Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 24

Mungathe Kupulumuka ku Misampha ya Satana

Mungathe Kupulumuka ku Misampha ya Satana

“Kuti awonjoke mumsampha wa Mdyerekezi.”​—2 TIM. 2:26.

NYIMBO NA. 36 Timateteza Mtima Wathu

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1. N’chifukwa chiyani tingayerekezere Satana ndi mlenje?

MLENJE amakhala ndi cholinga chimodzi chomwe ndi kugwira kapena kupha nyama. Mogwirizana ndi zimene ananena mmodzi wa anzake a Yobu omwe anabwera kudzamufooketsa, mlenje amagwiritsa ntchito misampha yosiyanasiyana. (Yobu 18:8-10) Kodi iye amanyengerera bwanji nyama kuti igwidwe mumsampha wake? Amaiyang’anitsitsa kuti adziwe zimene imachita. Amaganizira kuti, ‘Kodi imakonda kupita kuti? Imakonda chiyani? Kodi ndi msampha uti umene ungaigwire mosavuta?’ Satana ali ngati mlenje ameneyu. Iye amatiyang’anitsitsa kuti adziwe zimene timachita, kumene timakonda kupita komanso zimene zimatisangalatsa. Kenako amatiikira msampha umene ungatigwire tisakudziwa. Komabe Baibulo limatitsimikizira kuti ngati tingagwidwe mumsampha wa Satana, tikhoza kupulumuka. Limatithandizanso kudziwa zimene tingachite kuti tipewe kukodwa m’misampha yakeyi.

Satana wakhala akukola anthu ambiri pogwiritsa ntchito msampha wakunyada komanso dyera (Onani ndime 2) *

2. Kodi ndi misampha iwiri iti imene Satana amakonda kugwiritsa ntchito?

2 Misampha iwiri imene Satana amakonda kugwiritsa ntchito ndi kunyada komanso dyera * kapena kuti kusirira kwa nsanje. Kwa zaka zambiri Satana wakhala akugwiritsa ntchito makhalidwe awiri amenewa posokoneza anthu. Iye ali ngati wosaka mbalame amene amazinyengerera kuti azigwire pamsampha kapena pogwiritsa ntchito ukonde. (Sal. 91:3) Koma ife sitiyenera kukodwa m’misampha ya Satana. N’chifukwa chiyani tikutero? Tikutero chifukwa Yehova watidziwitsa misampha imene Satana amagwiritsa ntchito.​—2 Akor. 2:11.

Zitsanzo za anthu otchulidwa m’Baibulo zingatithandize kupewa komanso kupulumuka ku misampha ya Mdyerekezi (Onani ndime 3) *

3. N’chifukwa chiyani Yehova anaika nkhani zina m’Baibulo?

3 Yehova amatiphunzitsa kuopsa kwa kunyada komanso dyera potifotokozera zimene zinachitikira atumiki ena a m’mbuyo n’cholinga choti tisalakwitse ngati mmene iwo anachitira. Mu zitsanzo zimene tikambirane tiona kuti Satana anakwanitsa kukola ngakhale anthu amene anali atatumikira Yehova kwa nthawi yaitali. Kodi zimenezi zikutanthauza kuti n’zosatheka kupewa kugwidwa m’misampha ya Satana? Ayi. Yehova analola kuti nkhani zimenezi zilembedwe m’Mawu ake n’cholinga choti “zitichenjeze ifeyo.” (1 Akor. 10:11) Iye akudziwa kuti zitsanzozi zingatithandize kupewa kapena kupulumuka ku misampha ya Mdyerekezi.

MSAMPHA WAKUNYADA

Onani ndime 4

4. Kodi chingachitike n’chiyani ngati titakhala ndi mtima wonyada?

4 Satana amafuna kuti tiyambe kukhala ndi mtima wonyada. Iye amadziwa kuti tikakhala ndi mtima umenewu tingafanane ndi iyeyo ndipo tikhoza kutaya mwayi wodzapeza moyo wosatha. (Miy. 16:18) Choncho mtumwi Paulo anachenjeza kuti munthu ayenera kusamala kuti “angakhale wotukumuka chifukwa cha kunyada, n’kulandira chiweruzo chofanana ndi chimene Mdyerekezi analandira.” (1 Tim. 3:6, 7) Zimenezi zingachitikire tonsefe, kaya tangoyamba kumene choonadi kapena takhala tikutumikira Yehova kwa zaka zambiri.

