Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 24

Mungathe Kuwonjoka m’Misampha ya Satana!

Mungathe Kuwonjoka m’Misampha ya Satana!

Wonjokani mu msampha wa Mdyelekezi.’—2 Tim. 2:26.

NYIMBO 36 Titeteze Mitima Yathu

ZIMENE TIKAMBILANE *

1. N’cifukwa ciani tingayelekezele Satana na wosaka nyama?

COLINGA ca nkhumbalume kapena kuti wosaka nyama cimakhala cimodzi, cimene ni kugwila kapena kupha nyama. Iye angaseŵenzetse misampha yosiyana-siyana, ngakhale imene anafotokoza mmodzi wa anzake acinyengo a Yobu. (Yobu 18:8-10) Kodi nkhumbalume angaipusitse bwanji nyama kuti aikole mu msampha wake? Coyamba, amafuna kuidziŵa bwino nyamayo. Kodi imakonda kupita kuti? Imakonda ciani? Nanga ni msampha uti umene ungaigwile mosazindikila? Satana ali ngati nkhumbalume wotelo. Coyamba amafuna atidziŵe bwino. Amaona kumene timakonda kupita ndiponso zokonda zathu. Ndiyeno amachela msampha umene amaona kuti ungatikole mosazindikila. Ngakhale n’telo, Baibo imatitsimikizila kuti ngakhale titagwidwa mu msampha wake tingathe kuwonjoka. Imatiphunzitsanso mmene tingapewele misampha imeneyi.

Kunyada komanso dyela yakhala misampha iŵili yamphamvu kwambili ya Satana (Onani ndime 2) *

2. Ni misampha iŵili iti ya Satana imene ni yamphamvu kwambili?

2 Misampha iŵili yamphamvu kwambili ya Satana, ni kunyada, komanso dyela. * Kwa zaka masauzande, Satana wakhala akuseŵenzetsa makhalidwe oipa amenewa monga misampha yabwino kwambili. Ali monga wosaka mbalame amene amakopela mbalame mu msampha wake, kapena mu ukonde. (Sal. 91:3) Koma sitiyenela kugwidwa na Satana. Cifukwa ciani? Cifukwa Yehova wativumbulila macenjela amene Satana amaseŵenzetsa.—2 Akor. 2:11.

Tingaphunzile ku zitsanzo zoticenjeza kuti tipewe kapena kuwonjoka m’misampha ya Mdyelekezi (Onani ndime 3) *

3. N’cifukwa ciani Yehova anaikamo zitsanzo zina m’Baibo?

3 Imodzi mwa njila zimene Yehova amaticenjezela za kunyada komanso dyela, ni mwa kutilimbikitsa kuphunzila ku zimene zinacitikila ena. Mu zitsanzo zimene tikambilane, mudzaona kuti Satana anakwanitsa kukola ngakhale atumiki a Yehova olimba mwauzimu. Kodi izi zitanthauza kuti basi tidzalephela, ndipo tilibe mtengo wogwila? Kutalitali! Yehova anaikamo zitsanzo zimenezi m’Baibo “kuti ziticenjeze.” (1 Akor. 10:11) Iye amadziŵa kuti tingaphunzilepo kanthu pa zitsanzo zoticenjeza, na kupewa kapena kuwonjoka ku misampha ya Mdyelekezi.

MSAMPHA WA KUNYADA

Onani ndime 4

4. Kodi kunyada kungatitsogolele ku ciani?

4 Satana amafuna kuti tikhale onyada. Iye amadziŵa kuti tikalola kunyada kutilamulila tidzakhala ngati iye, ndipo tidzataya mwayi wokhala na moyo wosatha. (Miy. 16:18) Conco, mtumwi Paulo anacenjeza kuti munthu “angakhale wotukumuka cifukwa ca kunyada, n’kulandila ciweluzo cofanana ndi cimene Mdyelekezi analandila.” (1 Tim. 3:6, 7) Izi zingacitikile aliyense wa ife, kaya ndife atsopano m’coonadi kapena tatumikila Yehova kwa zaka zambili.

