakhale Ophunzila Obatizika

“Aliyense wa inu abatizidwe.”—MAC 2:38.

NYIMBO 72 Tilalikile Coonadi ca Ufumu

ZIMENE TIKAMBILANE *

1. M’zaka za zana loyamba, kodi namtindi wa anthu unauzidwa kucita ciani?

NAMTINDI wa anthu, amuna na akazi ocokela ku maiko osiyana-siyana, komanso okamba zinenelo zosiyana-siyana anasonkhana pamodzi. Pa tsikulo, panacitika zocititsa cidwi. Kagulu ka Ayuda wamba kanali kutha kulankhula zinenelo za alendo ocokela ku maiko ena. Zimenezi zinali zocititsadi cidwi. Koma zimene Ayudawo anauza anthuwo, ndiponso zimene mtumwi Petulo anauza anthu onse, n’zimene zinali zocititsa cidwi kwambili. Anthuwo anauzidwa kuti akhoza kupulumuka mwa kukhulupilila Yesu Khristu. Iwo anakhudzika mtima kwambili na uthengawo moti anafunsa kuti: “Ticite ciani?” Poyankha Petulo anawauza kuti: “Aliyense wa inu abatizidwe.”—Mac. 2:37, 38.

M’bale na mkazi wake akuseŵenzetsa buku lakuti, ‘Kondwelani na Moyo kwamuyaya!’ potsogoza phunzilo la Baibo kwa wacinyamat (Onani ndime 2)

2. Tikambilane ciani m’nkhani ino? (Onani cithunzi pacikuto)

2 Zimene zinatsatilapo zinali zocititsa cidwi koposa. Anthu pafupi-fupi 3,000 anabatizika pa tsikulo, ndipo anakhala ophunzila a Khristu. Ici cinali ciyambi ca nchito yaikulu yopanga ophunzila, imene Yesu analamula otsatila ake kuigwila. Nchitoyo imacitikabe mpaka pano. Masiku ano, n’zosatheka kuthandiza munthu kuti abatizike m’maola ocepa cabe. Pamapita miyezi kapena caka, ngakhale kuposapo, kuti wophunzila afike pobatizika. Ngati mumaphunzitsa munthu wina Baibo pali pano, mungavomeleze kuti nchito yopanga ophunzila imafuna kulimbikila. M’nkhani ino, tikambilane mmene mungathandizile wophunzila Baibo wanu kuti akakhale wophunzila wobatizika.

THANDIZANI WOPHUNZILA BAIBO WANU KUSEŴENZETSA ZIMENE AMAPHUNZILA

3. Malinga na mmene Mateyu 28:19, 20 ionetsela, kodi wophunzila ayenela kucita ciani kuti apite patsogolo mpaka kukabatizika?

3 Wophunzila Baibo asanabatizike, ayenela kuseŵenzetsa zimene Baibo imaphunzitsa. (Ŵelengani Mateyu 28:19, 20.) Ngati wophunzila aseŵenzetsa zimene amaphunzila, amafanana na “munthu wocenjela” wa m’fanizo la Yesu amene anakumba mozama kwambili kuti amange nyumba yake pa thanthwe. (Mat. 7:24, 25; Luka 6:47, 48) Tingacite ciani kuti tithandize wophunzila kuseŵenzetsa zimene amaphunzila? Tiyeni tikambilane zinthu zitatu.

4. Tingam’thandize bwanji wophunzila kuti mwa pang’ono-m’pang’ono akayenelele ubatizo? (Onaninso bokosi lakuti “ Thandizani Wophunzila Wanu Kudziikila Zolinga na Kuzikwanilitsa.”)

4 Thandizani wophunzila wanu kudziikila zolinga. N’cifukwa ciani muyenela kucita zimenezi? Ganizilani citsanzo ici: Ngati mwakonza zopita kwina kwake kutali na motoka yanu, mwina mungasankhiletu malo ocititsa cidwi amene mudzaimapo pa ulendowo. Mukatelo, ulendo wanu wautaliwo siudzakhala wolemetsa kwambili. Mofananamo, wophunzila Baibo akadziikila zolinga zing’ono-zing’ono na kuzikwanilitsa, cidzakhala cosavuta kwa iye kuona kuti n’zotheka kukwanilitsa colinga ca kubatizika. Seŵenzetsani mbali yakuti “Zocita” m’buku lakuti Kondwelani na Moyo Kwamuyaya! pothandiza wophunzila wanu kupita patsogolo. Mukatsiliza phunzilo lililonse, kambilanani mmene colingaco cigwilizanila na zimene wophunzila wanu wangophunzila kumene. Ngati muli na colinga cina m’maganizo cimene mufuna kuti wophunzila wanu acikwanilitse, cilembeni pa mbali yakuti “Kapena.” Muziseŵenzetsa mbali imeneyi ya phunzilo pokambilana na wophunzila wanu zolinga zake zing’ono-zing’ono, komanso zikulu-zikulu.