5. Mogwirizana ndi Mlaliki 7:16, 20, kodi munthu angasonyeze bwanji kuti ndi wonyada?

5 Anthu amtima wonyada amakhala odzikonda. Satana amayesetsa kutipangitsa kukhala odzikonda pochititsa kuti tizingoganizira za ife tokha osati za Yehova makamaka tikakumana ndi mavuto. Mwachitsanzo, kodi anthu ena akunenerani zinthu zabodza? Kapenanso ena akuchitirani zopanda chilungamo? Zikatero, Satana amasangalala ngati mukuimba mlandu Yehova kapena abale ndi alongo anu. Ndipo iye amafuna kuti muziganiza kuti njira yabwino yothetsera vuto lanulo ndi kuchita zinthu mongotsatira maganizo anu, osati kutsatira malangizo amene amapezeka m’Mawu ake.​—Werengani Mlaliki 7:16, 20.

6. Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene zinachitikira mlongo wina wa ku Netherlands?

6 Taganizirani chitsanzo cha mlongo wina wa ku Netherlands, yemwe anakhumudwa ndi zochita za anthu ena mumpingo. Iye anaona kuti sangakwanitsenso kupirira zimenezo. Mlongoyo anati: “Ndinkangoona kuti ndili ndekhandekha ndipo sindikanakwanitsa kuwakhululukira abale ndi alongowo. Choncho ndinauza mwamuna wanga kuti tisamukire kumpingo wina.” Kenako mlongoyo anaonera pulogalamu ya JW Broadcasting® ya March 2016. Pulogalamu imeneyo inafotokoza mfundo zimene zingatithandize tikasemphana maganizo ndi anthu ena. Mlongoyo ananena kuti: “Ndinaona kuti ndinkafunika kuganizira moona mtima komanso modzichepetsa zinthu zimene ndimalakwitsa m’malo moyesa kusintha mmene abale ndi alongo amachitira zinthu mumpingo. Pulogalamuyo inandithandiza kuti ndiziganizira kwambiri za Yehova komanso ulamuliro wake.” Kodi pamenepa tikuphunzirapo chiyani? Tikakumana ndi mavuto tizipitiriza kuganizira za Yehova. Muzimupempha kuti akuthandizeni kuona ena mmene iye amawaonera. Atate wanu wakumwamba amaona zimene abale ndi alongo amalakwitsa ndipo amawakhululukira. Choncho amafuna kuti inunso muzichita zomwezo.​—1 Yoh. 4:20.

Onani ndime 7

7. Kodi n’chiyani chinachitikira Mfumu Uziya?

7 Kunyada kunachititsa kuti Mfumu Uziya ya ku Yuda ikane malangizo komanso kuchita zinthu modzikuza. Uziya ankachita bwino pa zinthu zambiri. Iye anapambana pankhondo zambiri, anamanga mizinda yambiri komanso anali ndi minda yochuluka. Baibulo limati: “Mulungu woonayo anachititsa kuti zinthu zizimuyendera bwino.” (2 Mbiri 26:3-7, 10) Limanenanso kuti: “Koma atangokhala wamphamvu mtima wake unadzikuza mpaka kufika pom’pweteketsa.” Yehova anali atalamula kuti ndi ansembe okha amene azipereka nsembe zofukiza kukachisi. Koma Mfumu Uziya anadzikweza n’kuchita zimenezi. Yehova sanasangalale nazo ndipo anakantha munthu wonyadayu ndi khate. Uziya anakhala ndi khate kwa moyo wake wonse.​—2 Mbiri 26:16-21.

