Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 27

Tengelani Citsanzo ca Yehova pa Kupilila

Tengelani Citsanzo ca Yehova pa Kupilila

“Ngati inu mudzapilile, mudzapeza moyo.”—LUKA 21:19.

NYIMBO 114 “Khalani Oleza Mtima”

ZIMENE TIKAMBILANE *

 

“LIMBIKANI, MUSAFOOKE!” Uwu ndiwo unali mutu wolimbikitsa wa msonkhano wacigawo wa 2017. Msonkhanowo unationetsa mmene tingapililile tikakumana na mayeso. Papita zaka 4 lomba, ndipo mwa cilimbikitso cimeneco, tikuthabe kupilila mavuto m’dongosolo lino.

2 Kodi mwakumanapo na mavuto otani posacedwapa? Kodi munataikilidwa wa m’banja mwanu kapena mnzanu wapamtima? Kodi mukudwala matenda aakulu? Kodi mukulimbana na mavuto obwela cifukwa ca ukalamba? Kapena mwakumana na tsoka la zacilengedwe, ciwawa, kapena kuzunzidwa? Kapenanso zovuta zina cifukwa ca mlili wa kolona? Tiyembekezela mwacidwi nthawi pamene zinthu zonsezi zidzakhala zakale—sitidzazikumbukilanso ndipo sizidzacitikanso!—Ŵelengani Yesaya 65:16, 17.

3. Kodi tiyenela kucita ciani pali pano? Cifukwa ciani?

3 Umoyo m’dzikoli ni wovuta kwambili, ndipo mwina m’tsogolomu tidzakumana na mavuto aakulu kwambili. (Mat. 24:21) N’zoonekelatu kuti tiyenela kupitiliza kupilila. Cifukwa ciani? Cifukwa Yesu anati: “Ngati inu mudzapilile, mudzapeza moyo.” (Luka 21:19) Tikaganizila za ena amene amatha kupilila mayeso ngati athu, ifenso tidzakwanitsa kupilila.

4. N’cifukwa ciani tingati Yehova ni citsanzo cabwino ca kupilila?

4 Kodi ndani ali citsanzo cabwino koposa pa nkhani ya kupilila? Yehova Mulungu. Kodi yankho ili mwadabwa nalo? N’kutheka. Koma mukaliganizila bwino mungamvetse cifukwa cake. Dzikoli likulamulidwa na Mdyelekezi, ndipo ni lodzala na mavuto. Yehova ngati afuna angaliwononge dzikoli mosavuta, koma akuyembekezela nthawi yoikika kutsogolo kuti akacite zimenezi. (Aroma 9:22) Pali pano, Mulungu wathu akupitilizabe kupilila mpaka pamene nthawi yoikidwilatu idzafike. Tiyeni tikambilane zinthu 9 zimene Yehova wasankha kupilila.

KODI YEHOVA WASANKHA KUPILILA ZINTHU ZOTANI?

5. Kodi dzina la Mulungu likutonzedwa bwanji? Nanga inu mumamvela bwanji mukaona zimenezi?

5 Kutonzedwa kwa dzina lake. Yehova amalikonda dzina lake, ndipo amafuna kuti anthu onse azililemekeza. (Yes. 42:8) Koma kwa zaka ngati 6,000 zapitazo, dzina lake labwino lakhala likutonzedwa. (Sal. 74:10, 18, 23) Izi zinayambila m’munda wa Edeni pamene Mdyelekezi (kutanthauza “Woneneza”) anaimba mlandu Mulungu wakuti anamana Adamu na Hava cina cake cimene anali kufunikila kuti akhale acimwemwe. (Gen. 3:1-5) Kucokela panthawiyo, Yehova wakhala akuimbidwa mlandu wabodza wakuti amamana anthu zinthu zabwino zimene afunikila. Yesu anakhudzidwa kwambili kuona mmene dzina la Atate wake linali kutonzedwela. Ndiye cifukwa cake anauza ophunzila ake kupemphela kuti: “Atate wathu wakumwamba, dzina lanu liyeletsedwe.”—Mat. 6:9.

