NKHANI YOPHUNZIRA 27

Muzitsanzira Yehova pa Nkhani ya Kupirira

Muzitsanzira Yehova pa Nkhani ya Kupirira

“Ngati inu mudzapirire, mudzapeza moyo.”​—LUKA 21:19.

NYIMBO NA. 114 “Khalani Oleza Mtima”

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1-2. Kodi mawu a Yehova a pa Yesaya 65:16, 17, amatilimbikitsa bwanji kuti tisafooke?

MSONKHANO wachigawo wa 2017 unali ndi mutu wosangalatsa wakuti, “Musafooke!” Pulogalamu ya msonkhanowu inatithandiza kuona zimene tingachite kuti tizipirira mavuto amene timakumana nawo. Tsopano papita zaka 4 kuchokera nthawi imeneyo ndipo tikupitirizabe kupirira mavuto osiyanasiyana m’dziko loipali.

2 Kodi inuyo mwakumana ndi mavuto otani posachedwapa? Kodi mwaferedwa wachibale kapena mnzanu wa pamtima? Kodi mukuvutika ndi matenda aakulu kapena mavuto obwera chifukwa uchikulire? Kodi mwakumana ndi mavuto chifukwa cha ngozi zam’chilengedwe, chiwawa kapena kuzunzidwa? Kapena kodi mwakumana ndi mavuto obwera chifukwa cha mliri wa COVID-19? Tikuyembekezera mwachidwi nthawi imene zonsezi zidzatha, sizidzakumbukiridwanso ndipo sizidzachitikanso.​—Werengani Yesaya 65:16, 17.

3. Kodi tikufunika kuchita chiyani panopa, nanga n’chifukwa chiyani?

3 Masiku ano moyo ndi wovuta ndipo mwina tikhoza kukumana ndi mavuto aakulu m’tsogolomu. (Mat. 24:21) Choncho tiyenera kuphunzira zimene tingachite kuti tizipirira kwambiri. Chifukwa chiyani? Chifukwa Yesu ananena kuti, “Ngati inu mudzapirire, mudzapeza moyo.” (Luka 21:19) Kuganizira zimene zikuthandiza ena kupirira mavuto ofanana ndi amene ife tikukumana nawo, kungatithandize kuti tizipirira kwambiri.

4. N’chifukwa chiyani tinganene kuti Yehova ndi chitsanzo chabwino pankhani ya kupirira?

4 Kodi chitsanzo chabwino kwambiri pankhani ya kupirira ndi ndani? Yehova Mulungu. Kodi zimenezi zikukudabwitsani? Mwina n’kutheka. Koma mutaganizira nkhaniyi mungamvetse chifukwa chake tikutero. Mdyerekezi ndi amene akulamulira dzikoli, ndipo lili ndi mavuto adzaoneni. Yehova ali ndi mphamvu zoti akhoza kuthetsa mavutowa panopa, koma akudikira tsiku loti adzachite zimenezi. (Aroma 9:22) Mulungu wathu akupitirizabe kupirira mpaka nthawi imene anakhazikitsa itafika. Tsopano tiyeni tikambirane zinthu 9 zimene iye akuzipirira.

KODI YEHOVA AKUPIRIRA ZINTHU ZITI?

5. Kodi dzina la Mulungu lakhala likunyozedwa motani, nanga inuyo mumamva bwanji chifukwa cha zimenezi?

5 Kunyozedwa kwa dzina lake. Yehova amakonda dzina lake ndipo amafuna kuti aliyense azililemekeza. (Yes. 42:8) Koma kwa zaka 6000, dzina lake labwinoli lakhala likunyozedwa. (Sal. 74:10, 18, 23) Zimenezi zinayambira m’munda wa Edeni pamene Mdyerekezi (kutanthauza “Woneneza”) anaimba Mulungu mlandu woti ankamana Adamu ndi Hava zinthu zimene ankafunikira kuti azisangalala. (Gen. 3:1-5) Kuchokera nthawi imeneyo, Yehova wakhala akuimbidwa mlandu wabodza wakuti amamana anthu zinthu zimene amafunikira. Zinkamukhudza kwambiri Yesu kuona dzina la Atate wake likunyozedwa. Chifukwa cha zimenezi iye anauza otsatira ake kuti azipemphera kuti: “Atate wathu wakumwamba, dzina lanu liyeretsedwe.”​—Mat. 6:9.

6. N’chifukwa chiyani Yehova walola kuti padutse nthawi yokwanira kuti asonyeze kuti iyeyo ndi amene ali woyenera kulamulira?