8. Mogwirizana ndi 1 Akorinto 4:6, 7, kodi n’chiyani chingatithandize kuti tisakhale ndi mtima wonyada?

8 Kodi kunyada kungachititse kuti ifenso tikodwe mumsampha ngati mmene zinakhalira ndi Uziya? Taganizirani zimene zinachitikira m’bale wina dzina lake José. Bizinezi yake inkamuyendera bwino ndiponso anali mkulu amene abale ndi alongo ankamulemekeza. Iye ankakamba nkhani pamisonkhano yadera komanso yachigawo. Ndiponso oyang’anira madera ankamupempha malangizo. Iye ananena kuti: “Sindinkadalira Yehova koma ndinkadalira kwambiri luso langa komanso zimene ndimadziwa. Ndinkadziona kuti ndine wolimba, choncho sindinamvere zimene Yehova ankandichenjeza komanso kundilangiza.” José anachita tchimo lalikulu ndipo anachotsedwa mumpingo. Iye anabwezeretsedwa zaka zingapo zapitazo ndipo anati: “Yehova wandiphunzitsa kuti chofunika si kungokhala ndi udindo mumpingo koma kuchita zimene iye amafuna.” Tizikumbukira kuti luso lililonse limene tingakhale nalo komanso utumiki uliwonse umene tingapatsidwe mumpingo zimachokera kwa Yehova. (Werengani 1 Akorinto 4:6, 7.) Yehova sangatigwiritse ntchito ngati tili ndi mtima wonyada.

MSAMPHA WADYERA

Onani ndime 9

9. Kodi dyera linachititsa Satana ndi Hava kuti achite chiyani?

9 Nthawi zambiri tikamva mawu akuti dyera timakumbukira zimene Satana Mdyerekezi anachita. Popeza kuti anali mngelo wa Yehova ayenera kuti anali ndi mwayi wochita zambiri. Komabe iye sankakhutira ndi zimenezi. Iye ankafuna kuti ena azimulambira ngakhale kuti ndi Yehova yekha amene ayenera kulambiridwa. Satana amafuna kuti tizikhala ngati iyeyo, choncho amatipangitsa kuti tisamakhutire ndi zimene tili nazo. Iye anayamba kuchita zimenezi pa nthawi imene analankhula ndi Hava. Mwachikondi Yehova anapatsa Hava ndi mwamuna wake zakudya zambiri zabwino kuchokera ‘mumtengo uliwonse wa m’mundamo’ kupatulapo mtengo umodzi wokha. (Gen. 2:16) Koma Satana ananamiza Hava pomupangitsa kuganiza kuti ankafunika kudya zipatso za mtengo umene anawaletsawo. Hava sanayamikire zimene anali nazo ndipo ankafunanso zina. Timadziwa bwino zimene zinachitika pambuyo pake. Hava anachimwa ndipo kenako anafa.​—Gen. 3:6, 19.

Onani ndime 10

10. Kodi Mfumu Davide anakodwa bwanji mumsampha wadyera?

10 Dyera linachititsa Mfumu Davide kuiwala zonse zimene Yehova anamupatsa kuphatikizapo chuma, udindo komanso mmene anamuthandizira pankhondo zolimbana ndi adani ake. Poyamikira, Davide anafotokoza kuti mphatso zimene Mulungu anamupatsa zinali ‘zochuluka kwambiri moti sakanatha kuzifotokoza.’ (Sal. 40:5) Koma nthawi ina iye anaiwala zonse zimene Yehova anamupatsa. Sankakhutira ndi zomwe anali nazo moti ankafunanso zina. Ngakhale kuti anali ndi akazi ambiri, Davide anayamba kusirira mkazi wa mwiniwake. Mkaziyo anali Batiseba ndipo mwamuna wake anali Uriya Mhiti. Davide anagona ndi Batiseba ndipo anakhala ndi pakati. Kuwonjezera pamenepo, Davide anachitanso chinthu china choipa kwambiri pokonza zoti Uriya aphedwe. (2 Sam. 11:2-15) Kodi Davide ankaganiza chiyani? Kodi kapena iye ankaganiza kuti Yehova sakuona? Ngakhale kuti anali atatumikira Yehova mokhulupirika kwa nthawi yaitali, iye anachita zinthu modzikonda chifukwa cha dyera ndipo anakumana ndi mavuto aakulu. Komabe chosangalatsa n’chakuti patapita nthawi Davide anavomereza tchimo lake ndipo analapa. Iye anayamikira kwambiri Yehova chifukwa chakuti anamukhululukira.​—2 Sam. 12:7-13.