5. Malinga na Maliko 10:17-22, kodi Yesu anauza munthu wacuma kucita ciani Ndipo cifukwa ciani?

5 Thandizani wophunzila wanu kupanga masinthidwe mu umoyo wake. (Ŵelengani Maliko 10:17-22.) Yesu anadziŵa kuti zidzakhala zovuta kwa munthu wacuma kugulitsa zinthu zake zonse. (Maliko 10:23) Ngakhale n’telo, iye anauza munthu wacuma kuti apange masinthidwe aakulu mu umoyo wake. Cifukwa ciani? Cifukwa Yesu anam’konda munthuyo. Nthawi zina tingazengeleze kulimbikitsa wophunzila kuseŵenzetsa zimene amaphunzila, cifukwa coganiza kuti si wokonzeka kupanga masinthidwe ofunikila. Pangapite nthawi yaitali kuti munthu avule umunthu wake wakale, na kuvala umunthu watsopano. (Akol. 3:9, 10) Koma kukambilana mwamsanga, komanso momasuka za masinthidwe amene wophunzilayo ayenela kupanga, kudzam’thandizanso kuyamba kupanga masinthidwe amenewo mwamsanga. Mwa kukhala na makambilano otelo, mudzaonetsa kuti mumasamala za iye.—Sal. 141:5; Miy. 27:17.

6. N’cifukwa ciani tiyenela kuseŵenzetsa mafunso ofuna kudziŵa maganizo a munthu?

6 Timaseŵenzetsa funso lofuna kudziŵa maganizo a munthu pofuna kudziŵa maganizo a wophunzila pa nkhani ina yake. Kuseŵenzetsa mafunso amenewa kudzakuthandizani kudziŵa zimene wophunzila wanu amakhulupilila na kuzimvetsa. Ngati mucita zimenezi nthawi na nthawi, cidzakhala cosavuta kukambilana naye zinthu zimene zingakhale zovuta kwa iye kuzivomeleza. Buku lakuti, Kondwelani na Moyo Kwamuyaya! lili na mafunso ambili ofuna kudziŵa maganizo a munthu. Mwacitsanzo, phunzilo 4 lili na funso lakuti: “Muganiza Yehova amamvela bwanji mukamachula dzina lake?” Phunzilo 9 lili na funso lakuti: “Kodi ni zinthu zina ziti zimene mungafune kupemphelela?” Poyamba, mwina zingamuvute wophunzila wanu kuyankha mafunso ngati amenewa. Mungam’thandize mwa kum’phunzitsa kuganizila pa malemba ndiponso pa zithunzi za m’nkhaniyo.

7. Tingaseŵenzetse bwanji zocitika zeni-zeni mwaluso?

7 Wophunzila wanu akamvetsa zimene ayenela kucita, seŵenzetsani zocitika zeni-zeni pom’limbikitsa kucita zimenezo. Mwacitsanzo, ngati wophunzila wanu sasonkhana mokhazikika mungam’tambitse vidiyo yakuti, Yehova Amanikonda yopezeka pa mbali yakuti “Fufuzani” m’phunzilo 14. Maphunzilo ambili m’buku lakuti, Kondwelani na Moyo Kwamuyaya! ali na zocitika ngati zimenezi pa mbali yakuti “Kumbani Mozamilapo,” kapena pa mbali yakuti “Fufuzani.” * Samalani kuti musayelekezele wophunzila wanu na munthu wina mwa kukamba kuti, “Ngati iye anakwanitsa, inunso mungakwanitse.” Lolani kuti wophunzilayo avomeleze yekha kuti angakwanitse. Kambilanani naye mfundo zimene zinathandiza munthuyo mu vidiyo, kuseŵenzetsa zimene Baibo imaphunzitsa. Mwina mungam’chulile lemba lofunika kapena cina cake cothandiza cimene munthuyo anacita. Ngati n’kotheka, gogomezani mmene Yehova anathandizila munthuyo.