6 Kutsutsidwa kwa Ulamuliro wake. Yehova yekha ndi amene ali ndi ufulu wonse wolamulira kumwamba ndi dziko lapansi ndipo ulamuliro wake ndi wabwino kwambiri. (Chiv. 4:11) Koma Mdyerekezi wakhala akusocheretsa angelo komanso anthu powachititsa kuganiza kuti Mulungu si woyenera kulamulira. Nkhani yoti Yehova ndi woyenera kulamulira inkafunika nthawi yokwanira kuti ithetsedwe. Mwanzeru, Mulungu analola kuti padutse nthawi yambiri kuti anthu aone okha kuti sangathe kudzilamulira popanda kutsogoleredwa ndi Mlengi. (Yer. 10:23) Chifukwa chakuti Yehova wakhala akuchita zinthu moleza mtima, nkhani imeneyi idzathetsedwa m’njira yabwino kwambiri ndipo siidzachitikanso. Iye adzalemekezedwa pamene adzasonyeze kuti Ufumu wake wokha ndi umene ungabweretse mtendere weniweni komanso chitetezo padzikoli.

7. Kodi ndi ndani amene anasankha kusamvera Yehova, nanga iye adzawatani?

7 Kusamvera kwa ana ake ena. Yehova analenga ana ake omwe ndi angelo komanso anthu ali angwiro. Koma mmodzi wa angelowo yemwe ndi Satana (kutanthauza “Wotsutsa”) anasankha kusamvera ndipo anachititsanso kuti Adamu ndi Hava asamvere Yehova. Patapita nthawi, angelo ndi anthu enanso anasankha kugwirizana nawo. (Yuda 6) Ngakhalenso Aisiraeli omwe anali anthu osankhidwa a Mulungu anamukana ndipo anayamba kulambira milungu yonyenga. (Yes. 63:8, 10) Zimenezitu zinamupweteka kwambiri Yehova. Iye wakhala akupirira ndipo apitirizabe kupirira mpaka nthawi imene adzawononge onse osamvera. Kenako Yehova ndi anthu onse omwe ndi okhulupirika kwa iye adzasangalala chifukwa sadzafunika kupiriranso zinthu zoipa za m’dzikoli.

8-9. Kodi ndi mabodza ati amene anthu amanena okhudza Yehova, nanga ifeyo tiyenera kuchita chiyani?

8 Mabodza amene Mdyerekezi amanena. Satana ananena kuti mtumiki wokhulupirika wa Yehova, Yobu, komanso atumiki okhulupirika a Yehova masiku ano amatumikira Mulungu chifukwa cha dyera. (Yobu 1:8-11; 2:3-5) Satana amanenabe zimenezi mpaka pano. (Chiv. 12:10) Tingasonyeze kuti zimene Satana amanena ndi zabodza tikamapirira mayesero n’kukhalabe okhulupirika kwa Yehova chifukwa choti timamukonda. Mofanana ndi Yobu, ifenso Yehova adzatidalitsa ngati tingapirire.​—Yak. 5:11.

9 Satana amagwiritsa ntchito atsogoleri a chipembedzo kuti azinena kuti Yehova ndi wankhanza, komanso ndi amene amachititsa mavuto a anthu. Enanso amanena kuti ana akamwalira ndiye kuti Mulungu wawatenga kuti awonjezere angelo ena kumwamba. Kumenekutu ndi kunyoza kwambiri Mulungu. Koma ife timadziwa kuti Yehova ndi Atate wachikondi ndipo sangachite zimenezi. Tikamadwala matenda aakulu kapena munthu amene timamukonda akamwalira, sitimaimba mlandu Mulungu. M’malomwake timakhulupirira kuti tsiku lina iye adzakonza zinthu ndipo timauza aliyense amene angatimvetsere kuti Yehova ndi Mulungu wachikondi. Zimenezi zimachititsa kuti Yehova azitha kuyankha amene akumutonza.​—Miy. 27:11.

10. Kodi lemba la Salimo 22:23, 24, limasonyeza kuti Yehova ndi wotani?

10 Kuvutika kwa atumiki ake okondedwa. Yehova ndi Mulungu wachifundo. Iye sasangalala akationa tikuvutika ndi zinthu monga kuzunzidwa, matenda kapena mavuto ena omwe amabwera chifukwa choti ndife ochimwa. (Werengani Salimo 22:23, 24.) Yehova amamvetsa mavuto athu, amafuna kuwathetsa ndipo adzawathetsadi. (Yerekezerani ndi Eks. 3:7, 8; Yes. 63:9.) Nthawi ikubwera pamene “iye adzapukuta misozi yonse m’maso [mwathu], ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka.”​—Chiv. 21:4.