6. N’cifukwa ciani Yehova walola kuti papite nthawi yaitali kuti athetse nkhani ya ulamulilo wake?

6 Kutsutsidwa kwa ulamulila wake. Yehova ndiye woyenela kulamulila kumwamba na padziko lapansi, ndipo ulamulilo wake ndiye wabwino koposa. (Chiv. 4:11) Koma Satana wayesa kunamiza angelo na anthu kuganiza kuti Mulungu si woyenela kulamulila. Panafunika nthawi yokwanila kuti nkhani yotsutsa kuti Yehova ndiye woyenela kulamulila ithetsedwe. Conco mwanzelu, Mulungu walola anthu kudzilamulila okha. Wacita zimenezi kuti adzionele okha kuti ulamulilo wa anthu ni wolephela popanda Mlengi wawo kuwatsogolela. (Yer. 10:23) Cifukwa ca kuleza mtima kwa Mulungu, nkhaniyi idzathetsedwa mosavuta. Ndipo anthu adzadziŵa kuti iye yekha ndiye woyenela kulamulila, ndiponso kuti Ufumu wake ndiwo wokha umene udzakhazikitse bata ndi mtendele weniweni padziko lapansi.

7. Ndani amene anapandukila Yehova? Nanga iye adzawacita ciani?

7 Kupanduka kwa ena mwa ana ake. Yehova analenga ana ake auzimu komanso aumunthu angwilo. Koma mngelo wopandukayo, Satana (kutanthauza “Wotsutsa”), anapangitsanso anthu angwilo, Adamu na Hava, kupandukila Yehova. Komanso angelo ena, kuphatikizapo anthu ena, nawonso anapanduka. (Yuda 6) Patapita nthawi, ngakhale ena mwa anthu a mtundu wa Aisiraeli, anthu osankhidwa na Mulungu, anam’kana ndipo anayamba kulambila milungu yonyenga. (Yes. 63:8, 10) Izi zinam’khumudwitsa kwambili Yehova. Ngakhale n’telo, iye anapilila ndipo adzapitilizabe kupilila mpaka pa nthawi imene adzawononga onse om’pandukila. Izi zidzabweletsa madalitso kwa atumiki ake okhulupilika, amene akupilila naye limodzi zinthu zoipa m’dongosolo lino la zinthu.

8-9. Kodi Yehova akunenezedwa mabodza otani? Nanga ife tingacitepo ciani pa mabodza amenewa?

8 Mabodza a Mdyelekezi. Satana anati Yobu, komanso atumiki onse okhulupilika a Yehova amam’tumikila pa zifukwa zadyela. (Yobu 1:8-11; 2:3-5) Mpaka pano Mdyelekezi akali kukambabe zimenezi. (Chiv. 12:10) Tingaonetse kuti zonse zimene Satana amakamba n’zabodza, mwa kupilila mayeso athu na kukhalabe okhulupilika kwa Yehova cifukwa comukonda. Monga zinacitikila kwa Yobu, ifenso tidzadalitsidwa cifukwa ca kupilila kwathu.—Yak. 5:11.

9 Satana amaseŵenzetsa atsogoleli a zipembedzo zonyenga kukamba kuti Yehova ni wankhanza, ndipo ndiye amacititsa anthu kuvutika. Ena amafika pokamba kuti ana akamwalila, ndiye kuti Mulungu waatenga kuti akakhale angelo kumwamba. Uku ndiye kumunyoza Mulungu! Koma ife sititelo ayi. Tikadwala matenda aakulu, kapena munthu amene timam’konda akamwalila, sitiimba Mulungu mlandu. Mosiyana na anthu ena, timakhulupilila kuti tsiku lina iye adzakonza zinthu zonse. Timauza aliyense amene angatimvetsele kuti Yehova ni Mulungu wacikondi. Izi zimamuthandiza kuyankha amene akumutonza.—Miy. 27:11.

10. Kodi Salimo 22:23, 24 ionetsa ciani za Yehova?

10 Kuvutika kwa atumiki ake okondeka. Yehova ni Mulungu wacikondi. Iye cimamuŵaŵa akaona tikulila cifukwa ca mavuto amene tikupilila monga cizunzo, matenda, kapena zophophonya zathu. (Ŵelengani Salimo 22:23, 24.) Yehova amakhudzidwa kwambili tikamavutika. Ni wofunitsitsa kuthetsa mavuto, ndipo adzawathetsadi. (Yelekezelani na Ekisodo 3:7, 8; Yesaya 63:9) Nthawi idzafika pamene “Iye adzapukuta misozi yonse m’maso [mwathu], ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulila, kapena kubuula, ngakhale kupweteka.”—Chiv. 21:4.