11. Mogwirizana ndi Aefeso 5:3, 4, kodi n’chiyani chingatithandize kuti tisakhale ndi mtima wadyera?

11 Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene zinachitikira Mfumu Davide? Tikuphunzira kuti timapewa mtima wadyera tikamapitiriza kuyamikira zonse zimene Yehova watipatsa. (Werengani Aefeso 5:3, 4.) Tiyenera kukhala okhutira ndi zimene tili nazo. Anthu amene akuphunzira kumene Baibulo, amalimbikitsidwa kuti aziganizira chinthu chinachake chimene Yehova wawapatsa n’kumamuthokoza. Ngati atamachita zimenezi tsiku lililonse, ndiye kuti pomatha mlungu angakhale atatchula nkhani zosiyanasiyana 7 m’pemphero. (1 Ates. 5:18) Kodi inunso mumachita zofanana ndi zimenezi? Mukamaganizira mozama zimene Yehova wakuchitirani zingakuthandizeni kuti muziyamikira, ndipo kuyamikira kudzakuchititsani kuti mukhale okhutira. Mukamakhutira ndi zimene muli nazo simungakhale ndi mtima wadyera.

Onani ndime 12

12. Kodi dyera linachititsa Yudasi Isikarioti kuti achite chiyani?

12 Dyera linachititsa Yudasi Isikarioti kuchita zoipa kwambiri moti anapereka Yesu. Koma poyamba sanali munthu woipa. (Luka 6:13, 16) Yesu anamusankha kuti akhale mtumwi. Yudasi anali wodalirika chifukwa anapatsidwa udindo woyang’anira bokosi la ndalama. Yesu ndi atumwi ake ankagwiritsa ntchito ndalamazi pa ntchito yolalikira. Ndalama zimenezi tingaziyerekezere ndi ndalama zimene zimathandiza pa ntchito ya padziko lonse masiku ano. Koma patapita nthawi Yudasi ankaba ndalamazi ngakhale kuti anali atamumva Yesu akuchenjeza mobwerezabwereza zokhudza dyera. (Maliko 7:22, 23; Luka 11:39; 12:15) Yudasi ananyalanyaza machenjezo amenewa.

13. Kodi dyera la Yudasi linaonekera kwambiri pa nthawi iti?

13 Dyera la Yudasi linaonekera kwambiri Yesu atatsala pang’ono kuphedwa. Yesu ndi ophunzira ake kuphatikizapo Mariya ndi mchemwali wake Marita anapita kunyumba kwa Simoni wakhate. Pa nthawi ya chakudya, Mariya anadzuka n’kuthira pamutu pa Yesu mafuta onunkhira omwe anali okwera mtengo. Yudasi ndi ophunzira ena anakwiya kwambiri ndi zimenezi. N’kutheka kuti ophunzira enawo anaona kuti mafutawo akanagulitsidwa, akanapeza ndalama zambiri zothandizira pa ntchito yolalikira. Koma izi si zimene Yudasi ankaganiza. Iye “anali wakuba” ndipo ankafuna kuti adzabe ndalamazo. Kenako dyera linachititsa Yudasi kuti apereke Yesu pa mtengo wogulira kapolo.​—Yoh. 12:2-6; Mat. 26:6-16; Luka 22:3-6.

14. Kodi banja lina linachita chiyani potsatira malangizo a pa Luka16:13?

14 Yesu anakumbutsa otsatira ake mfundo ya choonadi yakuti: “Simungathe kutumikira Mulungu ndi Chuma nthawi imodzi.” (Werengani Luka 16:13.) Mfundoyi siinasinthe. Taganizirani mmene banja lina la ku Romania linagwiritsira ntchito mfundo ya Yesuyi. Iwo anapatsidwa mwayi woti akagwire ntchito kwa kanthawi m’dziko lina lolemera. Banjali linanena kuti: “Tinali ndi ngongole yaikulu kubanki yoti tibweze choncho poyamba tinaona ngati ntchitoyi ndi dalitso lochokera kwa Yehova.” Komabe ntchitoyi ikanachititsa kuti asamakhale ndi nthawi yokwanira yotumikira Yehova. Pambuyo powerenga nkhani yakuti, “Khalani Okhulupirika ndi Mtima Wonse,” yomwe ili mu Nsanja ya Olonda ya August 15, 2008, iwo anasankha zochita. Iwo ananena kuti: “Ngati tikanapita dziko lina kukagwira ntchito n’cholinga choti tipeze ndalama zambiri, tikanasonyeza kuti ubwenzi wathu ndi Yehova si wofunika kwambiri. Tinaona kuti moyo wathu wauzimu ukanasokonekera.” Choncho iwo anakana ntchitoyo. Ndiye kodi chinachitika n’chiyani? Mwamuna wa banjali anapeza ntchito m’dziko lawo lomwelo, yomwe inkawathandiza kupeza zofunika. Mkazi wake ananena kuti: “Nthawi zonse Yehova amathandiza atumiki ake.” Panopa banjali limasangalala chifukwa choti linasankha kutumikira Yehova osati chuma.