8. Tingam’thandize bwanji wophunzila wathu kuyamba kukonda Yehova?

8 Thandizani wophunzila wanu kuyamba kum’konda Yehova. Motani? Pezani mipata yom’thandiza kuzindikila makhalidwe a Yehova. Thandizani wophunzila wanu kuona Yehova kuti ni Mulungu wacimwemwe, amene amacilikiza anthu omukonda. (1 Tim. 1:11; Aheb. 11:6) Muonetseni wophunzila wanu kuti adzapindula kwambili akamaseŵenzetsa zimene akuphunzila, ndipo mufotokozeleni kuti izi zionetsa cikondi ca Yehova pa iye. (Yes. 48:17, 18) Mukatelo, wophunzila wanu adzasonkhezeledwa kwambili kupanga masinthidwe ofunikila pamene cikondi cake pa Yehova cikula.—1 Yoh. 5:3.

M’DZIŴITSENI WOPHUNZILA WANU KWA ALAMBILI ANZANU

9. Mogwilizana na Maliko 10:29, 30, n’ciani cingathandize munthu kudzimana zinthu zina kuti akhale wophunzila wobatizika?

9 Kuti wophunzila Baibo apite patsogolo mpaka kukabatizika, ayenela kudzimana zinthu zina. Mofanana na munthu wacuma amene tamuchula kumayambililo, ophunzila ena angafunike kudzimana zinthu zina zakuthupi. Ngati nchito yawo siigwilizana na mfundo za m’Baibo, mwina angafunike kusintha nchitoyo. Ambili angafunike kudula mayanjano awo na anzawo amene sakonda Yehova. Ena angakanidwe na a m’banja lawo amene sakonda Mboni za Yehova. Yesu anakamba kuti zingakhale zovuta kwa ena kudzimana mwa njila imeneyi. Koma analonjeza kuti amene amam’tsatila sadzagwilitsidwa mwala. Iwo adzadalitsidwa kwambili mwa kupatsidwa banja lacikondi lauzimu. (Ŵelengani Maliko 10:29, 30.) Kodi mungam’thandize bwanji wophunzila Baibo wanu kupindula na mphatso yabwino imeneyi?

10. Kodi mwaphunzila ciani pa cocitika ca m’bale Manuel?

10 Palanani ubwenzi na wophunzila wanu. N’kofunika kwambili kuonetsa wophunzila wanu kuti mumam’konda. Cifukwa ninji? Onani zimene m’bale Manuel wa ku Mexico anakamba. Pokumbukila nthawi pamene anali kuphunzila Baibo, iye anakamba kuti: “Nthawi zonse tisanayambe kuphunzila, mphunzitsi wanga anali kunifunsa za umoyo wanga. Iye ananithandiza kukhala womasuka, komanso kuti nizikambilana naye nkhani zina. N’nali kucita kuona kuti anali kunideladi nkhawa.”

11. Kodi ophunzila Baibo athu angapindule bwanji ngati ticeza nawo?

11 Muziceza na ophunzila anu, monga mmene Yesu anacitila na otsatila ake. (Yoh. 3:22) Ngati m’poyenela, itanilani wophunzila Baibo wanu wopita patsogolo ku nyumba kwanu, kuti mudzamwe naye thobwa kapena zozizilitsa kukhosi, kapenanso kudya naye cakudya, kapenanso kutamba naye pulogilamu yathu ya pa mwezi ya JW Broadcasting®. Wophunzila wanu angayamikile kwambili ngati ciitano cotele, cingamufike pa nthawi ya chuti pamene mwina angakhale wosungulumwa. M’bale Kazibwe wa ku Uganda anati: “Niona kuti zimene n’naphunzila zokhudza Yehova poceza na mphunzitsi wanga, zinali zoculuka mofanana na zimene n’nali kuphunzila pa phunzilo. N’naona kuti Yehova amawasamalila kwambili anthu ake, ndipo ni acimwemwe. Izi n’zimene n’nali kufuna mu umoyo wanga.”