11. Kodi Yehova amamvela bwanji za atumiki ake okhulupilika amene anamwalila?

11 Kutaikilidwa mabwenzi ake mu imfa. Kodi Yehova amamvela bwanji akakumbukila za amuna na akazi okhulupilika amene anamwalila? Iye amafunitsitsa kukawaonanso! (Yobu 14:15) Tangoganizilani mmene Yehova amayewela bwenzi lake Abulahamu. (Yak. 2:23) Kapena Mose amene analankhula naye “pamasom’pamaso.” (Eks. 33:11) Iye amayembekezela mwacidwi kudzamva Davide komanso olemba masalimo ena akuimba nyimbo zokoma zacitamando! (Sal. 104:33) Ngakhale kuti mabwenzi a Mulungu amenewa anagona mu imfa, Yehova sanawaiŵale. (Yes. 49:15) Iye amakumbukila zonse zokhudza iwo. Tingati “kwa iye onsewa ndi amoyo.” (Luka 20:38) Tsiku lina, adzawaukitsa, ndipo adzamvelanso mapemphelo awo ocokela pansi pa mtima na kuvomeleza kulambila kwawo. Ngati munataikilidwa okondedwa anu mu imfa, lolani zimenezi zikulimbitseni na kukutonthozani.

12. Kodi n’ciani cimam’khumudwitsa kwambili Yehova m’masiku otsiliza ano oipa?

12 Anthu oipa kupondeleza ena. Pamene kupanduka kunayamba mu Edeni, Yehova anadziŵa kuti zinthu zidzaipila-ipilabe kutsogolo. Yehova amadana na zoipa, kupanda cilungamo, na ciwawa, zimene zili m’dzikoli. Iye nthawi zonse amacitila cifundo anthu onyozeka, ofooka komanso opanda citetezo, ana amasiye komanso akazi amasiye. (Zek. 7:9, 10) Yehova cimamuwawa kwambili akaona atumiki ake okhulupilika, akupondelezedwa na kuponyedwa m’ndende. Dziŵani kuti iye amakukondani inu nonse amene mukupilila naye limodzi.

13. Kodi Mulungu amaona zonyansa zotani zimene anthu akucita? Nanga iye adzacitapo ciani?

13 Kuwonjezeleka kwa makhalidwe oipa a anthu. Tinalengedwa m’cifanizilo ca Mulungu, koma Satana amakonda kupangitsa anthu kucita zinthu zoipa. Pamene Yehova “anaona kuti kuipa kwa anthu kwaculuka” m’nthawi ya Nowa, iye “anamva cisoni kuti anapanga anthu padziko lapansi, ndipo zinam’pweteka kwambili mumtima.” (Gen. 6:5, 6, 11) Kodi mikhalidwe inasintha kucokela panthawiyo? Kutalitali! Mdyelekezi amamva bwino kwambili akaona kuculuka kwa zaciwelewele za mtundu uliwonse, kuphatikizapo ciwelewele pakati pa anthu ofanana ziwalo! (Aef. 4:18, 19) Satana amakondwela kwambili ngati anthu amene amalambila Yehova acita chimo lalikulu. Kuleza mtima kwa Yehova kukadzatha, iye adzaonetsa mwamphamvu kuti makhalidwe onse oipa amadana nawo.

14. Kodi anthu akucita ciani ku cilengedwe ca Mulungu?

14 Kuwonongedwa kwa cilengedwe cake. Kuwonjezela pa ‘kupweteka munthu mnzake pomulamulila,’ anthu awononganso dziko na zinyama zimene Yehova anapatsa anthu udindo wozisamalila. (Mlal. 8:9; Gen. 1:28) Asayansi ena amati cifukwa ca zocita za anthu, mtundu wa zinyama komanso zomela zokwana 1 miliyoni zingatheletu m’zaka zikubwelazi. Conco, m’pomveka anthu akamadela nkhawa zacilengedwe! Koma cokondweletsa n’cakuti Yehova, analonjeza kuti ‘adzawononga amene akuwononga dziko lapansi,’ ndiponso kuti adzasandutsa dziko lonse lapansi kukhala paradaiso.—Chiv. 11:18; Yes. 35:1.

ZIMENE TIPHUNZILAPO PA KUPILILA KWA YEHOVA

15-16. N’ciani ciyenela kutilimbikitsa kupilila naye limodzi Yehova? Pelekani citsanzo.