11. Kodi Yehova amamva bwanji akaganizira za atumiki ake okhulupirika omwe anamwalira?

11 Kusowana ndi anzake amene anamwalira. Kodi Yehova amamva bwanji chifukwa cha amuna ndi akazi okhulupirika omwe anamwalira? Iye amafunitsitsa kudzawaonanso. (Yobu 14:15) Tangoganizani mmene Yehova amamusowera mnzake Abulahamu. (Yak. 2:23) Taganiziraninso za Mose yemwe ankalankhula naye “pamasom’pamaso.” (Eks. 33:11) Yehova ayenera kuti amalakalaka kudzamvanso Davide ndi anthu ena omwe analemba nawo masalimo akuimba nyimbo zosangalatsa zomutamanda. (Sal. 104:33) Ngakhale kuti anzake a Mulungu amenewa anamwalira, Yehova sanawaiwale. (Yes. 49:15) Iye akukumbukira chilichonse chokhudza anthu amenewa ndipotu tinganene kuti “kwa iye onsewa ndi amoyo.” (Luka 20:38) Tsiku lina iye adzawaukitsa ndipo adzayambiranso kumvetsera mapemphero awo ochokera pansi pamtima komanso kuvomereza kuti azimulambira. Ngati munthu amene munkamukonda anamwalira ndiye kuti mfundo zimenezi zingakutonthozeni komanso kukulimbikitsani.

12. Kodi ndi zinthu ziti zimene zimamupweteka kwambiri Yehova m’masiku otsiriza oipawa?

12 Anthu oipa akamapondereza anzawo. Kusamvera kutayamba m’munda wa Edeni, Yehova anadziwa kuti zinthu zidzaipa kwambiri zisanakhalenso bwino. Iye amadana ndi zinthu zoipa, zachiwawa komanso zopanda chilungamo zomwe zimachitika m’dzikoli masiku ano. Nthawi zonse Yehova amadera nkhawa anthu omwe sangadziteteze monga ofooka komanso akazi ndi ana amasiye. (Zek. 7:9, 10) Zimamupwetekanso kwambiri akamaona atumiki ake okhulupirika akuponderezedwa komanso kuikidwa m’ndende. Dziwani kuti amakukondani kwambiri nonsenu amene mukupirira naye limodzi.

13. Kodi ndi zinthu zoipa ziti zimene Mulungu amaona zikuchitika padzikoli, nanga adzachitapo chiyani?

13 Makhalidwe oipa amene anthu ali nawo. Anthu analengedwa m’chifanizo cha Mulungu, koma Satana amasangalala kuwasokoneza kuti azichita zoipa. Pamene Yehova “anaona kuti kuipa kwa anthu kwachuluka” m’nthawi ya Nowa, “anamva chisoni kuti anapanga anthu padziko lapansi, ndipo zinam’pweteka kwambiri mumtima.” (Gen. 6:5, 6, 11) Kodi zinthu zinasintha kuchokera nthawi imeneyo. Ayi ndithu. Satana akusangalala akamaona kuti khalidwe lachiwerewere likufala kwambiri, zomwe zikuphatikizapo kugonana kwamtundu uliwonse kwa anthu osakwatirana komanso kumene kumachitika pakati pa amuna kapena akazi okhaokha. (Aef. 4:18, 19) Ndipotu amasangalala kwambiri akachititsa anthu amene amatumikira Mulungu woona kuti achite tchimo. Koma nthawi yoti Yehova azisonyeza kuleza mtima ikadzatha, adzaonetsa kuti amadana kwambiri ndi makhalidwewa powononga anthu onse oipa.

14. Kodi anthu akuchita zotani ndi dzikoli komanso nyama?

14 Kuwonongedwa kwa zinthu zimene analenga. Kuwonjezera pa kupweteka anthu anzawo powalamulira, anthu sakusamalira dziko ndi nyama zimene Yehova anawapatsa kuti azizisamalira. (Mlal. 8:9; Gen. 1:28) Akatswiri ena akuchenjeza kuti zimene anthu akuchita zipangitsa kuti mitundu 1 miliyoni ya zomera komanso nyama itheretu padzikoli m’zaka zochepa zikubwerazi. Choncho m’pake kuti iwo amanena kuti chilengedwe chili pamavuto. Tikuthokoza kwambiri Yehova chifukwa walonjeza kuti ‘adzawononga amene akuwononga dziko lapansi’ ndipo adzasintha dzikoli kuti likhale paradaiso.​—Chiv. 11:18; Yes. 35:1.

KODI TIKUPHUNZIRA CHIYANI PA KUPIRIRA KWA YEHOVA

15-16. N’chiyani chingatithandize kuti tizipirira ngati Yehova? Perekani chitsanzo.