Pamene mutsogoza phunzilo la Baibo na ofalitsa osiyana-siyana, cidzakhala copepuka kwa wophunzilayo kumapezeka ku misonkhano (Onani ndime 12) *

12. N’cifukwa ciani tiyenela kukhala na ofalitsa osiyana-siyana potsogoza phunzilo la Baibo?

12 Pemphani ofalitsa osiyana-siyana kukhala namwe potsogoza phunzilo la Baibo. Nthawi zina, tingaone kuti pali bwino kupita tekha ku phunzilo kapena na wofalitsa mmodzimodzi nthawi zonse. Ngakhale kuti kucita zimenezi kungakhale kosavuta kwa ife, wophunzila Baibo wathu angapindule kwambili ngati m’kupita kwa nthawi, tiyendako na ofalitsa osiyana-siyana. M’bale Dmitrii wa ku Moldova anati: “Wofalitsa aliyense amene anabwela na mphunzitsi wanga kudzaphunzila nane, anali kufotokoza zinthu m’njila yapadela. Izi zinanithandiza kuona njila zina za mmene ningaseŵenzetsele zimene n’nali kuphunzila. Sin’nacite manyazi kwambili n’tapita ku misonkhano kwa nthawi yoyamba, cifukwa n’nali n’tadziŵana kale na abale na alongo ambili.”

13. N’cifukwa ciani tiyenela kuthandiza ophunzila athu kumapezeka ku misonkhano?

13 Thandizani wophunzila wanu kumapezeka ku misonkhano ya mpingo. Cifukwa ciani? Cifukwa Yehova analamula alambili ake kuti azisonkhana pamodzi, ndipo ni mbali ya kulambila kwathu. (Aheb. 10:24, 25) Kuwonjezela apo, abale na alongo athu ni banja lathu lauzimu. Tikakhala nawo pa misonkhano, zimakhala monga kuti tikudyela nawo pamodzi cakudya cokoma ku nyumba. Mukathandiza wophunzila Baibo wanu kupezeka ku misonkhano, ndiye kuti mukum’thandiza kutenga imodzi mwa masitepu ofunika kwambili otsogolela munthu ku ubatizo. Koma zingakhale zovuta kwa iye kutenga sitepu imeneyi. Kodi buku lakuti Kondwelani na Moyo Kwamuyaya! lingam’thandize bwanji wophunzila wanu kugonjetsa zopinga zilizonse zimene angakumane nazo?

14. Kodi tingam’limbikitse bwanji wophunzila wathu kuti azipezeka ku misonkhano?

14 Gwilitsilani nchito phunzilo 10 m’buku lakuti Kondwelani na Moyo Kwamuyaya! pokuthandizani kulimbikitsa wophunzila wanu kumapezeka ku misonkhano. Ofalitsa amene ni aciyambakale anapemphedwa kuyesa phunzilo limeneli bukuli lisanatulutsidwe, ndipo panakhala zotulukapo zabwino pothandiza maphunzilo awo kuti azipezeka ku misonkhano. Koma sikuti muyenela kuyembekezela mpaka phunzilo 10, kuti muitanile wophunzila Baibo wanu ku misonkhano yathu. Musacedwe kumuitanila ku misonkhano, ndipo pitilizani kucita zimenezi nthawi zonse. Wophunzila Baibo aliyense amakhala na zopinga zake. Conco, khalani chelu kuona zosoŵa za wophunzila wanu, na kuona ngati mungapeleke thandizo lofunikila. Ngati patenga nthawi kuti ayambe kupezeka ku misonkhano, khalani woleza mtima, koma limbikilani.

THANDIZANI WOPHUNZILA BAIBO WANU KUTHETSA MANTHA

15. Kodi ophunzila athu angakhale na mantha otani?

15 Kodi mukumbukila nthawi imene munacitapo mantha kukhala Mboni ya Yehova? Mwina munaona kuti simungakwanitse kulalikila poyela. Kapena mwina munali kuopa kuti a m’banja lanu kapena anzanu angamakutsutseni. Ngati zinali conco, ndiye kuti mungamumvetse wophunzila Baibo wanu. Yesu anakamba kuti m’pomveka kukhala na mantha otelo. Komabe, analimbikitsa otsatila ake kusalola mantha kuwalepheletsa kutumikila Yehova. (Mat. 10:16, 17, 27, 28) Kodi Yesu anawathandiza bwanji otsatila ake kuthetsa mantha? Nanga mungatengele bwanji citsanzo cake?