5. Malinga na Mlaliki 7:16, 20, kodi munthu angaonetse bwanji kunyada?

5 Anthu onyada amakhala odzikonda. Satana amafuna kuti tikhale odzikonda, tiziganizila kwambili za ife eni kuposa Yehova, makamaka tikakumana na vuto. Mwacitsanzo, kodi wina anakunamizilamponi? Kapena munacitilidwapo zinthu zopanda cilungamo? Satana amafuna kuti muziimba mlandu Yehova kapena abale anu. Ndipo zimenezi zikacitika, Mdyelekezi amafuna muziganiza kuti cinthu cokha cothandiza nikucita zinthu mmene inuyo mufunila, m’malo motsatila citsogozo ca Yehova cimene amapeleka m’Mawu ake.—Ŵelengani Mlaliki 7:16, 20.

6. Kodi tingaphunzilepo ciani pa citsanzo ca mlongo wina wa ku Netherlands?

6 Ganizilani citsanzo ca mlongo wina wa ku Netherlands, amene anakhumudwa cifukwa ca zophophonya za ena. Iye anafika poona kuti zafika ponyanya kwambili cakuti sangapitilize kupilila. Mlongoyo sanafunenso kuceza na aliyense wa iwo. Anati: “N’nali wosungulumwa kwambili, ndipo sin’nathe kusintha maganizo anga. Conco, n’nauza mwamuna wanga kuti tisamukile ku mpingo wina.” Ndiyeno, anatamba pulogilamu ya March 2016, ya JW Broadcasting®. M’pulogilamu imeneyo, anapelekamo malingalilo a mmene tingacitile na zophophonya za ena. Mlongoyo anafotokoza kuti: “N’nazindikila kuti n’nafunika kudziunguza moona mtima komanso modzicepetsa, kuti nione zophophonya zanga, m’malo moyesa kusintha abale na alongo mu mpingo. Pulogilamu imeneyi inanithandiza kusumika maganizo pa Yehova na ucifumu wake.” Kodi mwaiona mfundo yake? Mukakumana na ciyeso, sumikani maganizo pa Yehova. M’condeleleni kuti akuthandizeni kuona ena mmene iye amawaonela. Atate wanu wakumwamba amaona zophophonya zawo. Ngakhale n’telo, amakhala wokonzeka kuwakhululukila. Iye amafuna kuti na imwe muzicita cimodzi-modzi.—1 Yoh. 4:20.

Onani ndime 7

7. N’ciani cinacitikila Mfumu Uziya?

7 Kunyada kunapangitsa Mfumu Uziya ya Yuda kukana uphungu na kucita zinthu modzikuza. Uziya anakwanitsa kucita zinthu zambili. Anapambana nkhondo zambili, anamanga zimango zambili, ndipo anali wocita bwino pankhani ya zaulimi. “Mulungu woonayo anacititsa kuti zinthu zizimuyendela bwino.” (2 Mbiri 26:3-7, 10) Baibo imati: “Koma atangokhala wamphamvu, mtima wake unadzikuza mpaka kufika pom’pweteketsa.” Yehova anali atalamula kuti ansembe okha ndiwo anayenela kupeleka zofukiza m’kacisi. Koma modzikuza, Mfumu Uziya anapita m’kacisi kukapeleka zofukiza. Yehova sanakondwele nazo zimenezo, moti anakantha munthu wodzikuzayo na khate. Uziya anakhalabe wakhate kwa moyo wake wonse.—2 Mbiri 26:16-21.

8. Mogwilizana na 1 Akorinto 4:6, 7, tingapewe bwanji kukhala onyada?

8 Kodi nafenso zingatheke kugwidwa mu msampha wa kunyada monga zinacitikila kwa Uziya? Ganizilani citsanzo ca m’bale José. Iye anali na bizinesi imene inali kumuyendela bwino kwambili, ndiponso anali mkulu wocita bwino mu mpingo. Anali kukamba nkhani pa misonkhano yadela na yacigawo, ndipo oyang’anila madela anali kufunsilako malangizo kwa iye. M’bale José anavomeleza kuti: “Koma n’nali kudalila luso langa na cidziŵitso canga. N’nali n’tam’kankhila kutali Yehova. N’nali kuganiza kuti ndine wolimba, conco sin’namvele macenjezo a Yehova na uphungu wake.” M’bale José anafika pocita chimo lalikulu ndipo anacotsedwa mu mpingo. Zaka zingapo kumbuyoku anabwezeletsedwa. Iye tsopano akuti: “Yehova waniphunzitsa kuti cinthu cofunika kwambili, si kukhala na udindo wina wake, koma kucita zimene iye amafuna.” Conco tizikumbukila kuti maluso aliwonse amene tili nawo, komanso mwayi uliwonse wa utumiki umene tingalandile mu mpingo, Yehova ndiye amatipatsa. (Ŵelengani 1 Akorinto 4:6, 7.) Ngati ndife onyada, Yehova sadzatigwilitsila nchito.