15 Taganizirani mavuto omwe Atate wathu wakumwamba wakhala akupirira kwa zaka zambiri. (Onani bokosi lakuti “ Zimene Yehova Akupirira.”) Yehova akanatha kuthetsa dziko loipali nthawi ina iliyonse. Koma zimene wachita pokhala woleza mtima zathandiza kwambiri tonsefe. Taganizirani chitsanzo ichi. Tiyerekezere kuti mwamuna ndi mkazi wake auzidwa kuti mwana wawo yemwe sanabadwe ali ndi vuto lalikulu ndipo azidzavutika akadzabadwa komanso adzamwalira ali wamng’ono. Makolowo akusangalalabe ndi kubadwa kwa mwanayo ngakhale kuti akudziwa kuti adzakumana ndi mavuto aakulu pomusamalira. Chifukwa choti amamukonda, iwo akupirira mavuto alionse amene akukumana nawo n’cholinga choti amusamalire mmene angathere.

16 Mofanana ndi zimenezi, ana onse a Adamu ndi Hava amabadwa ali ochimwa. Komabe Yehova amawakonda ndipo amawasamalira. (1 Yoh. 4:19) Ndipo mosiyana ndi makolo a m’chitsanzochi, Yehova akhoza kuchitapo kanthu. Iye wakonza nthawi imene adzathetse mavuto onse amene anthu akukumana nawo. (Mat. 24:36) Kodi zimenezi siziyenera kutichititsa kupirira naye limodzi mpaka nthawi imeneyo?

17. Kodi zimene lemba la Aheberi 12:2, 3, limafotokoza ponena za Yesu zingatilimbikitse bwanji kuti tizipirira?

17 Yehova ndi chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani ya kupirira. Yesu anatengera chitsanzo cha Atate wake chifukwa ali padzikoli anapirira kunyozedwa, zinthu zochititsa manyazi komanso kuzunzidwa pamtengo wozunzikirapo chifukwa cha ife. (Werengani Aheberi 12:2, 3.) N’zosakayikitsa kuti chitsanzo cha Yehova cha kupirira chinamuthandiza kwambiri Yesu, ndipo ifenso chingatithandize.

18. Kodi lemba la 2 Petulo 3:9, likutithandiza bwanji kuona ubwino wa kuleza mtima kwa Yehova?

18 Werengani 2 Petulo 3:9. Yehova akudziwa nthawi yabwino imene adzawononge dziko loipali. Kuleza mtima kwake kwathandiza kuti anthu mamiliyoni ambiri omwe ndi akhamu lalikulu asonkhanitsidwe ndipo amamulambira komanso kumutamanda. Anthu onsewa amasangalala kuti iye analeza mtima kwa nthawi yaitali kuti iwo abadwe, aphunzire kumukonda komanso adzipereke kwa iye. Yehova akadzapereka mphoto kwa anthu omwe adzapirire mpaka pamapeto, zidzasonyeza kuti iye anachita bwino kusankha kuti aleze mtima.

19. Kodi tiyenera kutsimikiza mtima kuchita chiyani, nanga tidzalandira mphoto yotani?

19 Timaphunzira kwa Yehova zimene tingachite kuti tizipirira mosangalala. Ngakhale kuti Satana akuchititsa mavuto ambiri padzikoli, Yehova akupitirizabe kukhala “Mulungu wachimwemwe.” (1 Tim. 1:11) Nafenso tikhoza kumasangalala pamene tikuyembekezera moleza mtima kuti Yehova ayeretse dzina lake, asonyeze kuti ndi woyenera kulamulira komanso athetse zoipa ndi mavuto onse amene anthu akukumana nawo. Choncho tiyeni titsimikize mtima kuti tizipirira komanso kulimbikitsidwa podziwa kuti Atate wathu wakumwamba nawonso akupirira. Tikatero mawu awa adzakwaniritsidwa kwa aliyense wa ife: “Wodala ndi munthu wopirira mayesero, chifukwa akadzavomerezedwa, adzalandira mphoto ya moyo, umene Yehova analonjeza onse omukonda.”​—Yak. 1:12.

NYIMBO NA. 139 Yerekezerani Kuti Muli M’dziko Latsopano

^ ndime 5 Tonsefe timakumana ndi mavuto. Padakali pano palibe njira yothetsera mavutowa, moti timangofunika kuwapirira. Koma si ife tokha amene tifunika kupirira. Nayenso Yehova akupirira zinthu zambiri. Munkhaniyi tikambirana zinthu zokwana 9 zimene akupirira. Tionanso zinthu zabwino zimene zakhala zikuchitika chifukwa chakuti Yehova wakhala akupirira komanso mmene chitsanzo chake chingatithandizire.