16. Tingam’thandize bwanji wophunzila wathu kuti aziuzako ena za cikhulupililo cake?

16 Pitilizani kuthandiza wophunzila wanu kuuzako ena za cikhulupililo cake. Ophunzila a Yesu ayenela kuti anacita mantha, iye atawatuma kuti akalalikile. Koma Yesu anawathandiza mwa kuwauza ku malo kumene anayenela kukalalikila, ndiponso uthenga umene anayenela kupita nawo. (Mat. 10:5-7) Kodi imwe mungatengele bwanji citsanzo ca Yesu? Thandizani wophunzila wanu kudziŵa kumene angalalikile. Mwacitsanzo, m’funseni ngati adziŵako wina amene angapindule akadziŵa mfundo inayake ya coonadi ca m’Baibo. Ndiyeno m’thandizeni kukonzekela zimene adzakamba mwa kumuonetsa njila yosavuta yofotokozela mfundo ya coonadi imeneyo. Pakakhala poyenela, mungayeseze naye mwa kuseŵenzetsa mbali yakuti, “Anthu Ena Amakamba Kuti” komanso mbali yakuti, “Wina Angafunse Kuti” m’buku la Kondwelani na Moyo Kwamuyaya! Mukacita zimenezi, sumikani maganizo pa kuthandiza wophunzila wanu kuseŵenzetsa Baibo popeleka mayankho osavuta, ndiponso mosamala.

17. Kodi Mateyu 10:19, 20, 29-31, tingaiseŵenzetse bwanji pothandiza wophunzila wathu kudalila Yehova?

17 Thandizani wophunzila wanu kudalila Yehova. Yesu anatsimikizila ophunzila ake kuti Yehova adzawathandiza cifukwa amawakonda. (Ŵelengani Mateyu 10:19, 20, 29-31.) Mukumbutseni wophunzila wanu kuti iyenso Yehova adzam’thandiza. Mungam’thandize kudalila Yehova mwa kupemphela naye limodzi pa zolinga zake. M’bale Franciszek wa ku Poland ananena kuti: “Nthawi zambili mphunzitsi wanga anali kuchula zolinga zanga m’mapemphelo ake. Pamene n’nali kuona mmene Yehova anali kuyankhila mapemphelo ake, inenso mwamsanga n’nayamba kupemphela. N’tayamba nchito yatsopano n’naona thandizo la Yehova n’tapempha kuti masiku ena nisamagwile nchito kuti nizipita ku misonkhano ya mpingo komanso ku msonkhano wacigawo.”

18. Kodi Yehova amamvela bwanji pa nchito imene aphunzitsi acikhristu amagwila?

18 Yehova amasamala kwambili za maphunzilo athu a Baibo. Iye amawayamikila aphunzitsi acikhristu amene amagwila nchito molimbika pothandiza anthu kuyandikila kwa iye, ndipo amawakonda cifukwa ca kulimbika kwawo kumeneku. (Yes. 52:7) Ngati palipano simutsogoza phunzilo la Baibo, mungathandizebe maphunzilo a Baibo kupita patsogolo mpaka kukabatizika, mwa kumapita na ofalitsa ena ku maphunzilo awo.

NYIMBO 60 Ni Moyo Wawo

^ ndime 5 Nkhani ino ifotokoze mmene Yesu anathandizila anthu kukhala ophunzila ake, na zimene tingacite kuti titengele citsanzo cake. Tikambilanenso mbali zina za buku latsopano lakuti Kondwelani na Moyo kwamuyaya! Bukuli linakonzedwa na colinga cothandiza maphunzilo athu a Baibo kupita patsogolo mpaka kukabatizika.

^ ndime 7 Mungapezenso zocitika zeni-zeni (1) mu Buku lofufuzila nkhani la Mboni za Yehova pansi pa mutu wakuti “Baibo,” pa kamutu kakuti “Ubwino wake,” ndiyeno pa kamutu kakuti “‘Baibulo Limasintha Anthu’ (Nkhani za mu Msanja ya Mlonda)” kapena (2) pa JW Laibulali® pa media pa mbali yakuti “Zocitika na Kufunsa Mafunso.”

^ ndime 62 MAWU OFOTOKOZELA CITHUNZI: M’bale pamodzi na mkazi wake, akuphunzitsa munthu wina Baibo. Nthawi zina, abale osiyana-siyana amakhalapo potsogoza phunzilolo.