MSAMPHA WA DYELA

Onani ndime 9

9. Kodi dyela linapangitsa Satana na Hava kucita ciani?

9 Tikaganizila za dyela, mwina mwamsanga Satana Mdyelekezi ndiye amabwela m’maganizo. Pokhala mmodzi wa angelo a Yehova, Satana ayenela kuti anali na maudindo ambili abwino. Koma anali kufunanso zina. Anali kufuna kuti nayenso azilambilidwa, pamene ni Yehova yekha woyenela kulambilidwa. Satana amafuna tikhale monga iye. Conco, amayesa kutipangitsa kukhala osakhutila na zimene tili nazo. Ulendo woyamba pamene anayesa kucita zimenezi, m’pamene anakamba na Hava. Yehova mwacikondi anapatsa Hava na mwamuna wake zakudya za mwana alilenji zokhutilitsa—‘zipatso za mtengo uliwonse wa m’mundamo’ kupatulapo cabe mtengo umodzi. (Gen. 2:16) Ngakhale n’telo, Satana anapusitsa Hava mwa kum’pangitsa kuganiza kuti anafunikiladi kudya cipatso ca mu mtengo umodziwo woletsedwa. Hava analephela kuyamikila zimene anali nazo, anali kufunanso zina. Tidziŵa zotsatila zimene zinacitika. Hava anacimwa ndipo pothela pake anamwalila.—Gen. 3:6, 19.

Onani ndime 10

10. Kodi dyela linakhala bwanji msampha kwa Mfumu Davide?

10 Dyela linapangitsa Mfumu Davide kuiŵala zimene Yehova anam’patsa, kuphatikizapo cuma, kuchuka, na kugonjetsa adani ake ambili pankhondo. Davide moyamikila anavomeleza kuti mphatso za Mulungu ‘zinali zoculuka kwambili moti sakanatha kuzifotokoza.’ (Sal. 40:5) Koma pa nthawi ina Davide anaiŵala zimene Yehova anam’patsa. Sanapitilize kukhala wokhutila, anali kufunanso zina. Olo kuti Davide anali na akazi ambili, analola cilako-lako cosayenela cokhumbila mkazi wa mwini kukula mu mtima mwake. Mkaziyo dzina lake anali Batiseba, ndipo mwamuna wake anali Uriya Mhiti. Modzikonda Davide anagona na Batiseba, ndipo anakhala na pathupi. Zimene anacita Davide zinali zoipa kwambili, koma anacita zoposa pamenepo. Anakonza zakuti Uriya aphedwe! (2 Sam. 11:2-15) Kodi Davide anali kuganiza ciani? Kodi anali kuganiza kuti Yehova sangaone? Mtumiki wa Yehova ameneyo yemwe poyamba anali wokhulupilika, anagwela mu msampha wa dyela ndipo anakumana na mavuto aakulu. Koma condweletsa n’cakuti pambuyo pake, Davide anavomeleza colakwa cake ndipo analapa. Iye anayamikila kwambili kuti wayanjidwanso na Yehova!—2 Sam. 12:7-13.