MUZIPEWA MISAMPHA YA SATANA

15. N’chifukwa chiyani tinganene kuti n’zotheka kupulumuka ku misampha ya Satana?

15 Kodi tiyenera kuchita chiyani ngati tazindikira kuti tayamba kukhala ndi mtima wonyada kapena wadyera? Tikhoza kusintha. Paulo ananena kuti anthu amene Mdyerekezi “wawagwira amoyo” mu msampha wake, akhoza kupulumuka. (2 Tim. 2:26) Ndipotu Davide anamvera uphungu umene Natani anamupatsa, n’kulapa komanso kukonza ubwenzi wake ndi Yehova. Tizikumbukira kuti Yehova ndi wamphamvu kuposa Satana. Choncho tikamavomera kuti Yehova atithandize tikhoza kupulumuka ku msampha uliwonse umene Mdyerekezi angatitchere.

16. Kodi n’chiyani chimene chingatithandize kuti tizipewa misampha ya Satana?

16 N’zoona kuti tikhoza kupulumuka ngati titagwidwa ku misampha ya Satana, koma zingakhale bwino ngati titapeweratu misampha yakeyi ndipo Mulungu ndi amene angatithandize. Koma sitiyenera kudzidalira n’kumaona kuti sitingakhale ndi mtima wonyada kapena wadyera. Tikutero chifukwa anthu ena amene atumikira Yehova kwa nthawi yaitali akodwapo m’misampha imeneyi. Choncho tsiku lililonse muzipempha Yehova kuti akuthandizeni kuzindikira ngati zoganiza komanso zochita zanu zikusonyeza kuti mwayamba kukhala ndi makhalidwe oipawa. (Sal. 139:23, 24) Muziyesetsa kuti musakhale onyada kapena adyera.

17. Kodi n’chiyani chichitikire mdani wathu Mdyerekezi posachedwapa?

17 Satana wakhala ali mlenje kwa zaka zambiri. Koma posachedwapa iye adzamangidwa ndipo kenako adzawonongedwa. (Chiv. 20:1-3, 10) Tikuyembekezera mwachidwi nthawi imeneyi. Koma panopa tiyenera kukhala tcheru kuti tisakodwe m’misampha yakeyi. Muziyesetsa kupewa mtima wonyada kapena wadyera. Ndipo khalani wotsimikiza ‘kutsutsa Mdyerekezi ndipo adzakuthawani.’​—Yak. 4:7.

NYIMBO NA. 127 Mtundu wa Munthu Amene Ndiyenera Kukhala

^ ndime 5 Satana ali ngati mlenje waluso. Iye amafuna kutikola m’misampha yake ngakhale titakhala kuti tatumikira Yehova kwa nthawi yaitali. Munkhaniyi tiona mmene iye amagwiritsira ntchito kunyada komanso dyera pofuna kusokoneza ubwenzi wathu ndi Yehova. Tionanso zimene tingaphunzirepo pa zitsanzo za anthu amene anakodwa mumsampha wakunyada komanso wadyera ndiponso zimene tingachite kuti tipewe misampha imeneyi.

^ ndime 2 MATANTHAUZO A MAWU ENA: Munkhaniyi kunyada kukutanthauza kudziona kukhala wabwino kwambiri kuposa ena. Ndipo dyera likutanthauza kulakalaka kukhala ndi ndalama kapena mphamvu zambiri, kumangokhala ndi chilakolako chofuna kugonana komanso zinthu zina ngati zimenezi.

^ ndime 53 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Chifukwa cha kunyada, m’bale wina akukana malangizo anzeru. Mlongo amene ali ndi zinthu zambiri akulakalaka zinanso.

^ ndime 55 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Kunyada kunasokoneza mngelo wina wa Mulungu komanso Mfumu Uziya. Dyera linachititsa kuti Hava adye chipatso cha mumtengo woletsedwa, Davide achite chigololo ndi Batiseba komanso kuti Yudasi aziba ndalama.