15 Ganizilani mavuto ambili amene Atate wathu wakumwamba wakhala akupilila kwa zaka masauzande. (Onani bokosi lakuti “ Zimene Yehova Akupilila.”) Yehova angawononge dziko loipali panthawi ina iliyonse. Koma kuleza mtima kwake kwakhala dalitso kwa ife! Ganizilani citsanzo ici. Tinene kuti mwamuna na mkazi wake auzidwa kuti mwana wawo ali m’mimba ali na matenda aakulu, cakuti akakabadwa umoyo wake udzakhala wovuta, ndipo adzafa ali wamng’ono. Ngakhale kuti zidzakhala zovuta kusamalila mwanayo, makolowo adzakondwela mwanayo akakabadwa. Cifukwa com’konda mwanayo, iwo adzapilila mavuto aliwonse kuti asamalile moyo wa mwanayo.

16 Mofananamo, mbadwa zonse za Adamu na Hava zimabadwa zopanda ungwilo. Ngakhale n’telo, Yehova amawakonda na kuwasamalila. (1 Yoh. 4:19) Koma mosiyana na makolo aumunthu amene tachula m’citsanzo cathu, Yehova angathetse mavuto a ana ake. Iye anaikilatu tsiku pamene adzathetse mavuto onse a mtundu wa anthu. (Mat. 24:36) Kodi cikondi cake sicitilimbikitsa kupilila naye limodzi mmene tingathele?

17. Kodi zimene zili pa Aheberi 12:2, 3 ponena za Yesu, zimatilimbikitsa bwanji kupitilizabe kupilila?

17 Yehova amapeleka citsanzo cabwino kwambili pa kupilila. Yesu anatengela citsanzo ca Atate wake pa kupilila. Ali munthu padziko lapansi, Yesu anapilila malankhulidwe omunyoza, kucititsidwa manyazi, komanso imfa pamtengo wozunzikilapo, kaamba ka ife. (Ŵelengani Aheberi 12:2, 3.) Ndithudi, citsanzo ca Yehova pa kupilila cinalimbikitsa Yesu nayenso kupilila. Nafenso cingatilimbikitse.

18. Kodi 2 Petulo 3:9 imatithandiza bwanji kuona zimene zakwanilitsika cifukwa ca kuleza mtima kwa Yehova?

18 Ŵelengani 2 Petulo 3:9. Yehova akudziŵa nthawi yoyenelela yodzawononga dziko loipali. Cifukwa ca kuleza mtima kwake, anthu ambili afika pom’dziŵa, ndipo khamu la anthu ofika m’mamiliyoni akumulambila na kum’tamanda. Onsewo amayamikila kuti Yehova wapilila kwanthawi yaitali mpaka iwo kubadwa, kuphunzila kum’konda, komanso kudzipatulila kwa iye. Yehova akadzawafupa anthu mamiliyoni amene adzapilila mpake mapeto, zidzaonetselatu kuti cisankho cake ca kupilila cinali canzelu!

19. Kodi tiyenela kutsimikiza mtima kucita ciani? Nanga tidzapeza madalitso otani?

19 Timaphunzila kwa Yehova mmene tingapililile mwacimwemwe. Olo kuti Satana wacititsa zinthu zowawitsa mtima komanso mavuto, Yehova wakhalabe “Mulungu wacimwemwe.” (1 Tim. 1:11) Ifenso tingakhalebe acimwemwe poyembekezela moleza mtima kuti Yehova akayeletse dzina lake, kuthetsa nkhani ya ulamulilo, makhalidwe onse oipa, komanso mavuto onse amene tikukumana nawo pali pano. Tiyeni tikhale otsimikiza mtima kupilila komanso kulimbikitsidwa podziŵa kuti Atate wathu wakumwamba nayenso akupilila. Tikacita zimenezi, mawu awa adzakwanilitsidwa pa ife akuti: “Wodala ndi munthu wopilila mayeselo, cifukwa akadzavomelezedwa, adzalandila mphoto ya moyo, umene Yehova analonjeza onse omukonda.”—Yak. 1:⁠12.

NYIMBO 139 Yelekeza Uli M’dziko Latsopano

^ ndime 5 Aliyense wa ife amakumana na mavuto osiyanasiyana. Pali pano, palibe njila yothetsela ambili mwa mavuto amenewa. Timangofunika kuwapilila. Koma sitili tekha. Yehova nayenso akupilila zambili. M’nkhani ino, tikambilane zinthu 9 zimene Yehova wakhala akupilila. Tikambilanenso zimene zatheka cifukwa ca kupilila kwa Yehova, komanso zimene tingaphunzilepo pa citsanzo cake ca kupilila.

[Mafunso Ophunzilila]