11. Malinga na Aefeso 5:3, 4, n’ciani cingatithandize kuthetsa dyela?

11 Kodi citsanzo ca Davide citiphunzitsa ciani? Citiphunzitsa kuti tingathetse dyela, ngati tikhalabe oyamikila pa zonse zimene Yehova watipatsa. (Ŵelengani Aefeso 5:3, 4.) Tiyenela kukhala okhutila na zimene tili nazo. Ophunzila Baibo atsopano, akulimbikitsidwa kuganizila cinthu cimodzi cimene Yehova waŵacitila na kumuyamikila pa cinthuco. Ngati munthu acita zimenezi tsiku lililonse pa mlungu, zingatanthauze kuti iye wapemphelela nkhani zosiyana-siyana pafupi-fupi 7. (1 Ates. 5:18) Kodi imwe mumacita zofanana na zimenezi? Kusinkha-sinkha pa zonse zimene Yehova wakucitilani kudzakuthandizani kukhala woyamikila. Ndipo mukakhala woyamikila mudzakhala wokhutila. Mukakhala wokhutila simudzakhala wadyela.

Onani ndime 12

12. Kodi dyela linapangitsa Yudasi Isikariyoti kucita ciani?

12 Dyela linapangitsa Yudasi Isikariyoti kukhala kapilikoni. Koma sikuti poyamba anali munthu woipa. (Luka 6:13, 16) Yesu anam’sankha kukhala mtumwi. N’zoonekelatu kuti Yudasi anali munthu wokhoza bwino, komanso wodalilika cifukwa anapatsidwa udindo woyang’anila bokosi la ndalama. Yesu na atumwi anali kuseŵenzetsa ndalamazo posamalila zofunikila pa nchito yolalikila. M’lingalilo lina tingati ndalamazo zinali monga zopeleka za padziko lonse masiku ano. Koma pa nthawi ina, Yudasi anayamba kuba, ngakhale kuti anamva mobweleza-bweleza macenjezo a Yesu pa nkhani ya dyela. (Maliko 7:22, 23; Luka 11:39; 12:15) Yudasi ananyalanyaza macenjezowo.

13. Ni liti pamene dyela la Yudasi linaonekela bwino?

13 Dyela la Yudasi linaonekela bwino pa zimene zinacitika Yesu atatsala pang’ono kuphedwa. Yesu na ophunzila ake, pamodzi na Mariya na m’bale wake Marita, anali alendo ku nyumba kwa Simoni wakhate. Mkati mwa cakudya, Mariya anaimilila na kuthila pamutu pa Yesu mafuta onunkhila odula kwambili. Yudasi na ophunzila ena anakwiya kwambili. Ophunzila ena anaona kuti cikanakhala bwino kuseŵenzetsa ndalamazo pa nchito yolalikila. Koma colinga ca Yudasi cinali cina. Iye “anali mbala,” inde anali wakadzanja, ndipo anali kufuna kuba ndalama m’bokosi. Pambuyo pake, dyela linapangitsa Yudasi kugulitsa Yesu pa mtengo wogulila kapolo.—Yoh. 12:2-6; Mat. 26:6-16; Luka 22:3-6.

14. Kodi banja lina linaseŵenzetsa bwanji mfundo ya pa Luka 16:13?

14 Yesu anakumbutsa otsatila ake mfundo ya coonadi yakuti: “Simungathe kutumikila Mulungu ndi Cuma nthawi imodzi.” (Ŵelengani Luka 16:13.) Mpaka pano mfundoyi ikali yoona. Ganizilani mmene mawu a Yesu anakhudzila banja lina la ku Romania. Iwo anapatsidwa mwayi wokagwila nchito kwa kanthawi ku dziko lotukuka kwambili. Anavomeleza kuti: “Tinali na nkhongole yaikulu ku banki. Conco, poyamba tinaona kuti nchitoyo inali dalitso locokela kwa Yehova.” Koma panali msampha. Nchitoyo ikanasokoneza utumiki wawo kwa Yehova. Pambuyo poŵelenga nkhani yakuti, “Khalani Okhulupilika ndi Mtima Wonse” mu Nsanja ya Olonda ya August 15, 2008, anapanga cisankho. Iwo anafotokoza kuti: “Tikanapita kukagwila nchito ku dziko lina na colinga cokapeza ndalama zambili, tikanaika ubale wathu na Yehova kumbuyo. Tinadziŵa kuti umoyo wathu wauzimu udzasokonezeka.” Conco, anakana mwayi wa nchitoyo. Cinacitika n’ciani? Mwamuna anapeza nchito m’dziko lawo, imene inawathandiza pa zofunikila zawo. Mkazi wake anakamba kuti: “Dzanja la Yehova si lalifupi.” Banjali ni lokondwa cifukwa linapanga Yehova kukhala Mbuye wawo, m’malo mwa ndalama.

PEWANI MISAMPHA YA SATANA

15. N’cifukwa ciani tingakhale otsimikiza kuti n’zotheka kuwonjoka m’misampha ya Satana?

15 Bwanji ngati tazindikila kuti tinagwela kale mu msampha wa kunyada kapena dyela? Tingathe kuwonjokamo! Paulo anakamba kuti anthu amene Mdyelekezi “wawagwila amoyo” angawonjokemo mu msampha. (2 Tim. 2:26) Izi n’zimene zinacitika kwa Davide. Iye anamvela uphungu wa Natani na kulapa pa dyela lake, ndipo anakonzanso ubwenzi wake na Yehova. Tisaiŵale kuti Yehova ni wamphamvu kuposa Satana. Conco, ngati tilandila thandizo la Yehova, tingawonjoke mu msampha uliwonse umene Mdyelekezi angachele.

16. N’ciani cingatithandize kupewa misampha ya Satana?

16 Koma m’malo moyembekezela kuti mpaka tikagwele m’misampha ya Satana kenako n’kuwonjokamo, tiyenela kuipewelatu misamphayo. Tingaipewe kokha mwa thandizo la Mulungu. Koma tisakhale na maganizo akuti ine sizinganicitikile! Cifukwa ngakhale atumiki a Yehova amene ni aciyambakale, anagwelapo mu msampha wa kunyada kapena dyela. Conco m’condeleleni Yehova tsiku lililonse, kuti akuthandizeni kuzindikila ngati makhalidwe oipa amenewo ayamba kusonkhezela kaganizidwe kanu na zocita zanu. (Sal. 139:23, 24) Musalole kuti makhalidwewo azike mizu mwa inu!

17. N’ciani cimene posacedwa cidzacitikila mdani wathu Mdyelekezi?

17 Kwa zaka masauzande, Satana wakhala nkhumbalume. Koma posacedwa adzamangidwa, ndipo pa mapeto pake adzawonongedwa. (Chiv. 20:1-3, 10) Tiiyembekezela mwacidwi nthawi imeneyo. Mpaka nthawiyo, tiyeni tikhalebe chelu ku misampha ya Satana. Citani zonse zotheka kuti musalole kunyada kapena dyela kukulamulilani. Tsimikizani mtima ‘kutsutsa Mdyelekezi ndipo adzakuthawani.”—Yak. 4:⁠7.

NYIMBO 127 Mtundu wa Munthu Amene Niyenela Kukhala

^ ndime 5 Satana ali monga wosaka nyama waluso. Amafuna kutikola m’misampha yake kaya tatumikila Yehova kwa nthawi yaitali motani. M’nkhani ino, tiphunzile mmene Satana amaseŵenzetsela kunyada ndiponso dyela kuwononga ubale wathu na Mulungu. Tionenso zimene tingaphunzile ku zitsanzo za ena amene anagwidwapo mu msampha wa kunyada komanso dyela. Ndiponso tione mmene tingapewele misampha imeneyo.

^ ndime 2 KUFOTOKOZELA MAWU ENA: Nkhani ino idzafotokoza kwambili za kunyada. Munthu akakhala na khalidwe limeneli amadziona kuti ni wofunika kwambili kuposa ena. Idzafotokozanso kwambili za dyela, kutanthauza cikhumbo cosalamulilika cofuna kukhala na ndalama zambili, mphamvu zoculuka, cilako-lako cosalamulilika ca kugonana, kapena zina zotelo.

^ ndime 53 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: M’bale monyada akukana malangizo anzelu. Mlongo amene ali kale na zinthu zambili wakopeka kuti akhalenso na zina.

^ ndime 55 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Mngelo wa Mulungu komanso Mfumu Uziya anakhala onyada. Dyela ndilo linapangitsa Hava kudya cipatso ca mu mtengo woletsedwa, linapangitsanso Davide kucita cigololo na Batiseba, komanso Yudasi kuba ndalama.